Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • my nkhani 70
  • Yona ndi Chinsomba

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yona ndi Chinsomba
  • Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova Anamulezera Mtima Yona
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Anaphunzira pa Zolakwa Zake
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Anaphunzira pa Zolakwa Zake
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Yona Aphunzira za Chifundo cha Yehova
    Nsanja ya Olonda—1996
Onani Zambiri
Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
my nkhani 70

NKHANI 70

Yona ndi Chinsomba

TAONANI munthu ali m’madzi’yo. Ali m’bvuto, kodi si choncho? Chinsomba’cho chatsala pang’ono kum’meza! Kodi mukudziwa munthu’yu? Dzina lake ndi Yona. Tiyeni tione m’mene analowera m’bvuto lalikulu kwambiri’lo.

Yona ndi mneneri wa Yehova. Sipanapite nthawi yaitali chifere mneneri Elisa pamene Yehova akuuza Yona kuti: ‘Muka ku mzinda waukulu wa Nineve. Kuipa kwa anthu kumene’ko n’kwakukulu kwambiri, ndipo ndikufuna kuti ukalankhule nawo za izi.’

Koma Yona sakufuna kupita. Chotero akukwera m’bwato limene likumka kwina kosakhala ku Nineve. Yehova sakukondwera naye chifukwa cha kuthawa’ko. Chotero Iye akuchititsa pfunde lalikulu. N’loipa kwambiri kwakuti bwato’lo lingamire. Amalinyero akuopa kwambiri, ndipo akuitanira kwa milungu yao kaamba ka chithandizo.

Potsirizira Yona akuwauza kuti: ‘Ine ndimalambira Yehova, Mulungu amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi. Ndipo ndikuthawa kuchita zimene Yehova wandiuza kuchita.’ Chotero amalinyero’wo akufunsa kuti: ‘Tichitenji kwa iwe kuti tiletse pfunde’li?

‘Ndiponyeni m’njyanjamo, ndipo nyanja idzakhala’nso bata,’ akutero Yona. Amalinyero’wo sakufuna kukuchita, koma pamene pfunde’lo likuipira-ipira potsirizira pake akuponyera Yona m’madzimo. Pompo pfunde’lo likuleka, ndipo nyanja’yo yakhala bata kachiwiri’nso.

Pamene Yona akumira m’madzimo, chinsomba chikum’meza. Koma sakufa. Kwa mausana ndi mausiku atatu ali m’mimba mwa nsomba’yo. Iye ali wachisoni kwambiri kuti sanamvere Yehova ndi kupita ku Nineve. Chotero kodi mukudziwa chimene iye akuchita?

Yona akupemphera kwa Yehova kaamba ka chithandizo. Ndiyeno Yehova akuchititsa nsomba’yo kum’sanzira pa mtunda pouma. Pambuyo pake Yona akumka ku Nineve. Kodi zimene’zi sizikutiphunzitsa m’mene kuliri kofunika kuti tiyenera kuchita zimene Yehova akunena?

Bukhu la Baibulo la Yona.

Mafunso

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena