Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • le tsamba 22-31
  • Kodi N’chiyani Chimene Muyenera Kuchita?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi N’chiyani Chimene Muyenera Kuchita?
  • Sangalalani Ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!
  • Nkhani Yofanana
  • Chikondi Cha Mulungu Sichimatha
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
  • Kodi Mulungu Adzawononganso Anthu Oipa?
    Sangalalani Ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!
  • Musasiyane ndi Yehova
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Njira Yoyenera Yolambirira Mulungu
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
Onani Zambiri
Sangalalani Ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!
le tsamba 22-31

Kodi N’chiyani Chimene Muyenera Kuchita?

50 Kodi inu mukufuna kukhala ndi moyo kosatha m’paradaiso wokongola?

Pamenepotu phunzirani zochuluka ponena za zimene Mulungu amanena. Yesani kuphunzira kuŵerenga Baibulo.—Yohane 17:3; Chivumbulutso 1:3

51 Phunzirani zochuluka ponena za Yesu.—Deuteronomo 18:18, 19; Yohane 3:16; Machitidwe 3:19-23

52 Yesani kuchita zinthu zabwino zokha ndi kumvera Yehova.—Aroma 6:17, 18, 22

53 Kumbukirani, Yehova amanena kuti sitiyenera kupha anthu.—Eksodo 20:13; 1 Yohane 3:11, 12

54 Sitiyenera kutenga zinthu zimene zili za ena.—Eksodo 20:15; Aefeso 4:28

55 Mwamuna sayenera kukhala kapena kugonana ndi mkazi kusiyapo atakhala mkazi wake.—Eksodo 20:14, 17; 1 Atesalonika 4:3

56 Kodi mukukumbukira kuti Mulungu amaloleza mwamuna kukhala ndi akazi angati? Kodi mwamuna ayenera kukhala ndi mkazi wake kwa utali wotani?—Genesis 2:22, 24; Mateyu 19:5, 6; 1 Akorinto 7:2, 10, 11

57 Kumbukirani kuti tiyenera kulambira Yehova yekha.—Mateyu 4:10; 1 Akorinto 8:6

58 Mafano ndi zifanizo sizingathandize. Chifukwa ninji?—1 Akorinto 8:4

Kodi n’kwabwino kukhala ndi mafano?—Deuteronomo 27:15; 1 Yohane 5:21

59 Kodi n’chifukwa ninji kuli koipa kukhala ndi zithumwa ndi kugwiritsira ntchito matsenga?—Deuteronomo 18:10-13; Chivumbulutso 21:8

60 Angelo oipa kapena ziwanda anapandukira Mulungu. Ife sitiyenera kuwatumikira.—Machitidwe 16:16

61 Tiyenera kupemphera kwa Mulungu. Pemphero limatanthauza kulankhula ndi Mulungu, kumuuza kuti timafuna kum’tumikira ndi kupempha thandizo lake.—Afilipi 4:6, 7

62 Tiyenera kumvera Yesu ndi kum’khulupirira.—Ahebri 5:9; Yohane 3:16

63 Kumbukirani kuti iye anafa kuti atipulumutse.—Aroma 5:8

64 Kumbukirani kuti Yesu ndiye mfumu yathu yosaoneka. Tiyenera kumumvera.—Afilipi 2:9-11; Chivumbulutso 19:16

65 Yesu ananena kuti muyenera kuuza ena za zinthu zabwino zimene mukuphunzira ndi kuti awo amene akufuna kutumikira Mulungu ayenera kubatizidwa.—Mateyu 28:19, 20; Yohane 4:7-15

66 Chotero mungathe kulankhula ndi mabwenzi anu za zinthu zabwino zimenezi.—Mateyu 10:32

67 Ngati muphunzira kuŵerenga, mungathe kuphunzira zinthu zina zambiri ndipo mudzakhala okhoza kuthandiza bwino kwambiri ena.—2 Timoteo 2:15

68 Yesu anaphunzitsanso tiana kumvera Mulungu. Iye sanali wotanganitsidwa kwakuti n’kusakhala ndi nthaŵi ya kulankhula nato.—Mateyu 19:13-15

69 Makolo nthaŵi zonse ayenera kuphunzitsa ana awo kumvera Mulungu ndi kum’konda.—Deuteronomo 6:6, 7; Miyambo 6:20-22; Aefeso 6:4

70 Pali matchalitchi ambiri osiyanasiyana. Zochuluka za ziphunzitso zawo sizochokera m’Baibulo. Yehova amatiuza kuchoka m’zipembedzo zimene simaphunzitsa choonadi.—Chivumbulutso 18:4; Yohane 4:23, 24

71 Yehova ali ndi anthu padziko lapansi amene angathe kukuphunzitsani zochuluka ponena za iye. Kodi mukudziŵa kuti iwo ndani?—Machitidwe 15:14; Aroma 10:14, 15

72 Iwo ndiwo Mboni za Yehova. Izo zili ndi mtendere pakati pawo. Kodi mukudziŵa chifukwa chake? Chifukwa chakuti izo zimakondana wina ndi mnzake.—Yesaya 43:10-12; Yohane 13:34, 35

73 Ndiponso chifukwa chakuti iwo amakonda Yehova, iwo abatizidwa. Umu ndimo mmene iwo amasonyezera poyera kuti iwo asiya njira yawo yoipa ya moyo ndipo akufuna kuwonongera miyoyo yawo akutumikira Mulungu.—Machitidwe 2:41

74 Mboni za Yehova zimayembekezera kukhala m’paradaiso watsopano wokongolayo.—Salmo 37:9-11, 29

Kodi mungachitenji kuti mudzakhale nawo mmenemo?—Yakobo 1:22, 25; 2:20-26

75 Gwirizana nazoni m’kuphunzira kutumikira Yehova. Izo zimakonda ndi kumvera Yehova ndi Kristu Yesu. Kodi inu mumawakonda? Kodi mumakonda kuthandiza ena kudziŵa Mulungu?—Yohane 6:45-47

76 Yehova ndi Kristu Yesu amakukondani ndipo amafuna kuti inu mukhale ndi moyo kwamuyaya m’paradaiso.—Yohane 3:16

Zimene mwaphunzira mwa kulingalira zithunzizo ndi chidziŵitso chimene chili m’kabukuka motsimikiziradi zakupatsani chikhumbo cha kusangalala ndi moyo pa dziko lapansi kosatha. Ngati mukakonda kuphunzira zochuluka ponena za zimenezi, tikupereka lingaliro lakuti mulankhule ndi mmodzi wa Mboni za Yehova kwanuko. Kapena, mungalembe kalata, kapena kuchita kuti wina wake akulembereni kalata, yomka ku ofesi yapafupi nanu kumene mukukhalako, monga momwe kwasonyezedwera mu mpambo wa makeyala umene uli pa tsamba lachiŵiri la kabuku kano.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena