Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • tr mutu 17 tsamba 151-156
  • Mmene Mungapemphelere ndi Kumvedwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Mungapemphelere ndi Kumvedwa
  • Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • NJIRA YA KUMFIKIRA MULUNGU MWA PEMPHERO
  • MAPEMPHERO AMENE ALI OMKONDWERETSA MULUNGU
  • MKHALIDWE WOYENERA WA KUPEMPHERA
  • KUMAUYAMIKIRA MWAI WA PEMPHERO
  • Pemphero Lingakuthandizeni Kukhala pa Ubwenzi ndi Mulungu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Mmene Mungapezere Chithandizo Kupyolera mwa Pemphero
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Mapemphero Amene Amayankhidwa
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Tili Ndi Mwayi Wopemphera kwa Mulungu
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
Onani Zambiri
Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
tr mutu 17 tsamba 151-156

Mutu 17

Mmene Mungapemphelere ndi Kumvedwa

1. Kodi nciani cimene Salmo 65:2 limanena ponena za Mulungu, ndipo kodi ndani amene angadze kwa iye ndi citsimikiziro cakuti adzamvedwa?

PONENA za Yehova Mulungu Baibulo limati: “Wakumva pemphero Inu, zamoyo zonse zidzadza kwa Inu.” (Salmo 65:2 [64:3, Dy]) Inde, Mulungu amamva mapemphero. Ndipo anthu a pa dziko lonse lapansi amene amakonda coonadi, amene amafunafuna kucita cifuniro cace, ndipo amene amamfikira iye mu njira imene amaibvomereza, angasangalale nawo mwai wa mtengo wapatali umenewu. (Macitidwe 10:34, 35) Ndithudi, ndi motani nanga mmene wakhalira mwai wa mtengo wapatali kukhala okhoza kulankhula ndi Wolamulira waulemerero wa mu cilengedwe caponseponseyo ndi kudziwa kuti akukumvani inu!—Salmo 8:1, 3, 4 [8:2, 4, 5, Dy]; Yesaya 45:22.

2. (a) Ponena za pemphero, kodi ndi lonjezo lotani limene Baibulo limalipereka pa Afilipi 4:6, 7? (b) Kodi ncifukwa ninji ena amaona kukhala okaikakaika ponena za pemphero?

2 Molimbikitsa, Mau ace olembedwa amalonjeza kuti: “Musadere nkhawa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana cidziwitso conse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) Komabe, ena angamakhale okaikakaika ponena za nkhani ya pemphero cifukwa cakuti ambiri a mapemphero ao amaonekera kukhala ngati sanayankhidwe. Kodi ici cifukwa ninji? Kuli kofunika kwambiri kwa ife kuti tidziwe. M’Mau ace, Mulungu amacilongosola momvekera bwino cimene ciri cifuniro cace ponena za pemphero.

NJIRA YA KUMFIKIRA MULUNGU MWA PEMPHERO

3. Kodi ndi kwa ndani kumene mapemphero athu anayenera kuperekedwako, ndipo ncifukwa ninji?

3 Baibulo limatiuza ife kuti “iye wakudza kwa mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna Iye.” (Ahebri 11:6) Taonani kuti lemba ili limanena kuti tiyenera ‘kudza kwa Mulungu.’ Monga Mulungu woona ndi wamoyo, Yehova amatifuna ife kuti tizipemphera kwa iye, osati kwa wina aliyense. Pemphero liri mbali yina ya kulambira kwathu ndipo pa cifukwa ca ici liyenera kuperekedwa kokha kwa Mlengiyo, Yehova. (Mateyu 4:10) Yesu Kristu anawaphunzitsa atsatiri ace kupemphera kwa ‘Atate wace wakumwamba.’ (Mateyu 6:9) Yesu sanawaphunzitse iwo kuti azipemphera kwa iyeyo, kapena kwa amai wace waumunthu Mariya, kapena kwa munthu wina aliyense. Yehova ali wamphamvuyonse, wanzeru zonse, wangwiro mu cilungamo ndi cikondi. Cotero, ncifukwa ninji tinayenera kupita kwa munthu wina amene ali wocepera? Kuonjezerapo, mtumwi Paulo wouziridwa amatitsimikizira ife kuti Mulungu “sakhala patari ndi yense wa ife,” ngati timfunafuna iye mu njira yoyenera.—Macitidwe 17:27.

4. Kuti mapemphero athu akhale obvomerezedwa kwa Mulungu kodi ayenera kuperekedwa m’dzina la ndani? Ncifukwa ninji?

4 Koma inu munganene kuti, “Kodi ndi motani mmene ife, monga zolengedwa zopanda ungwiro zokhala ndi ucimo wa colowa, tingapempherere kwa Mulungu amene ali wangwiro ndi wolungama?” Mwacikondi Yehova anazilingalira izizo ndipo anapereka “nkhoswe” yakutilankhulira kumwambako. Nkhoswe ameneyo ndiye “Yesu Kristu wolungama.” (1 Yohane 2:1, 2) Iye anaupereka moyo wace monga dipo kaamba ka mtundu wa anthu. Kuonjezerapo, Yehova anamsankha iye kukhala Mkuru Wansembe wace. Yehova amafuna kuti ife tiziwazindikira malo a nchito a Mwana waceyo m’cifuno Cace ndi kumawapereka mapemphero athu onse m’dzina lace. Ndico cifukwa cace Yesu anawauza atsatiri ace kuti: “Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.” (Yohane 14:6) Yesu anatinso: “Ngati mudzapempha Atate kanthu, adzakupatsani inu m’dzina langa.” (Yohane 16:23) Kuti mapemphero athu akhale olandirika kwa Mulungu, pamenepo, tiyenera kupemphera kwa Yehova Mulungu kupyolera mwa Mwana wace, ndiko kuti, m’dzina la Yesu.

MAPEMPHERO AMENE ALI OMKONDWERETSA MULUNGU

5. (a) Pomalingalira za cimene 1 Petro 3:12 amanena, kodi ndi motani mmene tinayenera kuyesa moona mtima kuitsogozera miyoyo yathu ngati mapemphero athu angati amvedwe ndi Mulungu? (b) Kodi ndani amene sanayenera kumuyembekezera Mulungu kuwamva mapemphero ao ofunsira cithandizo?

5 Pa 1 Petro 3:12 timawerenga kuti: “Maso a Ambuye ali pa olungama, ndi makutu ace akumva pembedzo lao.” Motero, ngati mapemphero athu angamkondweretse Mulungu, tiyenera kukhala oona mtima m’kumayesa kukhala ogwirizana ndi maprinsipulo olungama a Mau a mulungu. Ngati munthu awakana Mau a Mulungu limodzi ndi cifuniro cace iye sayenera kuyembekezera kuti Mulungu adzawamva mapemphero ace omapempha cithandizo mu nthawi ya bvuto. (Miyambo 15:29; 28:9) Mwacitsanzo, kwa awo amene samakulabadira kupatulika kwa moyo, Mulungu amawauza kuti: “Pocurukitsa mapemphero anu Ine sindidzamva; manja anu adzala mwazi.” (Yesaya 1:15) Mu “nthawi ya mapeto” iyi pamene ciwawa, cisembwere, kusaona mtima, kulambira konyenga ndi makhalidwe ena oipa zikumafikira kukhala zowanda moonjezerekaonjezereka, ife tiyenera kulingalira mosamalitsa za njira imene timakhalira m’moyo wathu wa tsiku ndi tsiku ngati tifuna kuti Mulungu awamve mapemphero athu.—1 Yohane 3:21, 22.

6. (a) Malinga ndi cilangizo ca Yesu, kodi nciani cimene ciyenera kukhala coyamba m’mapemphero athu? (b) Kodi ndi motani mmene Yesu anasonyezera kuti mapemphero athu sanayenera kungokhala kaamba ka ife tokha? Pamenepo, kodi ife tinayenera kupempherera ndani?

6 Zimene timazipemphazonso ndizo zimene ziri kanthu pomatsimikizira ngati Mulungu adzawayankha mapemphero athu. Yesu anawapatsa akuphunzira ace pemphero lacitsanzo kuwatsogoza iwo kuudziwa mtundu wa pemphero limene Mulungu amalibvomereza. (Mateyu 6:9-13) Pemphero limeneli limasonyeza kuti dzina la mulungu ndi zifuno zace ziyenera kukhala zinthu zoyambirira mwa ife. Kenaka, tingapemphe zosowa zathu zakuthupi, cikhululukiro ndi cilanditso ku ziyeso ndi kwa woipayo. Taonaninso kuti Yesu amatiphuzitsa ife kupemphera kwa “Atate wathu” kuti atipatse “ife lero cakudya cathu ca lero” ndi kuti atikhululukire ife.’ Ici cimasonyeza kuti, popemphera, munthu sanayenera kumangolingalira za iye mwini, kapena za zothetsa nzeru za iye mwini yekhayo ndi zosowa zace. M’malo mwace iye mopanda dyera ayenera kuwakuza mapemphero ace ndi kuwaphatikizamonso ena. Ife tiyenera kuphatikizamo, osangoti banja lathu lokha limodzi ndi anansi athu, komanso ena amene akufunafuna kumkondweretsa mulungu, ndipo makamaka awo amene akukumana ndi ziyeso ndi mabvuto mu utumiki wao kwa Mulungu.—Yakobo 5:16; Aefeso 6:18-20.

7. (a) Kodi cifukwa cacikuru ncotani cifukwa cace mapemphero ambiri samayankhidwa? (b) Kuti tipereke mapemphero obvomerezeka, kodi nciani cimene tiyenera kucicita coyamba?

7 Mtumwi Yohane amalemba kuti: “Ndipo uku ndi kulimbika mtima kumene tiri nako kwa iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa cifuniro cace, atimvera.” (1 Yohane 5:14) Inde, mbali iriyonse ya moyo wa Mkristu iri yoyenera kuipempherera. Koma cinthu cofunika ndico cakuti cimene akucipemphaco cikhale cogwirizana ndi cifuniro ca Mulungu. Cimeneci ndico cifukwa cacikurukuru cimene mapemphero ambirimbiri samayankhidwira. Munthuyo amakhala asanayambe wayesa coyamba kucizindikira cimene ciri cifuniro ca Mulungu. (Miyambo 3:5-7) Cotero, m’malo mwa kumasankha cimene tifuna kucicita kapena kukhala naco, ndi kumapemphera kwa Mulungu kaamba ka cimeneco, kodi sikuli koyenera coyambirira kuyamba tazindikira za cimene Mulungu amacifuna mwa ife, cimene cifuniro cace ciri kaamba ka ife, ndiye pamenepo kuwapanga mapemphero athu moyenerera?—Yakobo 4:3, 13-15.

8. (a) Kodi ndi motani mmene tingacizindikirire cifuniro ca Mulungu? (b) Kodi Mulungu adzatipatsadi nzeru ya kuutsogozera moyo wathu?

8 Mwa kuphunzira kwathu Mau a Mulungu ndi mwa cidziwitso cathu cimene tacipeza m’kumamtumikira iye mogwirizana ndi Akristu ena oona ife tingafikire pa kucizindikira cifuniro cace. (Aroma 12:2) Wamasalmoyo anapemphera kuti: “Mundizindikiritse, ndipo ndidzasunga malamulo anu; ndidzawasamalira ndi mtima wanga wonse. Mundiyendetse mopita malamulo anu; pakuti ndikondwera m’menemo. Linganitsani mtima wanga ku mboni zanu, si ku cisiriro ai.” (Salmo 119:34-36 [118:34-36, Dy]) Ngati tipemphera kwa Mulungu mwa cikhulupiriro, iye mwacifundo adzatipatsa ife nzeru imene tiifunayo kuti itithandize kuzigonjetsera zothetsa nzeru za moyo. (Yakobo 1:5-8) Iye adzatithandiza ife kucidziwa ndi kucicita cimene cidzatengera ulemu ku dzina lace lalikurulo, ndipo iciconso cidzatipatsa ife cimwemwe.—Salmo 84:11, 12 [83:12, 13, Dy].

MKHALIDWE WOYENERA WA KUPEMPHERA

9. (a) Pamene tikupemphera, kodi kumatofunikira kuti tikhale mu mkhalidwe wakutiwakuti? (b) Kodi nciani cimene Yesu anacisonyeza ponena za pemphero laumwini? (c) Kodi ndi mtundu wanji wa mapempheredwe umene Yesu anautsutsa?

9 Kodi Mulungu amafuna kuti tizikhala mu mkhalidwe wakutiwakuti pamene tikupemphera kapena kuti tizipita ku nyumba yakutiyakuti kukapemphera? Mau ace amasonyeza kuti iye satero. (Nehemiya 8:6; a Danieli 6:10; Marko 11:25; Yohane 11:41) Yesu anasonyeza kuti kuli bwino kupita m’tseri ndi kukapemphera, kumalowa m’cipinda ndi kukapemphera. (Mateyu 6:6) Ndipo ngakhale kunali kwakuti Yesu mwiniyo pa nthawi zina anali kupemphera poyera, iye anakutsutsa mwamphamvu kumapemphera ena akumaona ndi colinga cakuti muonedwe nawo ndi kudzisonyeza kukhala “wolungama.” Iyenso anasonyeza kuti Mulungu samakubvomereza kugwiritsira nchito mau amodzimodziwo mobwerezabwereza popemphera. (Mateyu 6:5, 7, 8) Kodi ncifukwa ninji?

10. (a) Talongosolani cifukwa cace mapemphero athu sanayenera kuwerengedwa kucokera m’bukhu. (b) Kodi ndi mau a mtundu wanji amene tingawagwiritsire nchito pamene tikupemphera?

10 Kuli cifukwa cakuti cimene ciri kanthu kwa Mulungu ndico cimene ciri mumtima mwathu. “Pakuti maso a Yehova ayang’ana uko ndi uko m’dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa awo amene mtima wao uli wangiwro ndi Iye.” (2 Mbiri 16:9)b Kodi ndi motani mmene pemphero lathu lingazilongosolere zimene ziri mumtima mwathu ngati ilo likhala longoliwerenga kucokera pa bukhu la mapemphero? Cotero, pamene tipemphera, tiyenera kupemphera kucokera mumtima, modzicepetsa. “Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa cisomo odzicepetsa.” (Yakobo 4:6) M’mapemphero athu kungakhale kosapindulitsa kugwiritsira nchito mau amene samanenedwa kawirikawiri kapena apamwambamwamba. M’malo mwace, tiyenera kulankhula ndi Mulungu monga momwe tingalankhulirane ndi bwenzi lapamtima ndi lodalirika ndiponse monga mwana wamwamuna kwa bambo wace. Pemphero lathu lingakhalenso la kacetecete, mu mtima mwathu mokhamo. (1 Samueli 1:12, 13)c Pa nthawi zina sitingawapeze mau enieni a kuwalongosolera malingaliro athu kwa Mulungu. Koma tingakhale ndi cidaliro cakuti Mulungu amadziwa zosowa zathu ndipo adzalimwa pemphero lathu lofewalo.

KUMAUYAMIKIRA MWAI WA PEMPHERO

11. (a) Kodi tinayenera kuyembekezera kufikira ticifuna cithandizo capadera ife tisanapemphere kwa Mulungu? (b) Kodi ncifukwa ninji pemphero liri loyenera pa nthawi za cakudya?

11 Ife tonse timakumana ndi nthawi zina m’moyo wathu pamene cithandizo caumunthu sicimakhalapo kapena pamene cithandizo cimene anthu angacipereke sicimakhala cokwanira pa zosowa zathuzo. Pamenepo sicimakhala cokwanira pa zosowa zathuzo. Pamenepo kuli kwa Mulungu kokha kumene tingatembenukireko. Komabe, ngati timamkonda Yehova ndi kuuyamikira mwai wa pemphero ife ndithudi sitidzayembekezera kufikira nthawi zoterozo zidza kuti tilankhule naye, M’malo mwace, ife tidzamfikira iye mokhazikika, kawirikawiri, limodzi ndi mau a cithokozo ndi citamando, limodzinso ndi zidandaulo zathu ndi zopempha. (Aefeso 6:18; 1 Atesalonika 5:17, 18) Banja limapindula kwakukuru ndi pemphero, ngakhale kukhale kuthokoza kwa Mulungu pa nthawi za cakudya, kumacitsatira citsanzo ca Yesu.—Mateyu 14:19.

12. Tawalongosolani ena a mapindu ozizwitsa a pemphero.

12 Ndithudi, pemphero lam’tseri, pemphero la banja ndiponso pemphero la mpingo mapemphero onsewo amapereka mapindu ozizwitsa. Pemphero limasonyeza kuzindikira kotheratu kwa kudalira kwathu kotsimikizirika pa Mulungu kaamba ka cinthu ciriconse. Limatipangitsa ife kugwirizana pamodzi ndi alambiri anzathu. Limatipatsa ife mtendere wa Mlengi wacikondiyo. Ilo limakupititsa patsogolo kuyenda kwa tawatawa kwa mzimu woyera wa Mulungu m’miyoyo yathu. Ilo limatithandiza ife kukhala ndi cidaliro ca mtsogolo. Ilo liri mphatso yocokera kwa Mulungu ndipo mphatso imene tinayenera kuiyamkikira ndi kuigwiritsira nchito.

[Mawu a M’munsi]

a 2 Esdras 8:6, Dy.

b 2 Paralipomenon 16:9, Dy.

c 1 Mafumu 1:12, 13, Dy.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena