Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 54 tsamba 130-tsamba 131 ndime 1
  • Yehova Anamulezera Mtima Yona

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yehova Anamulezera Mtima Yona
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Anaphunzira Kufunika Kochitira Ena Chifundo
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Anaphunzira Kufunika Kochitira Ena Chifundo
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Yona Aphunzira za Chifundo cha Yehova
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Yona ndi Chinsomba
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 54 tsamba 130-tsamba 131 ndime 1
Yona akumira m’nyanja ndipo chinsomba chachikulu chikusambira chapafupi

MUTU 54

Yehova Analezera Mtima Yona

Anthu a mumzinda wa Nineve ankachita zinthu zoipa. Choncho Yehova anauza mneneri wake Yona kuti apite kukawachenjeza kuti asiye zoipazo. Koma Yona anathawa ndipo anakwera sitima yapamadzi yopita ku Tarisi.

Ali pa ulendowu, panyanja panayamba chimphepo champhamvu moti oyendetsa sitima anachita mantha kwambiri. Iwo anapemphera kwa milungu yawo n’kumafunsa kuti: ‘Kodi izi zikuchitika chifukwa chiyani?’ Kenako Yona anawauza kuti: ‘Anthuni, wolakwa ndine. Yehova anandiuza kuti ndichite zinazake ndiye ndikuthawa. Mundiponye m’nyanjamu ndipo mphepoyi isiya.’ Oyendetsa sitimawo sankafuna kumuponya m’madzi koma Yona analimbikira kuti amuponye. Kenako anamuponyadi ndipo mphepo ija inasiyira pomwepo.

Yona ankangoganiza kuti afa basi. Pamene ankamira, anayamba kupemphera kwa Yehova. Zitatero, Yehova anatumiza chinsomba chimene chinameza Yona. Komabe iye sanafe. Ali m’mimba mwa chinsombacho anapempheranso kuti: ‘Yehova, ndikukulonjezani kuti ndizimvera chilichonse chimene mungandiuze.’ Yona anakhala m’mimba mwa chinsombacho kwa masiku atatu ndipo kenako chinakamulavulira kumtunda.

Yona atapulumuka, Yehova anamuuzanso kuti apite ku Nineve kuja. Pa nthawiyi Yona sanakane. Atafika kumeneko anauza anthu oipawo kuti: ‘Kwangotsala masiku 40 okha ndipo mzinda wa Nineve uwonongedwa.’ Kenako panachitika zinthu zimene aliyense samayembekezera. Anthu a ku Nineve atamva uthengawo anasinthiratu. Mfumu yawo inalamula kuti: ‘Tiyeni tipemphere kwa Mulungu ndipo tisiye zoipa. Mwina satiwononga.’ Yehova ataona kuti anthuwo alapa, sanawononge mzindawo.

Yona akufika mumzinda wa Nineve

Izi si zimene Yona ankayembekezera choncho anakwiya kwambiri. Ndiye tangoganiza, Yehova analezera mtima Yona komanso kumuchitira chifundo, koma iyeyo sanachitire chifundo anthu a ku Nineve. M’malomwake Yona anangotuluka mumzindawo n’kukakhala pansi pa chomera cha mtundu wa mphonda. Kenako chomeracho chinauma ndipo Yona anakwiyanso. Ndiyeno Yehova anamufunsa kuti: ‘Kodi ukumvera chisoni chomerachi koma osamvera chisoni anthu a ku Nineve? Inetu ndawachitira chifundo ndipo sindinawawononge.’ Kodi Yehova ankatanthauza chiyani pamenepa? Ankatanthauza kuti anthu a ku Nineve anali ofunika kuposa chomera chilichonse.

“Yehova . . . akukulezerani mtima chifukwa sakufuna kuti munthu aliyense adzawonongedwe, koma akufuna kuti anthu onse alape.”​—2 Petulo 3:9

Mafunso: Kodi Yehova anathandiza Yona kukhala ndi khalidwe liti? Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene zinachitikira Yona?

Yona chaputala 1 mpaka chaputala 4

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena