Kodi Dziko Lathu Lapansili Likudwala Kwambiri Motani?
YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU PHILIPPINES
Dziko lapansili lili ngati munthu amene akudwala kwambiri. Zizindikiro za matenda a munthuyu n’zambiri. Mpweya wake ndi wonunkha. Thupi lake latentha kwambiri, kutentha koti silinatentheponso ngati mmene latentheramo. Akuyesera kuti aliziziritseko koma zikulephereka. M’zinthu zonse zamadzimadzi za m’thupi mwake apezamo poizoni. Akachiza zizindikiro zina za matendaŵa ku mbali imodzi ya thupi lake, zizindikiro zina zikumayamba ku mbali ina. Wodwala ameneyu akanakhala wodwala wamba, madokotala akananena kuti matenda osiyanasiyana amene akudwalawo ndi okhalitsa ndipo ndi oti amwalira nawo. Posoŵa choti achite, madokotalawo akanangopanga zotheka kuti wodwalayo asavutike kwambiri podikira imfa.
KOMABE, wodwala ameneyu si munthu. M’malo mwake ndi malo athu amene tikukhala, dziko lapansili. Zomwe tafotokoza pamwambazi zikusonyeza bwino zimene zikuchitikira dziko lathu lapansili. Mpweya wowonongeka, kutentha kwa dziko lapansi, madzi owonongeka, komanso zinthu zotha ntchito zapoizoni, ndizo matenda ena ochepa chabe amene dziko lathu lapansili likudwala kwambiri. Mofanana ndi madokotala tinawatchula pamwamba aja, akatswiri sakudziŵa chochita ndi matenda ameneŵa.
Atolankhani nthaŵi zambiri amatiuza za kudwala kwa dziko lapansi polemba mitu ya nkhani ndi mawu ofotokozera zithunzi ngati aŵa: “Kusodza komaphulitsa pansi pa nyanja kukupha zamoyo zambiri za m’nyanja.” “Anthu Okwana Wani Biliyoni a ku Asia Angadzasoŵe Madzi Abwino Zaka 24 Zikubwerazi.” “Zinthu zotha ntchito zapoizoni zokwana matani 40 miliyoni padziko lonse zimatayidwa ku mayiko ena chaka chilichonse.” “M’zitsime 1,800 za ku Japan, pafupifupi m’zitsime ziŵiri mwa zitatu zilizonse muli poizoni.” “Bowo la Mumpweya wa Ozone Pamwamba pa Nyanja ya Antarctic Layambanso Kudetsa Nkhaŵa Ndipo Likukulirakulira.”
Anthu ena amazoloŵera kumva pafupipafupi nkhani zonena za kuwonongeka kwa chilengedwe, ndipo mwina amaganiza kuti, ‘Zimenezo si zodetsa nkhaŵa kwambiri, malinga ngati ineyo sizikundikhudza.’ Komabe, kaya tikudziŵa kapena ayi, kuwonongeka kwa mbali zonse za chilengedwe padziko lapansi kukukhudza anthu ambiri. Chifukwa chakuti panopa kuwonongeka kwa dziko lapansili kwakhudza malo ambiri, mwachionekere kwakhudza kale mbali zosiyanasiyana za moyo wathu. Choncho, anthu onse ayenera kudera nkhaŵa za mmene dziko lathuli lilili, ndi mmene tingalitetezere. Tikapanda kutero, kodi tikakhala kuti?
Koma kodi vutoli n’lalikulu bwanji? Kodi dziko lapansili likudwala kwambiri motani? Kodi miyoyo ya anthu ikukhudzidwa motani? Tiyeni tione mfundo zingapo zimene zikutithandiza kumvetsa kuti dziko lathuli sikuti likungodwala pang’ono ayi, koma likudwala mwakayakaya.
◼ NYANJA: M’madera ambiri a m’nyanja anthu amapha nsomba mopitirira muyeso. Lipoti la bungwe loyang’anira zachilengedwe la United Nations Environment Programme linati “70 peresenti ya malo a m’nyanja amene anthu amaphamo nsomba akuphamo mopambanitsa, moti nsomba zikamaswana sizikubwerera mwakale, kapena mwina zikungobwezeretsa chabe nsomba zimene zaphedwazo koma sizikuchulukananso.” Mwachitsanzo, chiŵerengero cha nsomba za mtundu wa cod, hake, haddock, ndi flounder kumpoto kwa nyanja ya Atlantic chinachepa ndi 95 peresenti pakati pa zaka za 1989 ndi 1994. Kodi zimenezi zikapitirira, anthu mamiliyoni ambiri amene amadalira chakudya chochokera m’nyanja zinthu zidzawathera bwanji?
Kuwonjezera apo, chaka chilichonse zamoyo za m’nyanja zokwana pafupifupi matani 20 miliyoni mpaka 40 miliyoni zimagwidwa kenaka n’kuponyedwanso m’nyanja, nthaŵi zambiri zitavulala kapena kufa. Chifukwa chiyani? Amazigwira pamodzi ndi nsomba zimene akuzifuna koma zimene amazibwezeranso m’nyanjazi zimakhala zoti sakuzifuna.
◼ NKHALANGO: Kudula mitengo mwachisawawa kumawononga zambiri. Kutha kwa mitengo kumachititsa kuti dziko lapansi lizilephera kugwiritsa ntchito bwino mpweya wa carbon dioxide, ndipo zimenezi akuti zikuchititsa kuti dziko lapansi lizitentha. Mitundu ina ya zomera, imene angapangire mankhwala opulumutsa miyoyo, idzatha. Komabe, kuwononga nkhalango kukungopitirirabe, popanda kubwerera m’mbuyo. Ndipo kuwononga nkhalangoku kwawonjezeka m’zaka zaposachedwapa. Akatswiri ena akuganiza kuti zimenezi zikapitirira, nkhalango za m’madera otentha zikhoza kutha m’zaka 20 zikubwerazi.
◼ ZINTHU ZOTHA NTCHITO ZAPOIZONI: Kutaya zinthu zoopsa pa mtunda ndi m’nyanja ndi vuto lalikulu limene lingavulaze anthu ambiri. Zinthu zotha ntchito zapoizoni, miyala yapansi panthaka imene ingayambitse matenda, ndiponso zimene amataya akamapanga zinthu za pulasitiki, ndizo zina mwa zinthu zimene zimatha kupundula, kudwalitsa, ngakhale kupha anthu ndi nyama zomwe.
◼ MANKHWALA: M’zaka 100 zapitazi, mankhwala atsopano okwana pafupifupi 100,000 ayamba kugwiritsidwa ntchito. Mankhwala ameneŵa amakalowa mu mpweya wathu, dothi, madzi, ndi chakudya. Ochepa chabe ndi amene anawayeza kuti aone mmene amakhudzira thanzi la anthu. Komabe, pa mankhwala amene anawayezawo, ambiri a iwo anawapeza kuti amayambitsa khansa kapena matenda ena m’njira zosiyanasiyana.
Pali zinthu zina zambiri zimene zikuopseza chilengedwe chathu: kuwonongeka kwa mpweya, zoipa zochokera m’zimbudzi zamadzi zomwe sanazithire mankhwala, mvula yokhala ndi asidi, ndi kusoŵa kwa madzi abwino. Zinthu zochepa zimene tazitchulazi pazokha n’zokwanira kutisonyeza kuti dziko lapansili likudwaladi kwambiri. Kodi dzikoli lingachiritsidwe, kapena palibenso chiyembekezo chilichonse?