Mutu 6
Mpingo Wodzozedwera Kulengeza Ufumu
1. Kodi mafunso onena za chipulumutso cha dziko anali otani zaka zikwi ziwiri zapita’zo?
MAFUNSO okhala ndi kufunika kwa pa dziko lonse akuyang’anzana nafe lero lino. Iwo ali ogwirizana ndi mafunso amene tikanayang’anizana nawo ngati tikanakhala ndi moyo pafupifupi zaka zikwi ziwiri zapita’zo, m’Middle East. Kale’lo mafunso amene’wo anali ndi kufunika kwa pa dziko lonse chifuka chakuti iwo anali onena za mpulumutsi wa dziko, Mesiya! Pamenepo nthawi inali itakwana kwa iye kuti aonekere choyamba. Chotero anthu okondweretsedwa anali kumuyembekezera. Pa kuonekera kwake kodi iye akalandiridwa mokondwera ndi dziko lonse la mtundu wa anthu? Kapena kodi iye akawagwiritsa mwala m’kuchita zimene iye anatumidwa kuchita pa nthawi imene’yo? Kodi ndani amene akakhutiritsidwa maganizo kuti iye anali Mesiya amene anachita zenizeni’zo zimene Malemba Oyera ananeneratu ponena za iye, ndipo, chotero kum’tsatira monga M’tsogoleri wao? Kodi ndani amene sakakhumudwa naye koma kukopedwera kwa Iye? Kodi ndani lero lino amene akukopedwera kwa Mesiya wopulumutsa dziko, ndipo motani.
2. (a) Wamkulu wa “mbeu” ya “mkazi” wa Mulungu anayenera kukwaniritsa ntchito yotani? (b) Kodi ena a “mbeu” ya mkazi’yo anayenera kukhala yani? ndi kuphunzitsidwa ndi yani?
2 Kaamba ka chitsogozo chathu chosungika lero lino, tiyeni tikumbukire kuti Mesiya weniweni anayenera kukhala Wamkulu wa “mbeu” ya “mkazi” wa Mulungu yonenedweratu’yo, ndipo anayenera ‘kuzunzundidwa chitende’ ndi Chinjoka Chachikulu’cho, Satana Mdierekezi. “Mkazi” kapena mai wa “mbeu” gulu lakumwamba la Mulungu longa mkazi lopangidwa ndi zolengedwa zoyera zauzimu, “ana amuna a Mulungu [woona] aungelo. “Mbeu” ya mkazi yolonjezedwa’yo yapangidwa ndi ana ake, Wamkulu wake akumakhala Mesiya ndipo ena’wo akumakhala atsatiri ake auzimu. Ponena za ziwalo zochepera zimene’zi za “mbeu” ya mkazi tiri ndi mau a Yesaya 54:13 monga momwe ananenedwera kwa “mkazi” wophiphiritsira’yo kuti: “Ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.” Moyenerera, “ana” akaphunzitsidwa ndi Mwamuna wakumwamba wa mkazi’yo, Yehova, Atate wa “mbeu.”—Yesaya 54:5.
3. Kodi Yesu anagwiritsira ntchito liu’lo “ana” kwa yani mu Yesaya 54:13, ndipo kodi ndi motani m’mene amene’wa tsopano akuphunzitsidwira popanda kuoneka kwa Mphunzitsi?
3 Wamkulu wa “mbeu” ya mkazi, Yesu Kristu, anapanga kutanthauzira mau onenedwa kwa mkazi’yo mu Yesaya 54:13. Mogwirizana ndi chiani? Eya, polankhula ndi Ayuda amene sanakopedwere kwa iye monga Mesiya ndipo chotero anali kung’ung’uza naye Yesu anati “Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine am’koka iye; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza Chalembedwa mwa aneneri, Ndipo adzakhala onse ophunzitsidwa ndi Mulungu. Yense amene adamva kwa Atate, naphunzira, adza kwa Ine.” (Yohane 6:44, 45) Ndithudi, Yehova sali Mphunzitsi wooneka kwa ife, koma iye wapereka Bukhu louziridwa kwa ife. Chotero mwa njira ya limene’li ndi mwa kugwira ntchito kwa mzimu wake woyera, iye amatiphunzitsa zinizeni zonena za “mbeu” Yaumesia ya “mkazi” wake. M’njira imene’yi iye amakokera ochepera a “mbeu” kwa Wamkulu’yo Mesiya, ndipo amapanga mpingo.
4. Pofika pa chaka chachitatu cha ntchito yapoyera ya Yesu, kodi ndi motani m’mene malingaliro a atumwi a Yesu anasiyanira ndi awo a anthu ponena za amene iye anali?
4 Pofika pa nthawi imene’yo m’chaka chachitatau cha ntchito yapoyera ya Yesu, Ayuda anayenera kukhala atafika pa chosankha china ponena za amene wochita zozizwitsa amene’yu anali m’chifuno cha Mulungu. Kodi ndi angati a iwo amene anasonyeza kuti iwo anali ‘kuphunzitsidwa ndi Yehova’ ponena za Mesiya wake? Inali thawi yoyenera kwa Yesu kufunsa atumwi ake izi:
“Anawafunsa iwo, kuti, Makamu’wo a anthu anena kuti Ine ndine yani? Ndipo anayankha nati, Yohane M’batizi; koma ena, Eliya; ndi ena, kuti anauka mmodzi wa aneneri akale. Ndipo anati kwa iwo, Koma inu munena kuti Ine ndine yani? Ndipo anayankha Petro, nati, Kristu wa Mulungu. Ndipo Iye anawauzitsa iwo, nalamulira kuti asanene ichi kwa munthu ali yense; nati, Kuyenera kuti Mwana wa munthu amve zowawa zambiri, ndi kukanidwa ndi akulu, ndi ansembe akulu, ndi alembi, ndi kuphedwa, ndi kuuka tsiku lachitatu.”—Luka 9-18-22; yerekezerani ndi Marko 8:27-32.
5. Malinga ndi kunena kwa Mateyu 16:16-19, kodi Yesu ananenanji kwa Petro poyankha yankho la funso lake?
5 Cholembedwa cha mtumwi Mateyu chinafutukula nkhani’yo, kuti: “Simoni Petro anayankha nati, Inu ndinu Kristu, Mwana wa Mulungu wamoyo. Ndipo Yesu anayankha iye, nati, Ndiwe wodala, Simoni BarYona: pakuti thupi ndi mwazi sizinakuululira ichi, koma Atate wanga wa Kumwamba. Ndipo’nso Ine ndinena kwa iwe, kuti ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe iri ndidzakhazika Mpingo wanga; ndipo makomo a dziko la akufa sadzaulaka iwo. Ndidzakupatsa mafungulo a Ufumu wa Kumwamba; ndipo chimene ukamanga pa dziko lapansi chidzakhala chomangidwa Kumwamba: ndipo chimene ukachimasula pa dziko lapansi, chidzakhala chomasulidwa Kumwamba.”—Mateyu 16:16-19.
6. Kodi n’chiani chimene chikusonyeza kuti Petro sanamve molakwa mau a Yesu onena za “thanthwe,” ndipo kodi Paulo anati ndani amene anali “thanthwe”?
6 Kuchokera m’chiyamikiro chimene’cho choperekedwa kwa Petro kuli koonekera bwino kuti iye anali munthu amene anaphunzitsidwa ndi Yehova ndipo anaphunzira kuchokera kwa Iye. Chotero iye anakopedwera kwa Yesu ndipo anadza kwa iye monga Mesiya kapena Kristu. Dzina la Petro limatanthauza “mwala,” kapena “chimwala.” Koma chimene’chi sichikutanthauza kuti iye anali “thanthwe” pa limene Yesu akamangapo mpingo wake. Ndipo’nso “thanthwe”silinali kubvomereza kumene Petro anapanga kuti: “Inu ndinu Kristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.” ‘Thanthwe’lo’ linali Yesu mwini’yo. Petro sanatanthauzire molakwa mau a Yesu’wo. Iye sananene kuti anali “thanthwe” (Chigriki, petra) malinga ndi kunena kwa 1 Petro 2:4-10. Ndipo’nso, mtumwi Paulo, amene zolemba zake Petro anazizindikira kukhala mbali ya Malemba ouziridwa, analemba kuti: “Namwa onse [Aisrayeli m’chipululu] chakumwa chauzimu chimodzimodzi; pakuti anamwa mwa thanthwe lauzimu lakuwatsata; koma thanthwe’lo ndiye Kristu.”—1 Akorinto 10:4; 2 Petro 3:15-16.
7, 8. (a) Kodi atumwi molakwa anaganiza kuti ufumu Waumesiya ukakhala chiani? (b) Kodi “mfungulo” za ufumu wakumwamba zinayenera kuperekedwa kwa yani, koma kodi mpingo unayenera kumangidwa pa yani?
7 Pamene Yesu analankhula ndi atumwi ake ponena za ufumu, iwo analingalira za ufumu wozikidwa pa boma limene likakhala ndi malikulu ake pa Yerusalemu, pamene Mfumu Davide analamulirapo. Iwo anayembekezera Yesu monga Mesiya kukhazikitsa boma lake pa Yerusalemu, monga wolowa m’malo mwa Mfumu Davide. Monga umboni wakuti limene’li linali lingaliro lao, iwo anati kwa Yesu pambuyo pa chiukiriro chake kuchokera kwa akufa: “Ambuye, kodi nthawi yino mubwezera ufumu kwa Israyeli?” (Machitidwe 1:6) Pa nthawi inoyo, tsiku la phwando la Pentekoste wa 33 C.E. lisanakwane, iwo sanazindikire kuti ufumu wa Kristu woukitsidwa’yo unayenera kukhala woposa wa anthu wolamulira koposa kwambiri mtundu wa pa dziko lapansi wa Israyeli. Zimene’zo pokhala choncho, kunali koyenera wa Yesu, pambuyo pa kubvomerezedwa kwake ndi Petro kukhala Kristu, kutulutsa nkhani yonena za “ufumu wa kumwamba.”
8 Iye anali kupereka “mfungulo” kwa Petro. (Mateyu 16:19) Komabe, mpingo’wo unayenera kumangidwa ndi Yesu Kristu pa “thanthwe” lachifumu mfumu Yaumesiya. Ndipo, monga momwe kuliri kuti ‘makomo a Hade’ sadzalaka “thanthwe” lamaziko’lo koma Yesu Kristu akaukitsidwa kuchokera kumanda pa tsiku lachitatu, chotero ‘makomo a Hade’ sakalaka mpingo wa Mesiya. Nawo’nso uyenera kuuka kuchokera kwa akufa.
WOTHANDIZA WOSAONEKA WA MPINGO
9. Kodi atsatiri a Kristu anayenera kusonkhanitsidwa pamodzi kupanga chiani, ndipo komabe kodi iwo akakhala’nso chiani, mofanana ndi Israyelo wakale?
9 Mosafanana ndi atumwi a Kristu, mtunda wa Israyeli unakhalabe wosokonezeka ponena za amene Yesu anali m’chifuno cha Yehova. Chotero Muisrayeli ali yense payekha amene anam’landira monga Mesiya kapena Kristu akasonkhanitsidwa pamodzi kupanga mtundu watsopano. Mtundu umene’wu ukakhala wonga mpingo monga momwe Israyeli wakale analiri. Iwo akakhala mpingo wa olengeza mfumu Yaumesiya ndi ufumu wake!
10. Mu 1 Petro 2:8-10, kodi ndi motani m’mene Petro amasonyezera chenicheni chokondweretsa chimene’cho, ndipo kodi n’chiani chimene chikuphatikizidwa pakati pa “zoposa’zo” zimene ziyenera kulengezedwa kuli konse?
10 Chenicheni chokondweretsa chimene’chi chinadziwidwa ndi mtumwi Petro monga munthu amene ‘anaphunzitzidwa ndi Yehova.’ Chimodzi cha zinthu zotsirizira zimene iye analembera okhulupirira anzake chinali ndi mau awa: “Kumeneko’nso [Aisrayeli osakhulupirira] adaikidwa’ko. “Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposa’zo za iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa” (1 Petro 2:8-10) “Zoposa’zo” za Wodabwitsa amene’yo zikaphatikizamo kukhoza kuchita chifuno chake ponena za Mesiya wake mosasamala kanthu za chitsutso cha awo amene anakana Mwana wake monga Mesiya. ‘Anthu ake apadera’ali ndi thayo la kutamanda Yehova kaamba ka ufumu wake Waumesiya.—Yesaya 43:21.
11, 12. Kodi n’chifukwa ninji Yesu analonjeza kutumizira ophunzira ake “nkhoswe” ndipo kodi Yesu ananenanji ponena za nkhoswe’yo?
11 Thayo lotero’lo “mtunda woyera” watsopano’wo sukanatha kulichita mwa nyonga ya uwo wokha pakati pa dziko laudani. Yesu, podziwa zimene’zi, anane kwa atumwi ake okhulupirika asanachotsedwa kwa iwo mogwida ndi adani kuti: “Sindidzakusiyani inu mukhale ana amasiye . . . Koma Nkhoswe’yo, Mzimu Woyera, amene Atate adzam’tuma m’dzina langa. Iyeyo adzaphunzitsa inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.” Ndipo’nso: “Pamene wafika Nkhoswe, amene Ine ndidzam’tuma kwa inu kuchokea kwa Atate, ndiye Mzimu wa choonadi, amene atuluka kwa Atate, Iyeyu adzandichitira Ine umboni. Ndipo inu’nso muchita umboni, pakuti muli ndi Ine kuyambira chiyambi.”—Yohane 14:18, 26; 15:26, 27.
12 Yesu anati’nso: “Ngati sindichoka, Nkhoswe’yo sadzadza kwa inu; koma ngati ndipita ndidzam’tuma Iye kwa inu; . . . atadza Iyeyo, Mzimu wa choonadi, adzatsogolera inu m’choonadi chonse; pakuti sadzalankhula za Iye mwini; koma zinthu ziri zonse adzazimva, adzazilankhula; ndipo zinthu zirinkudza adzakulalikirani. Iyeyo adzalemekeza Ine; chifukwa adzatenga za mwa Ine, nadzalalikira kwa inu. Zinthu ziri zonse Atate ali nazo ndi zanga; chifukwa chake ndinati, kuti atenga za mwa Ine, nadzalalikira kwa inu.”—Yohane 16:7, 13-15.
KUFIKA KWA “NKHOSWE” MZIMU WOYERA
13. Kodi “nkhoswe” yolonjezedwa’yo inayenera kuperekedwa m’dzina la yani, ndipo kwa okhulupirira dzina la yani?
13 Zosakwanira kwenikweni zaka mazana asanu Yesu Kristu asanapange lonjezo limene’lo kwa atumwi ake, Bwanamkubwa Nehemiya pa Yerusalemu analemba pemphero lonena za machitidwe a Mulungu ndi Aisrayeli kuti: “Munawalekerera zaka zambiri, ndi kuwachitira umboni ndi mzimu wanu, mwa aneneri anu.” (Nehemiya 9:30) Ndipo tsopano, m’kati mwa kusakhalapo kwakuthupi kwa Yesu Mesiya pamaso pa ophunzira ake, mzimu wa Yehova Mulungu umodzimodzi’wo unayenera kuwathandiza. Ukaperekedwa kwa iwo kokha m’dzina la Yesu. Ukaperekedwa kokha kwa awo amene akakhulupirira kuti Yesu linali dzina la Mesiya weniweni. Kodi ndi liti pamene unaperekedwa choyamba?
14, 15. (a) Kodi Yesu anafikitsa pachimake masiku ake makumi anai pambuyo pa chiukiriro chake mwa kulonjeza ophunzira ake chinthu chotani chosiyana ndi ubatizo wa Yohane? (b) Kodi ndi funso lotani limene likakhalapo ponena za ubatizo wolonjezedwa umene’wu
14 Kwa masiku makumi anai pambuyo pa chiukiriro cha Yesu kuchokera kwa akufa pa Sande, Nisan 16, 33 C.E., iye anakhalabe pano pa dziko lapansi, koma mosaoneka. Nthawi zina, iye anachita mofanana ndi angelo oyera akale, anabvala thupi longa la munthu, kupatsa ophunzira ake chitsimikiziro chakuti iye anaukadi kwa akufa, koma monga mzimu. M’kuonekera kotero’ko kwa iwo iye anapitirizabe “kunena zinthu za Ufumu wa Mulungu.” (Machitidwe 1:1-3) Ena a atumwi’wo anakhala ophunzira a Yohane M’batizi. Ndipo tsopano pa tsiku la makumi anai, tsiku la kukwera kwake kumwamba, Yesu Kristu anapangitsa ophunzira ake kukhala oyembekezera kwambiri pamene iye ananera kwa iwo kuti: “Yohane anabatiza’di ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera, asanapite masiku ambiri.” (Machitidwe 1:4, 5) Ubatizo wa Yohane wa Ayuda olapa unali m’chizindikiro cha kulapa kwao machimo ao ochimwira chilamulo cha Mulungu kupyolera mwa Mose.
15 Ubatizo wa m’madzi wotero’wo ungakhale utapatsa lingliro la mpumulo limodzi ndi chikumbu mtima chabwino. Koma kodi n’chiani chimene chikakhala chiyambukiro pa ophunzira a Yesu chochokera ‘m’kubatizidwa [kumizidwa] ndi Mzimu Woyera’? Unayenera kukhala wopatsa nyonga, chifukwa chakuti mzimu woyera wa Mulungu ndiwo mphamvu yake yogwira nchito, yoyera ndi yosaoneka.—Mateyu 3:11.
16. Malinga ndi mau a Yesu m’Machitidwe 1:6-8, kodi mzimu woyera unayenera kuwapatsa nyonga kuchitanji?
16 Pa kufika kwake, kodi mzimu woyera wa wa Mulungu ukapatsa nyonga oulandira’wo kuchita chiani? Atangotsala pang’ono kukwera kumwamba, Yesu kwa ophunzira ake anati: “Mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m’Yerusalemu, ndi m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero a dziko.” (Machitidwe 1:6-8) M’mau amene’wo muli yankho la funso lathu: Kupatsa nyonga olandira mzimu woyera’wo kupereka umboni wa pa dziko lonse wa chenicheni chakuti Yesu ndiye Mesiya, Kristu.
17. Pa tsiku la makumi asanu kuyambira pa chiukiriro chake, kodi lonjezo la Yesu kwa ophunzira ake linakwaniritsidwa m’mikhalidwe yotani?
17 Yesu Kristu akukwera kumwamba. Masiku khumi akupita. Tsiku la makumi asanu kuyambira pa chiukiriro chake likufika! Pa Yerusalemu tsiku la phwando Lachiyuda la Masabata kapena Pentekoste (kutanthauza ‘Lamakumi asanu’ ponena za tsiku) likufika. M’mamawa kwambiri ophunzira okwanira zana limodzi kudza makumi awiri akusonkhana pamodzi, osati pa kachisi wochitira phwando, koma m’chipinda cham’mwamba, akuyembekezera. “Mwadzidzidzi anamveka mau ochokera Kumwamba ngati mkokomo wa mphepo yolimba, nadzaza nyumba yonse imene analikukhalamo. Ndipo anaonekera kwa iwo malirime ogawanikana, onga moto; ndipo unakhala pa iwo onse wayekha wayekha. Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malirime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.”—Machitidwe 2:1-4.
18, 19. Monga momwe kunalongosoledwera ndi Petro, kodi ndi ulosi wotani umene unayamba kukwaniritsidwa pa tsiku la Pentekoste limene’lo, ndipo kwa utali wotani pambuyo pa kunenedwa kwake?
18 Aha, potsirizira pake, pake, pambuyo pa zaka zoposa mazana asanu ndi atatu kuyambira pa kunenedwa kwake, ulosi wa Yoweli 2:28-32 unayamba kukwaniritsidwa. Ayuda odabwa anasonkhana kudzaona chochitika’cho. Ena ananene za ophunzira’wo kukhala ataledzera. Molimba mtima mtumwi Petro anati kwa iwo:
19 “Komatu ichi ndi chimene chinanenedwa ndi mneneri Yoeli, Ndipo kudzali m’masiku otsiriza, anena Mulungu, ndidzathira cha Mzimu wanga pa thupi liri lonse, ndipo ana anu amuna, ndi akazi adzanenera ndipo anyamata anu adzaona masomphenya, ndi akulu anu adzalota maloto; ndipo’nso pa akapolo anga ndi pa adzakazi anga m’masiku awa ndizathira cha Mzimu wanga; ndipo adzanenera. Ndipo ndidzapatsa zodabwitsa m’thambo la kumwamba, ndi zizindikiro pa dziko lapansi; mwazi, ndi moto, ndi mpweya wa utsi; dzuwa lidzasanduka ndima, ndi mwezi udzasanduka mwazi, lisanadze tsiku la Ambuye, lalikulu ndi loonekera; ndipo kudzali, kuti yense amene akaitana pa dzina la Ambuye adzapulumutsidwa.”—Machitidwe 2:16-21.
20. Kodi ndi ubatizo wotani umene unachitika, ndipo kodi Petro anasonyeza yani kukhala wogwiritsiridwa ntchito kuchita kubatiza’ko
20 Kubatizidwa ndi mzimu woyera kunali kutachitika, monga momwe’di Yesu analonjezera. Kunenedwa kwa mzimu kukhala ‘utatsanulidwa ‘utathiridwa’ kukagwirizana ndi chenicheni chakuti uli ngati chinthu chamadzi chobatizira kapena kumizira. Tikukumbukira kuti Mulungu anapatsa Yohane M’batizi chizindikiro chonena za Yesu, chosonyeza kuti “yemweyu ndiye wakubatiza ndi Mzimu Woyera.” (Yohane 1:33) Mogwirizana ndi chenicheni chimene’chi, mtumwi Petro anadziwikitsa Yesu Kristu wolemekezedwa’yo kukhala woimira wa Mulungu m’kutsanulira mzimu woyera pa Akristu oyambirira amene’wa. Petro kwa ochita phwando Achiyuda’wo anati’nso: “Yesu amene’yo Mulungu anamukitsa; za ichi tiri mboni ife tonse. Potero, popeza anakwezedwa ndi dzanja lamanja la Mulungu, nalandira kwa Atate lonjezano la Mzimu Woyera, anatsanulira ichi, chimene inu mupenya nimumva.”—Machitidwe 2:32, 33.
21. Kodi ndi motani m’mene Petro akananenera kuti iwo anaona ndi kumva chija chimene Yesu wolemekezedwa’yo anatsanula?
21 Iwo anaona ndi kumva kugwira ntchito kwa mzimu woyera, m’chakuti iwo anaona malirime monga ngati a moto pamwamba pa mitu ya ophunzira ndi kumva zinenero zachilendo zikunenedwa mozizwitsa ndi ophunzira’wo.
22. Kodi n’chiani’nso chimene chinachitikira ophunzira, kuti chifanane ndi chimene chinachitikira Yesu pambuyo pa kubatizidwa kwake m’madzi?
22 Komabe, koposa ndi kubatizidwa chabe kwa ophunzira a Yesu ndi mzimu woyera kunachitika pa tsiku la Pentekoste limene’lo. Kudzozedwa kwao ndi mzimu woyera kunali’nso kutachitika. Monga momwe’di Yesu anadzozedwera ndi mzimu woyera pambuyo pa ubatizo wake wa m’madzi ndipo motero iye nakhala Kristu kapena Wodzozedwa, chimodzimodzi’nso ophunzira ake. Iwo anadzozedwa ndi chimene iwo anabatizidwa nacho.
23. Ndipon’nso, kodi ophunzira’wo anasindikizidwa chizindikiro ndi chiani, monga momwe kwalongosoledwera ndi Paulo mu 2 Akorinto 1:21, 22?
23 Ndipo’nso, iwo anasindikizidwa ndi mzimu umene’wo mosonyeza cholowa chao chauzimu chirinkudza. Zimene’zi zikugwirizana ndi zimene mtumwi Paulo anauza mpingo Wachikristu m’Korinto wakale, Grisi kuti: Iye wakutikhazika pamodzi ndi inu kwa Kristu, natidzoza ife, ndiye Mulungu; amene’nso anatisindikiza chizindikiro, natipatsa chikole cha Mzimu mu mitima yathu”—2 AKorinto 1:21, 22.
24. Kodi n‘chiani chimene mtumwi Yohane analemba pambuyo pake ponena za kudzoza mu 1 Yohane 2:20, 27?
24 Mtumwi Yohane, amene analipo pa kutsanulidwa kwa mzimu woyera kwa pa Pentekoste kumene’ko anazindikira zimene zinachitika. Chotero nazi zimene iye analembera okhulupirira anzake: “Inu muli nako kudzoza kochokera kwa Woyera’yo, ndipo mudziwa zonse. Ndipo inu kudzoza kumene munalandira kuchokera kwa Iye, kukhala mwa inu, ndipo simusowa kuti wina akuphunzitseni; koma monga kudzoza kwake kukuphunzitsani za zinthu zonse, ndipo kuli koona, sikuli bodza ai, ndipo monga kudaphunzitsa inu, mukhale mwa iye.”—1 Yohane 2:20, 27.
KUBALA NDI MZIMU WOYERA
25. Kuti Mkristu wobatizidwa akhale ndi chiyembekezo cha cholowa cha kumwamba, kodi ndi kugwira nchito kotani kwa mzimu woyera kumene kuli kofunika kwa iwo kukhala nako?
25 Pali mbali ina yonena za kugwira ntchito kwa mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu imene’yi. Yesu anaisonyeza pamene iye anati: “Ngati munthu sabadwa mwa madzi nsi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu.” (Yohane 3:3, 5) Mkristu wokhala ndi chiyembekezo cha cholowa chakumwamba ayenera kutsanzira Mbuye wake Yesu mwa kubatizidwa m’madzi. Motere iye amasonyeza kudzipereka kwake kwa Yehova Mulungu, kuchita chifuniro chaumulungu. (Mateyu 28:19, 20) Koma payenera’nso kukhala kugwira ntchito kwa mzimu woyera pa iye. Chifukwa ninji? Chifukwa chakukti, monga momwe mtumwi Paulo akulembera mu 1 Akorinto 15:50, “thupi ndi mwazi sizingathe kulowa Ufumu wa Mulungu; kapena chibvundi sichilowa chisabvundi.”
26. Pambuyo pa kulemba za kudzoza, kodi mtumwi Yohane akunena za unansi wotani wa anthu odzozedwa ndi Mulungu?
26 Kuti ophunzira’wo aikidwe mu mzera wa kulowa mu ufumu wakumwamba wa Mulungu, iwo anafunikira ‘kubadwa’nso’ ndipo motero kukhala ana auzimu a Mulungu. Monga m’chochitika cha Yesu iye mwini, ndiye mwana wauzimu wa Mulungu amene amadzozedwa ndi mzimu woyera. Ndicho chifukwa chake, atatha kunena za kudzoza, mtumwi Yohane wodzozedwa’yo akupitirizabe kunena, mu 1 Yohane 3:1-3 kuti:
“Taonani chikondi’cho Atate watipatsa, kuti tichedwe ana a Mulungu; ndipo tiri ife otere. Mwa ichi dziko lapansi silizindikira ife, popeza silim’zindikira Iye. Okondedwa, tsopano tiri ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Tidziwa kuti, pa kuoneka Iye, tidzakhala ofanana ndi Iye, Pakuti tidzamuona Iye monga ali. Ndipo yense wakukhala nacho chiyembekezo ichi pa Iye, adziyeretse yekha, monga Iyeyu ali Woyera.”
27. Kodi ndi motani m’mene kukusonyezedwera mu Yohane 1:11-13 kuti makolo aumunthu alibe chochita chiri chonse ndi “kubadwa’nso” kwa Mkristu?
27 Makolo aumunthu alibe kanthu kali konse kochita ndi ‘kubadwa’nso’ kwa munthu, Mwa chikhulupiriro cha munthu mwini’yo ayenera kulandira Yesu monga Mesiya ndi kum’tsatira monga munthu wodzozedwa ndi Mulungu kukhala Mfumu mu ufumu Waumesiya wakumwamba. Ndiye ziri kwa Mulungu ngati afuna kaya kubala wotsatira amene’yo wa Kristu ndi mzimu woyera. Osati makolo aumunthu, koma Mulungu amabala ana kaamba ka kumwamba. Ndizo zimene mtumwi Yohane akunena. Nawa mau a Yohane: “[Iye,]” ndiko kuti, Yesu Kristu pa kudza kwake ku mtundu Wachiyuda zaka mazana khumi ndi asanu ndi anai zapita’zo “anadza kwa zake za Iye yekha, ndipo ake a mwini yekha sanam’landira Iye. Koma onse amene anam’landira Iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lake; amene sanabadwa ndi mwazi, kapena ndi chifuniro cha thupi, kapena ndi chifuniro cha munthu, koma cha Mulungu.” (Yohane 1:11-13) Mwa kubala kwa Mulungu iwo anakhala ana ake auzimu. Iye samawabala m’mimba ya mai.
“WOLENGEDWA WATSOPANO”
28. Kodi ndani amene amatsimikizira kuti payenera kukhala ana auzimu a Mulungu, ndipo kodi ndi motani m’mene amene’wa, m’lingaliro’lo aliri ‘zipatso zoundukula za zolengedwa zake’?
28 Kodi makolo aumunthu samadzisankhira ponena za kukhala ndi ana okhala ndi thupi ndi mwazi za iwo eni’wo? Inde! Chimodzimodzi’nso, Mulungu amasankha ponena za amene iye adzawabala kukhala ana ake auzimu okhala ndi cholowa chakumwamba. “Mwa chifuniro chake mwini anatibala ife ndi mau a choonadi, kuti tikhale ife ngati zipatso zoudukula za zolengedwa zake.” Amalemba choncho wophunzira Yakobo kwa Akristu amene amawacha “mafuko khumi ndi awiri a m’chibalaliko.”(Yakobo 1:1, 18) M’malimidwe, “zipatso zoundukula” zimatengedwa ku zipatso zatsopano ndipo zimaperekedwa kwa Mulungu monga kanthu kena kopatulika ndi kanthu kena komuyenerera. Pamenepa, kodi ndani, amene ali zipatso zoundukula zauzimu? Awo amene Atate amawabala monga mwa chifuniro chake ndi mwa njira ya “mau a choonadi,” Amene’wa iye amawatenga mwa mtundu wa anthu kukhala kagulu Kaufumu kakumwamba.
29. Kuti Mkristu akhale wokhoza kulowa mu ufumu wakumwamba, kodi 1 Petro 1:3,4 amasonyezanji kukhala chofunika kwa iye?
29 Kwa kagulu la “zipatso zoundukula” komweka mtumwi Wachikristu Petro analemba kuti: “Inu mwapatsidwa kubadwa kwatsopano, osati mwa mbeu yokhosa kubvunda, koma mwa yosabvunda, mwa mau a Mulungu wamoyo ndi wosatha.” (1 Petro 1:23, NW) “Kubadwa kwatsopano” kapena “kubadwa’nso” kukufunika kaamba ka kulowa kotsirizira kwa Mkristu mu ufumu wakumwamba. Chotero Petro akulemba kuti: “Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibala’nso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Kristu; kuti tilandire cholowa chosabvunda ndi chosadetsa ndi chosafota, chosungikira m’Mwamba inu.”—1 Petro 1:3, 4; onani’nso 1 Yohane 3:9.
30, 31. (a) Kodi awo amene alandira ‘kulandiridwa monga ana’ amapanga mfuu yotani kwa Mulungu? (b) Awo okhala ndi kulandiridwa kotero’ko ali m’pangano lotani ndipo akupanga mtundu wotani?
30 Kwa Akristu okhala m’chigawo cha Roma cha Galatiya amene analandira “kulandiridwa monga ana,” mtumwi Paulo analemba kuti: “Tsopano chifukwa chakuti ndinu ana, Mulungu watumiza mzimu wa Mwana wake m’mitima yathu ndipo umapfuula kuti:’Abba, Atate! Chotero, pamenepa, simuli’nso kapolo koma mwana; ndipo ngati mwana, wolowa’nso nyumba mwa Mulungu.”
31 Ayuda opangitsidwa kukhala Akristu, monga Paulo iye mwini, sanali’nso akapolo okhala pansi pa pangano Lachilamulo limene linachitiridwa unkhoswe ndi mneneri Mose. Iwo tsopano anali ana auzimu a Mulungu ndipo anali mu “pangano latsopano” lochitiridwa unkhoswe ndi Yesu Kristu, Mneneri wokulira koposa Mose. Pangano latsopano limene’lo limatulutsa chimene pangano lakale Lachilamulo cha Mose linalephera kutulutsa, ndiko kuti “ufumu wa ansembe ndi mutundu woyera.” (Eksodo 19:5, 6; Ahebri 8:6-13, NW; 1 Timoteo 2:5, 6) “Mtundu woyera” umene uli m’pangano latsopano chifukwa cha chimene’cho uli Israyeli wauzimu, wopangika ndi Akristu amene ali Ayuda kapena Aisrayeli m’kati. Amene’wa adulidwa m’mitima mwao m’malo mwa kunja m’thupi. Timawerenga motero mu Aroma 2:28, 29.
32. Malinga ndi 2 Akorinto 5:16-18, kodi n’chifukwa ninji sitimadziwa Mkristu, ngakhale Kristu iye mwini, monga mwa thupi?
32 Polingalira mbali zonse zatsopano zimene’zi ponena za ana auzimu a Mulungu, kodi tingakhale odabwa ndi zonse zimene mtumwi Paulo akunena ponena za “kulengedwa kwatsopano”? Ai! Kuli chabe koyenera kwa iye kutero. Polingalira chenicheni chakuti Yesu Kristu anaukitsidwa kuchokera kwa akufa monga Mwana wauzimu wakumwamba wa Mulungu, mtumwi Paulo akuti: “Kotero kuti ife sitidziwa‘nso munthu [Mkristu] monga mwa thupi; koma tsopano sitim’zindikira’nso motero. Chifukwa chake ngati munthu ali yense ali mwa Kristu wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano. Koma zinthu zonse zichokera kwa Mulungu.”
33. Kuti kulowa mu ufumu wakumwamba kupezedwe, kodi mdulidwe m’thupi ulu wofunika, kapena, ngati ai, kodi n’chiani chimene chiri chofunika?
33 Mwa zonse’zi kuyenera kukhala kwakuti mdulidwe wakuthupi wa munthu monga mbadwa yakuthupi ya kholo Abrahamu kapena monga Myuda wachibadwidwe sukufunika kwa ife kuti tipeze chipulumutso kupyolera mwa Mesiya, Kristu. Ponena za anthu awo amene akuyembekezera kupita kuwamba, kodi n’chiani kwenikweni chiri chofunika? Mtumwi wouziridwa Paulo akuyankha ndi mau olunjika awa: “Pakuti mdulidwe suli kanthu kusadulidwa’nso sikuli kanthu, koma kulengedwa kwatsopano ndiko kuli kanthu. Ndipo awo onse amene atsatira chilangizo ichi, mtendere ndi chifundo zikhale pa iwo, ndi pa Israyeli wa Mulungu” (Agalatiya 6:15, 16, NW) “Israyeli wa Mulungu” yense amene’yu ali “wolengedwa watsopano.”
34. Kaamba ka kuthetsedwa kwa mkangano wonena zakuti kaya mdulidwe wakuthupi unali wofunika kaamba ka chipulumutso chamuyaya, kodi n’chiani chimene mpingo wa Antiokeya unachita?
34 Lero lino anthu ena amene ali ndi mdulidwe wakuthupi angatsutse mau a mtumwi wouziridwa Paulo amene’wo, Myuda wopangidwa kukhala Mkristu. Koma ngakhale zaka khumi ndi zisanu ndi chimodzi pambuyo pa imfa, chiukiriro ndi kukwera kumwamba kwa Yesu Kristu panali awo amene anaumirira kuti mdulidwe wakuthupi uli wofunika ku chipulumutso chamuyaya. Zinatsimikizira kukhala choncho mu Antiokeya, Suriya, kumene ophunzira a Kristu anachedwa choyamba Akristu. (Machitidwe 11:26) Ndiyeno chiani, tsono? Mpingo wa Antiokeya unatumiza Paulo ndi mmishonale mnzake Barnaba ndi ena “kuti akwere kunka ku Yerusalemu kwa atumwi ndi akulu kukanena za funso’lo.” (Machitidwe 15:1, 2) Chotero bungwe la upo wa atumwi ndi akulu a mpingo wa Yerusalemu unachitika, kuti upereke chosankha chonena zakuti kaya okhulupirira osakhala Ayuda mwa Kristu afunikira kudulidwa mwakunja m’thupi.
35. Kodi mzimu woyera unali n’chiani ndi lamulo lotulutsidwa ndi Upo wa pa Yerusalem, ndipo kodi lamulo’lo linanenanji?
35 Potsirizira pake, pambuyo pa kukambitsirana kwambiri ndi kutulutsidwa kwa umboni wochirikiza nkhani’yo, wophunzira Yakobo anatembenukira ku mau onena za nkhani’yo a Amosi 9:11, 12 amene anauziridwa ndi mzumu woyera wa Mulungu ndi amene anali kale kukwaniritsidwa pansi pa chitsogozo cha mzimu woyera. Moonekera bwino lomwe chimene’chi chinali chitsogozo cha mzimu woyera wa Mulungu kuti mdulidwe wakunja m’thupi sunali wofunika kwa okhulupirira a Amitundu amene anatengedwa mwa a mitundu kaamba ka dzina la Yehova. Mosakaikira mzimu woyera wa Mulungu unakumbutsa lemba lotsimikizirira limene’li m’maganizo mwa Yakobo ndipo’nso unam’tsogoza ponena za kuchula nsonga zapadera zoti zilowetsedwe m’chitsimikiziro choti chitulutsidwe ndi Upo wa pa Yerusalemu. Lamulo la Upo’wo linali motero.
“Chinakomera Mzimu Woyera ndi ife, kuti tisasenzetse inu chothodwetsa chachikulu china choposa izi zoyenera’zi; kuti musale nsembe za mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama; ngati mudzisungitsa pa zimene’zi, kudzakhala bwino kwa inu. Tsalani bwino.” (Machitidwe 15:3-29; 21:25)
Motero kunalingaliridwa kuti chimene chinali chofunika kwa Akristu kuti afikire cholowa chakumwamba chinali, osati mdulidwe wakunja m’thupi, koma kukhala kwa munthu “wobadwa watsopano.”
36. Mwa kudzozedwa kwao, kodi liri thayo pa mpingo wodzozedwa’wo kuchita ntchito yotani, ndipo mogwirizana ndi imene’yo kodi Yehova amawaphunzitsanji
36 Kale’lo m’zaka za zana loyamba C.E. okhulupirira Achikristu anasangalala ndi chosankha chimene’cho cha Upo wa pa Yerusalemu. Ife enife lero lino tingasanglalebe ndi chosankha chimene’cho cha Upo wa pa Yerusalemu. Ife enife lero lino tingasangalalebe ndi chosankha chouziridwa chofanana’cho. Kuchokera m’Malemba Oyera timazindikira kuti mpingo Wachikristu wobadwa ndi mzimu monga “wolengedwa watsopano” wadzozedwa ndi mzimu wa Yehova, mongofanana ndi Wamkulu wa mpingo umene’wo, Yesu Kristu. Chotero tsopano liri thayo pa mpingo umene’wo kuchita chimene kudzoza kumene’ko kumawalamula kuchita, ndiko kuti, ‘kulalikira mau abwino kwa ofatsa.’ Yesu Kristu iye mwini sanakankhire pambali thayo la kuchita chimene’chi koma anapereka chitsanzo kaamba ka atsatiri ake onse. (Yesaya 61:1-3) Monga ana auzimu a Mulungu iwo akuphunzitsidwa ndi Yehova zoti anene monga “mau abwino” ochokera kwa Iye. (Yesaya 54:13) Mwa chitsanzo chokhulupirika ndi mau a Mwana wake Yesu Kristu, Yehova amaphunzitsa mpingo Wachikristu kuti mbiri yopulumutsa moyo yoti ilengezedwe kuli konse iri mbiri yabwino yonena za ufumu Waumesiya wa Mulungu.