Masamba a Chinangwa—Chakudya Chatsiku ndi Tsiku cha Mamiliyoni Ambiri
YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU CENTRAL AFRICAN REPUBLIC
ZINAYAMBA m’chaka cha 1600, pamene Apwitikizi anabweretsa chinangwa, kapena manioc, ku Afirika kuchokera ku South America. Pali chikhulupiriro chakuti chinangwa ndi cha ku Brazil chifukwa chakuti liwulo “manioc” linachokera ku mitundu yachitupia ya ku Brazil ku Amazon Valley.
Mitsitsi yake imaŵerengeredwa kwambiri ndi anthu a mu Afirika, komano bwanji nanga za masamba ake obiriŵira kwambiriwo? Ena amawagwiritsira ntchito monga mankhwala pa zilonda kapena kuchiritsira nthonyola. Komabe, kwa mamiliyoni ambiri mu Central African Republic ndi maiko ena angapo a mu Afirika, masambawo ndiwo chakudya chatsiku ndi tsiku, popeza kuti akhoza kukonzedwa kukhala chakudya chokoma. Kwenikweni, limodzi la mawu oyamba limene amishonale a Watch Tower kunoko amaphunzira ndilo ngunza. Chimenechi ndicho chakudya chokoma chopangidwa ndi masamba a chinangwa ndipo ndicho chakudya cha dziko lino la Central African Republic—chakudya chimene mlendo ku chigawo cha pakati pa Afirika ayenera kuchilaŵa ndithu.
Azungu ochuluka okhala mu Afirika samadya konse chakudya cha masamba ameneŵa, popeza kuti amachiona kukhala chakudya cha nzika zakuno, osati cha alendo. Komano kodi zenizeni nzotani? M’maiko onga ngati Central African Republic, Sierra Leone, ndi Zaire, masamba ameneŵa ndiwo chakudya chachikulu chatsiku ndi tsiku m’mabanja ambiri.
Pamene mukuuluka ndi ndege kapena kupyola mu Central African Republic, mungathe kuona dziko lokongola lobiriŵira—mitengo, tchire, madambo, ndipo, pakati pake, minda yaing’ono ya chinangwa cha masamba ake obiriŵira kwambiri. Mudzi uliwonse waung’ono ngokwetezedwa ndi minda ya chinangwa. Anthu amachibzala pafupi ndi nyumba zawo, ndipo ngakhale m’likulu mmene, Bangui, mutha kupeza chinangwa patiminda ndi m’mikwamba pafupi ndi nyumba ya mpondamatiki kapena pafupi ndi msewu waukulu. Ndithudi, icho nchakudya chofunika kumbali ino ya dziko.
Laŵani Pang’ono Ngunza
Atafika, posapita nthaŵi amishonale atsopano amaitanidwa ndi mabwenzi kukalaŵa ngunza. Chimenechi nchakudya chimene chimaphatikizapo chakudya china chotchuka chokonzedwa ndi masamba a chinangwa. Akazi akuno amadziŵa mmene angachiphikire kukhala chokoma. Zichita ngati kuti mkazi aliyense ali ndi njira yake yophikira. Chimodzi cha zinthu zoyamba chimene atsikana amaphunzira kwa amawo ponena za kuphika ndicho mmene angaphikire ngunza.
Amanyadira poifotokoza ndi posonyeza mmene amaiphikira. Akazi amakondwa ngati musonyeza chidwi ndi chakudya chakuno chimenechi. Choyamba, amakuuzani kuti masamba a chinangwawo ngosakwera mtengo ndipo ngambiri ndi kuti mungawathyole m’nyengo yamvula ndi yachilimwe yomwe. Pamene ndalama zasoŵa ndi pamene zinthu zakwera mtengo, masamba a chinangwa amathandiza kwambiri kudyetsa mabanja. Ndipo chonde kumbukirani kuti mabanja a mu Afirika kaŵirikaŵiri ngaakulu. Pamakhala anthu ambiri ofunikira kudyetsedwa. Kuphika ngunza kumatenga maola angapo. Masambawo amafunikira kuti kuŵaŵa kwake kuthe asanadyedwe. Amaluluzidwa mwa mwambo wake, umene umaphatikizapo kuponda mu mtondo ndi kuŵiritsa kwanthaŵi yaitali.
Mafuta amene akazi a mu Afirika amakonda kugwiritsira ntchito pophika ngunza ndiwo mafuta a mngole. Mafuta opangidwa mommunowo ofiira ngofunika kwambiri. Ngunza imeneyo ndi chiponde pang’ono ndipo mwina anyenzi ndi adyo pang’ono zimakhala chakudya chatsiku ndi tsiku cha banja. Komano bwanji ngati mukuyembekezera kulandira alendo? Ndiye kuti ngunza iyenera kukhala yapadera, kanthu kena kamene sadzaiŵala. Chotero wochereza mlendo angawonjezere zokometsera zimene amakonda—nsomba yoŵamba kapena nthuli za nyama yoŵamba—kuphatikizapo adyo ndi anyenzi wambiri limodzi ndi chiponde chatsopano chambiri, chopangidwa panyumba. Zonsezi amaziika mumphika umodzi waukulu. Chotsalira ndicho kuyembekezera moleza mtima ndi kuziŵiritsa kwambiri.
Lero otichereza adzatipatsa ngunza ndi mpunga. Mbale yodzala ndi mpunga yothiridwa supuni imodzi kapena ziŵiri za ngunza yotentha ili chakudya chokondedwa kwa a Aafirika ndiponso ndi alendo ambiri. Wonjezerani mphiripiri pang’ono, ndipo tsopano mukudziŵa chimene chili ngunza. Pamodzi ndi chakudyacho, tambula ya vinyo wofiira idzachititsa kukoma kwa chakudyacho.
Bwanji Nanga za Kulaŵa Pang’ono Ngukassa Kapena Kanda?
Poyenda kuchokera kummaŵa kumka kumadzulo kwa dzikoli, mudzapeza kuti anthu amaphika ngunza m’njira zosiyanasiyana. Ndipo bwanji nanga za ngukassa? Patsiku lozizira la mvula, ngukassa, msuzi wophikidwa ndi zosiyanasiyana zotengedwa kudimba kapena kumunda, ungakhale chinthu choyenera kwa inu. Mafuta a mngole, nthochi, mtedza, mbatata, chimanga, ndiponso, masamba pang’ono a chinangwa amaziphika pamodzi, koma samaikamo mchere—ngakhale mpang’ono pomwe. Chimenecho ndicho chinsinsi chake! Chotulukapo chake ndicho chakudya chokoma ndi chomanga thupi. Ndipo ngati mukumka paulendo wautali, tengani kanda. Imeneyi imakonzedwa ndi masamba a chinangwa opondedwa mu mtondo pamodzi ndi nsomba kapena nyama yoŵamba. Kanda imakonzedwa mwa kukuta ndi masamba msanganizowu ndi kuuwotcha pamoto kwa maola angapo kufikira itauma gwagwagwa. Imakhala masiku ambiri ndipo ingadyedwe pamodzi ndi buledi. Njabwino kwambiri kwa apaulendo.
Ngati muyenda mu Afirika panthaŵi ina iliyonse bwanji osapempha chinangwa? Chilaŵeni, ndipo gwirizanani ndi mamiliyoni ambiri amene amachikonda!