Mutu 16
Kupanga Dziko Limodzi Pansi pa Ufumu wa Mulungu
1. Malinga ndi kunena kwa atsogoleri a dziko, kodi ndi zosankha ziwiri zotani zimene tsopano zikuyang’anizana ndi anthu?
KUKUFIKIRA kukhala koonekera bwino moonjezereka-onjezereka kuti anthu onse ali dziko limodzi ndipo ayenera kugwirizana pamodzi monga dziko limodzi ngati iwo ati apulumuke. Atsogoleri ambiri a dziko akuzindikira kwambiri cheni-cheni chimene’chi. Mwa chitsanzo, zaka zingapo zapita’zo, Prezidenti Ferdinand E. Marcos wa Philippine Republic anauza Msonkhano wa Onse wa Mitundu Yogwirizana kuti:
“Zobvuta za chisungiko cha dziko ndi chitukuko . . . ziri za pa dziko lonse lapansi mu ukulu wake ndipo zimagogomezera m’kutsatizana-tsatizanakwa mabvuto cheni-cheni chimodzi chachikulu cha kukhalako kwathu; chakuti dziko lathu-li ndi limodzi, m’ntchito zaluso, m’chuma, m’kukhoza kuonongedwa ndi zida zankhondo za atomeki, m’nkhondo ya nthawi yaitali, m’choikidwiratu chotsirizira cha mitundu ya anthu.”
Posachedwapa, nduna yaikulu ya Japan, Takeo Miki, inalengeza kuti:
“Dziko lirinkuchepa-chepa ndipo anthu onse ali ndi tsoka limodzi-modzi m’chombo chimodzi-modzi chimene akwera . . . Komabe, motimvetsa chisoni, dziko silinafikebe pa malo amene. . . kudalirana kukuzindikiridwa mokwanira. Ngati mkhalidwe umene’wu upitirizabe, kuli koonekera bwino kuti posachedwapa m’tsogolo muno tidzaonongeka.”
Zosankha’zo ziri zoonekera bwino kwa anthu ambiri olingalira: “Kugwirizanitsa anthu kukhala dziko limodzi, kapena kulola “mitundu ya anthu” kuonongeka.
2. Kodi n’chiani chimene chiri chiyembekezo chokha chogwirizanitsira anthu, ndipo chifukwa ninji? (Salmo 68:20)
2 Kodi ndi gulu la anthu lotani limene liripo pa dziko lapansi lero lino limene lingathe kugwirizanitsa anthu onse kukhala dziko limodzi? Ngakhale Mitundu Yogwirizana singathe kuyamba kusenza ntchito imene’yo. Chifukwa chake chiri choonekera bwino. Ngati anthu ati agwirizanitsidwe, kuyenera kukhala pansi pa ulamuliro wa Mulungu. Monga momwe’di chilengedwe chopanda malekezero’cho chikugwirizanitsidwira pamodzi ndi malamulo a chilengedwe a Yehova, chotero anthu, m’malo mwakuti apulumuke ndi kusangalala ndi mtendere ndi chimwemwe, ayenera kugwirizanitsidwa pansi pa malamulo a makhalidwe abwino a Mulungu.
3. (a) Kodi ndi njira yotani imene Yehova akugwiritsira ntchito kubwezeretsa umodzi ku chilengedwe chonse? (Danieli 7:13, 14) (b) Kodi Mfumu Davide anakweza ulamuliro wa yani, ndipo kodi ife tingagwirizane naye m’chilengezo chake chotani?
3 Njira imene Yehova akugwiritsira ntchito kubwezeretsera umodzi ndi mtendere m’chilengedwe chonse ndiyo ufumu Waumesiya wa Kristu Yesu. Umene’wu ndi ulamuliro waufumu wogwira ntchito pansi pa ulamuliro wa Yehova, koma nthawi zonse womakweza ufumu wapamwamba wa Mulungu. Ngakhale kuli kwakuti iye mwini anali mfumu yamphamvu, Davide analengeza kuti:
“Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi kulakika, ndi chifumu ndi zanu, Yehova; pakuti zonse zam’mwamba ndi pa dziko lapansi ndi zanu; ufumu ndi wanu, Yehova; ndipo mwakwezeka mutu wa pa zonse. Zolemera ndi ulemu zifuma kwanu, ndipo muchita ufumu pa zonse, ndi m’dzanja mwanu muli mphamvu yaikulu; kukuza ndi kupatsa onse mphamvu kuli m’dzanja lanu. Motero tsono, Mulungu wathu, tikuyamikani ndi kulemekeza dzina lanu lokoma.” (1 Mbiri 29:11-13)
Pamene tsopano tikupenda chifuno cha Yehova ponena za ufumu wake, tiyenera, mofanana ndi Davide, kufuna kuthokoza ndi kutamanda Iye kaamba ka chimene Iye akutichitira.
UFUMU MU ULOSI
4.Kodi ulamuliro wa Yesu ukufanana ndi uja wa Davide ndi wa Solomo m’njira zotani? (Chibvumbulutso 19:11; Yesaya 9:6)
4 Mngelo Gabrieli ponena za Yesu anati: “Ambuye Mulungu adzam’patsa Iye mpando wachifumu wa Davide atate wake [wakale] . . . ndipo ufumu wake sudzatha.” Ndipo’nso, Yesu anadzinena yekha kukhala “woposa Solomo [mwana wa Davide].” (Luka 1:32, 33; 11:31) Monga mfumu yomenya nkhondo, Davide anafutukula malire a Israyeli mpaka kukafika ku malire a dziko limene Yehova analonjeza anthu Ake, ndiyeno Mfumu Solomo analamulira kwa zaka zaulemerero makumi anai za mtendere pa mtundu wolemerera:
“Ayuda ndi Aisrayeli anachuluka ngati mchenga wa kunyanja, namadya namamwa namakondwera.” (1 Mafumu 4:20)
Koma wankhondo wamkulu kwambiri koposa Davide, Yesu adzatuluka “kukagonjetsa ndi kutsiriza kugonjetsa kwake” dziko lonse loipa. Pamenepo ndi ulamuliro wabwino kopambana ndi wanzeru kopambana woposa wa Solomo iye adzalamulira mu mtendere “kwa zaka chikwi.” (Chibvumbulutso 6:2, NW; 20:4) Ha, ndi nthawi yosangalatsa chotani nanga imene anthu onse adzasangalala nayo pamene Kristu yesu alamulira monga Mfumu pa dziko lapansi la paradaiso!
5. Kodi ndi kukwaniritsidwa kwa maulosi otani kumene kukudziwikitsa Yesu kukhala Mesiya? (Luka 24:25-27)
5 Aneneri ambiri okhulupirika a Mulungu anasonyeza m’tsogolo ku ufumu Waumesiya. Kweni-kweni mazana ochuluka a maulosi ao anakwaniritsidwa mwa Yesu, motero kutumikira kum’dziwikitsa bwino lomwe kukhala Mesiya wolonjezedwa. Mwa chitsanzo, amene’wa ananeneratu kuti iye akabadwa mwa namwali mu mzinda wa Betelehemu, kuti iye akanyozedwa, kusautsidwa ndi kukhomeredwa pa mtengo, ndi kuti iye akauka’nso pa tsiku lachitatu.
6. Kodi ndi motani m’mene Yesu anadziwikitsidwira kukhala Mfumu? (Mateyu 21:4-9)
6 Zobvuta zimene Yesu anakumana nazo “sizikangochitidwa” kweni-kweni kokha kuti zipangitse maulosi akale kukwaniritsidwa. Zizunzo zankhanza zimene anthu a mtundu wa yesu anaziunjika pa iye zinali zeni-zeni, ndipo umphumphu wa Yesu mochirikiza ulamuliro wa Yehova unali weni-weni. Zonse’zi zinam’tsimikizira kukhala Mesiya wolonjezedwa. Pamene anali kuweruzidwa pamaso pa Pilato, yesu anabvomereza kuti iye, Yesu, anali “mfumu,” koma anamveketsa bwino lomwe kuti ufumu wake suli “mbali ya dziko lino.” Pamenepo Pilato analemba chikwangwani choti aike pa mtengo wozunzirapo’wo chakuti: “yesu Mnazara’yo, Mfumu ya Ayuda.” (Yohane 18:36, 37, NW; 19:19) Komabe, ufumu wa Yesu unali ukadali m’tsogolo.
7. (a) Kodi ndi motani m’mene Salmo 110:1 linakwaniritsidwira? (Ahebri 12:2) (b) Kodi malo a ntchito a Yesu ndi otani lero lino? (Chibvumbulutso 12:10)
7 Chifukwa chakuti Yesu anasonyeza umphumphu kufikira imfa, Mulungu tsopano anamuukitsa mu mzimu ndi kum’kwezera ku dzanja lake lamanja la chiyanjo kumwamba. Mtumwi Petro anasonyeza m’mene zimene’zi zinakwaniritsirira ulosi wa Davide pa Salmo 110, kuti:
“Davide sanakwera Kumwamba ai; koma anena yekha, Ambuye anati kwa Mbuye wanga, Khalani ku dzanja lamanja langa, kufikira ndikaike adani ako chopondapo mapazi ako. Pamenepo lizindikiritse ndithu banja liri lonse la Israyeli, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Kristu, Yesu amene inu munam’pachika.” (Machitidwe 2:34-36)
“Yesu” uyu sali’nso khanda modyera ng’ombe. Ndipo’nso sali wofera chikhulupiriro wopanda chithandizo wokhomerezedwa pa mtanda. Ai, iye tsopano ali “mbuye wa ambuye ndi Mfumu ya mafumu” wamphamvu amene Yehova adzam’gwiritsira ntchito m’kubwezeretsa ulamuliro wake m’chilengedwe chonse.—Chibvumbulutso 17:14.
UFUMU UKULAMULIRA MU MPHAMVU
8. Kodi ndi chilgengezo chachikulu chotani chimene chikusimbidwa pa Chibvumbulutso 11:15-18?
8 M’malo kwakuti usonyeze ulamuliro wa Mulungu, Ufumu’wo uyenera kusonyeza mphamvu yeni-yeni. Nthawi yake tsopano yakwana! Iri nthawi pamene “ufumu wa dziko” ukukhala “ufumu wa Ambuye wathu [Yehova] ndi wa Kristu wake, ndipo adzalamulira monga mfumfu ku nthawi za nthawi.” Ponena za nthawi yosangalatsa imene’yi chilengezo chikupangidwa kumwamba kweni-kweni’ko kuti:
“Tikuyamikani, Yehova Mulungu, Wamphamvuyonse, amene muli ndi amene munali, chifukwa mwatenga mphamvu yanu yaikulu ndi kuyamba kulamulira monga mfumu. Koma mitundu inakwiya, ndipo mkwiyo wanu unafika, ndi nthawi yoikidwiratu ya akufa kuti aweruzidwe, ndi kupereka mphotho kwa akapolo anu aneneri ndi kwa oyera mtima ndi kwa iwo akuopa dzina lanu, ang’ono ndi akulu, ndi kuononga awo oononga dziko.”—Chibvumbulutso 11:15-18, NW.
9. Kodi n’chiani chimene chikutsimikizira kuti Yehova watenga mphamvu yake mwa ufumu wa Kristu? (Chibvumbulutso 6:3-8)
9 Kodi zonse’zi zikuchitika liti? Eya, kodi ndi liti mwapadera m’mbiri ya anthu pamene mitundu inakwiya motsutsana ndi kulengezedwa kwa Ufumu’wo ndi kuyamba kuononga dziko lapansi? Kodi sindimo m’zaka zino za zana la makumi awiri, ndipo makamaka kuyambira pa Nkhondo Yoyamba ya Dziko mu 1914, chakuti dziko lapansi lakanthidwa ndi chiwawa ndi kuipitsa pa mlingo wa m’mitundu yonse? Ndithudi ziri choncho. Pali umboni wina’nso wochuluka, wakuti Yehova anatenga mphamvu yake yaikulu ndi kuyamba kulamulira pa dziko lapansi kupyolera mwa Ufumu wa Kristu m’chaka chimene’cho cha 1914. Monga momwe Davide ananeneratu ponena za “Ambuye” Yesu Kristu tsopano wakonzekera ‘kuchita ufumu pakati pa adani ake.’—Salmo 110:1, 2.
10. (a) Kodi ndi ulosi wotani woperekedwa ndi Yesu umene ukukwaniritsidwa chiyambire 1914 kumkabe m’tsogolo, ndipo motani? (Luka 21:10, 11, 25, 26, 28) (b) Kodi ndi ntchito yapadera yotani imene inanenedweratu kaamba ka nthawi imodzi-modzi’yi? (Marko 13:10)
10 Komabe, choyamba, pali ntchito ya Ufumu yoti ichitidwe pano pa dziko lapansi. Yesu ananeneratu zimene’zi zaka mazana khumi ndi asanu ndi anai zapita’zo pamene ophunzira ake anam’funsa kuti, “Kodi n’chiani chimene chidzakhala chizindikiro cha kukhala kwanu pafupi [m’mphamvu ya Ufumu] ndi cha mapeto a dongosolo la zinthu?” M’yankho lake, Yesu analongosola nkhondo za dziko, kuperewera kwa zakudya, zibvomezi zazikulu, miriri, kusaweruzika, zizunzo, kuchita mantha ndi kubvutika kwa mitundu zimene zakantha anthu chiyambire 1914. Pamenepo iye anapitiriza kunena kuti:
“Mbiri yabwino imene’yi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni ku mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika . . . Pakuti pa nthawi imene’yo kudzakhala chisautso chachikulu chimene sichinachitike chiyambire chiyambi cha dziko kufikira tsopano, inde, ndipo sichidzachitika’nso. Kunena zoona, ngati akadapanda kufupikitsidwa masiku amene’wo, palibe munthu ali yense akadapulumutsidwa; koma chifukwa cha osankhidwa’wo masiku amene’wo adzafupikitsidwa.”—Mateyu 24:3-14, 21, 22, NW.
11. (a) Kodi umboni’wo wakhala waukulu motani, ndipo kodi n’chiani chimene chikutulukapo? (b) Kodi anthu ena adzapulumuka “chisautso chachikulu”? (Zefaniya 2:3)
11 M’kukwaniritsidwa kwa ulosi umene’wu, mboni Zachikristu za Yehova, chiyambire 1914, zakhala zikulengeza pa dziko lonse lapansi kuti Kristu wafika m’mphamvu ya Ufumu. Umboni umene’wo walowa m’zisumbu za nyanja, mpaka m’maiko oletsa kugawana chidziwitso ndi oletsa kulowamo kwa mabukhu ndi kulowa m’maiko odetsedwa ndi timagulu ta chipembedzo ta “Babulo Wamkulu.” Chotero tsopano “mapeto”—“chisautso chachikulu”—atsala pang’ono kudza. Koma “anthu” ena ochokera mwa mtundu wa anthu adzapulumuka!
12. Kodi “chisautso chachikulu” chikudza motani, ndipo limodzi ndi zochitika zotani? (Chibvumbulutso 17:16; 19:19-21)
12 Kodi ndi motani m’mene “chisautso chachikulu” chikuchitikira? Yesu akunena kuti chikudza mwadzidzidzi, monga mbala, m’kati mwa “mbadwo” wa awo amene aona kukwaniritsidwa kwa “chizindikiro” lero lino. (Mateyu 24:34) Monga momwe Chibvumbulutso chaputala 16 kufikira 19 chimalongosolera, Yehova akugwiritsira ntchito maulamuliro otsutsana onga chirombo a m’kati mwa Mitundu Yogwirizana monga ziwiya zake m’kupasula ufumu wa pa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga, “BabuloWamkulu.” Ndiyeno, pa mkhalidwe wa pa dziko lonse wochedwa Harmagedo, Kristu Yesu adzamenya “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse” yotha makani yolimbana ndi “mafumu [olamulira] a dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu.”—Chibvumbulutso 16:14, 16, NW.
13. (a) Kodi ndi motani m’mene Yehova akuchirikizira ulamuliro wake? (Yesaya 26:20, 21) (b) Kodi Mulungu akulinganiza kugwirizanitsa anthu onse kukhala dziko limodzi mwa njira yotani? (Yesaya 9:7)
13 Mneneri Danieli akulongosola maulamuliro a ndale za dziko a dziko lapansi amene’wa monga fano lalikulu, ndipo ufumu wa Kristu monga mwala umene Yehova akuusema m’phiri la ulamuliro Wake wa chilengedwe chonse. Mwala umene’wu Iye akuuponyera ku mapazi a fano’lo, kotero kuti aliphwanye ndi kulipera ngati ufa. (Danieli 2:31-35) Polongosola kachitidwe kamene’ka motsutsana ndi olamulira oipa, Danieli akupitirizabe, kuti:
“Masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzaonongeka ku nthawi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu ao onse, nudzakhala chikhalire.” (Danieli 2:44, 45)
Chotero ufumu wa Kristu ukuchirikiza ulamuliro wa Mulungu wa m’chilengedwe chonse kwa nthawi yonse! Mfumu’yo pamenepo ikuponya pansi Satana ndi angelo ake auchiwanda “mphompho” la kusayendayenda, ndipo ikulowa mu ufumu Wake wamtendere wa zaka chikwi umene potsirizira pake udzagwirizanitsa anthu onse monga dziko limodzi. Ha, mitima yathu ikukondwa chotani nanga ndi chiyembekezo cha zochitika zazikulu zimene’zi zimene “Mulungu wamkulu iye mwini’yo” akulinganiza kaamba ka m’tsogolo muno posachedwapa!—Chibvumbulutso 20:2, 3.
[Bokosi/Chithunzi pamasamba 148-149]
“CHIZINDIKIRO” CHA KUKHALA PAFUPI KOSAONEKA KWA MFUMU YATSOPANO YA DZIKO LAPANSI
(Mateyu 24:3-25:46; Luka 21:7-36)
“Mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina.” ‘Kusaweruzika kudzachuluka.’ (Mateyu 24:7,12)
Nkhondo Yoyamba ya Dziko mu 1914 inayambitsa “zaka za zana la nkhondo yotheratu”; mamiliyoni 69 anafa m’nkhondo za dziko ziwiri. Kuonjezeka kochititsa mantha kwa upandu kwatsatirapo.
“Kudzakhala zibvomezi zazikulu, ndi njala ndi miriri m’malo akuti akuti.” (Luka 21:11; Mateyu 24:7)
Chiyambire 1914, anthu 700,000 afa m’zibvomezi; mamiliyoni 21 anafa mu 1918-1919 ndi ‘Folowenza,’ ndipo mamiliyoni oposa 1,000 tsopano lino akubvutika ndi njala kapena ali osadya mokwanira. Mitengo ya zakudya ikukwera-kwera.
“Pa dziko lapansi chisauko cha mitundu ya anthu, alikuthedwa nzeru . . anthu akukomoka ndi mantha.” (Luka 21;25, 26)
Nyumba zosungiramo zida za nyuklea zophatikizidwa pamodzi za United States ndi Soviet zokha ziri ndi mabomba olingana ndi matani 5 a mphamvu yophulika kaamba ka munthu ali yense pa dziko lapansi. New York “Times” ya March 1, 1976, inali ndi mitu ya nkhani yakuti: “Ndalama za Dziko Zoonongeredwa pa Zida za Nkhondo pa Muyeso Waukulu Kopambana . . . Ndalama Zoonongedwa za Chaka ndi Chaka ziri pa madola mabiliyoni 300 . . . Mpikisano [wa Zida za nkhondo] ‘uli Wosaletseka.’’
“Mbiri yabwino imene’yi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni ku mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14, NW)
Mboni za Yehova zoposa mamiliyoni 2, tsopano ziri zokangalika m’maiko 210 ndi zigawo pa dziko lonse lapansi, zikuchititsa maphunziro a Baibulo m’nyumba zoposa 1,400,000 mlungu ndi mlungu. Chiyambire 1942 Mboni zodzipereka zapanga kuti agawiridwe m’munda Mabaibulo ndi mabukhu ophunzirira Baibulo mamiliyoni 415 ndi makope a magazini a “Nsanja ya Olonda” ndi “Galamukani!” mamiliyoni 5,950.
[Chithunzi]
Pakitale yosindikizira ya Watchtower Brooklyn, N.Y.
“Poyamba kuchitika izi weramukani, tukulani mitu yanu; chifukwa chiomboledwe chanu chayandikira.—Luka 21:28.
[Tchati patsamba 145]
(Onani m’buku lenileni kuti mumvetse izi)
M’MENE MESIYA ANAKWANIRITSIRA ULOSI WA BAIBULO
Ulosi Zinthu Zonenedweratu Kukwaniritsidwa Konenedwa
Maulosi m’Masalmo
Salmo 2:1, 2 Olamulira achita Mateyu 27:1, 2
motsutsana ndi Wodzozedwa
Salmo 16:10 Aukitsidwa asanabvunde Machitidwe 2:24, 27
Salmo 22:1 Akusiyiridwa kwa adani Mateyu 27:46
ndi Mulungu
Salmo 22:7, 8 Yesu akutonzedwa Mateyu 27:39-43
ali pa mtengo
Salmo 22:16 Anapachikidwa ndi manja Yohane 20:25
ndi mapazi
Salmo 22:18 Malaya ake Mateyu 27:35
akuchitiridwa maere
Salmo 27:12 Mboni zonama zom’tsutsa Mateyu 26:59-61
Salmo 34:20 Palibe liri lonse la Yohane 19:33, 36
mafupa a Yesu likuthyoledwa
Salmo 41:9 Mtumwi wosakhulupirika Yohane 13:18, 21-30
apereka
Salmo 69:4 Yesu anadedwa Yohane 15:24, 25
popanda chifukwa
Salmo 69:9 Wachangu kaamba ka Yohane 2:13-17
nyumba ya Yehova
Salmo 69:21 Ananinkhidwa vinyo Marko 15:23, 36
wosanganiza ndi mure
Salmo 78:2 Yesu alankhula Mateyu 13:34, 35
m’mafanizo
Salmo 118:22 Anakanidwa, koma maziko Mateyu 21:42-44
otsimikizirika
Ulosi wa Yesaya
Yesaya 7:14 Yesu anabadwa mwa Mateyu 1:23-25
namwali
Yesaya 9:1, 2 Kuunika m’Nafitali, Mateyu 4:13-16
Zebuloni
Yesaya 9:7 Mbadwa, wolowa nyumba Mateyu 1:1, 6-17
wa Davide
Yesaya 40:3 Yohane M’batizi Mateyu 3:1-3
akonza njira
Yesaya 42:1-4 Sakufuula m’makwalala Mateyu 12:14-21
Yesaya 53:1, 2 Ayuda sakum’khulupirira Yohane 12:37, 38
Yesaya 53:4 Akusenza zowawa za anthu Mateyu 8:16, 17
Yesaya 53:7 Anakhala chete Mateyu 27:11-14
pa om’tsutsa
Yesaya 53:9 Anaikidwa pa malo amodzi Mateyu 27:57-60
ndi olemera
Yesaya 53:11 Akusenza zolakwa Mateyu 20:28
za ambiri
Yesaya 53:12 Anawerengeredwa limodzi Luka 22:36, 37, 52
ndi ochimwa
Yesaya 61:1, 2 Anadzozedwa ndi mzimu Luka 4:16-21
kulalikira
Maulosi Ena
Genesis 49:10 Wolamulira wotuluka Luka 3:23-33
m’pfuko la Yuda
Yeremiya 31:15 Makanda anaphedwa Mateyu 2:16-18
pambuyo pa kubadwa
Danieli 9:25 Akuonekera pambuyo Luka 3:1, 21,22
pa “masabata 69”
Danieli 9:26, 27 Akudulidwa pambuyo pa Yohane 19:14-16
zaka 31/2
Hoseya 11:1 Anaitanidwa ku malo Mateyu 2:14, 15
othawira m’Igupto
Yona 1:17 Anaukitsidwa pa Machitidwe 10:40, 41
tsiku lachitatu
Mika 5:2 Anabadwira m’Betelehemu Mateyu 2:1-6
wa Yuda
Zekariya 9:9 Akulowa mu mzinda Mateyu 21:7-11
atakwera pa mwana wa bulu
Zekariya 11:12 Anaperekedwa kaamba ka Mateyu 26:15
ndalama za siliva 30
Zekariya 12:10 Anapyozedwa pamene anali Yohane 19:34
pa mtengo wozunzirapo
Zekariya 13:7 Mbusa akanthidwa, Mateyu 26:31, 56
nkhosa zibalalika