Mutu 4
Chakudya Chimene Chiri Chofunika Kaamba ka Moyo Wosatha
1. Kodi nchifukwa ninji zinthu zolembedwa m’Mawu a Mulungu ziri zofanana ndi uchi?
KWA munthu wanjala, wolefuka, ngakhale kunyambita uchi kungapatse nyonga yatsopano, kungapangitse maso ake kuwala. Ponena za mawu olembedwa m’Mawu a Mulungu, moyenerera kukunenedwa kuti ali ‘ozuna koposa uchi ndi zakukha za zisa zake.’ Izi ziri chifukwa cha mapindu akulu kwambiri amene zitsogozo za Mulungu zimapereka ku miyoyo ya awo amene amazilandira moyamikira. (1 Samueli 14:27; Salmo 19:9-11; 119:103) Kwa awo opeza nzeru yolembedwa m’Mawu ouziridwa, “padzakhala mphotho, ndipo chiyembekezo [chao] sichidzalephereka.”—Miyambo 24:13, 14.
2. Ngati mzimu wa Mulungu uti uchite zabwino mwa ife, kodi nchiyani chimene tiyenera kuchita?
2 Tiri ndi lonjezo la Mulungu lakuti ‘adzasunga atumiki ake kufikira ku moyo wosatha,’ akumachita izi mwa njira ya mzimu wake. (1 Petro 1:5) Zimenezi ndithudi nzolimbikitsa. Koma tikakhala tikulakwa ngati tiganiza kuti zimenezi zikadza popanda kufunikira kwa kuyesayesa kwa awo amene akuthandizidwa motero. Mzimu wa Mulungu ungathe kugwira ntchito kaamba ka ubwino wa ali yense wa ife kokha ku mlingo umene ife tikugwirizanira nawo, ndipo chigwirizano choterocho chimaphatikizamo kudya za m‘Malemba ouziridwa. Mwana wa Mulungu anasonyeza chifukwa chake ziri choncho.
3. Kodi Yesu Kristu anati mzimu ukachitiranji ophunzira ake?
3 Pofotokozera ophunzira ake mmene mzimu wa Mulungu ukwathandizira, Yesu anati: “Nkhosweyo, mzimu woyera, amene Atate adzatumiza m’dzina langa, ameneyo adzakhuphunzitsani zinthu zonse ndi ku kukumbutsani zinthu zonse zimene ndinakuuzani.” (Yohane 14:26, NW) Yesu atabwerera kumwamba, mzimu, pa udindo wa wokumbutsa, ukakumbutsa maganizo a ophunzira zonena zake ndipo, monga mphunzitsi, ukawatheketsa kumvetsetsa kugwira ntchito kwa zinthu zokumbukiridwazo.
4. Kodi ndi motani mmene mzimu wa Mulungu ungatithandizire, ndipo kodi ndi motani mmene zimenezi zimagogomezerera kufunika kwa kuonjezera chidziwitso chathu cha Baibulo?
4 Popeza kuti ndi kale lonse sitinaphunzitsidwe mwachindunji ndi Yesu Kristu, mkhalidwe wathu uli wosiyana ndi uja wa atumwi. Komabe, ziphunzitso zonse zofunika kwambiri za Mwana wa Mulungu zasungidwa kaamba ka ife m’Baibulo. Chotero, pamene kuli kofunika, mzimu woyera ungakumbutse maganizo athu mfundo zochokera m’Malemba ouziridwa ndi kutithandiza kuzindikira kugwira ntchito kwao koyenera. Popeza kuti mzimu wa Mulungu umagwira ntchito monga wokumbutsa ndi mphunzitsi, tiyenera kugwirizana nawo mwa kulingalira kosamalitsa Baibulo. Ngati nkhokwe yathu ya chidziwitso Chamalemba iri yochepa, kwambiri, ife sitingapeze kwenikweni phindu lokwanira kuchokera m’kugwira ntchito kwa mzimu kaamba ka ife monga wokumbutsa ndi mphunzitsi.
5. (a) Kuti tipindule mokwanira ndi kugwira ntchito kwa mzimu wa Mulungu, kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kuchotsa zizolowezi zoipa? (b) Kodi ndi uphungu wotani umene mtumwi Petro anapereka ponena za kudya a kwauzimu?
5 Ndiponso, mzimuwo ndi woyera ndipo, chifukwa cha chimenecho, umathandiza kokha awo amene ali oyera kapena opanda uchisi mwa lingaliro la Yehova. Ndicho chifukwa chake si kokwanira kungowerenga Baibulo kapena kuchititsa kuti liwerengedwe kwa ife. Pafunikiranso kukhala chikhumbo chochokera mu mtima cha kuchotsa zizolowezi zonse zimene zimasemphana ndi miyezo ya Mulungu ya ukhondo kapena chiyero. Onani mmene zimenezi zikugogomezeredwera m’mawu otsatirapowa a mtumwi Petro:
“Tayani choipa chonse ndi kunyenga konse ndi chiphamaso ndi kaduka ndi mitundu yonse ya kusinjirira, ndipo monga makanda obadwa chatsopano, muzilakalaka mkaka wosaipitsidwa wa mawu, kuti mukule nawo kufika ku chipulumutso, malinga ngati mwalawa kuti Ambuye ali wokoma mtima.”—1 Petro 2:1-3, NW.
6. Kodi ndani amene akufulumizidwa kumalakalaka “mkaka”?
6 Pamene ife mwakhama tiyesa kuchita chifuniro cha Mulungu, maganizo athu ndi mitima imakhala yokonzekera kudya za m’Malemba. Komabe zinanso zikulowetsedwamo m’kukulitsa kukhumba kudya kwabwino kwambiri kwauzimu. Mtumwiyo anafulumiza kuti: “Monga makanda obadwa chatsopano, muzilakalaka mkaka wosaipitsidwa wa mawu.” (1 Petro 2:2, NW) Mkaka umakhutitsa kotheratu makanda obadwa chatsopano. Iwo samafuna chakudya china chiri chonse. Mofanana ndi makanda amenewo, okhulupirira atsopano amafuna ‘mkaka wa mawu’ ndipo ayenera kukulitsa kuulakalaka. Ndiyeno, pamene afikira uchikulire Wachikristu, iwo ndithudi adzafuna kukhala ndi chilakolako chofananacho cha chakudya chauzimu cholimba.—Ahebri 5:12-14.
7. Kodi nchifukwa ninji sitingayembekezere kukhala ndi chidziwitso chokwanira cha Mawu a Mulungu m’zaka zowerengeka?
7 Inde, mosasamala kanthu za utali wa nthawi imene takhala tikuyenda m’njira ya chowandi, pakali zina zambiri zoti ziphunziridwe ponena za Mlengi wathu ndi chifuniro chake kwa ife. (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 13:12.) Chifukwa chakuti Malemba ali ndi malingaliro a Mulungu wanzeru zonse, Yehova, ngakhale angelo amapindula ndi zibvumbulutso zolembedwamo. (1 Petro 1:12) Nangano, ndi motani m’mene, munthu ali yense angalingalirire kuti angapeze kumvetsetsa kokwanira kwa Mawu oyera a Mulungu n’kati mwa zaka zowerengeka chabe? Chotero kukakhala kosayenera kwambiri kudzichititsa kukhutira ndi kudziwa kachigawo ka Mawu ake ndipo, chotero, nkumauza Atate wathu wakumwamba kuti zikanakhala bwino akanakhala woolowa manja mochepera ndi makonzedwe ake auzimu amene ali m’Malemba Oyera.
KUKULITSA KUKOMEDWA CHAKUDYA CHAUZIMU
8. Kodi nchiyani chimene chiyenera kutisonkhezera kufuna kupeza chidziwitso chabwino kwambiri cha Malemba?
8 Kukonda kwathu Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu kuyenera kutisonkhezera kufuna kumvetsetsa zochuluka ponena za Baibulo monga momwe kungathekere. Ndiko kupyolera mwa masamba a Malemba kuti ife timathandizidwa kudziwa Atate wathu wakumwamba ndi mwana wake bwino lomwe, akumatichititsa kuyandikira pafupi kwambiri kwa iwo. Monga momwe mtumwi Petro ananenera, ‘talawa kale kuti Ambuye ndi wokoma mtima.’ (1 Petro 2:3) Mosonyeza chikondi chake, Yesu Kristu anatifera napangitsa kukhala kothekera kwa ife kukhala ndi mkhalidwe woyera pamaso pa Atate wathu wakumwamba. (Yohane 15:13; 1 Yohane 2:2) Chifukwa cha chimenecho, tingathe kufikira Yehova Mulungu mwaufulu, tikumatula zosautsa ndi nkhawa zathu pa iye. (Ahebri 10:19-22; 1 Yohane 3:19-22) Madalitso, chitsogozo ndi chithandizo zimene talandira monga ophunzira a Yesu Kristu zimasonyeza bwino lomwe kuti Mbuye wathuyo ali wokoma mtima ndipo amatikonda kwambiri. (Mateyu 11:28-30) Ngati zimene talawa kale kapena kukumana nazo ziri zabwino, kodi sitiyenera kufuna kudzigwirizanitsa ife eni mwathithithi kwambiridi ndi chitsanzo cha Yehova Mulungu ndi cha Mwana wake? (Salmo 34:8) Kulingalira Baibulo mosamalitsa, mwapemphero kudzatithandiza kuchita zimenezozo.
9. (a) Kodi nchiyani chimene chingachite mosemphana ndi njala yambwino yauzimu, ndipo kodi nchifukwa ninji ziri choncho? (b) Kodi nchiyani chimene chingachitidwe kupititsa patsogolo njala yathu yauzimu?
9 Bwanji ngati muona kuti kulakalaka kwanu “mawu” sikuli kwakukulu kwambiri? Pamenepo, patulani nthawi, ya kulingalira moyamikira ponena za zimene Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu akuchitirani. Ndiponso, pendani kuti muone kaya ngati mwaononga njala yanu yauzimu mwa kusamalira mosayenera nthanthi, malingaliro ongoyerekezera ndi mawu onyengerera a dziko lotalikirana ndi Mulungu. Mdani wina wa njala yauzimu ndiye kuwerenga kwa munthu kongolekezera kwakukulukulu ku magazini a zithunzithunzi kapena zinthu zowerengedwa zimene sizimafunikira kulingalira kosamalitsa kapena kusinkhasinkha. Kuyenera kuzindikiridwadi kuti Baibulo linalembedwera kulangiza, osati kusangalatsa. Pamene kuli kwakuti mawu enieniwo sangakhale obvuta, kawirikawiri malingaliro operekedwa amapereka tanthauzo lozama limene lingangozindikiridwa kokha mwa kupatula nthawi ya kulingalira mwapemphero zimene zikunenedwazo.
10. Kodi ndi zenizeni zotani zonena za mafanizo a Yesu Kristu zimene zimatsimikizira kuti kungowerenga chiwerengewerenge Malemba nkosakwanira kuti munthu apeze chidziwitso cholongosoka?
10 Mwa chitsanzo, mafanizo ogwiritsiridwa ntchito ndi Yesu Kristu, ali osabvuta. Koma chowonadi chofunika chimene iwo amabvumbula sichingatumbidwe mwa kungowerenga mwachiwerengewerenge katembenuzidwe kali konse ka Baibulo. Kumbukirani, Ayuda amene anamva Mwana wa Mulungu akulankhula m’chinenero chao sanapeze tanthauzo lokwanira la zimene iye anaphunzitsa. Ngakhale kuli kwakuti anthu wamba anamva mawu amene iye anagwiritsira ntchito, tanthauzo la zimene yesu ananena linali lobisika ngakhale kwa ophunzira. Chifukwa ninji? Ochuluka a omvetsera a Yesu anali opanda kudzichepetsa ndi kulakalaka chakudya chauzimu. Chifukwa cha chimenecho, iwo sanafunsitsa kuti apeze luntha lenileni.—Mateyu 13:13-15.
11. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kukhutiritsidwa ndi chidziwitso chakunja kokha cha Malemba?
11 Ndithudi, sitikufuna kungokhutira ndi chidziwitso chapamwamba pokha cha Baibulo, mwina mwake kudziwa bwino lomwe zonena za Baibulo kapena “nthano,” kudzanso ziphunzitso zoyambirira. Ngati tinena kuti timakonda Mulungu ndi Kristu, tifunikira kukhala ofunitsitsa kuonongera nthawi tikuwerenga Baibulo, tikumayesetsa kupeza tanthauzolo, lingaliro ndi mzimu wa zimene likunena ndiyeno nkugwiritsira ntchito zimenezi. Palibe luso lopindulitsa limene limapezedwa popanda kuyesayesa. Chifukwa cha chimenecho, kodi sitiyenera kuyembekezera kupanga kuyesayesa kwakukulu m’malo mwakuti tionjezere chidziwitso chathu chonena za Yehova, magwero a nzeru zonse?—Yerekezerani ndi Miyambo 2:1-6; 1 Timoteo 4:13-16.
12. Kodi mkhalidwe wathu kulinga ku kupeza chidziwitso cholongosoka kuli nchiyani ndi madalitso amene tingalandire?
12 Mkhalidwe wathu kulinga ku kupeza kuzindikira kwabwino kwambiri Mawu a Mulungu udzakhala ndi chiyambukiro chachindunji pa madalitso amene adzaperekedwa pa ife. Kulephera kugwiritsira ntchito mwai wathu mokwanira m’kufikira pa kudziwa Yehova Mulungu bwino kwambiri sikungachititse kwenikweni kutayika kwa miyoyo yathu. Koma kungatsogolere ku kukhala kwathu ndi liwongo la kusachita chifuniro cha Mulungu m’mbali zina ndiyeno nkutayikiridwa madalitso. Mu limodzi la mafanizo, Yesu anasonyeza kuti kusadziwa sikudzatetezera munthu ku kutayikiridwa kwakutikwakuti. Mtumiki amene achita zinthu zofunikira mikwapulo chifukwa cha kusamvetsetsa chifuniro cha mbuye wake amalangidwabe basi, ngakhale kuli kwakuti osati mowawa kwambiri mofanana ndi kapolo amene, modziwa bwino lomwe, sanamvere mwadala. (Luka 12:47, 48) Chotero, iri nkhani yoopsa pamene munthu alephera kupeza mpata m’moyo wake kaamba ka phunziro lokhazikika la Mawu a Mulungu ndipo, chifukwa cha chimenecho, sakupanga kupita patsogolo kofunikako mu makhalidwe ndi ntchito Zachikristu.
13. Kodi Mawu a Mulungu angatithandize kupeza chiyani, ndipo kodi ndi motani mmene zimenezi ziyenera kuyambukirira kudya kwathu kwauzimu?
13 Mawu onse athunthu a Mulungu alinganizidwa kutithandiza ‘kukula kukafika pa chipulumutso,’ ndiko kuti, kupeza chipulumutso chathu chotsirizira monga ophunzira obvomerezedwa a Ambuye Yesu Kristu. Chifukwa cha chimenecho, ngati tiri okondweretsedwa kwenikweni ndi ubwino wathu wosatha, zimenezi ziyenera kusonyezedwa ndi chikhumbo chathu chaphamphu cha kufika pa kudziwa bwino kwambiri Yehova Mulungu ndi Mwana wake mwa njira ya Malemba ouziridwa.
14. Kodi chikondwerero chenicheni m’thanzi lauzimu la ena chingakhale ndi chiyambukiro chotani pa njala yathu yauzimu?
14 Ndithudi, woposa moyo wathu wokha ukulowetsedwamo. (Yerekezerani ndi 1 Timoteo 4:16.) Monga atsatiri a Yesu Kristu, tiri ndi ntchito ya kuthandiza ena kukhala ophunzira ake. (Mateyu 28:19, 20) Kodi ndi motani m’mene tingachitire zimenezi pamene moopsa kwambiri tiri opanda chidziwitso cha Baibulo? Kodi ife tinganane kuti tiri okondweretsedwa moona mtima ndi ubwino wauzimu wa ena pamene tikungopanga kuyesayesa kwapang’ono kuonjezera chidziwitso chenichenicho chimene chikawathandiza iwo? Nthawi zina chisonkhezero chofunika cha kuongolera njala yauzimu chimadza pamene munthu ayamba kuphunzitsa munthu winanso. Kawirikawiri awo amene amaonjezera kuchuluka kwa nthawi imene amaonongera m’kugawira ena chowonadi cha Baibulo amapeza kuti chikhumbo cha iwo eni cha chakudya chauzimu chimakulitsidwa. Mwa chitsanzo, mafunso ofunsidwa ndi anthu okondwerera angapereke chisonkhezero chofunikacho kwa munthuyo cha kupereka mayankho okhutiritsa.
15. Kodi ndi motani mmene anthu amene sangathe kuwerenga kapena amene ali ndi bvuto la kuwerenga angapindulire ndi zimene ziri m’Malemba?
15 Koma bwanji za anthu amene ali ndi bvuto lalikulu m’kuwerenga kapena amene ali osakhoza kudziwerengera okha Malemba? Iwo angathe kupeza mapindu a zimene ziri m’Baibulo mwa kuchita kuti liwengeredwe ndi kufotokozedwa kwa iwo. Pamenepo iwo angathe kusinkhasinkha pa chidziwitso chimene iwo akuchimva ndipo angathe kuchigwiritsira ntchito m’miyoyo yao. (Chibvumbulutso 1:3; Nehemiya 8:8) Ndithudi, ngati bvutolo likulowetsamo maphunziro osakwanira, kukakhala bwino kwa anthu oterowo kugwiritsira ntchito makonzedwe opezeka ophunzirira kuwerenga kapena kupititsa patsogolo luso lao la kuwerenga. Pamene mbali chabe za Malemba ziri zopezeka m’chinenero china, thayo lalikulu limakhala pa awo amene akuphunzitsa ena ndi amene amadziwa zinenero m’zimene Baibulo lathunthu liri lopezeka. Mofanana ndi mtumwi Paulo, iwo ayenera kupanga kuyesayesa kumveketsa “uphungu wonse wa Mulungu.”—Machitidwe 20:27.
CHIYAMBUKIRO CHA MAWU PA MIYOYO YATHU
16, 17. (a) Malinga ndi kunena kwa mtumwi Petro, kodi ndi chiyambukiro chotani chimene Mawu a Mulungu anakhala nacho pa Akristu a m’zaka za zana loyamba? (b) Kodi nchiani chimene chimasonyeza kuti kuyesayesa kwa munthu mwini kunali kufunika kuti “mawu” agwiredi ntchito mwa okhulupirira?
16 Kulingalira kwathu Mawu a Mulungu mwapemphero, ndi kudzichepetsa konse, kungathe kukhala ndi chiyambukiro chabwino pa miyoyo yathu pa tsopano lino. Zimenezi ziri zoonekera bwino mwa zimene mtumwi Petro analembera okhulupirira anzake kuti:
“Tsopano popeza kuti mwayeretsa miyoyo yanu mwa kumvera kwanu chowonadi mwa chikondi chopanda chiphamaso motero, mukondane kwambiri kuchokera mu mtima. Pakuti mwapatsidwa kubadwa kwatsopano, osati ndi [mbeu imene imachititsa kukhalapo kwa anthu athupi, imene iri yokhoza kufa] yokhoza kuola, koma ndi mbeu yobala yosaola mwa Mulungu wamoyo ndi wosatha. Pakuti ‘amoyo onse akunga udzu, ndi ulemerero wake wonse uli ngati duwa la udzu; udzuwo ufota, ndipo duwalo naligwa, koma mawu a Yehova akhala kosatha.’ Eya, awa ndiwo “mawu,” awa amene alengezedwa kwa inu monga mbiri yabwino.”—1 Petro 1:22-25, NW.
17 Lingalirani mmene mau a Petrowo anagwirira ntchito kwa Akristu mu zaka za zana loyamba C.E. Pamene ophunzira amenewawo a Yesu Kristu analowetsa chowanadi cha “mbiri yabwino,” iwo anasonkhezeredwa kupanga kuyesayesa kudziyeretsa iwo eni, kuchotsa machitachita olakwa. Mwa chithandizo cha mzimu wa Mulungu, iwo momvera anadzigwirizanitsa ndi zimene chowonadi chinafuna kwa iwo. Chifukwa cha chimenecho, iwo anayamba kusonyeza chikondi chenicheni kwa awo ogwirizana nawo m’chikhulupiriro. (Yohane 13:34, 35) Komabe, kusandulika kodabwitsa kumeneku m’miyoyo yao sikunadze popanda kuyesayesa kwa iwo eni. Kokha mwa kugonjera momvera ku chisonkhezero cha chowonadi ndi cha mzimu wa Mulungu ndi pamene iwo angathe kusonyeza chikondi chaubale chosanyenga. Chifukwa cha ichi, Petro akanatha kuwafulumiza kuti: “Mukondane kwambiri kuchokera mu mtima.” (1 Petro 1:22, NW) Liwu Lachigriki lotembenuzidwa kukhala “kwambiri” limatanthauza kwenikweni “mofutukuka.” Chotero, kusonyeza chikondi kumeneku sikuyenera kukhala kochepa kapena chokhala ndi malire chifukwa cha kunyumwira, kaduka kapena nsanje koma chiyenera kusonyezedwa kuchokera mu mtima woyera. Sichiri chikondi chamwambo chopanda kutenthedwa maganizo koona mtima koma chikondi chosonyezedwa ndi malingaliro amphamvu ndi chikondi chomvera chifundo. Chifukwa chakuti Mulungu wa chikondi, Yehova, anali atapanga ophunzira Achikristu amenewo kukhala ana ake, akumawapatsa kubadwa kwatsopano, kunali kokha koyenera kuti iwo adzigwiritsire ntchito iwo eni mwakhama m’kupereka umboni wa umwana wao mwa kusonyeza chikondi chachikulu kwa okhulupirira anzao.—1 Yohane 3:10, 11.
18. (a) Kodi nchifukwa ninji masinthidwe amene angachokere m’kusinthira ku Mawu a Mulungu Sali akunja kokha kapena a kanthawi chabe? (b) Kodi ndi motani m’mene zimene zikuchitidwa kupyolera mwa “mawu” ndi mzimu wa Mulungu zimasiyanira ndi chokumana nacho cha anthu ochimwa?
18 Ponena za ophunzira onse a Yesu Kristu lero lino, masinthidwe amene angachititsidwe ndi kudya ndi kuchita mogwirizana ndi “mawu a Mulungu wamoyo ndi wosatha” Sali achiphamaso kapena akanthawi. “Mawu” amenewo ali osaola. Chifukwa cha chimenecho, onse amene amapitirizabe kukhala pansi pa chisonkhezero cha chowonadi cha “mbiri yabwino” mosalekeza akuchititsidwa kukhala abwino. Pamene kuli kwakuti anthu ochimwa, mofanana ndi udzu, amataya kaonekedwe kao kabwino ndi kufa, masinthidwe ochititsidwa ndi “mawu” osathawo ndi mzimu wa Mulungu adzakhalabe.
19. Kodi ndi motani mmene tiyenera kulingalirira ponena za zosowa zathu zauzimu?
19 Chifukwa cha chimenecho, tiyenitu, tisanyalanyaze konse zosowa zathu zauzimu koma tikhale akhama m’kudzaza maganizo athu ndi mitima ndi chowonadi. Mwa njala yathu yabwino kwambiri yauzimu tingathe kupeza thanzi lauzimu ndi nyonga. Pamenepo, pamene ife modzichepetsa tigonjera ku chisonkhezero cha “mbiri yabwino” ndi mzimu woyera wa Mulungu, tiyenitu tidzitsimikizire ife eni kukhala ophunzira okhulupirika a Yesu Kristu, tikumathandiza ena kufikira pa kukhala ndi chidziwitso cholongosoka cha Malemba. Motero kudya kwathu “mawu” osatha kudzatithandiza kukula kufika ku chipulumutso, kukumatichititsa kukhala ndi m’tsogolo mwamuyaya.