Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 9/8 tsamba 16-17
  • Njira ya ku Afirika Yopangira Chiponde

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Njira ya ku Afirika Yopangira Chiponde
  • Galamukani!—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Malimidwe a Mtedza
  • Mtedza Kuusandutsa Chiponde
  • Masamba a Chinangwa—Chakudya Chatsiku ndi Tsiku cha Mamiliyoni Ambiri
    Galamukani!—1996
  • Kufufuza Choonadi
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2020
  • Msika wa ku Africa
    Galamukani!—2010
  • Kudzipangira Ntchito m’Maiko Osatukuka
    Galamukani!—1994
Onani Zambiri
Galamukani!—1999
g99 9/8 tsamba 16-17

Njira ya ku Afirika Yopangira Chiponde

YOSIMBIDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU CENTRAL AFRICAN REPUBLIC

KUMAYIKO a Kummaŵa chiponde chimaonedwa ngati chakudya chongopaka pa buledi basi. Komabe, m’mayiko ena a mu Afirika, chimagwiritsidwa ntchito yofunika kwambiri pamoyo wa tsiku ndi tsiku. Motani?

M’madera a pakati pa Afirika m’zakudya zambiri amaikamo chiponde. Kumeneko, monga mmene kulilinso kumadera ena ongotukuka kumene, ufa wokometsera ndiwo wopangidwa kuchokera ku zakudya zina komanso ku chimanga, umene umagwiritsidwa ntchito pophika nyama komanso kulimbitsira msuzi, umavuta kupeza. M’malo mwake amagwiritsa ntchito chiponde.

Komabe, sikuti amangopita kusitolo n’kukagula botolo la chiponde. Kumeneko chimakhala choyeza m’sipuni ndipo n’chokwera mtengo kwabasi. Choncho amayi ambiri a mu Afirika amaona kuti ndibwino kungopanga okha. Mmene ntchito yovuta imeneyi amaichitira, ndi zochititsa chidwi kwabasi. Poyankhula ndi amayi angapo a mu Afirika panapezeka chidziŵitso chotsatirachi.

Malimidwe a Mtedza

N’zodziŵika kuti mbewu ya mtedza siyovuta kuisamalira. Mbali yovuta kwambiri ndiyo kulima munda wake. Amachita zimenezi pamayambiriro a nyengo ya mvula pamene nthaka idakali youma ndiponso yolimba. Mu April amadzala ndi manja, ndipo mvula ikabwera msanga mtedzawo ungathe kukumbidwa kumapeto kwa August kapena kumayambiriro kwa September.

M’madera a pakati pa Afirika minda yambiri ya mtedza kukula kwake m’litali ndi pafupifupi mamita 90 ndipo m’lifupi ndi pafupifupi mamita 50. Anthu ena amaudzala pakamunda kapafupi ndi nyumba yawo. Khasu la mpini waufupi komanso chikwanje zimagwiritsidwa ntchito kwambiri polima mundawo. Ntchito yake ingakhale yowawa kwabasi! Mbewuyi imafunika kumaiyang’anira kwabasi, makamaka pachiyambi. Munda wake uyenera kuyang’aniridwa kuti mbeŵa zisafukule ndi kudya mtedzawo. Ndiponso mundawo uyenera kutipuliridwa bwino ndi kuzuliridwa kuti uzikhala woyera.

Mundawo umafunika kuuyang’anira bwino makamaka nthaŵi yokumba. Ana amadikirira mtedzawo nthaŵi yokumba ikayandikira. Mayi wina ananena kuti mnansi wake anapeza masangwe a mtedza wake ali lendelende m’mitengo. Anyani ndiwo anatenga mtedzawo ndipo anaudya n’kukhuta, nasiya mayiyo padzuŵa!

Nthaŵi zambiri ntchito yokumba imakhala ya banja lonse. Aliyense amapita kumunda kukathandiza. Mtedzawo umazulidwa ndi manja ndipo umayanikidwa. Kenaka amauthothola ndi kuupititsa kumudzi m’madengu, amene amasenzedwa ndi okololawo.

Kodi kenaka mtedzawo amautani? Mtedzawo amauphika atautsuka, n’kuuthira mchere. Ndipo wina anthu a pabanjapo amaudya nthaŵi yomweyo, koma wambiri amausunga kuti adzaugwiritse ntchito pophika zakudya. Amaumwaza pabwalo pafupi ndi nyumbayo ndi kuusiya kuti uume gwa. Payenera kukhala wina wake kuti aziuona kuopera kuti mbuzi zingabwere piringupiringu kudzadya.

Mtedzawo ukauma amausunga m’nkhokwe yomatidwa bwino. Zimenezi zimathandiza kuti mtedzawo ukhale wouma, ndiponso zimautetezera ku mbeŵa komanso ana amene angafune kena kake kakuti adye pamene amayi ali kumunda.

Mtedza Kuusandutsa Chiponde

Mtedzawo ayenera kuuswa kaye asanausandutse chiponde. Akatero amaukazinga, nthaŵi zambiri m’chiwaya chachikulu chimene amachiika pamoto wankhuni wochepa ndithu umene amasonkha pansi. Zimenezi zimauchititsa kuti ununkhire bwino ndipo kutinso ukhale wosavuta kufulufuta. Kenaka mtedzawo amauphula kuti uzizire, ndipo amaufulufuta. Ndiye pambuyo pake amausinja n’kuusandutsa chiponde. Ngati palibe mtondo, mayi wapanyumbapo amauthira pamphero ndi kuupera ndi botolo kapena nkhulungo.

Posachedwa chipondechi ndiye kuti chithiridwa m’ndiwo. Ndiwo zimene zimatenderedwazo amadyera chinangwa, nthochi, kapena mpunga. Ngati mukufuna kudziŵa mmene chakudya chotenderedwa ndi chiponde chimakomera, bwanji osangophika chanu?

Mungathe kutsatira njira yodziŵika bwino ndipo n’kuphika nyama, yothira anyezi, adyo, ndi matimati. Ziphikeni pamodzi mpaka nyamayo itapsa, ndipo ngati mukufuna mungaphatikizeko sipinachi wochekedwa. Izi zikutokota, sungunulani chiponde ndi madzi ochepa kuti chisanduke phalaphala—tingoti kapu imodzi pa kilogalamu imodzi iliyonse ya nyama—ndipo muthire m’nyamayo ndi kutakasa. Muzisiye zitokote mutaika moto wamphamvu kwa mphindi khumi kapena kuposa apo kuti chipondecho chisamveke fungo kwambiri. Ngati msuzi uli wamadzimadzi mungathe kuwonjezamo chiponde china mmene mungakondere. Tsirani mchere wokukwanani. Ngati m’makonda zinthu zowawa mungathe kuthiramo tsabola.

Anthu ambiri amaona kuti ndiwo zoterezi kuziika kumpunga, sikukoma kwake! Ndiye ngakhale kuti mwina chakudya chimene muphikecho sichichita kukhala chokoma kwambiri, komabe mutha kugwiritsako ntchito nokha chiponde—ngati mu Afirika!

[Zithunzi patsamba 16]

Mtedza umakumbidwa ndipo kenaka amaupititsa kunyumba kuti akauswe ndi kuusinja

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena