Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gh mutu 19 tsamba 166-173
  • Ana—“Cholandira cha kwa Yehova”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ana—“Cholandira cha kwa Yehova”
  • Mbiri Yabwino Yokusangalatsani
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KUPANGA ANA KUKHALA “ANZERU KAAMBA KA CHIPULUMUTSO”
  • PAMENE ANA AKUKULA
  • Phunzitsani Mwana Wanu Kuyambira Paukhanda Wake
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Kumanga Banja Lolimba Mwauzimu
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Ana Athu Ndi Cholowa Chamtengo Wapatali
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Makolo Phunzitsani Ana Anu Mwachikondi
    Nsanja ya Olonda—2007
Onani Zambiri
Mbiri Yabwino Yokusangalatsani
gh mutu 19 tsamba 166-173

Mutu 19

Ana—“Cholandira cha kwa Yehova”

1. Kodi ndi motani m’mene makolo ndi ana ayenera kuonanira? (Salmo 128:1, 3, 4)

MFUMU Solomo analongosola ana kukhala “mphotho” ndi “cholandira cha kwa Yehova.” (Salmo 127:3) Ngati inu muli kholo, ndithudi mumaona ana anu kukhala chuma chamtengo wapatali! Ndipo ngati inu muli mwana, ndithudi mumafuna kupangitsa makolo anu kukhala osangalala ndi kukhala ndi moyo wachimwemwe ndi wopindulitsa limodzi nawo!

2. Kodi ndi thayo lotani limene ana ayenera kuona kukhala ali nalo kwa makolo, ndipo chifukwa ninji? (Eksodo 20:12)

2 Atatha kupereka chilangizo chothandiza kwa amuna ndi akazi, mtumwi Paulo anapitirizabe kulangiza ana ndi makolo, m’mau awa:

“Ana inu, mverani akubala inu m’zonse, pakuti ichi Ambuye akondwera nacho. Atate inu, musaputa ana anu, kuti angataye mtima.” (Akolose 3:20, 21)

Chotero, ana kumbukirani kuti makolo anu amakukondani, ndi kuti muyenera kuyesa kuwamvera m’zinthu za tsiku ndi tsiku za moyo. Ndipo makolo, thandizani ana anu kuona chikondi chanu kwa iwo, ndi kuti iwo ali mbali yofunika ya gulu la banja.

3. Kodi ndi liti ndipo ndi motani m’mene chiongolero chiyenera kuperekedwera? (Miyambo 13:24)

3 Ndithudi, pali nthawi zina, pamene mwana ali yense amafunikira chilango, ngakhale ndi ndodo yeniyeni, koma chimene’chi chiyenera kuchitidwa-ndipo osati kuchitidwa mopambanitsa-mwamphamvu ndi mwa chikondi, popanda kusonyeza kupsya mtima. Ana adzafikira pa kuzindikira chilango champhamvu choyenerera, ndipo sichidzawachititsa ‘kutaya mtima.’ Iwo adzazindikira’nso, kukoma mtima ndi chisamaliro chachikondi chimene iwo amalandira pa nthawi zina.

KUPANGA ANA KUKHALA “ANZERU KAAMBA KA CHIPULUMUTSO”

4. (a) Kodi n’chiani chimene chinali chotulukapo cha kuphunzitsa Timoteo kwakhama kwa Yunike? (Machitidwe 16:1, 2) (b) Kodi mwana ayenera kuthandizidwa kudziwa “malemba opatulika” kuyambira pa usinkhu wotani? (Salmo 22:9, 10)

4 M’kalata yotsirizira yolembedwa atangotsala pang’ono kuphedwa, Paulo ananena motenthedwa maganizo za “chikhulupiriro chosanyenga” chimene mnzake wachinyamata Timoteo anachipeza kwa gogo wake loisi ndi mai wake Yunike, Wachiyuda. Ngakhale kuli kwakuti atate Wachigriki wa Timoteo anali wosakhulupirira, mai wake anayesa-yesa zolimba, monga momwe makolo onse okhulupirira ayenera kuchitira, m’kulera mwana wake m’chikhulupiriro. Osati kokha kuphunzitsa kwapakamwa, koma’nso chitsanzo choona mtima cha kholo m’kudzisungira nthawi zonse “mu mkhalidwe woyenera mbiri yabwino,” zidzapereka chitsanzo cha mkhalidwe wa mwana’yo. Kodi ndi kuyambira pa usinkhu wotani kumkabe m’tsogolo Timoteo analandira chilangizo chotero’cho? Paulo anam’lembera kuti “kuyambira ukhanda wako wadziwa malemba opatulika, amene ali okhoza kukupangitsa kukhala wanzeru kaamba ka chipulumutso mwa chikhulupiriro m’chigwirizano ndi Kristu Yesu.”​—2 Timoteo 1:5; 3:15; NW; Afilipi 1:27.

5. Kodi n’chifukwa ninji kuli kofunika kuika malingaliro a Mulungu mwa mwana kuyambira pa usinkhu wachichepere? (Luka 2:40)

5 Komabe, kodi mwana wakhanda ali wokhoza kumvetsetsa zinthu zauzimu? Inde, ali wokhoza! Talingalirani izi: Pa kubadwa ubongo wa mwana umakhala chigawo chimodzi chokha mwa zinai cha kulemera kwa ubongo wa wachikulire. Koma m’zaka ziwiri zokha ubongo umene’wo umakula mofulumira kwambiri kwakuti umafika zigawo zitatu mwa zinai za kulemera kwa wachikulire. M’nthawi yochepa imene’yo, mwana’yo amalandira chochuluka cha chidziwitso chamaziko chimene chidzam’yambitsa m’moyo, kuphatikizapo kuyamba ntchito yobvuta ya kuphunzira chinenero.

6. Kodi n’chiani chimene chidzathandiza makolo kufika mitima ya ana ao? (Miyambo 4:23)

6 Chiri chonse chimene khanda limamva ponena za nkhani zauzimu chimalandiridwa’nso! Ndipo limakhala ndi kufunikira chidziwitso cha zauzimu, pakuti munthu analengedwa “m’chifanizo cha Mulungu.” (Genesis 1:27) Ndicho chifukwa chake Mulungu amalangiza atate, pa Deuteronomo 11:18, 19 kuti: “Muzisunga mau anga awa mumtima mwanu ndi m’moyo mwanu . . . Ndipo muziwaphunzitsa ana anu.” Makolo angathandizidwe kufika mitima ya ana ao ngati iwo apereka chitsanzo chabwino m’kugwiritsira ntchito malamulo aumulungu a khalidwe labwino m’miyoyo ya iwo eni. Awo amene amaumba mitima ndi miyoyo ya ana ao “kuyambira pa ukhanda” adzakhala ndi mphotho yao!

7. (a) Kodi n’chifukwa ninji kuli kofunika kuononga nthawi limodzi ndi ana? (Miyambo 4:1-4) (b) Longosolani chokumana nacho chosonyeza m’mene makolo angapezere chisangalalo m’kuphunzitsa ana.

7Kodi ndi motani m’mene kumene’ku kungachitidwire? Mwina mwake anthu angaphunzire kuchokera kwa zinyama zina zimene nthawi zonse zimakhala ndi ana ao, kuwaphunzitsa ndi kuwalanga kaamba ka moyo. Palibe china cholowa m’malo mwa nthawi yoonongedwa limodzi ndi ana athu. Amai Akum’mawa amene ali ozolowera kubereka ana ao kumbuyo, ndi amene amalankhula nawo nthawi zonse pa mapewa ao pamene akuchita ntchito zao za panyumba ndi kupita ku msika kapena kukacheza, akhala ndi chipambano chabwino m’kukhomereza nkhani zopindulitsa pa ana ang’ono.

Mai wina anaphunzitsa khanda lake kuyimba, ndipo kenako kulowetsamo nkhani Zamalemba monga mau. Pofika pa nthawi imene khanda’lo linali ndi zaka ziwiri za kubadwa iro linali kutha kuyimba maina a mabukhu a Malemba Achikristu Achigriki. Pa usinkhu wa zaka ziwiri ndi miyezi itatu iro linali kutha kuyimba maina a mabukhu makumi asanu ndi limodzi mphambu asanu ndi limodzi kuyambira pa Genesis mpaka Chibvumbulutso. Pamene iye anaphunzira kubwereza mikhalidwe ya Mulungu ya nzeru, chiweruzo cholungama, mphamvu ndi chikondi, ndipo’nso zipatso zisanu ndi zinai za mzimu za pa Agalatiya 5:22, 23, imene’yi inakhomerezedwa pa iye mwa kum’phunzitsa m’mene angalongosolere uli wonse ndi zizindikiro zosonyeza zokhala ndi tanthauzo. Pamene mwana’yo anali “kuchita upainiya” ndi kukhalapo pa maphunziro a Baibulo m’nyumba za anthu okondwerera, chiyamikiro chake cha zinthu zauzimu chinaonjezeka mwezi ndi mwezi.

Makolo ena okhulupirira zikwi zambiri akhala ndi chisangalalo chofanana’cho m’kuphunzitsa ana ao ang’ono.

8. Kodi ndi motani m’mene makolo angakondweretsere ana m’ntchito ndi nzeru za Yehova? (Salmo 78:2-4)

8 Nkhani ya kuononga nthawi mopindulitsa ndi ana anu ikugogomezeredwa m’Malemba Achihebri. Motero, pamuyo pa kulongosola momvekera bwino lamulo lalikulu kopambana​—“Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse”​—Mose anapitiriza kuuza atate Achiisrayeli kuti:

“Mau awa . . . azikhala pamtima panu; ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.” (Deuteronomo 6:4-7)

Kuyambira pa nthawi ya kudzuka m’mawa kufikira pa nthawi ya kugona usiku, makolo angajpindulitse ana ao mwa kuwaphunzitsa, pamene kuli koyenera, ponena za nzeru yodabwitsa ya Yehova yoonekera bwino kwambiri m’zipatso za chilengedwe.

9. (a) Ponena za utali wa nthawi za phunziro, kodi n’chiani chimene kholo liyenera kukumbukira? (b) Kodi ndi motani m’mene mbiri yabwino ingaperekedwere kwa ana ake mu mkhalidwe wotsimikizira, ndipo limodzi ndi chonulirapo chotani? (Salmo 71:17, 18)

9 Komabe, kuyenera kukumbukiridwa kuti maganizo a ana amatopa msanga, ndi kuti ana amafuna nyengo za kusewera ndi kusangulutsa. Nthawi za phunziro la Baibulo ndi ana ang’ono zingapangidwe kukhala zosalinganizidwa, zachidule ndi zokondweretsa, koma pamene kuonedwa kuti maganizo ao akuyamba kuyenda-yenda, kungakhale bwino kwambiri kusiya chilangizo’cho kufikira pa nthawi ina. Kuli kofunika kwambiri kaamba ka chipambano kuti makolo onse ndi ana omwe apeze chisangalalo ndi chikondwerero m’zimene iwo akuphunzira. Makolo, kulitsani kukonda Mulungu m’mitima ya ana imene’yo! Musapangitse konse “mbiri yabwino” kuonekera ngati mpambo wa “musachite” ndi “a simuyenera kuchita.” M’malo mwake, thandizani ana anu kudalira Mulungu monga momwe’di iwo amadalirira inu, makolo ao a pa dziko lapansi, ndi kuyamikira ubwino Wake, kukoma mtima Kwake ndi kuolowa manja Kwake. M’kupita kwa nthawi iwo adzafuna kutumikira Yehova chifukwa cha chikondi ndi kuthokoza kaamba ka makonzedwe ake onse abwino kwambiri a moyo, tsopano ndi m’tsogolo.

10. Kodi ndi motani m’mene ana okhulupirira angapindulitsire kholo losakhulupirira? (Miyambo 10:1)

10 Ana amene ali ophunzitsidwa bwino mogwirizana ndi malamulo a khalidwe labwino a Baibulo angathe kukula kudzakhala thamo ndi chisangalalo kwa makolo okhulupirira. Ndipo kawiri-kawiri kholo losakhulupirira, poona mikhalidwe yabwino kwambiri imene chilangizo cha Baibulo chimakhomereza mwa mwana wake, lingasonkhezeredwe kukhala ndi chikondwerero ‘m’mbiri yabwino.’

Mutu wina wa banja unasimba zotsatirapo’zi pa tsiku la ubatizo wake: ‘Ndinali woyang’anira pa malo omangapo nyumba, koma madzulo ali onse ndinali kuledzera, ndipo kumene’ku kunayamba kuyambukira ntchito yanga. Mkazi wanga ndi ana anali kuphunzira ntchito yanga. Mkazi wanga ndi ana anali kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Usiku wina kamnyamata kanga, kosakwanira usinkhu wa zaka zisanu, mwadzidzidzi kanadza kwa ine, kanagoneka mutu wake paphewa langa, nakati: “Atate, usiku uli wonse mumakhala woledzera ndipo mumasuta fodya. Zimabvutitsa maganizo kwambiri amai ndi alongo anga, ndipo n’zodedwa kwambiri ndi Yehova Mulungu. Baibulo limanena kuti monga mwana ndiyenera kumvera atate wanga, ndi kuti atate ayenera kumvera Yesu Kristu. Chotero chonde phunzirani Baibulo monga momwe amachitira amai.” Kwa maora awiri iye analankhula mokakamiza kwa ine, ndipo anali ndi mkhalidwe wabwino wa maganizo. Chotero ndinalonjeza kuyesa kuphunzira. Mwamsanga pamene ndinayamba kuphunzira choonadi, ndinaona kuti ndikanatha kuleka njira zanga za kudzidalira ndi kukulitsa kudziletsa. Banja lathu linakhala malo abwino ndi achimwemwe.’

Zachitika kawiri-kawiri kuti wa mu ukwati wosakhulupirira wamvetsera mwana wophunzitsidwa bwino Baibulo ndi kukondweretsedwa.

PAMENE ANA AKUKULA

11. Kodi n’chifukwa ninji mabanja ayenera kufikira pamodzi pa misonkhano? (Salmo 84:4, 10-12)

11 Kwa mabanja a anthu a Mulungu, kufika kokhazikika kwa mlungu ndi mlungu pa misonkhano ya mpingo kumapereka chigwirizano chosangalatsa. Ndithudi, linali lamulo mu Israyeli, ‘kusonkhanitsa anthu, amuna ndi akazi ndi ana ang’ono . . . kuti amve, ndi kuti aphunzire.’ (Deuteronomo 31:12) Pamene ana akhala pambali pa makolo, akumayesa-yesa kumvetsera, kuphunzira ndi kukhala ndi phande m’misonkhano, timagulu ta banja tachimwemwe timathandizira kupanga mpingo Wachikristu wosangalala, wachikondi ndi wogwirizana.

12. (a) Kodi ndi chisamaliro chapadera chotani chimene makolo afunikira kutenga pamene ana ao alowa sukulu? (1 Akorinto 15:33) (b) Kodi ndi dalitso la nthawi yaitali lotani limene mwana wophunzitsidwa bwino angadzetse? (Deuteronomo 11:18-21)

12 Polowa sukulu, ana amakumana ndi mabwenzi atsopano ndipo’nso ziphunzitso, monga ngati chisinthiko, zimene zingatsutse Baibulo. Makolo afunikira kukhala ndi chisamaliro chapadera kuwatetezera ku zisonkhezero zolakwa, kukhala ndi chikondwerero m’ntchito zao zonse ndi kulingalira limodzi nao chimene chiri chabwino ndi chimene chiri choipa mogwirizana ndi malamulo a khalidwe labwino a Baibulo. Monga momwe Miyambo 22:6 imalongosolera kuti:

“Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.”

13. Monga momwe kwalongosoledwera m’bukhu’li, kodi ndi lingaliro labwino kwambiri lotani limene ana ophunzitsidwa Baibulo angapange?

13 Khalidwe labwino pa sukulu la ana ophunzitsidwa Baibulo nthawi zonse lapanga lingaliro labwino kwambiri, monga momwe lipoti lotsatirapo’li limasonyezera:

Tsiku lina pa sukulu mtsikana wina wa m’gredi lachisanu ndi chimodzi ndi mng’ono wake anaitanidwa ku ofesi wa aphunzitsi. M’menemo, aphunzitsi makumi asanu mphambu awiri, mwachionekere obvutika maganizo ndi kupulupuza koonjezereka pakati pa ophunzira, anawafunsa kwa maora awiri pamaso pa ophunzira anzao, kufufuza-fufuza mwapang’ono chiyambi chao cha kuphunzitsidwa Baibulo, ziletso zimene makolo ao anaika pa kuonera maprogramu a TV, kuwerenga mabukhu osangalatsa, ndi zina zotero. Potsirizira hedimasitala ananena kuti, “Ngati ana onse akanaphunzitsidwa ngati awo a Mboni za Yehova, tikanakhala ndi sukulu yabwino kwambiri, yopanda ana amene amabvutitsa anzao kapena kubwezera chipongwe.” Chotulukapo cha msonkhano umene’wu chinali chakuti mtsikana wachichepere’yo anali wokhoza kuyambitsa maphunziro a Baibulo makumi awiri mphambu asanu ndi limodzi ndi anzake ophunzira nao m’kalasi limodzi.

14. Kodi n’chiani chimene chimachitira umboni cheni-cheni chakuti kakonzedwe ka Mulungu kaamba ka mabanja kamagwira’di ntchito?

14 Banja limene liri logwirizana pa Baibulo, ndi limene limaika zabwino zauzimu choyamba m’moyo, liri lokonzekera bwino kwambiri kulimbana ndi ziyeso za “nthawi zowawitsa zobvuta kuchita nazo.” (2 Timoteo 3:1, NW) M’paradaiso wabwino kwambiri wauzimu amene tsopano akufutukukira ku malekezero a dziko lapansi, unyinji wa timagulu ta banja tochokera m’mitundu yonse, mafuko ndi anthu tingathe kuchitira umboni kuti kakonzedwe ka Yehova ka mabanja kamagwira’di ntchito, modzetsa dalitso kwa awo amene amam’konda! Iwo amatamanda Yehova monga Mutu wa “banja liri lonse kumwamba ndi “pa dziko lapansi,” ndipo akuyembekezera m’tsogolo ku kupereka kwake madalitso pa mabanja onse amene amachirikiza ulamuliro wake, kupyola kulowa m’dziko lapansi la paradaiso limene tsopano liri pafupi kwambiri.​—Aefeso 3:15.

[Chithunzi patsamba 167]

Maluso a mwana amakula mofulumira ngakhale kuyambira pa ukhanda

[Chithunzi patsamba 168]

Ana afunikira kudyetsedwa mwauzimu

[Chithunzi patsamba 170]

Onongani nthawi ndi ana anu. Kudzakhala kopindulitsa

[Chithunzi patsamba 173]

Achimwemwe ali mabanja awo amene amayesa-yesabe mogwirizana kumka ku moyo wamuyaya

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena