Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g16 No. 3 tsamba 3
  • Ntchito Yomasulira Yathetsa Vuto la Kusiyana Zinenero

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ntchito Yomasulira Yathetsa Vuto la Kusiyana Zinenero
  • Galamukani!—2016
  • Nkhani Yofanana
  • Mawu Oyamba
    Galamukani!—2016
  • Uthenga Wabwino Ukupezeka M’zinenero 500
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Buku Limene “Limalankhula” Zinenero Zomwe Zilipo
    Buku la Anthu Onse
  • Kusonkhanitsa Anthu a Zinenero Zonse
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
Onani Zambiri
Galamukani!—2016
g16 No. 3 tsamba 3
Anthu a mitundu ndi zikhalidwe zosiyanasiyana

NKHANI YA PACHIKUTO | A MBONI ZA YEHOVA AKUMASULIRA M’ZINENERO ZAMBIRI

Ntchito Yomasulira Yathetsa Vuto la Kusiyana Zinenero

PADZIKO lapansi pali zinenero pafupifupi 7,000. Zimenezi zimapangitsa kuti anthu azivutika kumvana pa nkhani zokhudza maulendo, maphunziro, malonda ndi maboma. Ndipotu mavuto amenewa anayamba kalekale. Mwachitsanzo, zaka 2,500 zapitazo, mu ulamuliro wa Mfumu Ahasiwero (yemwe mwina anali Sasta 1), Aperisi anapereka makalata ochokera kwa mfumu, kuyambira “ku Indiya kukafika ku Itiyopiya, zigawo 127.” Ndipo chifukwa cha kusiyana kwa zinenero, “chigawo chilichonse anachilembera makalata amenewa malinga ndi mmene anthu a m’chigawocho anali kulembera ndiponso m’chinenero chawo.”a

Masiku ano, maboma ambiri kapenanso mabungwe sayesa n’komwe kugwira ntchito yovutayi. Komabe pali gulu limodzi lokha limene lakwanitsa kuchita zimenezi. A Mboni za Yehova amafalitsa magazini, mabuku, Baibulo ngakhalenso mavidiyo ndi zinthu zina zongomvetsera, m’zinenero zoposa 750. Amamasuliranso zinthu zimenezi m’zinenero zamanja pafupifupi 80. Ndiponso amasindikiza mabuku ambiri a zilembo za anthu amene ali ndi vuto losaona.

A Mboni za Yehova sagwira ntchitoyi n’cholinga choti apeze ndalama. Komanso amene amagwira ntchito yomasulirayi ndi ongodzipereka. Kodi n’chifukwa chiyani amagwira ntchitoyi modzipereka chonchi, nanga amaigwira bwanji?

a Onani lemba la Esitere 8:9.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena