Kamzimbi—Mbalame Yokongola kwambiri
YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU COSTA RICA
COSTA RICA n’kadziko kakang’ono kosakwana n’komwe 0.03 peresenti ya nthaka ya dziko lapansi. Komabe, m’dzikoli muli mitundu ya mbalame 875 yolembedwa m’kaundula. Malinga ndi zimene buku lina linanena, chiŵerengerochi n’chachikulu kuposa chiŵerengero cha mitundu ya mbalame zonse pamodzi zopezeka ku Canada ndi ku United States. Choncho, n’zosadabwitsa kuti dziko la Costa Rica lasanduka malo otchuka zedi kwa anthu okonda kuona mbalame. Tiyeni tiyendere limodzi ulendo wathu wokaona imodzi mwa mbalame zokongola kwambiri zimenezi yotchedwa kamzimbi.
Kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1500, m’tsogoleri wa gulu la ogonjetsa wachisipaniya wotchedwa Hernán Cortés anafika ku Mexico. Kumeneko, anapatsidwa chisoti cha nthenga za kamzimbi monga mphatso kuchokera kwa anthu achi Aztec. Anthu akubanja lachifumu la Aztec okha ndi amene anali ndi mwayi wovala zinthu zokongola zapamwamba kwambiri zoterozo. Nthenga za kamzimbi zobiriŵira kwambiri zimenezo mwina zinali kuonedwa mwamtengo wapatali kuposa golidi.
Lero mbalame yokongola modabwitsa imeneyi imapezeka m’gawo lalikulu la mayiko a Mexico mpaka kufika ku Panama. Kamzimbi angapezeke m’nkhalango zamvula zimene zimapezeka kumadera okwera mamita 1,200 ndi 3,000. Mitambo imene ili m’nkhalangozo imabwera chifukwa chakuti kuli mphepo yofunda imene imakwera n’kufika m’mitambo n’kuzizira mofulumira. Chifukwa cha zimenezi, kuli zomera zobiriŵira chaka chonse ndi mitengo yaikulu komanso yaitali kwambiri kufika mamita 100 m’mwamba kapena kuposerapo oti mpaka n’kuzimilirika m’nkhungu.
Nkhalango yotetezedwa yotchedwa Santa Elena Forest Reserve, pafupifupi makilomita 200 kumpoto kwa mzinda wa San José, ndi malo abwino kwabasi kukaona kamzimbi atafatsa m’malo ake okhala achilengedwe. Moperekezedwa ndi munthu wolondolera njira alendo, tinayamba ulendo wathu wokaona mbalame yokongolayo yotchedwa kamzimbi. Chifukwa cha maonekedwe ake wobiriŵira, mbalameyi n’njovuta kuti muione pakuti imabisika m’masamba obiriŵira a mitengo ndi zomera za m’nkhalangoyo. Wotiperekezayo anayamba kuyesezera kulira kwake kodekhako. Mawu ake amamveka ngati mawu a kamwana ka galu kakamasisima. Mwakuti, pamene tinamva kulira kwa kamzimbi poyankha, mayi wina pagulu lathulo ankaganiza kuti kuthengoko kuli kagalu kosokera!
Mosakhalitsa, mwinamwake pa utali wa mamita 15, panatulukira kamzimbi wamwamuna wooneka kuti akukayikira n’kutera panthambi ina kuti adzafufuze. Titamuona pafupi pogwiritsa ntchito zipangizo zoonera zinthu patali, mitundu yake yonyezimira inaonekera bwino kwabasi koposa mmene tinkaganizira. Pamtima pake m’pofiira, mogwirizana ndi nthenga zake zobiriŵira. Chinanso chimene chimawonjezera kukongola kwake ndi nthenga zake zoyera zakuchipsepse zimene zimagwirizana ndi nthenga zake zina ziŵiri zomwe n’zobiriŵira zedi. Nthenga zimenezi amazitcha kuti mchira, ndipo n’zazitali masentimita 60. N’zosangalatsa kwabasi kuyang’ana kamzimbi atatera pamwamba pa nthambi ya mtengo uku mchira wake wautali uli kupikupi chifukwa cha mphepo.
Kuona kamzimbi ndi chinthu chosaiŵalika. Ndiponso, woperekeza alendo amene tinayenda naye ananena kuti nthaŵi zambiri kuti munthu aone kamzimbi zimam’tengera maulendo angapo akupita kunkhalango. Nthaŵi yabwino yoonera akamzimbi ndi mu March mpaka June pakuti ndi nthaŵi imene amaikira ndi kufungatira mazira. Panthaŵiyi mwina amakhala akufungatira zisa ziŵiri zokhala ndi mazira aŵiri chisa chilichonse.
Titabwerera ku ofesi ya pankhalangopo, tinamva kulira kwa kamzimbi wina. Anali kuuluka mochititsa chidwi popanda kukupiza mapiko n’kutera panthambi yamtengo umene unali pafupi ndi pamene tinakhala ife! Woperekeza alendo anatiuza kuti zikatere ndiye kuti mwana wake kapena kuti chiunda wasoŵa pa chisa. Chotero bamboyu akufunafuna mwana wakeyo mumtengo uliwonse. Tinauzidwa kuti dzira limodzi lokha mwa mazira anayi a kamzimbi ndi limene limapulumuka mpaka kukonkhomola mwanapiye. Mazira enawo amadyedwa ndi nyama zina zolusa monga, agologolo, akaligondo, akabaŵe, avumbwe, ndi nyama zina zambiri. Komanso vuto lina lokhudza miyoyo ya akamzimbi ndilo malo amene amamanga zisa zawo. Amamanga zisa m’mphako zangati za mbalame yotchedwa gogomole zimene amaboola pamtengo wakale umene ukufumbwa pa utali wa mamita atatu mpaka 20 kuchokera patsinde la mtengowo. Chotero kukagwa mvula yambiri mphakozo zingathe kudzala madzi kapena kufafanizika.
Tinadziŵanso kuti chakudya chomwe mbalamezi zimakonda ndi mapeyala akutchire. Kamzimbi amatera pa nthambi ya mtengo wina n’kumayang’ana peyala lili lendelende panthambi za mtengo umene uli chapafupi. Kenako, amauluka pamodzimodzi n’kuthyola peyalalo ndi mlomo wake, akatero amabwereranso ku chisa chake. Amameza peyala lonse lathunthu ndipo pakatha mphindi pafupifupi 20 mpaka 30 amabzikula njere yake imene ili yaikulu.
Akamzimbi pofunafuna mapeyala akutchire ameneŵa, amayenda n’kupita ku mitunda yosiyanasiyana ya ku Zidikha Zazikulu za ku America. Mwachitsanzo, kuchokera m’mwezi wa July kufika September, amakhala ali ku zidikha za ku Nyanja ya Pacific. Kenako mu October amasamukira ku dera la Caribbean kukadya mapeyala amene panthaŵiyi amakhala atangocha kumene.
Pamene tinkawoloka mlatho wina wokongola kwambiri umene uli pamwamba papatali pafupifupi mamita 30 kuchokera pansi pa nkhalangoyo, kamzimbi wina anatsala pang’ono kutitera pamutu! Zinkaoneka kuti mbalameyi inali kufunafuna chakudya chamasana pamene ife tinaisokoneza. Kamzimbi wamkazi anali atangokhala pamwamba poteropo n’kumatiyang’ana mozonda chifukwa chom’sokoneza.
Tinauzidwanso kuti zipatso zina zimene kamzimbi amakonda kudya ndi malubeni kapena kuti mabulosi akutchire amene amamera m’nkhalango zaminga. Pamene akamzimbi auluka kuti akathyole chipatsocho, nthenga zawo zazitalizo nthaŵi zina zimakodwa m’minga ndipo zimasosoka. Komabe, mkupita kwanthaŵi, nthengazo zimaphukanso.
Motero mbalameyi imayenereranadi ndi dzina lake. M’chingelezi dzina lakuti “quetzal” lotanthauza kuti kamzimbi linachokera ku mawu achinenero cha a Aztec akuti “quetzalli,” kutanthauza kuti “chamtengo wapatali” kapena kuti “chokongola.” Tsoka ilo, kukongola kwakeko kumamuika kamzimbiyo pangozi. Ndiponso, kamzimbi ali pa mndandanda wa mitundu ya mbalame zimene zili pangozi kwambiri. Mbalamezi zakhala zikusakidwa chifukwa chofuna kupezako nthenga zimene zagulitsidwa monga chikumbukiro. Zina mwa mbalamezi zimagwidwa zamoyo ndi kuzigulitsa kuti akaziŵete. Komabe, malinga ndi zimene wotiperekeza wathu ananena, kamzimbi tsopano akutetezedwa mwalamulo ku anthu osaka mowononga ameneŵa.
Komabe vuto linanso limene likuopseza miyoyo ya akamzimbi ndi kudula mitengo kumene kukuchititsa kuti malo okhala akamzimbi azitha. Choncho pofuna kuteteza mbalame zokongolazi ndiponso zamoyo zina zakuthengo, madera okwana pafupifupi 27 peresenti ya Costa Rica, aikidwa padera monga otetezedwa.
Ulendo wathu wokaona kamzimbi wakhaladi wosangalatsa kwabasi. Ndithudi, kunyumba yoonetsera zinthu zamakedzana yotchedwa British Museum ku London mungathe kukaonako chisoti cha nthenga za kamzimbi chimene anapatsa Hernán Cortés. Komatu nthenga za kamzimbi zimakongola kwambiri pamene mukuziona zili ku mbalame yamoyo kuthengo! Padakali pano, akamzimbi akupitirizabe kukhala mwaufulu ndiponso motetezeka m’nkhalango zamvula za ku Central America.