Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 1/15 tsamba 3
  • Kodi Moyo Unayamba Bwanji?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Moyo Unayamba Bwanji?
  • Galamukani!—2015
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Moyo Unayamba Bwanji?
    Nkhani Zina
  • ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA-Kodi Zinthu Zinachita Kulengedwa?—Gawo 2
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Chisinthiko Chizengedwa Mlandu
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Kodi Mfundo Yoti Zamoyo Zinachita Kusanduka ndi Yogwirizana ndi Baibulo?
    Nsanja ya Olonda—2008
Onani Zambiri
Galamukani!—2015
g 1/15 tsamba 3
Chipangizo choonera tizinthu ting’onoting’ono

NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi Moyo Unayamba Bwanji?

Pa ziganizo zili kumanjazi,

NDI CHITI CHOMWE MUKUONA KUTI NDI CHOLONDOLA?

  1. ZAMOYO ZINACHITA KUSINTHA KUCHOKERA KU ZINTHU ZINA

  2. ZAMOYO ZINACHITA KULENGEDWA

ANTHU ena angaganize kuti asayansi anganene kuti chiganizo cholondola ndi choyambacho, pomwe anthu amene amakhulupirira kuti kuli Mulungu angati cholondola ndi chachiwiricho.

Komatu si asayansi onse omwe amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina.

Mfundo ndi yakuti pali anthu ambiri ophunzira kuphatikizapo a sayansi ambiri omwe amakayikira zoti zamoyo zinachita kusitha kuchokera ku zinthu zina.

Wasayansi wina dzina lake Gerard, yemwe anaphunzira zoti zinthu zamoyo zinasintha kuchokera ku zinthu zina, anati: “Polemba mayeso, ndinkalemba zoti zamoyo zinachokera ku zinthu zina. Koma sikuti ndinkazikhulupirira. Ndinkangolemba zimenezi n’cholinga choti ndikhoze.”

Koma kodi n’chifukwa chiyani asayansi ena zimawavuta kukhulupirira kuti zamoyo zinachokera ku zinthu zina? Kuti tiyankhe funsoli, choyamba tiyeni tikambirane mafunso amene amazunguza mutu akatswiri akachita kafukufuku pa nkhaniyi. Mafunso ake ndi awa: (1) Kodi moyo unayamba bwanji? (2) Kodi mitundu yosiyanasiyana ya zamoyo inachokera kuti?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena