Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • pe mutu 27 tsamba 225-230
  • Mmene Mungapezere Chithandizo Kupyolera mwa Pemphero

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Mungapezere Chithandizo Kupyolera mwa Pemphero
  • Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • MAPEMPHERO AMENE MULUNGU AMAMVA
  • MAPEMPHERO KUTI ATHANDIZE ENA
  • Pemphero Lingakuthandizeni Kukhala pa Ubwenzi ndi Mulungu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Tili Ndi Mwayi Wopemphera kwa Mulungu
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Mmene Mungapemphelere ndi Kumvedwa
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Pemphero Lingakuthandizeni Kuti Mulungu Akhale Mnzanu
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
Onani Zambiri
Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
pe mutu 27 tsamba 225-230

Mutu 27

Mmene Mungapezere Chithandizo Kupyolera mwa Pemphero

1. Kodi tikufuna chithandizo chotani kwa Mulungu, ndipo kodi timachilandira motani?

KUTI AKHALE OPANDA chiyambukiro choipa cha dziko, Akristu amafunikira kwenikweni chithandizo cholandiridwa kupyolera mwa pemphero. Yesu anati: “Atate kumwamba adzapereka mzimu woyera kwa awo ompempha.” (Luka 11:13, NW) Tifunikira mzimu woyera wa Mulungu, kapena mphamvu yogwira ntchito, monga momwedi timafunira kuphunzira Mawu ake ndi kugwirizana ndi gulu lake. Koma kuti tilandire mzimu woyera, tiyenera kuupempha.

2. (a) Kodi pemphero nchiyani? (b) Kodi mipangidwe yosiyanasiyana ya pemphero njotani? (c) Kodi nchifukwa ninji pemphero liri lofunika?

2 Pemphero ndilo kulankhula ndi Mulungu kwaulemu. Lingakhale mu mpangidwe wa pempho, monga ngati popempha Mulungu zinthu. Koma pemphero lingakhalenso kusonyezedwa kwa chiyamiko kapena chitamando kwa Mulungu. (1 Mbiri 29:10-13) Kuti tikhale ndi unansi wabwino ndi Atate wathu wakumwamba, tiyenera kulankhula naye nthawi zonse m’pemphero. (Aroma 12:12; Aefeso 6:18) Mphamvu yake yogwira ntchito, imene imalandiridwa mwa kuipempha kwathu, ingatilimbikitse kuchita chifuniro chake mosasamala kanthu za mavuto kapena ziyeso zirizonse zimene Satana kapena dziko lake angadzetse pa ife.—1 Akorinto 10:13; Aefeso 3:20.

3. (a) Kodi tingalandire nyonga yotani kwa Mulungu? (b) Kodi tingasunge kokha motani unansi wabwino ndi Mulungu?

3 Mungakhale muli ndi nkhondo yeniyeni yakuchotsa chizolowezi china kapena kachitidwe kamene sikakukondweretsa Mulungu. Ngati ndichoncho, funafunani chithandizo cha Mulungu. Pitani kwa iye m’pemphero. Mtumwi Paulo anatero, ndipo analemba kuti: “Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.” (Afilipi 4:13; Salmo 55:22; 121:1, 2) Mkazi wina amene anamasuka kunjira ya chisembwere anati: “Iye ndiye yekha amene ali ndi mphamvu yakuthandiza kuchoka mu mkhalidwe umenewo. Muyenera kukhala ndi unansi weniweni umenewo ndi Yehova, ndipo njira yokha yosungira unansi weniweni umenewo ndiyo kupemphera.

4. Kodi ndimotani mmene munthu wina analandirira nyonga ya kumasuka ku chizolowezi cha kusuta fodya?

4 Komabe munthu anganene kuti: ‘Ndapempha chithandizo cha Mulungu kambirimbiri, koma sindikulekabe kuchita choipa.’ Anthu amene amasuta fodya anena zimenezi. Pamene munthu woteroyo anafunsidwa: “Kodi umapemphera liti?” iye anayankha: “Madzulo ndisanakagone, mamawa pamene ndidzuka, ndipo nditafooka ndi kusuta, ndimauza Yehova kuti ndiri ndichisoni chifukwa cha zimene ndachita.” Bwenzi lake limati: “Nthawi imene umafunikiradi chithandizo cha Mulungu ndiyo nyengo imene ukutenga ndudu, kodi sichoncho? Imeneyo ndiyo nthawi imene uyenera kupemphera kwa Yehova kuti akulimbikitse.” Pamene munthuyo anatero, analandira chitandizo chakuleka kusuta.

5. (a) Kodi kumafunikiranji kutumikira Mulungu moyenera? (b) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti kuvutika kawirikawiri kumalowetsedwamo mkuleka kachitidwe koipa?

5 Uku sindiko kunena kuti pemphero kwa Mulungu, limodzi ndi kuphunziridwa kwa Mawu ake ndi kugwirizana ndi gulu lake lowoneka, kudzapangitsa kukhala kusavuta kwa inu kuchita chimene chiri chabwino. Kumafunabe kuyesayesa; inde, nkhondo yamphamvu, imene ingaphatikizepodi kuvutika. (1 Akorinto 9:27) Zizolowezi zoipa zingachititse kulakalaka kwamphamvu chimene chiri choipa. Motero kuvutika kawirikawiri kumapezeka pamene munthu aleka kachitidwe koipa. Kodi mukufunitsitsa kuvutika kuti muchite chimene chiri chabwino?—1 Petro 2:20, 21.

MAPEMPHERO AMENE MULUNGU AMAMVA

6. (a) Kodi nchifukwa ninji ambiri amawona kukhala kovuta kupemphera? (b) Kodi tikufunikiranji kuti mapemphero athu amvedwe?

6 Anthu ambiri amawona kukhala kovuta kupemphera. “Ndiri ndivuto kupemphera kwa munthu amene sindingamuwone,” anatero mkazi wina wachichepere. Popeza kuti palibe munthu wawona Mulungu, tifunukira chikhulupiriro kuti tipemphere ndi kumvedwa ndi Mulungu. Tifunikira kukhulupirira kuti Yehova alikodi ndi kuti iye angachite zimene tikupempha. (Ahebri 11:6) Ngati tiri ndi mtundu umenewo wa chikhulupiriro, ndipo ngati tifikira Mulungu ndi mtima wowona, tingakhale otsimikizira kuti iye adzatithandiza. (Marko 9:23) Motero, ngakhale kuli kwakuti mkulu wa gulu lankhondo Wachiroma Korneliyo pa nthawiyo sanali mbali ya gulu la Mulungu, pamene iye mowona mtima anapempha chitsogozo, Mulungu anayankha pemphero lake.—Machitidwe 10:30-33.

7. (a) Kodi ndimtundu wotani wa mapemphero umene umakondweretsa Mulungu? (b) Kodi Mulungu sadzamvetsera mtundu wotani wa mapemphero?

7 Anthu ena amavutika ndi kulankhula. Komabe, kumeneku sikuyenera kuwalepheretsa kulankhula ndi Mulungu m’pemphero. Tingatsimikizire kuti iye amadziwa zosowa zanthu ndipo adzazindikira zimene tikufuna kunena. (Mateyu 6:8) Taganizirani zimenezo: Kodi mumayamikira koposa mawu ati ochokera kwa mwana—kuthokoza kwake kwakufupi ndi kuwona mtima kapena mawu apadera amene munthu wina anamuuza kuti anene? Momwemonso Atate wathu wakumwamba amayamikira mawu afupi ndi owona mtima ochokera mwa ife. (Yakobo 4:6; Luka 18:9-14) Mawu apadera kapena kanenedwe kachipembedzo sizikufunikira. Iye sadamvera konse awo amene amapemphera m’kanenedwe kapadera kapena kokukumaza kuti achititse ena kaso, kapena amene amanena zinthu zimodzimodzizo mobwerezabwereza m’njira yosawona mtima.—Mateyu 6:5, 7.

8. (a) Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti Mulungu angamve mapemphero operekedwa mwakachetechete? (b) Kodi Baibulo limasonyeza kuti tiyenera kupemphera mu mkhalidwe wina uliwonse kapena malo?

8 Ngakhale pamene mupemphera mwakachetechete, Mulungu angamve. Pamene Nehemiya anatero, Mulungu anachita kanthu pa pempho lake lowona mtima, ndipo chomwechonso ndi Hana. (Nehemiya 2:4-8; 1 Samueli 1:11-13, 19, 20) Ngakhale kaimidwe kathupi ka munthu popemphera sikali chinthu chofunika. Mungapephere pamene muli m’kaimidwe kalikonse, pa nthawi iriyonse ndi pamalo alionse. Komabe, Baibulo limasonyeza kuti mkhalidwe wodzichepetsa, monga ngati kuweramitsa mutu kapena kugwada, ngwoyenera. (1 Mafumu 8:54; Nehemiya 8:6; Danieli 6:10; Marko 11:25; Yohane 11:41) Ndipo Yesu anasonyeza kuti kuli bwino pamene mapemphero aumwini anaperekedwe m’malo obisika ndi osawoneka kwa anthu.—Mateyu 6:6.

9. (a) Kodi nkwayani kumene mapemphero anthu onse ayenera kuperekedwa, ndipo chifukwa ninji? (b) Kuti mapemphero anthu akhale olandirika kwa Mulungu, kodi iwo ayenera kuperekedwa m’dzina la yani?

9 Pemphero ndilo mbali ya kulambira kwathu. Kaamba ka chifukwa chimenechi mapemphero athu ayenera kuperekedwa kokha kwa Mlengi wathu, Yehova Mulungu, osati kwa wina aliyense. (Mateyu 4:10) Ndipo Baibulo limasonyeza kuti Akristu ayenera kuyandikira Mulungu kupyolera mwa Yesu, amene anapereka moyo wake kuchotsa machimo athu. Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kupereka mapemphero athu m’dzina la Yesu.—Yohane 14:6, 14; 16:23; Aefeso 5:20; 1 Yohane 2:1, 2.

10. (a) Kodi ndimapemphero a yani amene sali okondweretsa kwa Mulungu? (b) Kodi nchofunika chachikulu chotani chimene tiyenera kukwaniritsa ngati mapemphero athu ati amvedwe ndi Mulungu?

10 Komabe, kodi mapemphero onse amakhala okondweretsa Yehova? Baibulo limati: “Wopewetsa khutu lake kuti asamve chilamulo, ngakhale pemphero lake linyansa.” (Miyambo 28:9; 15:29; Yesaya 1:15) Chifukwa chake ngati tifuna kuti Mulungu amve mapemphero athu, chofunika chachikulu ndicho chakuti tichite chifuniro chake, kuti timvere malamulo ake. Zitapanda kutero Mulungu sadzatimvera, monga momwedi munthu wolungama sakamvetserera programu ya rediyo imene akuilingalira kukhala yoipa. Baibulo limati: “Chimene chirichonse tipempha, tilandira kwa Iye, chifukwa tisunga malamulo ake, ndipo tichita zomkondweretsa pamaso pake.”—1 Yohane 3:22.

11. Kodi kumatanthauzanji kuchita zimene timapempha?

11 Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kuchita zimene tikupempha. Mwa chitsanzo, kukakhala kolakwa kwa munthu kupempha Mulungu chithandizo chake kuti aleke kugwiritsira ntchito fodya kapena chamba ndiyeno nkupita ndi kukagula zinthu zimenezi. Ndiponso sakapempha Yehova kuti amthandize kupewa chisembwere ndiyeno nkumakuwerenga mabukhu ndi kuwonera akanema ndi maprogramu atelevizheni amene amasonyeza chisembwere. Kapena ngati kutchova juga ndiko chofooka cha munthu, iye sakapempha Mulungu kuti amthandize kuleka ndi kenako kupita kumijaho kapena malo ena oterowo kumene kutchova juga kumachitidwa. Kuti mapemphero anthu amvedwe ndi Mulungu, tifunikira kumsonyeza mwa machitidwe athu kuti tikutanthauzadi zimene tikunena.

12. (a) Kodi ndizinthu zotani zimene tingaphatikize m’mapemphero athu? (b) Kuti mapemphero anthu akhale okhondweretsa kwa Mulungu, kodi tiyenera kuphunziranji?

12 Pamenepa, kodi zinthu zaumwini, zimene tingaphatikize m’mapemphero athu kwa Yehova nzotani? Kwenikweni, chinthu chirichonse chimene chidzayambukira unansi wathu ndi Mulungu ndicho nkhani yoyenera ya pemphero, kuphatikizapo thanzi lathu lakuthupi, kudzanso kuleredwa kwa ana. (2 Mafumu 20:1-3; Oweruza 13:8) Mtumwi Yohane analemba kuti: “Ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera.”(1 Yohane 5:14) Motero chinthu chofunika nchakuti zopempha zathu zikhale zogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Zimenezi zikutanthauza kuti ife choyamba tifunikira kuphunzira chimene chifuniro cha Mulungu ndi chifuno pamene tipemphera, koposa ndi kungokondweretsedwa ndi zikondwerero zathu za ife eni, mapemphero athu adzakhala olandirika kwa Yehova. Nkoyenera kuti tithokoze Yehova tsiku lirilonse kaamba ka zinthu zabwino zimene amapereka.—Yohane 6:11, 23; Machitidwe 14:16, 17.

13. (a) Kodi ndimotani mmene Yesu anasonyezera chimene chiyenera kukhala zinthu za nkhawa yoyambirira m’mapemphero athu? (b) Kodi ndizinthu zachiwiri zofunika zotani zimene tiyenera kupempherera?

13 Yesu anapatsa omtsatira pemphero lachitsanzo kuti liwatsogoze ponena za mtundu wa pemphero umene Mulungu amalandira. (Mateyu 6:9-13) Pemphero limeneli limasonyeza kuti dzina la Mulungu, ufumu wake ndi kuchitidwa kwa chifuniro chake padziko lapansi zimayambirira. Kenako, tingapemphe zosowa zathu za ife eni, monga ngati chakudya chathu chatsiku ndi tsiku, kukhululukidwa kwa machimo, ndi kupulumutsidwa ku chiyeso ndi kwa woipayo, Satana Mdyerekezi.

MAPEMPHERO KUTI ATHANDIZE ENA

14. Kodi ndimotani mmene Baibulo limasonyezera kufunika kwa kupempherera ena?

14 Yesu anasonyeza mwa chitsanzo chake kufunika kwa kupempherera ena. (Luka 22:32; 23:34; Yohane 17:20) Mtumwi Paulo anadziwa phindu la mapemphero oterowo ndipo kawirikawiri anapempha ena kuti ampempherere. (1 Atesalonika 5:25; 2 Atesalonika 3:1; Aroma 15:30) Pamene anali m’ndende analemba kuti: “Ndiyembekeza kuti mwa mapemphero anu ndidzapatsidwa kwa inu.” (Filemoni 22; Aefeso 6:18-20) Chakuti posapita nthawi Paulo anamasulidwa chimasonyeza phindu la mapemphero amene anaperekeredwa iye.

15. Kodi ndimapempho a mtundu wotani amene tingapange ponena za anthu amene timakonda?

15 Paulo anaperekeranso ena mapemphero othandiza. Iye analemba kuti, “Tikupemphereraninso nthawi zonse, kuti Mulungu wathu akakuyeseni inu oyenera kuitanidwa kwanu.” (2 Atesalonika 1:11) Ndipo kumpingo wina iye anafotokoza kuti: “Tipemphera Mulungu kuti musachite kanthu koipa . . . koma kuti inu mukachite chabwino.” (2 Akorinto 13:7) Ndithudi kuli bwino kutsatira chitsanzo cha Paulo ndi kupempherera motsimikizirika anthu amene timakonda. Ndithudi, “pemphero [kudandaulira kuwona mtima] la munthu wolungama likhoza kwakukulu m’machitidwe ake.”—Yakobe 5:13-16.

16. (a) Kuti tipeze chithandizo chofunika, kodi tiyenera kupemphera liti? (b) Kodi nchifukwa ninji pemphero liri mwayi waukulu kwambiri?

16 Pochititsa phunziro Labaibulo, minisitala wina amafunsa kawirikawiri kuti: “Kodi mumapemphera nthawi zina kuphatikiza pa nthawi ya phunziro lanu Labaibulo lamlungu ndi mlungu?” Kuti tipeze chithandizo chimene tikuchifunikira, tiyenera kulankhula ndi Mulungu kawirikawiri m’pemphero. (1 Atesalonika 5:17; Luka 18:1-8) Phunzirani kulankhula naye modzichepetsa monga momwe mukachitira ndi bwenzi lokondedwa ndi lodaliridwa. Ndithudi, uli mwayi wabwino kwambiri chotani nanga kukhala wokhoza kupereka pemphero kwa Wolamulira waulemerero wa chilengedwe chonse, Wakumva pempheroyo, ndi kudziwa kuti akukumvani!—Salmo 65:2.

[Chithunzi patsamba 227]

Kodi munthu ayenera kuchitanji pamene achititsidwa dyokodyoko kuti asute fodya—kupempha chithandizo kapena kugonja?

[Chithunzi patsamba 229]

Kodi mumapempha chithandizo ndiyeno kudzilowetsa m’kachitidwe kamene kangatsogolere ku kuchita choipa?

[Chithunzi patsamba 230]

Kodi mumapemphera panokha kapena kokha pamene muli ndi ena?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena