Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • go mutu 6 tsamba 90-108
  • Woimira Wamkulu wa Mulungu m’Boma la Dziko

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Woimira Wamkulu wa Mulungu m’Boma la Dziko
  • Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ULAMULIRO WA DZIKO WA UWIRI WA ANGELEZI NDI AMEREKA
  • OWERUZA AUMULUNGU AKUWERUZA
  • WOIMIRA WAMKULU WA MULUNGU AKUSONYEZEDWA
  • Ndani Adzalamulira Dziko?
    Samalani Ulosi wa Danieli!
  • Masinthidwe a Dziko Onenedweratu Kufikira ku Ufumu wa Mulungu
    Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu
  • Ndani Angalimbane ndi Kalonga wa Akalonga?
    Samalani Ulosi wa Danieli!
  • Labadirani Mawu Aulosi a Mulungu a M’tsiku Lathu
    Nsanja ya Olonda—2000
Onani Zambiri
Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu
go mutu 6 tsamba 90-108

Mutu 6

Woimira Wamkulu wa Mulungu m’Boma la Dziko

1. Kodi ndi motani m’mene 1914 C.E. analiri chaka chodalitsidwa ndipo’sno chotembereredwa?

CHINALI chaka chotembereredwa, chinali chaka chodalitsidwa, chaka chimene’cho cha 1914 C.E. “Chotembereredwa,’ m’chakuti pa nthawi imene’yo Nkhondo Yoyamba ya Dziko inaulika, kuyambitsa Nyengo ya Chiwawa imene yakhala ikungoipira-ipira kufikira m’nthawi yathu ino’yo. “Chodalitsidwa,” m’chakuti, mosaoneka ndi maso a anthu, kumwamba koyera’ko boma lamphamvu linapangidwa ndi Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi kuti lichititse mtendere wosatha wa anthu.

2. Kodi Woimira Wamkulu wa Mulungu kaamba ka boma la dziko akuyembekezera chiani?

2 Monga momwe kunalengezedwera pasadakhale ndi “amithenga” a Mulungu ku mitundu yonse, “nthawi za Akunja” za ulamuliro wa dziko wolamulidwa ndi maulamuliro a dziko Akunja popanda chidodometso chochokera ku ufumu wa Mulungu zinatha. (2 Akorinto 5:20; Aefeso 6:20) Mitundu Yachikunja’yo inakana kuzindikira cheni-cheni chimene’cho ndipo inalowa m’nkhondo yolimbanira kusungabe ulamuliro wa ndale za dziko wa dziko lonse. Komabe, pa nthawi yake yeni-yeni, mu 1914 C.E., pa mapeto a “nthawi zisanu ndi ziwiri” zimene’zo (zaka 2,520) za kulamuliro dziko kwa Akunja, Mulungu anatulutsa boma lake lakumwamba, mwamsanga kuletsa kotheratu mitundu Yachikunja yotanganitsidwa ndi nkhondo’yo imene tsopano iri chabe popanda chilolezo pa “chopondapo” cha Mulungu, dziko lapansi. (Danieli 2:44; 4:16, 23, 25, 32; Luka 21:24; Salmo 2:1-9) Mu ufumu wakumwamba umene’wo Woimira Wamkulu wa Mulungu kaamba ka boma la dziko akulamulira, akumayembekezera nthawi ya Mulungu yakuti mitundu yonse Yachikunja yaudani imene’yi iikidwe pansi pa mapazi ake m’chionongeko chosatha. (Salmo 110:1-6; Ahebri 10:12, 13) Pamenepo mtendere wosatha, wofanana ndi uta-wa-leza, udzakongoletsa dziko lapansi.

3. Mu 1914 kapena pambuyo pake kodi munthu ali yense anayenera kukhala Wolamulira wa Dziko?

3 Pa dziko lapansi, kale’lo mu 1914, panalibe munthu amene akanayenerera kukhala woimira wamkulu wa Mulungu kaamba ka boma la dziko lodzetsa mtendere. Ai, panalibe ngakhale mmodzi, ngakhale mu Yerusalemu wa pa dziko lapansi m’Middle East, kapena’nso m’Betelehemu. M’chaka chobvuta kwambiri chimene’cho mizinda yochuka imene’yo inali m’manja mwa Aturk Achisilamu, monga mbali ya Ufumu wa Turkey, umene unalowetsedwa m’Nkhondo Yoyamba ya Dziko pa October 30, 1914. M’December wa 1917 Yerusalemu anamka m’manja mwa anthu ena, pamene magulu ankhondo a Britain otsogozedwa ndi Mkulu wa Nkhondo Allenby anagonjetsa mzinda’wo. M’masiku amene’wo nzika ya Britain, wogulitsa mankhwala wochuka Wachiyuda wochedwa Chaim Weizmann, anapanga kuthandizira kofunika kwambiri kwa kuyesa-yesa kwa nkhondo kwa Britain. Kumene’ku kunatumikira monga chosonkhezera kutulutsidwa kwa chilengezo chochedwa Balfour Declaration, chimene boma la Britain linabvomereza nacho kukhazikitsidwa kwa dziko la Ayuda m’Palestina. Zaka zambiri pambuyo pake, m’May wa 1948, pambuyo pa nkhondo ya pakati pa Aluya ndi Ayuda, Ripabliki la Israyeli linakhazikitsidwa. Chaim Weizmann anakhala prezidenti wake woyamba, koma osati mfumu yake Yaudavide. Iye sanayenerere kukhala Woimira Wamkulu wa Mulungu.

4. Kodi n’chifukwa ninji panalibe ufumu watsopano uli wonse umene unabadwa pa Yerusalemu mu 1914 C.E?

4 Maufumu anaonongedwa monga chotulukapo cha Nkhondo ya Dziko I. Mogwirizana ndi mkhalidwe wononga umene’wu, palibe ufumu watsopano umene unabadwa pa dziko lapansi mu 1914, pa mapeto a “nthawi zoikidwiratu za amitundu,” kapena, “nthawi za Akunja.” Pambuyo pake Chigwirizano cha Mitundu chinapatsa Britain ulamuliro pa Yerusalemu ndi zigawo zina za ku Middle East zolandidwa ndi magulu ankhondo a Britain. Lamulo lololeza limene’li linathera pa May 15, 1948. Ripabliki la Israyeli linatsatirapo. Komabe, palibe ufumu wooneka wa Mulungu umene unakhazikitsidwa pa dziko lapansi woti utumikire monga woimira Ulamuliro wa Yehova wa m’chilengedwe chonse kulinga ku dziko lathu lapansi’li. Palibe munthu wa pfuko Lachiyuda amene anapezeka kukhala woyeneretsedwa kukhala Woimira Wake Wamkulu m’boma Lake la dziko lolonjezedwa’lo. Panalibe Myuda wodulidwa amene akanatha kutulutsa zisonyezero zoyenera zotsimikizira kuti iye anali mbadwa yeni-yeni ya Mfumu Davide, wokhala ndi kaya kuyenera kwachibadwidwe kapena kwalamulo ku mpando wachifumu wa Mfumu Davide pa Yerusalemu.

5. Pamenepo kodi kufunidwa kwa Woimira Wamkulu wa Mulungu kunayenera kupangidwa kuti?

5 Chotero kodi n’kuti, pa nthawi yobvuta kwambiri’yo, kumene wolowa nyumba wa Mfumu Davide akanapezeka, wofunika’yo amene Yehova akanam’khazika kukhala Woimira wake Wamkulu m’boma la dziko lonenedweratu’lo? Pansi pa mikhalidwe’yo, kodi ndi ku malo ena ati kumene tikayang’ana mosakaikira koposa kumwamba m’malo osaoneka okhala mizimu, miyamba kumene Mfumu ya Chilengedwe Chonse iye mwini amalamulira? Kumene’ko ndiko kumene mneneri wakale Danieli anasonya’ko kaamba ka kuperekedwe kwa Woimira Wamkulu wa Yehova. Kumene’ko ndiko kumene kufuna-funa’ko kuyenera kupangidwa kwa munthu wobvomerezedwa mwaumulungu ndi woyeneretsedwa. Kumeneko’nso, ndiko kumene Yohane Mgalileya’yo mwana wa Zebedayo, m’bukhu lotsirizira la Baibulo, Chibvumbulutso, anabvumbula kuti kufufuza kukapangidwa kwa munthu woyenera kuchita ntchito za Woimira Wamkulu wa Yehova.—Chibvumbulutso 5:3-12.

6, 7. Kodi ndi zirombo zitatu zotani zimene Danieli anaziona choyamba m’masomphenya?

6 Tiyeni tsopano, ndi maso a ulosi, tiyang’ane kumwamba limodzi ndi mneneri Danieli ndi kuona kufotokoza kwake Woimira Wamkulu wolakalakidwa kwambiri’yo. Danieli akusonyeza kuti panali pafupi ndi mapeto a ukapolo wa nthawi yaitali wa Ayuda m’Babulo pamene Mulungu anam’sonyeza masomphenya onena za Woimira Wake Wamkulu. Danieli akusonyeza deti la masomphenya’wo pamene iye akulemba kuti: “Chaka choyamba cha Belisazara [chidzukulu cha Nebukadinezara] mfumu ya ku Babulo Danieli anaona loto, naona masomphenya a m’mtima mwake pakama pake; ndipo analemba loto’lo, nalifotokezera, mwachidule. Danieli ananena, nati:

7 “Ndinaona m’masomphenya anga usiku, taonani, mphepo zinai za mumlengalenga zinabuka pa nyanja yaikulu. Ndipo zinatuluka m’nyanja zirombo zazikulu zinai zosiyana-siyana. Choyamba chinanga mkango, chinali nao mapiko a chiombankhanga, ndinapenyerera mpaka mthenga zake zinathothoka, nichinakwezeka kudziko, ndi kuimitsidwa ndi mapazi awiri ngati munthu, nichinapatsidwa mtima wa munthu. Ndipo taonani, chirombo china chachiwiri chikunga chimbalangondo chinatundumuka mbali imodzi; ndi mkamwa mwake munali nthiti zitatu pakati pa mano ake; ndipo anatero nacho, Nyamuka, lusira nyama zambiri. Pambuyo pake ndinapenya ndi kuona chinangati nyalugwe, chinali nao mapiko anai a nkhuku pamsana pake, chirombo’cho chinali nayo’nso mitu inai, nichinapatsidwa ulamuliro.”—Danieli 7:1-6.

8. Kodi zirombo zitatu zimene’zo zinaphiphiritsiranji, kwa utali wotani?

8 Zirombo zitatu zazikulu kwambiri zimene’zo zotuluka m’nyanja yoomba mphepo zinaphipphiritsira maulamuliro atatu. Iwo anaphiphiritsira maulamuliro amodzi-modzi’wo amene anasonyezedwa m’mutu wa golidi, chifukwa ndi manja za siliva, mimba ndi chuuno zamkuwa za fano la m’loto la Nebukadinezara, ndiko kuti, Ulamuliro wa Dziko wa Babulo, Ulamuliro wa Dziko wa Amedi ndi Aperisi ndi Ulamuliro wa Dziko wa Grisi. Maulamuliro a dziko amene’wa anali m’nyengo ya “nthawi ya Akunja” kuyambira pa kupasulidwa kwa Yerusalemu ndi dziko la Yuda mu 607 B.C.E. kudzafika mu 30 B.C.E. M’chaka chambuyo’cho wotsirizira wa maufumu anai a Ahelene amene anatuluka mu Ufumu wa Grisi wa Alexander the Great unagonjetsedwa kotheratu ndi magulu ankhondo apanyanja a Roma wakale wachikunja.

9. Kodi ndi chirombo chachinai chotani chokhala ndi nyanga chimene Danieli anachiona m’masomphenya amene’wa?

9 Komabe, pa nthawi ino, Danieli sanatsirize kutiuza loto lake lolosera. Iye akuti’nso: Pambuyo pake ndinaona m’masomphenya a usiku, ndi kuona chirombo chachinai, choopsya ndi chochititsa mantha, ndi champhamvu choposa, chinali nao mano akulu achitsulo, chinalusa ndi kuphwanya ndi lopondereza chotsala ndi mapazi ake; chinasiyana ndi zirombo zonse zidachitsogolera; ndipo chinali ndi nyanga khumi. Ndinali kulingirira za nyanga’zi, taonani, pakati pa izo panaphuka nyanga yina, ndiyo yaing’ono; patsogolo pake zitatu za nyanga zoyamba’zi zinazulidwa ndi mizu yomwe; ndipo taonani, m’nyanga m’menemo munali maso ngati maso a munthu, ndi pakamwa palikunena zazikulu.”—Danieli 7:7, 8.

10. Kodi chirombo chimene’chi chikufanana ndi chiani mu “fano” la m’loto’lo?

10 Pano tiri ndi chija chimene chikufanana ndi miyendo yachitsulo ya “fano” la ulamuliro wa dziko loonedwa m’loto la Nebukadinezara. Chirombo chachinai chinaimira woposa Ufumu Wachiroma chabe kapena Ulamuliro wa Dziko Wachisanu ndi Chimodzi wa ulosi wa Baibulo. Timaphunzira zimene’zi kuchokera m’kukambitsirana kumene Danieli anali nako ndi mngelo womasulira, amene anauza Danieli kuti: “Zirombo zazikulu izi zinai ndizo mafumu anai amene adzauka pa dziko lapansi. Koma opatulika a Wam’mwamba-mwamba adzalandira ufumu’wo, ndi kukhala nao ufumu kosatha, ku nthawi zomka muyaya.” (Danieli 7:17, 18) Mosasamala kanthu za chidziwitso chimene’chi, panali chikhalirebe chinsinsi kwa Danieli ponena za chirombo chachinai.

11. Kodi ndi mbali yake yoonjezereka yotani imene Danieli anafuna kuti ilongosoledwe?

11 “Pamenepo ndinafuna kudziwa choonadi cha chirombo chachinai. . . ndi za nyanga khumi zinali pamutu pake, ndi nyanga khumi zinali pamutu pake, ndi nyanga yina idaphuka’yi, imene zidagwa zitatu patsogolo pake; nyanga’yo idali ndi maso ndi pakamwa pakunena zazikulu, imene maonekedwe ake anaposa zinzake. Ndinapenya, ndipo nyanga yomwe’yi inachita nkhondo ndi opatulika’wo, niwalaka, mpaka inadza Nkhalamba ya kale lomwe; ndi mlandu unakomera opatulika a Wam’mwamba-mwamba, nifika nthawi yakuti ufumu unali wao wa opatulika’wo.”—Danieli 7:19-22.

12, 13. Kodi ndi motani m’mene mngelo analongosolera nyanga yaing’ono’yo kaamba ka ife?

12 Mofanana ndi Danieli, ife lero lino tikakonda kudziwa chimene kanyanga kamene’ko kamene kanali ndi maso ndi pakamwa kanaphiphiritsira. Tiyenera kufika pa tanthauzo lake motsogozedwa ndi mzimu woyera wa Mulungu, maka-maka choncho popeza kuti takhala ndi moyo kufikira pa kuona kukwaniritsidwa kwa loto lolosera la Danieli. Chifukwa cha chimene’cho, tsopano tichita bwino kumvetsera zimene mngelo womasulira’yo ananena kwa Danieli polongosola:

13 “Anatero, chirombo chachinai ndicho ufumu wachinai pa dziko lapansi, umene udzasiyana nao maufumu onse, nudzalusira dziko lonse lapansi, nudzalipondereza ndi kuliphwanya. Kunena, za nyanga khumi, m’ufumu uwu adzauka mafumu khumi [kuchokera mwa wachinai], ndi pambuyo pao idzauka yina; iyo idzasiyana ndi oyamba aja, nidzachepetsa mafumu atatu. Nidzanena mau akutsutsana ndi Wam’mwamba-mwamba, nidzayesa kusintha nthawi’zo ndi chilamulo; ndipo adzaperekedwa m’dzanja lake mpaka nthawi imodzi, ndi nthawi zina, ndi nthawi yanusu. Koma woweruza mlandu adzakhalako, ndipo adzachotsa ulamuliro wake, kuutha ndi kuuononga kufikira chimariziro.”—Danieli 7:23-26.

14. Kodi “nthawi imodzi, ndi zinthawi zina, ndi nthawi yanusu” ziri za utali wotani?

14 M’vesi la makumi awiri mphambu asanu kumene “nthawi imodzi, ndi zinthawi zina, ndi nthawi yanusu” zimapezeka, The New American Bible (Lachiroma Katolika) limati: “Iwo [Oyera’wo] adzaperekedwa kwa iye kwa chaka chimodzi, zaka ziwiri, ndi theka la chaka.” Kutembenuza kwa Moffatt kumati: “Kwa zaka zitatu ndi theka oyera adzaperekedwa kwa iye.” Mofananamo, The Complete Bible – An American Translation limati: “Ndipo iwo adzaperekedwa kwa iye kwa chaka chimodzi, zaka ziwiri, ndi theka la chaka.” Mogwirizana ndi mbiri, kodi izo zinali zaka zotani?

ULAMULIRO WA DZIKO WA UWIRI WA ANGELEZI NDI AMEREKA

15. Kodi nyanga “yaing’ono” yokhala ndi maso ndi pakamwa inakhalako motani?

15 “Ufumu wachinai,” Ufumu Wachiroma, unagawanika kukhala mitundu ingapo, ndipo mphukira imodzi yapadera yochokera mu ufumu’wo inali Great Britain. Kuti adzitsimikizire kukhala mfumu yaikazi ya nyanja zisanu ndi ziwiri Great Britain limodzi ndi maiko olamulidwa ndi iye anayenera kudzitsimikizira kukhala wapamwamba kwambiri pa mphamvu za magulu ankhondo a panyanja a Spanya, a Dutch ndi Achifrenchi. Zimene’zi zinachitidwa pofika chaka cha 1763 C.E., kotero kuti Ufumu wa Britain pa nthawi imene’yo unakhala Ulamuliro wa Dziko Wachisanu ndi Chiwiri wonenedweratu wa ulosi wa Baibulo. Pa July 4, 1776, maiko olamulidwa papitapo ndi Britain mu North America analengeza kuima paokha ndipo anakhala United States of America. Mwa kugwirizana kwapambuyo pake m’mbali zosiyana-siyana zokhala ndi kufunika kwa m’mitundu yonse Ufumu wa Britain ndi United States, motero, unakhala, Ulamuliro wa Dziko wa Uwiri wa Angelezi ndi Amereka. Pofika mu 1914 C.E., Ulamuliro wa Dziko Wachisanu ndi Chiwiri umene’wu unalamulira choposa chigawo chimodzi mwa zinai za nkhope ya dziko lapansi ndi chiwerengero chake cha anthu. Ndiwo nyanga “yaing’ono” imene inathyola nyanga zina zitatu’zo (magulu ankhondo a panyanja a Spanya, a Dutch ndi Achifrenchi) ndi imene inakhala ndi maso a munthu ndi pakamwa polankhula zinthu zazikulu.—Danieli 7:8.

16, 17. Kodi ndi motani m’mene zaka zitatu ndi theka zimene’zo zinathera mu 1918?

16 Munali m’kati mwa Nkhondo Yoyamba ya Dziko, kuyambira pa July 28, 1914, mpaka November 11, 1918, chakuti “oyera” kapena opatulika” anaperekedwa ku ulamuliro wa Dziko Wachisanu ndi Chiwiri kuti uchite nawo monga momwe ufunira. Panali pa April 6, 1917, pamene United States of America analowetsedwa m’nkhondo ya dziko lonse imene’yo kuimira kumodzi ndi Ufumu wa Britain. Ulosi wa Danieli ukusonya mwapadera pa zaka zitatu ndi theka za mwezi wokhala m’kati mwa Nkhondo ya Dziko Yoyamba imene’yi, kukhala nthawi pamene Ulamuliro wa Dziko Wachisanu ndi Chiwiri, nyanga “yaing’ono” yophiphiritsira’yo, inaphwanya “oyera” a Mulungu Wam’mwamba-mwamba, Yehova. Zimene’zi zinafika pachimake mwa kuweruzidwira kukhala m’ndende kwa zaka zambiri m’ndende yachibalo ya chigwirizano pa Atlanta, Georgia, kwa amuna asanu ndi awiri Achikristu onamiziridwa amene anali kukhala ndi phande kwambiri m’kufalitsa pa dziko lonse lapansi mbiri yabwino ya ufumu wokhazikitsidwa wa Mulungu mwa mau apakamwa ndi mwa masamba osindikizidwa.

17 Chiweruzo chimene’chi chinachitika pa June 21, 1918, ndipo pa July 4, 1918, opititsa patsogolo kuphunziridwa kwa Baibulo asanu ndi awiri amene’wa anatengedwa ndi treni kuchokera ku Brooklyn, New York, kumka ku Atlanta, Georgia. Kumene’ku kunakhala ngati nkhonya yauzimu yophwanya kwa Ophunzira Baibulo a m’Mitundu Yonse ozunzidwa pa nthawi’yo, amene, tsopano, kuyambira m’chaka cha 1931, akuchedwa Mboni za Yehova.

18. Kodi “oyera’wo” akusonyezedwa kukhala akufafanizidwa ndi nyanga ‘yaing’ono’yo’?

18 Ulosi wa Danieli sukusonyeza kuti “oyera a Wam’mwamba-mwamba’yo” anafafanizidwa ndi kubvutitsa kwa nyanga “yaing’ono,” Ulamuliro wa Dziko wa Uwiri wa Angelezi ndi Amereka. Mulungu Wam’mwamba-mwamba’yo, amene ulamuliro wake wa m’chilengedwe chonse iwo amaumamatira ndi kuulengeza, ali ku mbali yao. (Luka 18:7,8) Komabe, Ulamuliro wa Dziko Wachisanu ndi Chiwiri ndi mitundu ina yonse simalingalira mwamphamvu chidziwitso choperekedwa kwa iwo ndi Mboni za Yehova. Chidziwitso chimene’chi chachititsa kuti, chiyambire pa mapeto a Nthawi za Akunja mu 1914, iwo akhala ali pa chiweruzo pamaso pa Wam’mwamba-mwamba’yo. Loto la Danieli la zirombo zinai ndi nyanga “yaing’ono” molosera limasonyeza cheni-cheni chotsimikizirika chimene’chi.

OWERUZA AUMULUNGU AKUWERUZA

19. Kodi ndi motani m’mene Khothi Lakumwamba linachitira ndi “zirombo” zinai’zo?

19 Ponena za nthawi ya pambuyo pa kukhalapo kwa nyanga “yaing’ono” ndi kulankhula zinthu zazikulu, Danieli akupitirizabe kufotokoza loto lake lolosera’lo kuti: “Ndinapenyerera mpaka anaikapo mipando yachifumu, nikhalapo Nkhalamba ya kale lomwe, zobvala zake zinali za mbu ngati chipale chofewa, ndi tsitsi la pa mutu pake ngati ubweya woyera, mpando wachifumu unali malawi amoto, ndi njinga zake moto woyaka. Mtsinje wamoto unayenda wotuluka pamaso pake, zikwi zikwi anam’tumikira, ndi unyinji wosawerengeka unaima pamaso pake, woweruza mlandu anakhalapo, ndipo mabukhu anatsegulidwa. Pamenepo ndinapenyerera chifukwa cha phokoso la mau akulu idanena nyanga’yi; ndinapenyerera mpaka adachipha chirombo’chi [chachinai], ndi kuononga mtembo wake, ndi kuupereka utenthedwe ndi moto. Ndipo zirombo zotsala’zo adazichotsera ulamuliro wao, koma anatalikitsa moyo wao, ukhale’nso nyengo ndi nthawi.”—Danieli 7:9-12.

20. Kodi n’chifukwa ninji “Nkhalamba ya kale lomwe” simafunikira mabukhu oyang’anamo?

20 Ndi pano pokha m’masomphenya a kwa Denieli amene’wa pamene Mulungu wosakhoza kufa’yo amene ali wopanda chiyambi akuchedwa “Nkhalamba ya kale lomwe.” Iye ali woyambirira pa ali yense ndi kanthu kena kali konse, iye akumakhala Mlengi wao. (Salmo 90:2) Monga Munthu wa nzeru zonse ndi wa chilungamo chonse amene anayambirira zolengedwa zake zonse, iye moyenerera amakhala pa mpando wachiweruzo monga Woweruza wa zinthu zonse, kuphatikizapo dziko lathu lapansi’li. Popeza kuti masiku ake ndi akale-kale, iye amadziwa mbiri yonse yakale ya anthu monga ngati kuti inalembedwa m’bukhu. Motero iye waona maulamuliro a dziko anai onse onga chirombo amene’wo m’njira yao ya kachitidwe. Iye amapereka chiweruzo pa iwo, osati pa maziko a chimene ena amachitira umboni, koma mogwirizana ndi zimene iye amadziwa ponena za iwo mwachindunji. Iye samatofunikira kufuzafufuza m’mbiri yolembedwa, yokhala ndi nkhani za angelo zolembedwamo. M’makhothi aumunthu a pa dziko lapansi, mabukhu a malamulo ndi mabukhu a umboni akayenera kusanthulidwa. Koma siziri choncho ndi Yehova, “Khalamba ya kale lomwe.”

21. Kodi ndi motani m’mene miyoyo ya “zirombo zina’zo” inatalikitsidwira?

21 Monga momwe mabukhu a mbiri amasonyezera, “zirombo” zinai zaufumu’zo zinachoka pa dziko motsatana-tsatana, mogwirizana ndi zitsulo zinai zoonedwa m’loto la Nebukadinezara la fano la maulamuliro a dziko. Choyamba Ulamuliro wa Dziko wa Babulo unachoka pa chionetsero, pambuyo pake Ulamuliro wa Dziko wa Amedi ndi Aperisi, kenako Ulamuliro wa Dziko wa Grisi, ndipo potsirizira pake Ulamuliro wa Dziko wa Roma. Ngakhale kuli kwakuti maulamuliro a dziko amene’wo anataya ualmuliro wao motsatana-tsatana, zigawo za ufumu wao ndi anthu okhalamo zinapitirizabe kukhalapo, otsalira ena a amene’wa akalipobe mpaka lero. Ndicho chifukwa chake Danieli 7:12 amati: “Ndipo zirombo zotsalo’zo anazichotsera ulamuliro wao, koma anatalikitsa moyo wao, ukhale’nso nyengo ndi nthawi.”

22. Kodi n’chifukwa ninji chirombo chachinai ndi nyanga yake “yaing’ono” chikuonongedwa?

22 “Chirombo” chachinai chophiphiritsira’cho, limodzi ndi nyanga yake “yaing’ono” youkira’yo,” ikukumana ndi chionongeko chifukwa cha njira yake yachiwawa yotsendereza pa dziko lapansi, chifukwa cha mau ake ochitira mwano Mulungu Wam’mwamba-mwamba, ndi chifukwa cha kubvutitsa kwake kosalekeza “oyera” a Mulungu. Zinthu zopanda umulungu zotero’zo zachitidwa posachedwapa kwambiri ndi nyanga ya Angelezi ndi Amereka pa mutu wa chirombo chachinai chimene’chi.

23. Kodi n’chiani chimene chikuchitikira maulamuliro amene sanaphiphiritsiridwe ndi zirombo zinai’zo?

23 Chotero, chirombo chachinai chophiphiritsira’cho chikuchitiridwa chithunzi-thunzi kukhala chikuonongedwa limodzi ndi nyanga “yaing’ono.” Komabe, monga momwe mbiri ikunenera kweni-kweni, chirombo chachinai chophiphiritsira’cho, chimene chiri, Ulamuliro wa Dziko wa Roma, chinalandidwa mphamvu yake ya ufumu, kuchitira kuti upatse malo Ulamuliro wa Dziko wa Uwiri wa Angelezi ndi Amereka. “Mafumu” osiyana-siyana, kapena “nyanga” zophiphiritsira, zimene zinalowetsedwa m’kati mwa Ulamuliro wa Dziko wa Roma, anapitirizabe kulamulira monga “nyanga” zosanunkha kanthu, zolamulidwa ndi nyanga “yaing’ono” yochenjera imene inali ndi maso a munthu ndi pakamwa polankhula zochuluka. Chotero, pamene Ulamuliro wa Uwiri wa Angelezi ndi Amereka ulowa m’chionongeko pansi pa ziweruzo zaukali za Nkhalamba yakale lomwe, “mafumu” onga nyanga amene’wo, monga otsalira a Ulamuliro wa Dziko wa Roma, adzaonongedwa limodzi nawo. (Danieli 7:23-26) Koma bwanji ponena za maufumu, maulamuliro, maripabliki ndi magulu a ndale za dziko amene’wo amene sanali mbali ya Ufumu wa Roma kapena ya Ulamuliro wa Dziko wa Uwiri wa Angelezi ndi Amereka, kuphatikizapo Mitundu ya British Commonwealth? Onsewa’nso, ayenera kuonongedwa pamene Nkhalamba ya kale lomwe ipereka chiweruzo chaukali pa dziko lino.—Chibvumbulutso 16:13 kufikira 19:21.

WOIMIRA WAMKULU WA MULUNGU AKUSONYEZEDWA

24. Kodi kuonongedwa kwa ulamuliro wa anthu kukusiya dziko lapansi liri losalamuliridwa?

24 Kodi kuonongedwa kotero’ko kwa maboma aumunthu a pa dziko lapansi onse ndi maulamuliro kudzasiya zochitika za anthu ziri mu mkhalidwe wa chipolowe, wokhoza kuchititsa chipwirikiti, kusaweruzika, ndi zosalamuliridwa? Tiyeni tisaope chionongeko chaukali chikudza’cho cha dongosolo iri la zinthu. Woweruza Wamkulu’yo, Nkhalamba ya Kale Lomwe, ndiye woyendetsa dziko lathu lapansi’li. Iye ayenera kuchotsa maboma opangidwa ndi anthu a ndale za dziko a kulamulira molakwa ndi kutsendereza m’malo mwakuti apatse malo boma labwino kopambana limene mtundu wa anthu ungakhale nalo. Lidzakhala chisonyezero cha Ulamuliro wake wa m’Chilengedwe Chonse kulinga ku malo okhala mtundu wa anthu dziko lapansi. Lidzakhala Boma la Dziko losaoneka limene lidzasonyeza mphamvu ndi ulamuliro wake kuchokera kumwamba, malo apamwamba kwambiri koposa London, Washington, Moscow, Peking, Tokyo, kapena malikulu ali onse a mtundu pa dziko lapansi. Yehova akutisonyeza Woimira Wake Wamkulu m’Boma la Dziko limene’lo loto lolosera limene iye anauzira Danieli kulota. Danieli akusonyeza kumwamba pamene iye tsopano akulemba kuti:

25. Kodi ndi motani m’mene Woimira Wamkulu wa Mulungu akusonyezedwera m’Danieli 7:13, 14?

25 “Ndinaona m’masomphenya a usiku, taonani, anadza ndi mitambo ya kumwamba wina ngati mwana wa munthu, nafika kwa Nkhalamba ya kale lomwe; ndipo anam’yandikizitsa pamaso pake. Ndipo anam’patsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse am’tumikire; ulamuliro wake ndi ulamuliro wosatha wosapitirira, ndi ufumu wake sudzaonongeka.”—Danieli 7:13, 14.

26. Kodi anthu ena amanena kuti “wina ngati mwana wa munthu” amaphiphiritsira yani?

26 Kodi ndani amene ali “wina ngati mwana wa munthu” amene’yo amene akudza, osati kuchokera pa dziko lapansi, koma kuchokera kumwamba “ndi mitambo” nafika kwa Nkhalamba ya kale lomwe wokhala pa mpando wachifumu m’khothi lachiweruzo? Ena amaganiza kuti, chifukwa chakuti “wina ngati mwana wa munthu” amene’yu sakuchulidwa pambuyo pake mu ulosi’wo koma “oyera a Wam’mwamba-mwamba’yo” akunenedwa kukhala akulandira ulamuliro wa ufumu, akunena munthu wachiungwe, “mtundu woyera” wa Mulungu monga gulu. Koma pali munthu wodalirika amene amasonyeza amene “wina ngati mwana wa munthu” amene’yo ali kweni-kweni. Kodi ziri choncho motani?

27, 28. (a) Kodi ndi motani m’mene wina wokhala ndi ukumu anakakamizikira kudziwikitsa amene “wina ngati mwana wa munthu” amene’yo anali? (b) Kodi ndi motani m’mene iye anachitiridwira pa nthawi imene’yo?

27 Zaka zoposa mazana khumi ndi asanu ndi anai zapita’zo, pa usiku wa Paskha (Nisan 14) wa chaka cha 33 C.E., mbadwa yachibadwidwe ya Mfumu Davide inaimirira pa chiweruzo kaamba ka moyo wake pa Bwalo lalikulu lachiweruzo la Yerusalemu. Mwamuna amene’yu atakana kuyankha maumboni oneneza amene ananenedwa mom’tsutsa, mkulu wansembe wotsogoza anati kwa iye:

28 Cholembedwa chonena za kuweruzidwa kwa mlandu’wo chimatiuza kuti: “Yesu anati kwa Iye, Mwatero, koma ndinena’nso kwa inu, kuyambira tsopano mudzaona Mwana wa munthu ali kukhala ku dzanja lamanja la mphamvu, ndi kufika pa mitambo ya kumwamba. Pomwepo mkulu wa ansembe anang’amba zobvala zake, nati, Achitira Mulungu mwano: tifuniranji mboni zina? Onani tsopano mwamva mwano’wo; muganiza bwanji? Iwo anayankha nati, Ali woyenera kumupha. Pomwepo iwo anathira malobvu pankhope pake, nam’bwanyula Iye; ndipo ena anam’panda kofu, nati, Utilote ife, Kristu Iwe; wakumenya Iwe ndani?”—Mateyu 26:63-68.

29. Kodi n’chiani’nso chimene chimasonyeza kuti Danieli 7:13 samatanthauza gulu la chiungwe?

29 Ndiyeno, panali, munthu wina pa dziko lapansi amene akanatha mwa chidaliro kusonya ku ulosi wa Danieli, chaputala chachisanu ndi chiwiri, vesi la khumi ndi chitatu, ndi kusonyeza molondola amene “wina ngati mwana wa munthu” amene’yo anali kweni-kweni. Zaka makumi asanu ndi limodzi mphambu zitatu pambuyo pake Yesu Kristu, woukitsidwa kuchokera kwa akufa ndi kulemekezedwa kumwamba’yo, anatulutsa chibvumbulutso kwa mtumwi wake Yohane pa dziko lapansi, ndipo Yohane anauziridwa kulemba ponena za iye: “Taonani, adza ndi mitambo; ndipo diso liri lonse lidzam’penya Iye, iwo’nso amene anam’pyoza; ndipo mafuko onse a pa dziko adzam’lira Iye. Terotu. Amen.” (Chibvumbulutso 1:7) Amene’wa ndi mau ena a Baibulo amatsimikizira kuti “wina wonga mwana wa munthu” wonga amene anaonedwa m’masomphenya a Danieli ndiye yesu Kristu Mbadwa ya Mfumu Davide. Mu Salmo 8:4 Davide ananena molosera za iye monga “mwana wa munthu.” (Ahebri 2:5-8) Mobwereza-bwereza Yesu ananena za iye mwini monga “Mwana wa munthu.” Osati gulu la “oyera a Wam’mwamba-mwamba,” koma Mbadwa yachifumu ya Davide ndiye munthu amene akuphiphiritsiridwa mu Danieli 7:13 kukhala ‘akudza ndi mitambo ya kumwamba.’—Mateyu 24:30.

30, 31. Danieli 7:13 anakwaniritsidwa, koma kodi n’chifukwa ninji osati mu 70 C.E. ?

30 Kodi ndi liti pamene kudza kweni-kweni kumene’ku kukuchitika? Malinga ndi kunena kwa mavesi a patsogolo pa Danieli 7:13 kunayenera kuchitika nyanga “yaing’ono” yothyola nyanga zina zitatu’zo pa mutu pa chirombo chachinai itakula, m’mene munali m’mbali yotsirizira ya zaka za zana lakhumi ndi chisanu ndi chitatu C.E. Chifukwa cha chimene’cho kudza kwa Mwana wa munthu “ndi mitambo ya kumwamba” sikunali nthawi imene’yo isanakwane, osati’nso mu 70 C.E., pamene ulosi wake unakwaniritsidwa “[Ayuda opanduka’wo] adzagwa ndi lupanga lakuthwa, nadzagwidwa ndende kunka ku mitundu yonse ya anthu; ndipo mapazi a anthu akunja [mitundu yosakhala Yachiyuda], adzapondereza kufikira kuti nthawi zao za anthu akunja zakwanira.” (Luka 21:24) “Nthawi za Akunja” zimene’zo zinali zitayamba pa kupasulidwa kwa Yerusalemu kochitidwa ndi Ababulo mu 607 B.C.E. M’kati mwa Nthawi za Akunja zimene’zo mitundu yosakhala Yachiyuda inaloledwa kulamuliro dziko lapansi popanda chidodometso cha ufumu wa Mulungu Waudavide.

31 Pa mapeto a Nthawi za Akunja zimene’zo, mu 1914 C.E., Wolowa nyumba wachifumu wa Davide moyenerera akanatha kupempha Mulungu ulamuliro wa Ufumu.

32, 33. Kodi n’chifukwa ninji sitinaone kudza kwa munthu wokhala ndi kuyenera kwalamulo?

32 Zochitika zokwaniritsa maulosi a Baibulo kuyambira mu 1914 C.E. kufikira lero lino zikutsimikizira kuti kudza kwa Mwana wa munthu kunachitika m’chaka chimene’cho. Ndithudi, palibe ali yense wa ife anaona kudza kotero’ko ndi maso athu eni-eni. Sitikanatha kutero, pakuti Danieli 7:13, 14 amalongosola Mwana wa munthu kukhala akudza, osati ku dziko lapansi, koma kwa Nkhalamba ya kale Lomwe, Woweruza’yo kumwamba amene “amasanduliza nthawi ndi nyengo, achotsa mafumu, nalonga mafumu.” (Danieli 2:21) Iye anadza moitanidwa ndi Nkhalamba ya kale lomwe’yo, monga momwe kwalembedwera pa Salmo 2:8, 9 kuti: “Undifunse, ndipo ndidzakupatsa amitundu akhale cholowa chako, ndi malekezero a dziko lapansi akhale ako ako. Udzawatyola ndi ndodo yachitsulo; udzawaphwanya monga mbiya ya woumba.” Ndiyeno popanda kuipita patsogolo programu ya nthawi ya chiweruzo imene’yi Nkhalamba Yakale lomwe’yo ikachita chimene iyo inaneneratu pa Ezekieli 21:25-27. Pamenepo, atatha kulamula kuchotsedwa kwa nduwira ndi chipewa chachifumu za ufumu wa Davide, iyo inati:

33 “Kweza chopepuka, chepsya chokwezeka. [wokhala pa mpando wachifumu wa Mfumu Davide]. Ndidzagubuduza gubuduza gubuduza ufumu uno, sudzakhala’nso kufikira akadza Iye mwini chiweruzo; ndipo ndidzaupereka kwa Iye.”

34. Chotero kodi ndi motani m’mene Mulungu anasonyezera ulamuliro wa m’chilengedwe chonse mu 1914?

34 Umboni wonse kufikira pa tsopano lino ndi wakuti Nkhalamba ya Kale lomwe inapatsa Wolowa nyumba wa Davide wokhala ndi “kuyenera” kwa ufumu Waumesiya pa mapeto a Nthawi za Akunja mu 1914. Monga momwe Danieli 7:14 ananeneratu kuti: “Anam’patsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse am’tumikire; ulamuliro wake ndi ulamuliro wosatha wosapitirira, ndi ufumu wake sudzaonongeka.” Imene’yo inali nthawi yeni-yeni yakuti mikombero yachitsulo ndi mkuwa yophiphiritsira’yo ichotsedwe pa “tsinde” la Ulamuliro Waumulungu wa m’Chilengedwe Chonse tsopano popeza kuti “nthawi zisanu ndi ziwiri” za zaka 2,520 zinali zitatha. Imene’yo inali nthawi yapadera yakuti Ulamuliro wa Yehova wa m’Chilengedwe Chonse udzatsimikizira kukhala ndi kuyenera kachiwiri’nso kulinga ku dziko lathu lapansi’li. Motani? Mwa kuchititsa “mphukira” kuphuka pa “tsinde” lokhala losaphuka kwa nthawi yaitali limene’lo, ndipo mwa njira imene’yo kutsimikizira kuti “Wam’mwamba-mwamba alamulira m’ufumu wa anthu, naupereka kwa ali yense Iye afuna, nauutsira wolubukira anthu.”—Danieli 4:17, 23, 32; Yesaya 11:1; Zekariya 3:8; 6:12.

35. Kodi ndi “mwala” wachifumu wotani umene pa nthawi imene’yo unayambitsidwa kuyenda, motsutsana ndi chiani?

35 Imene’yo inali’nso nthawi yakuti “mwala” wophiphiritsira usemedwe ‘m’phiri’ la Ulamuliro wa Mulungu wa m’Chilengedwe Chonse ndiyeno n’kuponyeredwa pa “fano” la ulamuliro wa ndale za dziko lonse wa pa dziko lapansi. Uwo walunjikitsidwa kukantha “mapazi” a chitsulo ndi dongo. Pamenepo uyenera kupera kukhala ufa fano lonse lolambiridwa’lo. Potsirizira pake uyenera kukula kukhala phiri, kudzaza dziko lonse lapansi. – Danieli 2:34, 45.

36. Kodi ndi kubadwa kwachifumu kotani kumene pa nthawi imene’yo kunachitika, ndipo’nso chilengezo chotani?

36 Mofananamo, mu 1914 ufumu Waumesiya unatuluka m’mimba ya gulu longa mkazi la yehova kumwamba, ndipo mau a Chibvumbulutso 12:5 anakwaniritsidwa: “Anabala mwana wamwamuna, amene adzaweruza mitundu yonse ndi ndodo yachitsulo: ndipo anakwatulidwa mwana wake amuke kwa Mulungu, ndi ku mpando wachifumu wake.” Pamenepo, mosakaikira, zinachitika kuti miyanda miyanda ya angelo amene anatumikira Nkhalamba ya Kale lomwe ndi zikwi khumi kuchulukitsa zikwi khumi zimene zimaimirira pamaso pake peni-peni zinagwirizana nawo m’kulengeza m’chilengedwe chonse kuti: “Ufumu wa dziko unakhala ufumu wa Ambuye wathu ndi wa Kristu wake, ndipo adzalamulira monga mfumu kwamuyaya.”—Chibvumbulutso 11:15, NW; Danieli 7:10.

37. Chifukwa cha chimene’cho, kodi ndani amene ayenera kukhala Woimira Wamkulu wa Mulungu mu ulamuliro’wo?

37 Mothandizidwa ndi zonse zapamwambapo’zo, pamenepa, kodi ndani, amene ali Woimira Wamkulu wa Mulungu wa boma lathu la dziko likudza’lo? Yesu Kristu, tsopano Wolowa nyumba wolemekezedwa Wachikhalire wa Mfumu Davide. Monga munthu wangwiro wa m’mzera wachifumu wa Davide, iye “adapereka nsembe imodzi chifukwa cha machimo, anakhala pa dzanja lamanja la Mulungu chikhalire [mu 33 C.E.], kuyambira pomwepo alindirira, kufikira adani ake aikidwa akhale mpando ku mapazi ake.”—Ahebri 10:12, 13; 1:3, 4; Salmo 110:1-6.

38 Mu ulamuliro wa dziko ukudza’wo padzakhala olamulira limodzi ndi Woimira Wamkulu wa Mulungu’yo, pakuti Danieli 7:27, 28 amati: “Ndipo ufumu, ndi ulamuliro, ndi ukulu wa maufumu, pansi pa thambo lonse, zidzapatsidwa kwa anthu opatulika a Wam’mwamba-mwamba; ufumu wake ndiwo ufumu wosatha, ndi maiko onse adzam’tumikira ndi kum’mvera. Kutha kwake kwa chi’nthu’chi nkuno.” Chotero tsopano funso likubuka lakuti, Kodi “anthu amene ali opatulika a Wam’mwamba-mwamba” ndiwo mtundu wakuthupi wa mneneri Danieli, mtundu wachibadwidwe wodulidwa wa Ayuda kapena Aisrayeli? Kodi mafuko khumi ndi awiri a Israyeli amene anali mbadwa zeni-zeni za Abrahamu, Isake ndi Yakobo anayenera kukhala anthu apamwamba m’kati mwa nyengo yosadziwika mapeto ya ulamuliro wa Mesiya (Kristu), mitundu yonse ya Akunja ikumakhala yogonjera kwa iwo monga olamulira a dziko? Anthu a mafuko onse afunsa funso limene’li. Kodi tsopano tingalilingalire pamodzi?

38. Kodi ndi mafunso otani amene amabuka ponena za “oyera” amene akukhala ndi phande mu kulamulira?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena