Mutu 1
Chigwirizano m’Kulambiridwa—Kodi Chiyenera Kutanthauzanji kwa Inu?
1, 2. (a) Kodi chigwirizano chowona cha kulambira chikubweretsedwa pa maziko m’tsiku lathu? (b) Kodi ndimotani mmene Baibulo limalongosolera chimene chikuchitika?
KUZUNGULIRA dziko pali kuyenda kochititsa chidwi kumka kuchigwirizano cha kulambira. Kukusonkhanitsa pamodzi anthu amitundu yonse ndi mafuko ndi manenedwe. Chigwirizano chawo sichinachititsidwe ndi kugonjera kulikonse kwa zikhulupiriro. Sichikupezedwa mwa kusiya kwawo njira zamoyo zosulizidwa zimene ziri zotsutsana ndi Mawu a Mulungu. Kodi nanga chachititsidwa nchiyani? Chenicheni chakuti anthu achiyambi chirichonse akufikira pa kudziwa Yehova monga Mulungu yekha wowona ndipo mofunitsitsa akuchititsa miyoyo yawo kugwirizana ndi njira zake zolungama.—Yerekezerani ndi Chivumbulutso 15:3, 4.
2 Ichi chiri kukwaniritsidwa kwa ulosi umene unalembedwa zaka zokwanira 2,700 zapitazo ndi mneneri Mika. Ponena za “masiku otsiriza,” iye analemba: “Amitundu ambiri adzamuka, nadzati, Tiyeni, tikwere ku phiri la Yehova, ndi kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo tidzayenda m’mabande ake.” (Mika 4:1, 2)a Kodi mukuwona zimenezo zikuchitika?
3, 4. (a) Kodi ndimotani mmene kuliri kowona kuti “mitundu” ikutembenukira kwa Yehova? (b) Kodi ndimafunso otani amene tiyenera kudzifunsa?
3 Palibe “mitundu” yathunthu imene ikudzipereka panyumba yauzimu ya Yehova ya kulambirira. Koma anthu payekha payekha am’mitundu imeneyo akutero. Pamene akuphunzira za chifuno cha chikondi ndi umunthu wochititsa chidwi za Yehova Mulungu, mitima yawo imasonkhezeredwa kwambiri. Modzichepetsa amafunafuna kupeza zimene Mulungu amafuna kwa iwo. Pemphero lawo liri lofanana ndi lija la Davide, mwamuna wachikhulupiriro amene anati: “Mundiphunzitse chokonda inu; popeza inu ndinu Mulungu wanga.”—Sal. 143:10.
4 Kodi inu mukudziwona pakati pa khamu lalikulu limenelo la olambira a Yehova? Kodi kulabadira kwanu malangizo olandiridwa kumapereka umboni wakuti mukuzindikiradi kuti Yehova ndiye magwero ake? Kodi ‘mukuyenda m’mabande ake’ kumlingo wotani?
Mmene Chikupezedwera
5. (a) Kodi chigwirizano cha kulambira potsirizira pake chidzapezedwa ku mlingo wotani? (b) Kodi nchifukwa ninji kuli kofulumira kukhala mlambiri wa Yehova tsopano, ndipo kodi ndimotani mmene tingathandizire ena kuchita ichi?
5 Chifuno cha Yehova nchakuti zolengedwa zonse zaluntha zikhale zogwirizanitsidwa m’kulambira—popanda chosokeretsedwa ndi mabodza, popanda chopupulikapupulika chifukwa cha kulephera kupeza tanthauzo lenileni la moyo. Ha tikulakalaka chotani nanga tsikulo pamene onse okhala ndi moyo adzadalitsa Mulungu wowona yekha! (Sal. 103:19-22) Koma zimenezo zisanachitike, Yehova ayenera kuchotsa m’chilengedwe chake awo onyozera ufumu wake wachikondi ndi amene amaumirira pa kuwononga moyo wa ena. Mwa chifundo akupereka chenjezo lapasadakhale la zimene adzachita. Anthu kulikonse ali ndi mpata wa kusintha njira yawo. Chotero m’tsiku la ife eni mfuu yofulumira iyi ikuperekedwa padziko lonse: “Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthawi ya chiweruziro chake; ndipo mlambireni iye amene analenga m’mwamba ndi mtunda ndi nyanja ndi akasupe amadzi.” (Chiv. 14:6, 7) Kodi inu mwavomereza chiitano chimenecho? Ngati mwatero, tsopano uli mwayi wanu kugwira ntchito ndi gulu la Yehova kuthandiza ena kutero.
6. Pambuyo pa kuphunzira ziphunzitso zamaziko za Baibulo, kodi ndikupita patsogolo kowonjezereka kotani kumene mwaphamphu tiyenera kuyesayesa kupanga?
6 Sichiri chifuno cha Mulungu kubweretsa m’gulu lake anthu amene amangonena kuti amakhulupirira mwa Yehova ndi kuti amafuna kukhala ndi moyo m’Paradaiso koma amene panthawi imodzimodziyo akupitirizabe kulondola zinthu za iwo eni zadyera. Amafuna anthu kukhala ndi ‘chidziwitso cholongosoka cha chifuniro chake,’ ndipo ichi chiyenera kusonyezedwa m’miyoyo yawo. (Akol. 1:9, 10) Anthu oyamikira ataphunzira ziphunzitso zamaziko za Baibulo, amafunikira kupitirizabe kufikira uchikulire Wachikristu. Chikhumbo chawo chiri kudziwa Yehova monga mwaubwenzi wapamtima, kukulitsa ndi kuzamitsa kumvetsetsa kwawo Mawu ake, ndi kuwagwiritsira ntchito mokwanira kotheratu m’miyoyo yawo. Iwo amafunafuma kukhala ofanana ndi Atate wawo wakumwamba, akumasonyeza mikhalidwe yake ndi kuwona nkhani monga momwe iye amachitira. Izi zimawasonkhezera kufunafuna njira zokhalira ndi mbali mokwanira monga momwe kungathekere m’ntchito imene akuichititsa m’dziko lapansi m’tsiku lathu. Kodi zimenezo ndizo zimene mukuchita?—Aef. 5:1; Aheb. 5:12–6:3; 1 Tim. 4:15.
7. Kodi chigwirizano chowona chiri chotheka patsopano lino m’njira zotani, ndipo kodi chimapezedwa motani?
7 Baibulo limasonyeza kuti awo otumikira Yehova ayenera kukhala anthu ogwirizana. (Aef. 4:1-3) Chigwirizano chimenechi chiyenera kukhalako tsopano, ngakhale kuti tikukhala ndi moyo m’dziko logawanika ndipo tikali kulimbanabe ndi kupanda ungwiro kwa ife eni. Yesu anapemphera mwaphamphu kuti ophunzira ake onse akakhale amodzi, okhala ndi chigwirizano chowona. Kodi ichi chikanatanthauzanji? Kuti choyamba akakhala ndi unansi wabwino ndi Yehova ndi Mwana wake. Ndiponso kuti akakhala ogwirizana wina ndi mnzake. (Yoh. 17:20, 21) Izi tsopano zikukwaniritsidwa pamene akugwiritsira ntchito malangizo olandiridwa pa “nyumba” ya Yehova.
Kodi Ndizinthu Ziti Zimene Zimathandizira Chigwirizanocho?
8. (a) Kodi timakulitsa chiyani pamene ife enife tigwiritsira ntchito Baibulo kusinkhasinkha mayankho amafunso amene amatiyambukira? (b) Mwa kuyankha mafunso osanjidwa pamwambapowo, pendani zinthu zimene zimathandizira chigwirizano Chachikristu.
8 Zina za zinthu zazikulu zothandizira chigwirizano chimenechi zasanjidwa pansipa. Pamene muyankha mafunso amene amatsatira zimenezi, lingalirani mmene chirichonse chimayambukirira unansi wanu ndi Yehova ndi Akristu anzanu. Kusinkhasinkha pamfundo zimenezi mothandizidwa ndi malemba otchulidwa kudzathandizira kukulitsa kwanu luso la kuganiza zochokera kwa Mulungu, imene iri mikhalidwe yomwe ife tonse tifunikira. (Miy. 5:1, 2; Afil. 1:9-11) Chotero pendani zinthu izi chimodzi panthawi imodzi:
(1) Tonsefe tikulambira Yehova ndi kuvomereza kuyenera kwake kwa kukhazikitsa muyezo wa chabwino ndi choipa.
Kodi ndimotani mmene Yehova akanawonera ngati mwadala tinanyalanyaza uphungu wake pa nkhani imene inawonekera kukhala yaing’ono kwa ife? (Luka 16:10; yerekezerani ndi Malaki 1:6-8.)
Kodi ena akuyambukiridwa ngati nthawi zonse ife sitimvera malamulo a Yehova? (Yerekezerani ndi Aroma 5:12; Yoswa 7:20-26; 1 Maf. 14:16.)
(2) Kulikonse kumene tiri m’dziko, tiri ndi Mawu a Mulungu kutitsogoza.
Pamene tipanga zosankha, kodi ndi ngozi iti imene iripo m’kungochita chimene ife “tichilingalira” kukhala chabwino? (Yer. 17:9; Miy. 14:12)
Ngati sitidziwa uphungu umene Baibulo limapereka pa nkhani yakutiyakuti, kodi tiyenera kuchitanji? (Miy. 2:3-5)
(3) Tonsefe timapindula ndi programu ya chakudya chauzimu yofanana.
Kodi ndimikhalidwe yotani imene iripo pakati pa awo amene samazindikira makonzedwe a Yehova a chakudya chauzimu? (Yerekezerani Yesaya 1:3; 9:16; 65:14.)
(4) Yesu Kristu, ndipo osati munthu, ndiye mtsogoleri wathu ndi kupyolera mwa amene tonsefe timayandikira Yehova m’kulambira.
Kodi aliyense wa ife ali ndi chifukwa chenicheni cho-khulupiririra kuti monga anthu tiri apamwamba koposa ena? (Aroma 3:23, 24; 12:3; Mat. 23:8-10)
(5) Mosasamala kanthu ndi kumene timakhala, timayang’ana ku Ufumu wa Mulungu monga chiyembekezo chokha cha anthu.
Kodi ichi chimatitetezera motani ku zisonkhezero zogawanitsa? (Mat. 6:9, 10; Mika 4:3)
(6) Mzimu woyera umatulutsa mwa alambiri a Yehova mikhalidwe imene iri yofunika ku chigwirizano Chachikristu.
Kodi ndimotani mmene timatsegulira njira ya mzimu wa Mulungu kubala zipatso zake mwa ife? (Sal. 1:2; Miy. 22:4; Chiv. 3:6; Mac. 5:32)
Kodi ndimotani mmene kukhala kwathu ndi zipatso zamzimu kumasonkhezerera unansi wathu ndi Yehova? Ndi abale athu? (Agal. 5:22, 23)
(7) Tonsefe tiri ndi thayo la kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu.
Kodi ndimotani mmene kukhala kwathu otanganitsidwa m’kukhala ndi phande m’ntchito ya kulalikira imeneyi ndi Akristu anzathu kumasonkhezerera mmene timalingalirira ponena za iwo? (Yerekezerani Akolose 4:7, 11.)
9. Kodi nchiyani chimene chiri chiyambukiro pamene tigwiritsiradi ntchito chowonadi chimenechi m’miyoyo yathu?
9 Kuvomereza zinthu zimenezi ndiko chinthu china. Kukhala ndi moyo mogwirizana nazo kumafunikira zowonjezereka kwambiri. Koma pamene titero, timakokedwera pafupi ndi Yehova. Mayanjano athu ndi okhulupirira anzathu nawonso amakhala magwero achitsitsimulo. Monga momwe Salmo 133:1 akunenera kuti: “Wonani, nkokoma ndi kokondweretsa ndithu kuti abale akhale pamodzi!” Kodi inu mwininu simunamve mmene kungakhalire kotsitsimula kuchoka kudziko, limodzi ndi dyera lake lonse, ndi kukhala pamisonkhano limodzi ndi ena amene amakondadi Yehova?
Pewani Zisonkhezero Zogawanitsa
10. Kodi nchifukwa ninji timafunikira kukhala osamala kupewa mzimu wa kudzigangira?
10 Kotero kuti tisawononge chigwirizano chamtengo wapatali chimenecho, tiyenera kupewa zisonkhezero zogawanitsa. Chimodzi cha zazikulu pakati pa zimenezi ndicho mzimu wa kudzigangira. Yehova amatithandiza kuupewa mwa kutiululira woyambitsa wake Satana Mdyerekezi. Ndiye amene ananyenga Hava kuti alingalire kuti kukakhala kompindulitsa kunyalanyaza chimene Mulungu anali atanena ndi kupanga zosankha za iye mwini. Adamu anagwirizana naye njira yopanduka imeneyo. Chotulukapo chinali tsoka kwa iwo ndi kwa ife. (Gen. 2:16, 17; 3:1-6, 17-19) Tikukhala ndi moyo m’dziko limene liri lomwerekera ndi mzimu wodzigangira umenewo, chotero sikuyenera kutidabwitsa ngati tifunikira kulamulira mzimu umenewo mwa ife eni. Mwachikondi Yehova amatithandiza kutero mwa uphungu kupyolera mwa gulu lake.
11. Kodi nchiyani chimene chidzasonyeza kuti kaya tikukonzekera mowona mtima kaamba ka moyo m’Dongosolo Latsopano lolungama la Mulungu?
11 Kupyolera mwa gulu limenelo taphunzira za lonjezo lalikulu la Yehova la kudzalowetsa mmalo dongosolo liripoli ndi miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano mmene “mukhalitsa chilungamo.” (2 Pet. 3:13) Tikukondweretsedwa ndi chiyembekezo chakuti posachedwapa dziko loipa iri lidzakhala litachoka ndipo dziko lapansi lidzasandulizidwa kukhala Paradaiso. Koma kodi njira yathu ya moyo imasonyeza kuti tikukonzekera mowona mtima kaamba ka moyo m’dziko limene chilungamo chidzakhala chizolowezi chofala? Baibulo limatiuza momvekera bwino kuti: “Musakonde dziko lapansi, kapena za m’dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichiri mwa iye.” (1 Yoh. 2:15) Nzowona kuti pali zinthu zambiri za dziko zimene palibe aliyense wa ife amazikonda. Koma kodi timada kwakukulukulu zinthu zadziko zimene zimadodometsa chisangalalo chathu chamoyo cha nthawi ino? Kapena kodi timakananso mzimu wake—mkhalidwe wake wa kudzigangira, nkhawa yake yopambanitsa yaumwini? Kodi ife mowona mtima tikuchipanga kukhala chizolowezi cha kumvetsera Yehova ndi kuyesa kumvera iye kuchokera m’mtima mwathu, mosasamala kanthuza zikhoterero zirizonse zotsutsa zathupi? Njira yathu yathunthu ya moyo—mosasamala kanthu za kumene ife tiri, mosasamala kanthu za chimene tikuchita—iyenera kupereka umboni wakuti maganizo athu ndi zisonkhezero zathu ziri zozikidwa pa Mulungu.—Miy. 3:5, 6.
12. (a) Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kupindula ndi mwayi wa kuphunzira njira za Yehova ndi kuzitsatira m’miyoyo yathu tsopano? (b) Kodi malemba olembedwa m’ndimeyi amatanthauzanji kwa ife yense payekha?
12 Pamene nthawi yoikidwiratu ya Yehova ya kuwononga dongosolo loipa lazinthu iri ndi onse okonda njira zake ifika, iye sadzazengereza. Iye sadzasunthira nthawi imeneyo patsogolo kapena kusintha miyezo yake kotero kuti apatse mpata awo amene akali kuyesayesa kuumirira kudziko, awo amene ali kokha amitima iwiri ponena za kuphunzira chifuniro cha Mulungu ndi kuchichita. Tsopano ndiyo nthawi ya kuchitapo kanthu! (Luka 13:23, 24; 17:32; 21:34-36) Chifukwa chake, ndikokondweretsa mtima chotani nanga mmene kuliri kuwona “khamu lalikulu” la anthu limene likupindula ndi mwayi wofunika uwu, akumafunafuna mwaphamphu malangizo amene Yehova amapereka kudzera mwa gulu lake lachikondi ndiyeno mogwirizana kuyenda m’mabande ake!
[Mawu a M’munsi]
a Malemba ogwidwa m’bukhu lino ngochokera mu Revised Union Nyanja Version, kusiyapo ngati kwasonyezedwa mwa njira ina.
Makambitsirano Openda
● Kodi nchiyani chimene chiri chifuno cha Yehova ponena za kulambira?
● Pambuyo pa kuphunzira ziphunzitso zamaziko za Baibulo, kodi ndikupita patsogolo kowonjezereka kotani kumene tiyenera kufunafuna kukupanga mwaphamphu?
● Kodi nchiyani chimene ife aliyense payekha tingachite, kotero kuti zinthu zogwirizanitsa zimene takambitsiranazi zisonkhezere miyoyo yathu monga momwe ziyenera kuchitira?
[Chithunzi chachikulu patsamba 4]