Phunziro 33
Kuonetsa Kutengeka Mtima ndi Mzimu Waubwenzi
1. N’chiyani chingapatse munthu kutengeka mtima?
1 Kutengeka mtima ndiko moyo wa nkhani. Ngati zimene mukulankhulazo sizikutengani mtima, omvetsera anunso adzachita mphwayi. Ngati zimene mukulankhula sizikukhudzani, iwonso siziwakhudza. Koma kuti inuyo monga mlankhuli muonetse nsangala yeniyeni, muyenera kukhala wotsimikiza kuti n’kofunikadi kuti omvetsera anu amve zimene mukufuna kulankhula. Zimenezo zikutanthauza kuti munawaganizira pokonzekera nkhani yanu, mukumasankha mfundo zowapindulitsa kwambiri, ndi kuzikonza m’njira yoti omvetsera anu ayamikire phindu lake. Ngati mwachita zimenezo, mudzakhala wosonkhezereka kulankhula mogwira mtima, ndipo omvetsera anu adzalabadira.
2-5. Kodi kulankhula kwaumoyo kumasonyeza motani kutengeka mtima?
2 Kuonetsa kutengeka mtima mwa kalankhulidwe kaumoyo. Kaŵirikaŵiri kutengeka mtima kumaonekera mwa kalankhulidwe kanu kaumoyo. Simuyenera kukhala wamphwayi ndi wozizira. Muyenera kukhala waumoyo ndi nkhope yomwe, mawu anu ndi kalankhulidwe kanu. Zimenezo zikutanthauza kuti muyenera kulankhula ndi nyonga komanso ndi mphamvu. Muyenera kumveka wokhutira ndi zimene mukunena koma osati wolamula. Ngakhale kuti muyenera kukhala wotengeka mtima, musatengeke mopambanitsa. Kutaya kudziletsa kumakhalanso kutaya omvetsera anu.
3 Kutengeka mtima kumayambukira. Ngati muli wotengeka mtima ndi nkhani yanu, omvetsera anu adzatengekanso mtima. Ndiponso, mwa kuyendera limodzi ndi omvetsera, iwonso adzaonetsa kutengeka mtima. Koma, ngati muli wozizira, omvetsera anunso adzazizira limodzi nanu.
4 Paulo anati tiyenera kukhala achangu mu mzimu wa Mulungu. Ngati inuyo muli wachangu, kalankhulidwe kanu kaumoyo kadzapangitsa mzimu wa Mulungu kusonkhezera omvetsera kuchitapo kanthu. Apolo anaonetsa mzimu umenewo m’kalankhulidwe kake, ndipo amatchedwa mlankhuli waluso.—Aroma 12:11; Mac. 18:25; Yobu 32:18-20; Yer. 20:9.
5 Kuti mukhale wotengeka mtima ndi nkhani muyenera kukhala wokhutira kuti muli ndi uthenga wofunikira kugaŵira ena. Konzanibe nkhani imene mukukailankhula kufikira mutaona kuti yafika poti ikakulimbikitsani ndi inu nomwe wolankhula. Siichita kufunikira kukhala nkhani yatsopano, koma njira imene mukaiperekera ingakhale yatsopano. Ngati mukuona kuti muli ndi mfundo zimene zikalimbikitsa omvetsera anu m’kulambira kwawo, zimene zidzawathandiza kukhala alaliki kapena Akristu abwino, pamenepo muli ndi chifukwa chabwino chokhalira wotengeka mtima ndi nkhani yanu, ndipo mosakayika konse mudzatengekadi mtima.
6-9. Kodi kulankhula kwaumoyo kumadalira motani mfundo za m’nkhani yanu?
6 Kutengeka mtima koyenerana ndi nkhani. Pofuna kukometsa nkhani yanu komanso kuti mupindulitse omvetsera, simuyenera kungoti yambeni nkhani yanu, basi uyo! mpaka kutsiriza muli wotengeka mtima chomwecho. Ngati mutero, omvetsera anu adzatopa asanayambe kugwirapo kanthu. Izi zikusonyezanso phindu lokonza nkhani yokhala ndi kusinthasintha kwa mitundu yonse kuti mukakhoze kusinthasintha polankhula. Zikutanthauza kuti mfundo zina zimene mukuzifotokoza mwachibadwa zimafuna kulankhula kwaumoyo kuposa zina, ndipo zifunika kuziika mwaluso m’malo osiyanasiyana m’nkhani yonse.
7 Makamaka mfundo zazikulu ziyenera kukambidwa mwaumoyo. Nkhani yanu iyenera kukhala ndi mokwera mwake, pachimake pamene mfundo zimakufikitsani. Popeza kuti mmenemo ndimo mokwera mwa nkhani yanu, kaŵirikaŵiri mudzakhala molimbikitsa omvetsera, momveketsera tanthauzo la mfundo zanu, zifukwa zanu kapena uphungu wanu. Mutakhutiritsa omvetsera, mufunikira kuwalimbikitsa, kuwasonyeza mapindu a mfundo zanuzo, madalitso ndi mwayi umene angaphulepo ngati atsata mfundo zimenezo. Zimenezo zimafuna kulankhula mwaumoyo.
8 Ngakhale ndi choncho, simuyenera konse kugwa mphwayi mutafika penapake m’nkhani yanu ndi kuyamba kulankhula mozizira. Simuyenera kutaya mzimu wa nkhani yanu kapena kuonetsa mphwayi. Yerekezani m’maganizo mwanu gwape amene alikudya udzu mwakachetechete pamalo poyera m’dambo. Ngakhale akuoneka wodekha, m’timinyendo takemo mwagona nyonga yamphamvu, imene ikhoza kum’lumphitsa ndi kuthaŵa kodetsa nkhaŵa atangoopsezedwa pang’ono. Inde, ali mtima phee koma watcheru nthaŵi zonse. Ndi mmenenso inu mungakhalire, ngakhale musakulankhula ndi umoyo wonse.
9 Kodi zonsezo zikutanthauzanji? Zikutanthauza kuti kulankhula kwaumoyo sikuchitika modziumiriza. Payenera kukhala chifukwa chake ndipo nkhani yanu ndiyo iyenera kukupatsani chifukwa chimenecho. Phungu wanu adzafuna kuona ngati kutengeka mtima kwanu kuli koyenerana ndi nkhani yanu. Kodi n’kopambanitsa, kochepa kwambiri kapena kosayenerera? N’zoona kuti iye adzaganiziranso za umunthu wanu, koma adzakulimbikitsani ngati muli wamanyazi ndi wosamasuka kwambiri. Komanso adzakuchenjezani ngati aona kuti mukutengeka maganizo kwambiri pachilichonse chimene munena. Choncho kutengeka kwanu kuyenerane ndi nkhani yanu ndipo siyanitsani mfundo zanu kuti kalankhulidwe kanu kakhale kosinthasintha moyenerera.
**********
10-12. Kodi mzimu waubwenzi ndi wachifundo n’chiyani?
10 Kutengeka mtima kumafanana kwambiri ndi mzimu waubwenzi ndi wachifundo. Komabe, kuti zimenezo zionekere zimasonkhezeredwa ndi mikhalidwe yosiyana ndipo zimachititsa omvetsera kulabadira mosiyana. Monga mlankhuli, kaŵirikaŵiri mumakhala wotengeka mtima chifukwa cha nkhani yanu, koma mumakhala waubwenzi pamene muganiza za omvetsera anu ndi cholinga chanu chofuna kuwathandiza. “Mzimu waubwenzi ndi wachifundo,” zimene zaikidwa pasilipi la Uphungu wa Kulankhula, n’zofunika kuzipenda mosamalitsa.
11 Ngati muonetsa ubwenzi ndi chifundo, omvetsera anu adzaona kuti ndinu munthu wachikondi, wokoma mtima ndi womvera ena chisoni. Iwo adzakopeka monga mmene timakopekera ndi moto kukazizira. Nkhani yokambidwa mwaumoyo imalimbikitsa, komanso kusonyeza chifundo n’kofunika. Si nthaŵi zonse pamene kukopa maganizo kumakhala kokwanira, muyeneranso kusonkhezera mtima.
12 Mwachitsanzo, kodi kungakhale koyenerera kuŵerenga Agalatiya 5:22, 23 ponena za chikondi, kuleza mtima, kukoma mtima ndi chifatso popanda kuonetsa mzimu wa mikhalidweyo m’njira inayake? Onaninso, chifundo chosonyezedwa m’mawu a Paulo pa 1 Atesalonika 2:7, 8. Ameneŵa ndi mawu ofuna kusonyeza mzimu waubwenzi ndi wachifundo powatchula. Kodi tingausonyeze motani?
13, 14. Kodi mzimu waubwenzi tingausonyeze motani pankhope?
13 Mzimu waubwenzi uonekera pankhope. Ngati muli ndi mzimu waubwenzi kwa omvetsera anu, uyenera kuonekera pankhope panu. Ngati suonekera pankhope, omvetsera anu sangakhutire kuti mulidi waubwenzi kwa iwo. Koma uyenera kukhala mzimu weniweni waubwenzi. Suyenera kukhala wachiphamaso. Ndiponso tisaganize kuti ubwenzi ndi chifundo ndizo kutengeka maganizo kapena kungokhudzika mtima. Nkhope yokoma mtima imasonyeza kuona mtima.
14 Nthaŵi zambiri mudzalankhula kwa anthu aubwenzi. Chifukwa chake, ngati muyang’anitsitsa omvetsera anu mudzakopeka nawo. Mudzamva kukhala womasuka komanso bwenzi lawo. Sankhani wina mwa omvetserawo wa nkhope yaubwenzi. Lankhulani kwa iyeyo kwa timphindi pang’ono. Sankhaninso wina ndi kulankhulanso kwa iye. Zimenezo zidzapangitsa kuyendera limodzi ndi omvetsera, komanso mudzakopeka nawo, ndiponso nkhope yanu yaubwenziyo idzawakopanso kwa inu.
15-19. Tchulani zimene zingapangitse ubwenzi ndi chifundo kuonekera m’mawu a mlankhuli.
15 Mzimu waubwenzi ndi wachifundo uonekera m’kamvekedwe ka mawu. Chakhala chotsimikizika kuti ngakhale nyama zikhoza kuzindikira chifundo chanu pamlingo wina wake mwa kamvekedwe ka mawu anu. Ngati zili choncho, kuli bwanji nanga za omvetsera anu! Ndithudi, iwo adzalabadira mawu omveka aubwenzi ndi achifundo.
16 Ngati mulibe chidwi kwenikweni kwa omvetsera anu, ngati mungoganiza kwambiri za mawu amene mukunena m’malo mwa mmene omvetsera anu adzalabadirira mawuwo, kudzakhala kovuta kuti zimenezo muzibise kwa omvetsera atcheru. Koma ngati muli ndi chidwi chachikulu kwa amene mukulankhula nawo ndipo ndinu wofunitsitsa kuwapatsa malingaliro anu kuti aganize mmene mukuganizira, chidwi chanucho chidzaonekera m’kusintha kulikonse kwa mawu anu.
17 Komabe, chidwi chimenecho chiyenera kukhala chenicheni. N’kosatheka kuti munthu angodziveka mzimu weniweni waubwenzi, monganso kutengeka mtima. Mlankhuli sayenera konse kuvala nkhope yokoma yachiphamaso. Ndipo ubwenzi ndi chifundo tisazisokoneze ndi kutengeka maganizo kapena chifundo chachiphamaso chongonjenjemetsa mawu.
18 Ngati mawu anu ndi ouma, omveka aukali, n’kovuta kuti musonyeze ubwenzi m’mawu anu. Muyenera kuyesetsa mwakhama kuti mugonjetse vuto limenelo. Chofunika ndi kusinthako kamvekedwe ka mawu, ndipo kumatenga nthaŵi, koma khama loyenera lingakuthandizeni kwambiri kupangitsa mawu anu kumveka aubwenzi.
19 Chinthu chimodzi chimene chingakuthandizeni pakamvekedwe kokha ka mawu ndicho kukumbukira kuti kutchula mawu kofupikitsa mavawelo n’kumene kumapangitsa kulankhula kumveka kouma. Phunzirani kutalikitsako mavawelo. Kuteroko kudzawafeŵetsa ndipo mwachibadwa kudzapangitsa mawu anu kumvekerapo aubwenzi.
20, 21. Kodi mfundo za m’nkhani zimalimbikitsa motani mzimu waubwenzi ndi chifundo polankhula?
20 Mzimu waubwenzi ndi wachifundo woyenerana ndi nkhani. Mofanana ndi kutengeka mtima, mzimu waubwenzi ndi chifundo umene mumaika m’mawu anu umadalira kwambiri zimene mukunena. Chitsanzo cha zimenezi ndi nkhani ya Yesu pamene anadzudzula alembi ndi Afarisi pa Mateyu 23. Sitingamuyerekeze iye akulankhula mawu oŵaŵa achidzudzulo ameneŵa m’njira yamphwayi ndi yozizira. Koma m’katikati mwa mawu a kunyansidwa ndi aukali amenewo tikupezamo mawu ena odzaza mzimu waubwenzi ndi chifundo cha Yesu pamene anati: “Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m’mapiko ake, koma inu simunafuna ayi!” Apa tikuona kusonyezedwa kwa chifundo chomvera chisoni. Koma mawu otsatira akuti: “Onani, nyumba yanu yasiyidwa kwa inu yabwinja,” sali ndi mzimu wofananawo. Akumveka otsutsa ndi a kunyansidwa.
21 Nangano ndi pati pamene mzimu waubwenzi ndi wachifundo zingakhale zoyenerera? Zambiri zimene munganene mu utumiki wakumunda kapena m’nkhani ya wophunzira zingayenere mzimu umenewo, koma makamaka pokambirana, polimbikitsa, polangiza, popepesa, ndi zina zotero. Pokumbukira kukhala waubwenzi, musaiŵale kukhala wotengeka mtima ngati kuli koyenerera. M’zinthu zonse musachite mopambanitsa, koma polankhula zilizonse onetsani mzimu wake wonse.