Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 8/8 tsamba 11-13
  • Kodi Mungayembekezere Kudzakhala Kosatha?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mungayembekezere Kudzakhala Kosatha?
  • Galamukani!—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuyankha “Funso Lofunika Kwambiri”
  • Chimene Chinayambitsa Imfa
  • Chilango Ndiponso Lonjezo
  • Mmene Mungatalikitsire Moyo Wanu—Kosatha
  • Mmene Mungakhalire ndi Moyo Kosatha
    Galamukani!—1995
  • Kodi Moyo Wosatha Ndi Wothekadi?
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Kodi Mungapewe Kukalamba?
    Galamukani!—2006
  • Nchifukwa Ninji Timakalamba ndi Kufa?
    Galamukani!—1995
Onani Zambiri
Galamukani!—1999
g99 8/8 tsamba 11-13

Kodi Mungayembekezere Kudzakhala Kosatha?

“PALI chinachake chimene chimachitika m’thupi la munthu chimene chingachititse kuti athe kukhala ndi moyo kwa zaka zokwanira 115 kapena mpaka 120,” anatero Dr. James R. Smith, amene ali polofesa wa sayansi ya maselo a zamoyo. “Pali mlingo winawake wa zaka za munthu—kungoti sitikudziŵa kuti chimauchititsa ndi chiyani.” Katswiri wa sayansi ya zamoyo Dr. Roger Gosden ananena kuti n’chifukwa chake zili zosadabwitsa kuti “asayansi sanapezebe njira yotalikitsira moyo wa munthu, ndipo ndi ochepa chabe mwa iwo amene amaiganizira n’komwe.” Kodi zinthu zatsala pang’ono kusintha?

Kuyankha “Funso Lofunika Kwambiri”

Ngakhale kuti pali njira zambirimbiri zoganiziridwa kuti zingathetse ukalamba, akatswiri ambiri amagwirizana ndi maganizo a Dr. Gene D. Cohen, amene ali pulezidenti wa bungwe loona za anthu okalamba lotchedwa Gerontological Society of America, akuti “njira zodabwitsa zonsezi zimene amati zingathetse ukalamba zaonedwa kuti n’zosatheka.” N’chifukwa chiyani zili zosatheka? Chifukwa chimodzi, n’chimene anatchula wolemba za sayansi wina wotchedwa Nancy Shute, mu U.S.News & World Report, kuti: “Mpaka pano palibe aliyense amene akudziŵa chimene chimachititsa ukalamba komanso chotsatirapo chake chimene sichingapeŵedwe, chotchedwa imfa. Ndipo kuyesa kupeza mankhwala a matenda amene sukudziwa chimene chimawachititsa n’kosapindulitsa ngakhale patakhala chilichonse chofunika kuti kutheke.” Dr. Gosden nayenso ananena kuti ukalamba ndi wovutabe kuulongosola: “Tonsefe umatichitikira koma zimene zimauchititsa mpaka pano sizikudziŵika.” Iye ananenanso kuti, “funso lofunika kwambiri lakuti n’chifukwa chiyani umachitika” limanyalanyazidwa nthaŵi zambiri.a

Mwachionekere monga mmene palili malire a liŵiro limene anthu angathe kuthamanga, malire a utali wa pamene munthu angathe kudumpha, ndi malire a kuya kumene angathe kuloŵa posambira, palinso malire a kuganiza ndi a nzeru. Ndipo kuyankha funso “lofunika kwambiri limeneli—lakuti n’chifukwa chiyani timakalamba”—n’koonekeratu kuti n’kopitirira malire amenewo. Choncho, njira yokhayo yopezera yankho ndiyo kupita ku gwero limene lili lopitirira malire a chidziŵitso cha anthu pachokha. Zimenezo ndi zimene buku lina lakale lokhala ndi nzeru, lotchedwa Baibulo, limanena kuti muchite. Ponena za Mlengi amene ali “chitsime cha moyo” Baibulo limatitsimikizira kuti: “mukam’funa Iye, mudzam’peza.” (Salmo 36:9; 2 Mbiri 15:2) Kodi nanga, kufufuza m’Mawu a Mulungu, Baibulo, kumavumbula chiyani pa nkhani imeneyi ya chifukwa chimene munthu amafa?

Chimene Chinayambitsa Imfa

Baibulo limanena kuti pamene Mulungu analenga anthu oyamba, anaika “lingaliro la umuyaya m’mitima mwawo.” (Mlaliki 3:11, Beck) Komabe, Mlengi sanapatse makolo oyambirira a anthuwa, kokha chikhumbo chokhala kosatha; anawapatsanso mwayi woti akhaledi kosatha. Iwo analengedwa ndi thupi komanso maganizo angwiro, ndipo anali kusangalala pokhala mumtendere. Mlengi anafuna kuti anthu oyambirira ameneŵa akhale kosatha ndi kuti pakupita kwa nthaŵi dziko lapansi lidzadzaze ndi mbadwa zawo zangwiro.— Genesis 1:28; 2:15.

Komabe, moyo wosatha umenewu sunangoperekedwa. Unadalira pa kumvera Mulungu. Ngati Adamu samvera Mulungu “adzafa ndithu.” (Genesis 2:16, 17) Tsoka ilo, anthu oyambirira ameneŵa sanamvere Mulungu. (Genesis 3:1-6) Potero anasanduka ochimwa, chifukwa “tchimo ndilo kusayeruzika.” (1 Yohane 3:4) Zotsatirapo zake zinali zakuti, analibenso mwayi wa moyo wosatha, “pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa.” (Aroma 6:23) Choncho, mmene anali kupereka chilango kwa anthu oyambawo, Mulungu anati: “Ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.”—Genesis 3:19.

Chotero, anthu oyambawo atachimwa, zotsatirapo za kuchimwa zimene zinali zitanenedwa kalezo anazitenga m’magazi mwawo, ndipo mapeto a moyo anakhazikitsidwa. Monga chotsatirapo chake, anayamba kukalamba, ndipo imfa pambuyo pake. Kuphatikizanso apo, atachotsedwa m’mudzi wawo woyamba wa Paradaiso, wotchedwa Edene, anthu oyambawa anakumananso ndi chinthu china chimene chinakhudza moyo wawo moipa—moyo wovuta umene unali kunja kwa Edene. (Genesis 3:16-19, 23, 24) Kuphatikiza kulephera kwa pachiyambi kumeneku pamwamba pa mikhalidwe yovuta, kunakhudza anthu oyamba ameneŵa komanso mbadwa zawo zam’tsogolo.

Chilango Ndiponso Lonjezo

Chifukwa chakuti kusintha koipa kwa moyo wawo kumeneku kunachitika anthu oyamba ameneŵa asanabereke ana, ana amene anabereka nawonso anayenera kukhala ngati iwowo—opanda ungwiro, ochimwa, ndiponso oti adzakalamba. Baibulo limati: “Imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.” (Aroma 5:12; yerekezerani ndi Salmo 51:5.) Buku lotchedwa The Body Machine—Your Health in Perspective linanena kuti “Timayenda titanyamula makalata otiloleza kufa m’maselo athu.”

Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti palibe chiyembekezo cha moyo wopanda malire—moyo wopanda kukalamba ndi imfa. Choyamba n’chakuti, ndi kwanzeru kukhulupirira kuti Mlengi wanzeru zonse amene analenga moyo wa munthu ndi miyoyo ina yosiyanasiyana imene ili yozizwitsa, angathe kuchiritsa vuto lililonse lachibadwa ndi kupereka mphamvu zimene zili zofunika kuti moyo wa munthu uzikhala kosatha. Ndipo chachiŵiri n’chakuti, zimenezi ndi zimene Mlengi walonjeza kuti achita. Atapereka chilango cha imfa kwa anthu oyamba aja, Mulungu anavumbula kwa nthaŵi zingapo kuti chifuno chake chakuti anthu akhale kosatha padziko lapansi sichinasinthe. Mwachitsanzo, iye akutitsimikizira kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:29) Kodi muyenera kuchitanji kuti lonjezo limeneli lidzakwaniritsidwe pa inunso.

Mmene Mungatalikitsire Moyo Wanu—Kosatha

N’zochititsa chidwi, kuti wolemba za sayansi wina, Ronald Kotulak atatha kufunsa anthu ofufuza zachipatala okwanira 300, ananena mawu akuti: “Kwa nthaŵi yaitali asayansi akhala akudziŵa kuti ndalama, ntchito, ndi maphunziro zili zinthu zofunika kwambiri zomwe zimachititsa anthu kukhala athanzi komanso kukhala ndi moyo wautali . . . Koma makamaka maphunziro ndi amene akuoneka kuti amapangitsa anthu kukhala ndi moyo wautali.” Iye analongosola motere: “Monga mmene chakudya chimene timadya chimapatsa thupi lathu mphamvu zomenyana ndi tizilombo toopsa kumoyo wathu, maphunziro nawo amatiteteza kuti tisasankhe zinthu zoipa.” Monga mmene wofufuza wina ananenera, “chifukwa cha maphunziro, munthu angathe kuliyenda dziko” ndi kugonjetsa “zonse zimene zingam’tsekereze.” Motero, monga mmene Kotulak ananenera, m’njira inayake, maphunziro ali “chinsinsi cha moyo wathanzi, ndi wautali.”

Chinthu choyamba kuchita kuti mukhale ndi moyo wosatha m’tsogolo ndicho kuphunzira—kuphunzira Baibulo. Yesu Kristu ananena kuti: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.” (Yohane 17:3) Kutengera mumtima chidziŵitso cha Yehova Mulungu, amene ali Mlengi, cha Yesu Kristu, ndi cha makonzedwe a dipo amene Mulungu wapereka, ndiwo maphunziro okha amene angam’konzekeretse munthu kuyamba kuyenda pamsewu wopita kumoyo wosatha.—Mateyu 20:28; Yohane 3:16.

Mboni za Yehova zili ndi makonzedwe a maphunziro a Baibulo amene angakuthandizeni kupeza chidziŵitso cha m’Baibulo chopatsa moyo chimenechi. Pitani ku Nyumba ya Ufumu yawo kuti mudziŵe zambiri zokhudza maphunziro aulere ameneŵa, kapena apempheni kuti akupezeni panthaŵi ina yabwino. Mudzaona kuti Baibulo lili ndi umboni wamphamvu wakuti nthaŵi yayandikira yakuti moyo usakhalenso ndi mikwingwirima kapena malire. N’zoona, imfa yalamulira kwa zaka zikwi zambiri, koma posachedwapa idzagonjetsedwa kosatha. Chimenechi ndi chiyembekezo chosangalatsa kwambiridi kwa anthu okalamba ndi achinyamata omwe!

[Mawu a M’munsi]

a Akatswiri a zamaphunziro a ukalamba aganizira njira zosiyanasiyana (zitaŵerengedwa nthaŵi ina, zinalipo zopitirira 300!) zimene zimalongosola mmene mwina ukalamba umachitikira. Komabe, njira zimenezi sizilongosola chifukwa chimene umachitikira.

[Zithunzi patsamba 13]

Chinthu choyamba chimene muyenera kuchita kuti mukhale ndi moyo wosatha ndicho kuphunzira Baibulo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena