Achinyamata Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndingatani ndi Kusoŵa Chilungamo?
“Achuma okha ndiwo amalemekezeka, koma ife amene tilibiretu chakudya kapena malo ogona amangotiyesa nyama. Moti ngati ndikuyembekeza kanthu m’tsogolo, ndiko imfa yosoŵa ndi wonditola yemwe.”—Arnulfo, mnyamata wa zaka 15 amene alibe kokhala.
PADZIKO lapansi pali kusoŵa chilungamo kwakukulu. Lipoti lochokera ku nthambi ya United Nations yoona za ana ya United Nations Children’s Fund (UNICEF) inati: “M’zaka khumi zapitazi, ana oposa 2 miliyoni aphedwa pankhondo, ndipo ena opitirira pa 4 miliyoni apulumuka ku nkhanza, komanso ena oposa 1 miliyoni akhala amasiye kapena atayana ndi achibale awo chifukwa cha nkhondo.” Nthaŵi zambiri njala ndi umphaŵi, zimenenso zikuvutitsa anthu ochuluka padziko lonse, zimachitika pamene kwinaku kuli olemera ndi osasoŵa kanthu. M’mayiko amene akutukuka kumene, ana ambiri ovutika ngati Arnulfo sapatsidwa mwayi woti aphunzire.
Kusoŵa chilungamo kumakhala kopweteka makamaka ngati kukuchitidwa ndi anthu amene ayenera kukukonda ndi kukuteteza. Tanganizirani za mtsikana wina wa zaka 17 dzina lake Susana. Mayi ake anam’thaŵa iye pamodzi ndi azilongo ake aang’ono aŵiri. Susana akudandaula kuti: “Papita zaka tsopano, ndipo amayi sanandiitanepo kukakhala nawo, ngakhale kuti tonse tikukhala m’tauni imodzi. Iwo sanandiuzepo ngakhale n’kamodzi komwe kuti, ‘Ndimakukonda mwana wanga,’ ndipo zimenezi zakhala zikundipweteka kwambiri mpaka pano.” Pamene mukuchitidwa nkhanza ngati zimenezi, kungakhale kovuta kuti musakwiye. Mkazi wina amene anaipitsidwa pamene anali mwana anati: “Zimenezi zandichititsa ngakhale kukhumudwa ndi Mulungu.”
Mwachibadwa anthufe timakwiya ndi kuŵaŵidwa mtima pamene wina atizunza. Baibulo limanena kuti: “Nsautso iyalutsa wanzeru.” (Mlaliki 7:7) Kukhalira kulimbana ndi kusoŵa chilungamo masiku onse m’moyo wanu kungakuchititseni kukhala wopsinjika maganizo. (Yerekezani ndi Salmo 43:2.) Choncho mungalakelake kuti kusoŵa chilungamo kumeneku kuthe. Mtsikana wina wa ku Central America ananena kuti: “Pamene ndinali ndi zaka 13 zakubadwa, ndinaloŵa kabungwe kena ka ana asukulu. Ndinali ndi cholinga choti ndithandize kusintha zinthu kuti ana asamakhale ndi njala . . . Kenako ndinamenya nawo nkhondo.” Komabe, m’malo mopeza chilungamo iye anachitidwa chipongwe chosaneneka ndi asilikali anzake.
Zochitika ngati zimenezi zimatikumbutsa kuti anthu ambiri alibe mphamvu zoti n’kuchepetsera mavuto awo. Komano, kodi amene achitiridwa mopanda chilungamo angatani?a Ndipo ndi motani mmene mungachitire ndi kuŵaŵidwa mtima ndi mkwiyo umene mungakhale nawo?
Kuchotsa Kuŵaŵidwa Mtima ndi Mkwiyo
Nthaŵi ndi nthaŵi, mungafunikire kungokumbukira kuti tikukhala ‘m’masiku otsiriza’ a dongosolo lino la zinthu. Baibulo linalosera kuti anthu masiku ano adzakhala “amwano . . . opanda chikondi, osakhululuka, osinjirira, osadziletsa, ankhanza, osakonda zabwino, onyenga.” (2 Timoteo 3:1-4, New International Version) Ambiri ali “opandiratu khalidwe.” (Aefeso 4:19, NW) Choncho, kusoŵa chilungamo ndi khalidwe losapeŵeka m’moyo. Chotero “ukaona anthu alikutsendereza aumphaŵi, ndi kuchotsa chilungamo ndi chiweruzo mwachiwawa pa dera lina la dziko, usazizwepo.”—Mlaliki 5:8.
N’chifukwa chake Baibulo limachenjeza kuti musalole kuŵaŵidwa mtima kukhazikika m’mitima yanu. Mwachitsanzo, limanena kuti: “Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo . . . zichotsedwe kwa inu.” (Aefeso 4:31) Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti kukhalabe wokwiya kwanthaŵi yaitali n’kovulaza ndiponso n’kungodzivuta chabe. (Yerekezani ndi Miyambo 14:30; Aefeso 4:26, 27.) Zimenezi zingakhale choncho makamaka ngati ‘tikwiyira Yehova.’ (Miyambo 19:3, NW) Kukwiyira Mulungu kumakuchititsani kuti mukhale wosayanjidwa ndi Iye amene angakuthandizeni kwambiri. Baibulo limanena kuti: “Maso a Yehova ayang’ana uko ndi uko m’dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wawo uli wangwiro ndi Iye.”—2 Mbiri 16:9.
Baibulo limanenanso za Yehova kuti: “Njira zake zonse ndi chiweruzo [“n’zolungama,” NW]; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; Iye ndiye wolungama ndi wolunjika.” (Deuteronomo 32:4) Kusoŵa chilungamo kunabwera chifukwa cha kupanduka kwa Adamu ndi Hava. (Mlaliki 7:29) Si Mulungu koma munthu ndiye “apweteka mnzake pom’lamulira.” (Mlaliki 8:9) Kumbukiraninso kuti “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo,” Satana Mdyerekezi. (1 Yohane 5:19) Si Yehova, koma ndi iyeyu Satana, amene akuchititsa kusoŵa chilungamo padziko lapansi.
Kutha kwa Kusoŵa Chilungamo
Chosangalatsa n’chakuti kusoŵa chilungamo sikupitirira mpaka kalekale. Kukumbukira zimenezi kungakuthandizeni kuti mugonjetse vutoli. Taganizirani zimene zinachitikira Asafu, mwamuna amene anakhalako m’nthaŵi ya Baibulo. Panthaŵiyo kusoŵa chilungamo kunali kofala m’dera limene iye ankakhala, ngakhale kuti anthu akumeneko anali kudzinenera kuti amatumikira Yehova. M’malo molangidwa chifukwa chochitira nkhanza anthu ena, anthu ankhanza ameneŵa ankaoneka kuti amakhala ndi moyo wopanda mavuto ndi wolemera! Asafu anavomereza kuti: ‘Ndinachita nsanje . . . pakuona mtendere wa oipa.’ Asafu kwanthaŵi yochepa anasokonezeka ndi kuyamba kutengeka maganizo ndi zinthu zimenezo.—Salmo 73:1-12.
Patapita nthaŵi, Asafu anachita kudzidzimuka atazindikira. Iye ananena za oipawo kuti: “Indedi muwaika poterera [Mulungu]: muwagwetsa kuti muwawononge.” (Salmo 73:16-19) Inde, Asafu anazindikira kuti m’kupita kwa nthaŵi anthu kwenikweni sapulumuka pa zoipa zawo. Kaŵirikaŵiri, tchimo lawolo limawapeza ndipo amakhaula ndi ukaidi, kusoŵa ndalama, kuchotsedwa ntchito, kapenanso kuchotsedwa pa maudindo awo. Ndipo pomaliza penipeni, oipa ‘adzagwa kuti awonongeke’ pamene Mulungu adzapereka chiweruzo pa dongosolo loipali la zinthu.—Salmo 10:15, 17, 18; 37:9-11.
Kuzindikira kuti Mulungu adzakonza zinthu m’tsogolo kungakuthandizeni kulamulira mkwiyo wanu. Baibulo limachenjeza kuti: “Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse. Ngati n’kutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse. Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye.”—Aroma 12:17-19; yerekezani ndi 1 Petro 2:23.
Kupeza Chithandizo ndi Chichirikizo
Komabe, mwina mtima wanu umazunzikabe kwambiri chifukwa chokumbukira zoipa zomwe munachitiridwa. Malinga ndi zimene lipoti la UNICEF linanena, “ana amene akhala akuchitidwa kapena kuonera ziwawa kaŵirikaŵiri amadzasintha kwambiri pa zikhulupiriro zawo ndi maganizo awo, kuphatikizapo kusiya kudalira anthu ena. Zimenezi zimakhala choncho makamaka kwa ana amene achitidwa chipongwe kapena nkhanza ndi anthu omwe kale ankayesa ngati anansi kapena mabwenzi.”
Palibe njira yachidule yothetsera mavuto otere. Koma ngati mungovutika mtima chifukwa chokhumudwa kapena kukumbukira zopweteka zimene anakuchitirani, mufunika chithandizo. (Yerekezani ndi Salmo 119:133.) Choyamba, mungaŵerenge nkhani zimene kwenikweni zimafotokoza mavuto amene muli nawo. Mwachitsanzo, magazini a Galamukani!, afalitsa nkhani zambiri zimene zimapereka malangizo othandiza kwa anthu amene anagwiriridwa, kuberedwa, ndiponso kuipitsidwa ali ana. Kufotokoza nkhaŵa ndi malingaliro anu kwa munthu wachidziŵitso ndi wokhoza kumvetsa vuto lanu kungakuthandizeni kwambiri. (Miyambo 12:25) Mwinanso mutha kufotokozera makolo anu.
Koma bwanji ngati mulibe makolo? Ngati zili choncho kafuneni chichirikizo mu mpingo wachikristu. Pakati pa Mboni za Yehova, akulu a mpingo amakhala ngati populumukira anthu amene akuvutika. (Yesaya 32:1, 2) Kuwonjezera pa kumvetsera zomwe mukuwauza, iwo adzaperekanso malangizo oti akuthandizani. Komanso, musaiŵale kuti abale ndi alongo ena achikulire angakhale ngati “abale, kapena alongo, kapena amayi” kwa inu. (Marko 10:29, 30) Kodi mukukumbukira za Susana, amene mayi ake anam’thaŵa? Iye ndi azilongo ake anapeza chichirikizo kuchokera mumpingo wachikristu. Mtumiki wachikristu wina anachita chidwi ndi banja la Susana kufikira kuti iye anatcha mbaleyo bambo wake wom’lera. Susana ananena kuti chichirikizo chotere “chatithandiza kukhala achikulire komanso kukhala olimba m’choonadi.”
Akatswiri ena amanena kuti kukhala ndi chizoloŵezi chochita zinthu zopindulitsa tsiku ndi tsiku n’kothandizanso. Kupita ku sukulu ndi kugwira ntchito zapakhomo kungakuthandizeni kwambiri kusaika maganizo anu pa zopweteka za mtima. Komabe, mudzapindula kwambiri makamaka mwa kukhala ndi chizoloŵezi cha zinthu zauzimu monga kupezeka pa misonkhano yachikristu ndi kulalikira uthenga wabwino.—Yerekezani ndi Afilipi 3:16.
Kosoŵa chilungamo sikudzatha padziko lapansi kufikira pamene Ufumu wa Mulungu udzadza ndi kuchita chifuniro chake padziko lonse lapansi. (Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10) Padakali pano, yesetsani kuchita zomwe mungathe kuti mupirire. Khutirani ndi lonjezo lakuti, Yesu Kristu monga Wolamulira wa Ufumu wa Mulungu, “adzapulumutsa waumphaŵi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe m’thandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphaŵi, nadzapulumutsa moyo wa aumphaŵi.”—Salmo 72:12, 13.
[Mawu a M’munsi]
a Ngakhale kuti nkhani ino ikukhudza kwambiri kusoŵa chilungamo kumene achinyamata angachitiridwe m’mayiko osauka, komabe, mfundo zomwe tikukambiranazi zikukhudza mtundu uliwonse wa kusoŵa chilungamo kumene munthu angakumane nako.
[Mawu Otsindika patsamba 29]
“Zimenezi zandichititsa ngakhale kukhumudwa ndi Mulungu”
[Chithunzi patsamba 30]
Chichirikizo cha Akristu anzanu chingakuthandizeni kupirira vuto la kusoŵa chilungamo