Mutu 7
Kusankha Okhala ndi Phande mu Ulamuliro wa Dziko
1. Kodi ndi nsonga zotani zonena za okhala ndi phande mu ulamuliro wa dziko zimene pa nthawi ina zinali chinsinsi?
KODI ndani amene adzakhala okhala ndi phande limodzi ndi Wolowa Nyumba wolemekezedwa Wachikhalire wa Mfumu Davide m’Boma la Dziko lolonjezedwa’lo? Kodi ndi okhala ndi phande angati amene adzakhalapo? Ndipo kuti—pano pa dziko lapansi, kapena kumwamba? Pa nthawi ina mafunso amene’wo anali chinsinsi. Koma sali’nso chinsinsi!
2, 3. Kodi Yohane anali kuti polandira Chibvumbulutso, ndipo chifukwa ninji?
2 Cha kumapeto kwa zaka za zana loyamba za Nyengo yathu Ino, Wolowa Nyumba Wachikhalire wa Mfumu Davide mu ufumu Waumesiya, ndiko kuti, Yesu Kristu, anabvumbula mayankho ofunika’wo. Mwa bvumbulutso lozizwitsa loperekedwa kuchokera kumwamba chidziwitso chinaperekedwa kwa munthu pano pa dziko lapansi, osati pa Yerusalemu, koma pa chisumbu cha akaidi cha Patmo m’Nyanja ya Aegaen, osati kutali kwambiri ndi Efeso wakale, Asia Minor. Inde, munthu amene’yo anali Myuda wachibadwidwe ndi wodulidwa. Kodi Myuda amene’yo anali pa chisumbu cholangira Chachiroma chimene’cho chifukwa chakuti iye anali atagwirizana nawo m’chipanduko cha Ayuda, m’chaka cha 66 C.E., chimene chinatsogolera ku chionongeko cha mtundu’wo chochitidwa ndi magulu ankhondo Achiroma mu 70 C.E.? Eya, tiyeni tilole wandende Wachiyuda amene’yu atiuze:
3 “Ine Yohane, mbale wanu ndi woyanjana nanu m’chisautso ndi ufumu ndi chipiriro zokhala m’Yesu, ndinakhala pa chisumbu chochedwa Patmo, chifukwa [cha chiani?] cha mau a Mulungu ndi umboni wa Yesu. Ndinagwidwa ndi Mzimu tsiku la Ambuye, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau akulu, ngati a lipenga, ndi kuti, Chimene upenya, lemba m’bukhu, nulitumize kwa Mipingo isanu ndi iwiri, ku Efeso, ndi ku Smurna, ndi ku Pergamo, ndi ku Tiyatira, ndi ku Sarde, ndi ku Filadelfeya, ndi ku Laodikaya.”—Chibvumbulutso 1:9-11.
4, 5. (a) Kodi ndi motani m’mene Yohane anagwirizanira ndi Yesu Kristu? (b) Kodi Yohane anali wokhala ndi phande m’chiani pa nthawi’yo limodzi ndi awo amene iye anawalembera kalata?
4 Yohane amene’yu, mwana wa Zebedayo, anali msodzi m’Nyanja ya Galileya, koma anasiya ntchito yake ya kusodza imene’yi nakhala ‘msodzi wa anthu,’ mmodzi wa atumwi khumi ndi awiri a Mesiya Yesu. (Mateyu 4:18-22; Luka 5:1-11) Chotero Yohane anali Myuda wotembenuzidwa kukhala Mkristu, wophunzira wokhulupirika wa Yesu Mesiya, Kristu, uyo “wodzozedwa” ndi mzimu wa Mulungu kukhala Mfumu Yaumesiya. Yohane anakhala mboni yoona ndi maso ya kupachikidwa kwa Yesu Kristu amene’yu pa Kalvari, ndipo pa tsiku lachitatu pambuyo pake iye anaona Yesu woukitsidwa’yo. Pa tsiku la makumi anai pambuyo pake iye ndi atumwi anzake anaona Yesu Kristu woukitsidwa’yo akukwera kumwamba, kukakhala pa dzanja lamanja la Mulungu, Atate wake wakumwamba.
5 Ndipo’nso, Yohane mtumwi analimo m’Yerusalemu pa tsiku la Pentekoste wa 33 C.E., pamene Yehova Mulungu anagwiritsira ntchito Yesu monga Woimira wake Wamkulu m’kutsanulira mzimu woyera pa ophunzira osonkhana okwanira zana limodzi mphambu makumi awiri. (Machitidwe 1:1 mpaka 2:36) Chotero pofika pa nthawi imene Yohane analemba Chibvumbulutso mu 96 C.E., iye anali atapirira chisautso ndi kubvutika monga Mkristu kwa zaka makumi asanu ndi limodzi mphambu zitatu. Yohane ananena za iye mwini kukhala “woyanjana nawo” mu ufumu limodzi ndi ophunzira anzake a Kristu. Kodi ndi okhala ndi phande angati amene anayenera kukhala m’boma Laufumu la dziko limene’lo? Yohane akunena za iye mwini kukhala “wophunzira amene Yesu anam’konda,” ndipo anapatsidwa chidziwitso chimene’chi.—Yohane 13:23, NW; 21:20.
6, 7. (a) Kodi ndi pa phiri lotani pamene Yohane anaima kawiri-kawiri ndi Mwanawankhosa Yesu Kristu? (b) Kodi ndi angati amene Yohane anawaona akuima ndi Iye pa Phiri la Ziyoni wakumwamba?
6 Mtumwi Yohane akanatha kukumbukira m’mene, kale’lo mu 29 C.E., Yohane Mbatizi anasonyera kwa Yesu wodzozedwa ndi mzimu’yo nati: “Onani! Mwanawankhosa wa Mulungu!” Ndipo Yohane mwana wa Zebedayo anatsatira Yesu kaamba ka chifukwa chimene’cho. (Yohane 1:36-36) Chifukwa cha chimene’cho, zaka makumi asanu ndi limodzi phambu zisanu ndi ziwiri pambuyo pake, pamene Yohane anaona ndi kumva m’masomphenya ouziridwa Yesu Kristu wolemekezedwa’yo wonenedwa kukhala “mwana wankhosa,” iye anazindikira amene anali kunenedwa-osati wina’nso koma Yesu Kristu, amene, pa dziko lapansi, anaperekedwa nsembe monga mwanawankhosa wopanda chimo pa guwa lansembe la Mulungu. (Yohane 1:29; 1 Petro 1:18, 19) Nthawi zambiri m’kati mwa zaka’zo 30-33 C.E., Yohane anaima limodzi ndi Mwanawankhosa wophiphiritsira amene’yu, Yesu Kristu, pa Phiri la Ziyoni la pa dziko lapansi, phiri pa limene Yerusalemu weni-weni anali. Koma phiri la pa dziko lapansi limene’lo linafikira pa kugwiritsiridwa ntchito monga chizindikiro cha malo a kumwamba kumene boma la dziko Laumesiya likakhala ndi malikulu ake. Kodi ndani amene adzaimirira pamenepo monga okhala ndi phande limodzi ndi Yesu Kristu m’boma la dziko lakumwamba? Yohane anaona chiwerengero nati;
7 “Ndipo ndinapenya, taonani, Mwanawankhosa’yo alikuimirira pa phiri la Ziyoni, ndipo pamodzi ndi Iye zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai, akukhala nalo dzina lake ndi dzina la Atate wake lolembedwa pamphumi pao. Ndipo ayimba ngati nyimbo yatsopano ku mpando wachifumu, ndi pamaso pa zamoyo zinai, ndi akulu; ndipo palibe munthu anakhoza kuphunzira nyimbo’yi, koma zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai, ogulidwa kuchokera kudziko. Iwo ndiwo amene sadetsedwa pamodz ndi akazi; pakuti ali anamwali. Iwo ndiwo amene atsata Mwanawankhosa kuli konse amukako. Iwowa anagulidwa mwa anthu, zipatso zoundukula kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa. Ndipo m’kamwa mwao simunapezedwa bodza; ali opanda chirema.”—Chibvumbulutso 14:1, 3-5.
8. Kodi n’chiani chimene chinasonyeza kuti pakakhala kuwerengeka kwa okhala ndi phande mu Ufumu?
8 Aha, chabwino, zikwi zana kudza makumi anai mphambu anai chabe ‘anagulidwa kuchokera ku dziko lapansi,’ “anagulidwa mwa anthu, zipatso zoundukula mwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa,” kaamba kukakhala ndi malo pa Phiri la Ziyoni la boma kumwamba. Chiani? 144,000 okha kuchokera pakati pa anthu mabiliyoni ambiri amene akhala ndi moyo ndi kufa m’kati mwa zaka mazana khumi ndi asanu ndi anai zapita’zo chiyambire m’masiku a atumwi a Kristu? 144,000 ali owerengeka kwambiri poyerekezera? Cheni-cheni Chamalemba chimene’chi n’chosiyana motani nanga m’mene chiriri ndi lingaliro la m’Chikristu cha Dziko lakuti mamiliyoni mazana ochuluka a ziwalo zake za chalichi adzapita kumwamba pa imfa! Pano tiyeni tikumbukire kuti “zipatso zoundukula” za kututa kuli konse sindizo zokolola zonse, koma ziri chizindikiro chaching’ono chabe chosankhidwa pa mbeu zonse. Yesu anachulapo za kuwerengeka kwa ziwalo za Ufumu pamene iye ananena ndi ophunzira ake kuti: “Musaopa, kagulu ka nkhosa inu; chifukwa Atate wanu akonda kukupatsani Ufumu. Gulitsani zinthu muli nazo, nimupatse mphatso zachifundo; mudzikonzere matumba a ndalama amene sakutha, chuma chosatha m’Mwamba.”—Luka 12:32, 33.
AISRAYELI AUZIMU
9, 10. (a) Kodi 144,000’wo anayenera kusindikizidwa chizindikiro ndi chiani? (b) Kodi iwo anasindikizidwa chizindikiro kuchokera mu mtundu uti, ndipo kodi ndi angati m’chigawo chiri chonse?
9 Chiwerengero chaching’ono kwambiri chimene’cho, 144,000, sindicho kuwerengera molakwa. Chinaperekedwa’nso kale-kale ndi Yohane, m’Chibvumbulutso 7:1-8. Pamenepo kukumveketsedwa bwino lomwe kuti chimodzi cha zofunika za kukhala mmodzi a “kagulu ka nkhosa’ ka olowa nyumba a Ufumu ndicho chija cha kukhala wolembedwa chizindikiro pa mphumi ndi “chizindikiro cha Mulungu wamoyo,” kuphatikiza pa kukhala atalembedwa pa mphumi, kunena kwake titero, dzina la Mwanawankhosa ndi dzina la Atate wake, Yehova Mulungu. Kodi ndi angati amene amakwaniritsa chiyeneretso chofunika chimene’chi, ndipo kodi iwo ndi a mtundu kapena pfuko liti? Mtumwi Yohane sakutisiya ndi chikaikiro chiri chonse ponena za zimene’zi, pamene akuti:
10 “Ndipo ndinamva chiwerengero cha iwo osindikizidwa chizindikiro, zikwi makumi khumi ndi makumi anai mphambu anai, osindikizidwa chizindikiro mwa mafuko onse a ana a Isryaeli. Mwa pfuko la Yuda anasindikizidwa chizindikiro zikwi khumi ndi ziwiri: mwa pfuko la Rubeni zikwi khumi ndi ziwiri: mwa pfuko la Gadi zikwi humi ndi ziwiri: mwa pfuko la Aseri zikwi humi ndi ziwiri: mwa pfuko la Nafitali zikwi khumi ndi ziwiri: mwa pfuko la Manase zikwi khumi ndi ziwiri: mwa pfuko la Simeoni zikwi khumi ndi ziiri: mwa pfuko la Levi zikwi khumi ndi ziwiri: mwa pfuko la Isakara zikwi khumi ndi ziwiri: mwa pfuko la Zebuloni zikwi khumi ndi ziwiri: mwa pfuko la Yosefe zikwi khumi ndi ziwiri: mwa pfuko la Benjamini anasindikizidwa chizindikiro zikwi khumi ndi ziwiri.”—Chibvumbulutso 7:4-8.
11, 12. (a) Kodi 144,000’wo ayenera kukhala Israyeli wa mtundu wotani? (b) Malinga ndi kunena kwa Aroma 9:29 ndi 11:5, kodi ndi Ayuda angati achibadwidwe amene anayenerera?
11 Maina a mapfuko khumi ndi awiri amene’wa akusiyana ndi mpambo wa maina a mafuko khumi ndi awiri oyambirira a Israyeli wachibadwidwe, monga momwe waperekedwera m’Genesis 49:3-28. Moyenerera’di choncho, pakuti Chibvumbulutso 7:4-8 chikupereka maina a mafuko a Israyeli wauzimu. Iwo ayenera kukhala Aisrayeli auzimu ngati iwo ati aime limodzi ndi Mwanawankhosa Yesu Kristu pa Phiri la Ziyoni wakumwamba. (Chibvumbulutso 14:1-3; Ahebri 12:22) Pano tiyenera kulingalira mau onenedwa kwa Mwanawankhosa Yesu Kristu, pa Chibvumbulutso 5:9, 10: “Mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu [a yani? Mwa Israyeli wachibadwidwe ndi wodulidwa? Ai, koma mwa] a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse, ndipo mudawayesa iwo ufumu ndi ansembe kwa Mulungu wathu; ndipo achita ufumu padziko lapansi.” Mbiri ya Baibulo imasonyeza kuti panali “otsalira” chabe a Ayuda monga mwa thupi amene anakhala Akristu. Kunali monga momwe’di Myuda wotembenuzidwa kukhala Mkristu, mtumwi Paulo, ananenera kuti:
12 “Akadapanda Yehova wa makamu kutisiyira mbeu, tikadakhala ngati Sodumu, ndipo tikadapangidwa kukhala ngati Gomora.” Ndipo’nso kuti: “Chifukwa cha chimene’cho, mwa njira imene’yi, pa nyengo ino’nso pali otsalira monga mwa kusankha kochitidwa chifukwa cha kukoma mtima kwapadera [ndipo osati mwa umbadwa wakuthupi wa Israyeli].”—Aroma 9:29, 11:5, NW.
13, 14. (a) Kodi 144,000’wo ayenera kukhala Aisrayeli akuthupi? (b) Kodi iwo ayenera kukhala Aisrayeli auzimu ku mlingo wotani?
13 M’malo mwakuti anthu 144,000 “ochokera mwa mtundu uli wonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe” alingaliridwe kukhala Aisrayeli iwo akayenera kukhala otero m’lingaliro lophiphiritsira, ndiko kuti, kukhala Aisrayeli cham’kati. Monga momwe Aroma 2:29 amatikumbutsira kuti: “Myuda ndiye amene akhala wotero mumtima; ndipo mdulidwe uli wa mtima, mumzimu.”
14 Ndipo’nso, chinthu china chofunika kwambiri chimafunikiritsa okhala ndi phande limodzi ndi Yesu Kristu’wo mu ulamuliro wa dziko kukhala Aisrayeli a mtundu wauzimu. Chinthu chofunika kwambiri chimene’chi ndicho chimene Yesu anauza wolamulira Wachiyuda Nikodemo, kuti: “Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sakhoza kuona Ufumu wa Mulungu . . . Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu. Chobadwa m’thupi chikhala thupi, ndipo chobadwa mwa Mzimu, chikhala mzimu . . . chotero ali yense wobadwa mwa Mzimu.” (Yohane 3:3-8) Chifukwa cha chimene’cho, Ayuda achibadwidwe kudza’nso osakhala Ayuda amene akukhala ophunzira odzipereka, obatizidwa a Kristu ndi amene Mulungu akuwasankha kukakhala ndi phande limodzi ndi Kristu mu ulamuliro wa dziko Mulungu amawabala ndi mzimu wake. Onse otero’wo amakhala Aisrayeli auzimu.
15. Kodi ndi ndani amene tsopano akupanga “Israyeli wa Mulungu”?
15 Chifukwa cha chimene’cho tingathe kuzindikira kuti Akristu onse obadwa ndi mzimu otero’wo (otengedwa kwa Ayuda ndi Akunja omwe) ali “cholengedwa chatsopano.” Amene’wa amadzisungira mogwirizana ndi “lamulo” laumulungu, ndipo osati mogwirizana ndi mpambo wa malamulo wa Chilamulo choperekedwa kupyolera mwa Mose pa Phiri la Sinai, Arabia. Ndiko mogwirizana ndi awo okhala “cholengedwa chatsopano” chimene’chi kuti Myuda wotembenuziridwa ku Chikristu’yo Paulo akulemba kuti: “Awo onse amene adzayenda molongosoka mogwirizana ndi lamulo la khalidwe limene’li, pa iwo pakhala mtendere ndi chifundo, ngakhale pa Israyeli wa Mulungu.”— Agalatiya 6:15, 16, NW.
16. Kodi Akunja adzalowa mu ulamuliro wa Myuda pa Yerusalemu wa pa dziko lapansi?
16 Chifukwa cha chimene’cho, n’kolakwa, kosagwirizana ndi malemba, kwa ali yense kunena kuti Ayuda achibadwidwe ndi odulidwa, “uja amene ali Israyeli mwa njira yakuthupi,” adzakhala olamulira a dziko lapansi okhala ndi Yerusalemu wa Ripabliki la Israyeli monga malikulu ake. (1 Akorinto 10:18, NW) Anthu amene tsopano ali a mitundu Yachikunja sadzalowa mu ulamuliro wina uli wonse wa Aisrayeli achibadwidwe ndi odulidwa. M’malo mwake, mitundu yonse, kuphatikizapo Ayuda akuthupi, idzalowa mu ulamuliro wa dziko wa “mafuko khumi ndi awiri” akumwamba a Israyeli wauzimu, limodzi ndi Mfumu yake Yesu Kristu, pa nthawi yokwanira ya Mulungu, posachedwapa.
KUUKITSIDWIRA KU ULAMULIRO M’BOMA LA DZIKO
17, 18. Kodi n’chiani chimene Mulungu anaikiratu ponena za okhala ndi phande mu ulamuliro wa dziko?
17 Yehova Mulungu, Mfumu ya Chilengedwe Chonse, analinganiziratu kapena anaikiratu chiwerengero chimene chikakhala ndi phande limodzi ndi Kristu mu ulamuliro wa Ufumu pa dziko lonse lapansi. Iye anaikiratu’nso zofunika ndi ziyeneretso za munthu ali yense kaamba ka awo oyenera kukhala ndi phande mu ulamuliro wa dziko. Ndicho chifukwa chake padzakhala 144,000 okha amene adzakhala ndi phande limodzi ndi Yesu Kristu m’boma la dziko. Iwo ayenera kukhala Aisrayeli auzimu. Kusiyapo Mwana wake Yesu Kristu, Yehova sanalinganiziretu kapena kusankhiratu anthu. M’malo mwake, iye anakhazikitsa pasadakhale zofunika ndi ziyeneretso za munthu ali yense kaamba ka olowa nyumba a Ufumu. Mothandizidwa ndi zimene’zi tikumvetsetsa Aroma 8:29, 30, NW:
18 “Awo amene iye anawadziwa choyamba iye anawaikiratu’nso kukhala ofanana ndi chifanizo cha Mwana wake, kuti akakhale woyamba kubadwa pakati pa abale ambiri. Ndipo’nso, awo amene iye anawairkiratu ndiwo anthu amene’nso iye anawaitana; ndipo awo amene iye anawaitana ndiwo anthu amene iye anawalengeza kukhala olungama [kapena, amene iye akuwalungamitsa]. Potsirizira pake awo amene iye anawalengeza kukhala olungama ndiwo’nso anthu amene iye anawalemekeza.”
19. Kodi ndi mabvuto otani amene aikiridwatu kaamba ka okhala ndi phande mu ulamuliro wa dziko?
19 Mogwirizana ndi zofunika za kuikiratu’ko, awo amene “akukhala ofananandi chifanizo” cha Mwana wa Mulungu ayenera kubvutika limodzi naye tsopano, monga momwe’di mtumwi Yohane anasonyezera pa Chisumbu cha Patmo. Iwo akufunikira kupirira ngakhale kufikira imfa. Koma kaamba ka chitonthozo chao mtumwi Paulo analemba kuti: “Okhulupirika mau’wa: Pakuti ngati tidamwalira ndi Iye, tidzakhala’nso moyo ndi Iye: ngati tipirira, tidzachita’nso ufumu ndi Iye.” (2 Timoteo 2:11, 12) Ndipo mtumwi Yohane wandende’yo analangizidwa kulembera makalata mpingo wa pa Smurna kuti: “Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taonani, mdierekezi adzaponya ena a inu m’nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso masiku khumi. Khala wokulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.”—Chibvumbulutso 2:10.
20, 21. Kodi chao chiyenera kukhala chiukiriro cha mtundu wotani? Chifukwa ninji?
20 Popeza kuti Aisrayeli auzimu 144,000 ndiwo awo amene ‘agulidwa kuchokera ku dziko lapansi’ ndipo “anagulidwa mwa anthu,” m’tsogolo mwao simuli’nso pa dziko lapansi ndi pakati pa mtundu wa anthu. Monga “zipatso zoundukula kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa,” iwo ayenera kuperekedwa kwa amene’wa kumwamba. Chotero chiukiriro chao kuchokera kwa akufa, kumene iwo anafikako atatsimikizira kukhala okhulupiririka, chiyenera kukhala kumka ku moyo wauzimu kumwamba. Chao’cho chiri chiukiriro chauzimu chimene chikulongosoledwa mu 1 Akorinto 15:42-55. (Chibvumbulutso 14:3, 4) Chifukwa cha kubvutika m’chigwirizano ndi Kristu ndi kutsimikizira kukhala okhulupirika kwa Mulungu ngakhale kufikira imfa, Aisrayeli auzimu 144,000 amafupidwa kwambiri ndi Mulungu amene angathe kuukitsa akufa. Mphotho yosungidwira anthu okhulupirika amene’wa ikusonyezedwa kwa ife m’Chibvumbulutso 20:4-6. Pamenepo mtumwi Yohane, amene iye mwini akuyembekezera mphotho yakumwamba, akulemba kuti:
21 “Ndipo ndinaona mipando yachifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa chiweruziro; ndipo ndinaona mizimu ya iwo amene adawadula khosi [chifukwa ninji?] chifukwa cha umboni wa Yesu, ndi chifukwa cha mau a Mulungu,ndi iwo amene sanalambira chirombo, kapena fano lake, nisanalandira lemba’lo pamphumi ndi pa dzanja lao; ndipo anakhala ndi moyo, nachita ufumu pamodzi ndi Kristu zaka chikwi . . . Ndiko kuuka kwa akufa koyamba. Wodala ndi woyera mtima ali iye amene achita nao pa kuuka koyamba; pa iwowa imfa yachiwiri iribe ulamuliro; komatu adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Kristu, nadzachita ufumu pamodzi ndi Iye zaka chikwi’zo.”
22-24. Kodi ndi motani m’mene amene’wa samalambirira chirombo kapena fano lake?
22 Kuyambira m’zaka za zana loyamba C.E. kufikira tsopano, Aisrayeli auzimu 144,000, amene akusankhidwira ulamuliro wa kumwamba monga mafumu limodzi ndi Yesu Kristu, akana kulambira “chirombo” chophiphiritsira, ndiko kuti, gulu la ndale za dziko kaamba ka ulamuliro wa dziko lonse lapansi mwa njira ya maboma aumunthu. M’kati mwa nthawi ya moyo wa Aisrayeli auzimu kuyambira m’masiku a atumwi kufikira tsopano Ulamuliro wa Dziko wa Roma ndi Ulamuliro wa Uwiri wa Angelezi ndi Amereka akhala ziwalo zazikulu za “chirombo” cha ndale za dziko, mofanana ndi “mitu” iwiri yotsirizira pa chirombo cha mitu isanu ndi iwiri chimene’chi.
23 Ulamuliro wa Dziko wa Uwiri wa Angelezi ndi Amereka, Ulamuliro wa Dziko Wachisanu ndi Chiwiri wa ulosi wa Baibulo, wakhala waukulu pa kulinganiza ndi kusungabe “fano” la “chirombo.” “Fano” limene’li la ulamuliro wa dziko lonse lapansi lopangidwa ndi maboma opangidwa ndi anthu linali, poyamba, Chigwirizano cha Mitundu, ndipo, tsopano, ndiro Mitundu Yogwirizana, kaamba ka kusungitsa mtendere ndi chisungiko za dziko. Ulamuliro wa Dziko wa Uwiri wa Angelezi ndi Amereka unachitiridwa chithunzi-thunzi, monga momwe tidzakumbukirira, ndi nyanga “yaing’ono” yokhala ndi maso ndi pakamwa pamutu pa “chirombo chachinai” choonedwa m’masomphenya a Danieli onena za zirombo zinai’zo.
24 Otsalira okhulupirika a Aisrayeli auzimu 144,000 akana kulambira “chirombo” cha ndale za dziko mwa kuchita kulambira boma kapena chiri chonse cha zizindikiro zake. Akana kulambira ngakhale “mutu” wapadera wa “chirombo,” ndiko kuti, Ulamuliro wa Dziko wa Britain ndi Amereka. Ndipo popeza kuti iwo anakana kulambira “chirombo” chophiphiritsira’cho, iwo mosasintha amakana kulambira “fano” lake longa limene linalinganizidwa ndi Ulamuliro wa Dziko Wachisanu ndi Chiwiri, nyanga “yaing’ono” yokhala ndi maso ndi pakamwa.—Chibvumbulutso 13:1-17.
25. Kaamba ka kukana kulambira kotero’ko kodi ndi motani m’mene iwo anabvutikira m’Nkhondo Yoyamba ya Dziko?
25 Chifukwa chakuti iwo amakana kulambira Boma la ndale za dziko mokonda dziko lao, nyanga “yaing’ono” yophiphiritsira’yo, Ulamuliro wa Dziko wa Angelezi ndi Amereka, unachitapo kanthu. Uwo unabvutitsa otsalira amene’wa a “oyera a Wam’mwamba-mwamba’yo,” monga momwe Danieli 7:25 anali ataneneratu. Kaamba ka chiyeso cha kudzipereka kwao ku ufumu wake Waumesiya umene unakhazikitsidwa pa mapeto a Nthawi za Akunja mu 1914, Wam’mwamba-mwamba’yo anapereka “oyera” ake m’manja mwa nyanga “yaing’ono yophiphiritsira” “mpaka nthawi imodzi, ndi nthawi zina, ndi nthawi yanusu,” kapena zaka zitatu ndi theka, m’kati mwa Nkhondo Yoyamba ya Dziko. Koma zobvuta zimene “oyera” anazipirira pa nthawi imene’yo zalephera kuwapangitsa kugonjera.
26. Kodi ndi mtundu wotani wa imfa umene okhala ndi phande mu ulamuliro wa dziko amakumana nawo?
26 “Oyera a Wam’mwamba-mwamba’wo” amadziwa kuti, ngakhale ngati anthu atawapha kaamba ka kukhala ndi moyo mokhulupirika mogwirizana ndi umboni umene iwo amapereka ku ufumu wa Mulungu Waumesiya, iwo adzakhala ndi chiukiriro. Imfa yao sindiyo “imfa yachiwiri” mu imene mulibe chiukiriro. (Chibvumbulutso 2:10, 11; 20:6; 21:8) Akristu obadwa ndi mzimu okhala ndi kudzipereka kotheratu kotero’ko ndiwo amene Mulungu Wam’mwamba-mwamba amawasankhira kukhala ndi phande limodzi ndi Mwana wake Yesu Kristu m’boma la dziko likudza’lo. Kodi zabwino za mtundu wa anthu zikakhala m’manja osungika kwambiri koposa mwa awo amene Mulungu akuwasankha? Ai?
27. Kodi ndi motani m’mene boma la Mulungu lidzakhalira labwino kopambana kaambaka mtundu wa anthu?
27 Kaamba ka chifukwa chachikulu chimene’cho onse okonda chilungamo ndi kupanda chibvundi m’boma angayembekezere ulamuliro wa zaka chikwi wa Mfumu Yesu Kristu ndi anzake 144,000. Yehova Mulungu monga Mfumu ya m’Chilengedwe Chonse walinganiza kupatsa mtundu wonse wa anthu boma labwino kopambana kwa iwo. Lidzakhala boma la dziko loposa laumunthu, lokhala ndi mphamvu mokwanira kuthetsa ziyambukiro zonse zoipa za zaka zikwi zambiri zapita’zo za kulamuliro molakwa kwa anthu ndi kupanda mphamvu. Pamaso pa boma la dziko losagonjetseka limene’li Ulamuliro wa Dziko Wachisanu ndi Chiwiri wamphamvu’wo ndi mitundu ina yonse ya dziko m’kati ndi kunja kwa gulu la Mitundu Yogwirizana, uyenera kugwada pansi mogonja ndi kufafanizika m’kati mwa “chisautso chachikulu” chimene tsopano chiri pafupi kwambiri’cho. Ngakhale Satana Mdierekezi ndi ziwanda zake, mphamvu yosaoneka kutseri kwa “chirombo” cha mitu isanu ndi iwiri’cho cha ulamuliro wa ndale za dziko, ayenera kuona kulimba-limba konse kukhala kopanda pake. Iwo adzalandidwa ulamuliro wao wonse wosaoneka wa dziko ndi kuikidwa m’ndende m’phompho losindikizidwa chizindikiro kwa zaka chikwi za kulamulira kwa Kristu ndi mafumu ndi ansembe anzake 144,000.—Chibvumbulutso 20:1-3.
28. Kodi n’chifukwa ninji tikuyang’ana m’tsogolo mwaphamphu ku ufumu umene’wo kukhala uli pafupi kwambiri?
28 Mwa pemphero laphamphu ndi lofunitsitsa kwa Mfumu Ambuye Yehova tikuyembekezera kukwaniritsidwa kwa mau otsimikiziritsa a mngelo kwa Danieli akuti: “Ndipo ufumu, ndi ulamuliro, ndi ukulu wa maufumu, pansi pa thambo lonse zidzapatsidwa kwa anthu optatulika a Wam’mwamba-mwamba’ ufumu wake ndiwo ufumu wosatha, ndi maiko onse adzam’tumikira ndi kum’mvera.” (Danieli 7:27) Kupatsa kwa Yehova ulamuliro wa dziko kwa Yesu Kristu ndi “oyera” Ake ena onse tsopano kuyenera kukhala kuli pafupi kwambiri. Kwa zaka zoposa mazana khumi ndi asanu ndi anai kudza makumi anai chiyambire pa Pentekose wa 33 C.E., Yehova wakhala akusankha 144,000 kukagwirizana ndi Mwana wake Woyera Yesu Mesiya mu ulamuliro wa Ufumu pa dziko lonse lapansi. Pofika pa tsopano lino tiyenera kukhala tikukhala ndi moyo m’masiku a otsalira otsirizira a gulu losankhidwa la “oyera” 144,000 limene’lo. Ndipo’nso papita zaka zoposa makumi asanu ndi limodzi chiyambire pamene Nthawi za Akunja zinatha mu October wa 1914. Chifukwa cha chimene’cho nthawi iyenera kukhala iri pafupi yakuti Mfumu yakumwamba yokhazikitsidwa pa mpando wachifumu’yo Yesu Kristu aphwanye mitundu kukhala zidutswa-zidutswa m’nthawi ya nsautso yaikulu kopambana ya mtundu wa anthu.—Salmo 2:5-9.
29. Kodi n’chifukwa ninji tikukhumba kupulumuka “nthawi ya mapeto” a mitundu?
29 “Nthawi ya mapeto” tsopano yatsala pang’ono kuthera mitundu! Tiyenitu zimene’zo zisasonyeze athu limodzi ndi mitundu yaudziko imene’yo. (Chibvumbulutso 19:11-21) Tiyenitu tsiku ndi tsiku tichite ntchito zathu kwa Mfumu Ambuye Yehova Mulungu kotero kuti, ngati iye afuna, tipulumuke kulowa mu ulamuliro wa dziko wa zaka chikwi wa Kristu.