Phunziro 8
Moyo wa Banja Umene Umakondweretsa Mulungu
Kodi mwamuna ali ndi malo otani m’banja? (1)
Kodi mwamuna ayenera kum’chitira motani mkazi wake? (2)
Kodi tate ali ndi mathayo otani? (3)
Kodi mkazi ali ndi mbali yotani m’banja? (4)
Kodi Mulungu amafunanji kwa makolo ndi ana? (5)
Kodi lingaliro la Baibulo n’lotani pa kupatukana ndi chisudzulo? (6, 7)
1. Baibulo limati mwamuna ndiye mutu wa banja lake. (1 Akorinto 11:3) Mwamuna ayenera kukhala ndi mkazi mmodzi yekha. Iwo ayenera kukhala okwatirana bwino monga mwa lamulo.—1 Timoteo 3:2; Tito 3:1.
2. Mwamuna ayenera kukonda mkazi wake monga adzikonda yekha. Ayenera kum’chitira monga momwe Yesu amachitira otsatira ake. (Aefeso 5:25, 28, 29) Sayenera kumenya mkazi wake kapena kum’chitira nkhanza mwanjira iliyonse. M’malo mwake, ayenera kumuŵerengera ndi kumlemekeza.—Akolose 3:19; 1 Petro 3:7.
3. Tate ayenera kugwiritsa ntchito kuti asamalire banja lake. Ayenera kupeza chakudya, zovala, ndi nyumba yokhalamo mkazi ndi ana ake. Ndiponso tate ayenera kugaŵira banja zosoŵa zawo zauzimu. (1 Timoteo 5:8) Amatsogolera banja polithandiza kuphunzira za Mulungu ndi zifuno Zake.—Deuteronomo 6:4-9; Aefeso 6:4.
4. Mkazi ayenera kukhala mthandizi wabwino kwa mwamuna wake. (Genesis 2:18) Ayenera kuthandiza mwamuna wake kuphunzitsa ndi kulangiza ana awo. (Miyambo 1:8) Yehova amafuna kuti mkazi asamalire banja lake mwachikondi. (Miyambo 31:10, 15, 26, 27; Tito 2:4, 5) Ayenera kukhala ndi ulemu waukulu kwa mwamuna wake.—Aefeso 5:22, 23, 33.
5. Mulungu amafuna kuti ana amvere makolo awo. (Aefeso 6:1-3) Amafuna kuti makolo alangize ana awo ndi kuwawongolera. Makolo afunika kucheza ndi ana awo ndi kuphunzira nawo Baibulo, akumawapatsa zofunika zawo zauzimu ndi kuwasonyeza chikondi. (Deuteronomo 11:18, 19; Miyambo 22:6, 15) Makolo sayenera kulanga ana awo mwaukali kapena mwankhanza.—Akolose 3:21.
6. Pamene okwatirana akhala ndi vuto la kusamvana, ayenera kuyesa kutsatira uphungu wa Baibulo. Baibulo limatilangiza kusonyezana chikondi ndi kukhululukirana. (Akolose 3:12-14) Mawu a Mulungu samalimbikitsa kupatukana monga njira yothetsera mavuto aang’ono. Koma mkazi angasankhe kusiya mwamuna wake ngati (1) amakaniratu kusamalira banja lake, (2) ngwachiwawa kwambiri kwakuti moyo ndi thanzi la mkazi zikhala pangozi, kapena (3) kutsutsa kwake kopambanitsa kumalepheretsa mkaziyo kulambira Yehova.—1 Akorinto 7:12, 13.
7. Okwatirana ayenera kukhala okhulupirika kwa wina ndi mnzake. Chigololo ndi kuchimwira Mulungu ndi mnzakeyo. (Ahebri 13:4) Kugonana kunja kwa ukwati ndiko maziko okha a m’Malemba osudzulirana olola munthu kukwatiranso. (Mateyu 19:6-9; Aroma 7:2, 3) Yehova amakwiya pamene anthu asudzulana popanda zifukwa za Malemba nakwatiranso wina.—Malaki 2:14-16.
[Zithunzi pamasamba 16, 17]
Mulungu amafuna kuti makolo azilangiza ana awo ndi kuwawongolera
[Chithunzi patsamba 17]
Atate wachikondi amasamalira banja lake kuthupi ndi kuuzimu