Mawu Oyamba
Kodi mukudziwa kuti a Mboni za Yehova amamasulira ndi kufalitsa mabuku m’zinenero zoposa 750?
N’chifukwa chiyani timachita zimenezi? Timafuna kuti uthenga wa m’Baibulo ufikire anthu “kudziko lililonse, fuko lililonse, chinenero chilichonse, ndi mtundu uliwonse.”—Chivumbulutso 14:6.
Magaziniyi ikufotokoza zomwe zimachitika tikamagwira ntchito yomasulira.