Kodi Mulungu Adzawononganso Anthu Oipa?
22 Anthu lerolino alinso oipa kwambiri. Kodi ndi zinthu zoipa zotani zimene zikuchitidwa?
23 Ena amapha anthu ena. Mulungu amanena kuti simuyenera kuchita izi.—Eksodo 20:13; 1 Yohane 3:11, 12
24 Ena amaba. Mulungu amanena kuti simuyenera kuba.—Eksodo 20:15; Aefeso 4:28
25 Anthu ena amakwatira akazi ambiri. Ena amakhala ndi akazi aŵiri kapena oposerapo m’nyumba zosiyanasiyana. Enanso mwamuna ndi mkazi amakhalira limodzi popanda kukwatirana. Zonsezi ndi zosemphana ndi zimene Baibulo limanena.—Mateyu 19:4-6; 1 Akorinto 7:1-4; 1 Timoteo 3:1, 2
26 Kodi mukukumbukira kuti Mulungu anapatsa Adamu mkazi mmodzi yekha?—Genesis 2:22, 24
27 Ena amalambira mafano. Mulungu amanena kuti musagwiritsire ntchito mafano kapena zifanizo m’kulambira.—Eksodo 20:4, 5; Yesaya 44:9-17; 1 Yohane 5:21
28 Yehova adzawononga oipa amene sakasintha.—Salmo 37:9, 10; Luka 13:5; 1 Akorinto 6:9, 10