Mutu 1
Kugwirizana pa Kulambira Masiku Athu Ano—Kodi Kumatanthauzanji?
N’ZOSANGALATSA kuti anthu ochuluka padziko lonse lapansi akugwirizana pa kulambira. Kulambira kumeneku kukugwirizanitsa anthu mamiliyoni ambiri a mitundu yonse, mafuko onse, ndi zilankhulo zonse. Chaka chilichonse anthu ambiri akusonkhanitsidwa. Baibulo limati anthu ameneŵa ndi “mboni” za Yehova ndipo amatchedwa kuti “khamu lalikulu.” Amatumikira Mulungu “usana ndi usiku.” (Yesaya 43:10-12; Chivumbulutso 7:9-15) N’chifukwa chiyani amachita zimenezi? Chifukwa chakuti adziŵa kuti Yehova ndiye Mulungu woona yekha. Zimenezi zimawalimbikitsa kusintha miyoyo yawo kuti igwirizane ndi miyezo yake yolungama. Ndiponso, aphunzira kuti tikukhala mu “masiku otsiriza” a dziko loipa lomwe tilimoli. Aphunziranso kuti Mulungu awononga dzikoli posachedwa, ndi kuti abweretsa dziko latsopano la paradaiso kuti liloŵe m’malo mwake.—2 Timoteo 3:1-5, 13; 2 Petro 3:10-13.
2 Mawu a Mulungu amalonjeza kuti: “Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti . . . Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” (Salmo 37:10, 11) “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:29) “[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:4.
3 Anthu amene akugwirizana pa kulambira koona masiku ano ndiwo adzakhala nzika zoyambirira m’dziko latsopano limenelo. Iwo aphunzira za chifuniro cha Mulungu ndipo akuchichita malinga ndi mphamvu zawo. Yesu, posonyeza kuti zimenezi n’zofunika, anati: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.” (Yohane 17:3) Mtumwi Yohane analemba kuti: “Dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi zonse.”—1 Yohane 2:17.
Tanthauzo Lake Lenileni
4 Kodi kusonkhanitsidwa kwa anthu ambirimbiri kuti azilambira mogwirizana masiku athu ano kukutanthauza chiyani makamaka? Ndi umboni wosatsutsika wakuti tayandikira kwambiri mapeto a dziko loipali, ndipo dziko latsopano la Mulungu liyamba lilipoli likangotha. Tikudzionera ndi maso athuŵa maulosi a Baibulo akukwaniritsidwa amene ananeneratu za kusonkhanitsa anthu ochuluka kumeneku. Ulosi wina wofotokoza zimenezi umati: “Kudzachitika masiku otsiriza [anoŵa], kuti phiri la nyumba ya Yehova [kulambira kwake koona ndi kokwezeka] lidzakhazikika pamwamba pa mapiri [pamwamba pa kulambira kwina kulikonse], . . . ndi mitundu ya anthu idzayendako. Ndipo amitundu ambiri adzamuka, nadzati, Tiyeni, tikwere ku phiri la Yehova, ndi ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo; kuti Iye atiphunzitse njira zake, ndipo tidzayenda m’mabande ake.”—Mika 4:1, 2; Salmo 37:34.
5 Ngakhale kuti mitundu yathunthu sikubwera ku nyumba yolambiriramo yauzimu ya Yehova, anthu mamiliyoni ochuluka ochokera m’mitundu yonse akutero. Pamene akuphunzira za cholinga cha Yehova Mulungu chozikidwa pa chikondi, ndi umunthu wake wosangalatsa, mitima yawo imadzala chiyamikiro. Modzichepetsa amafuna kudziŵa zimene Mulungu akufuna kuti iwo azichita. Pemphero lawo n’lofanana ndi la wamasalmo yemwe anati: “Mundiphunzitse chokonda Inu; popeza Inu ndinu Mulungu wanga.”—Salmo 143:10.
6 Kodi mukaganiza mukuona kuti muli pakati pa khamu lalikulu la anthu amene Yehova akuwasonkhanitsa masiku ano kuti azilambira mogwirizana? Kodi malangizo amene mwalandira m’Mawu ake mukuwalabadira, kusonyeza kuti mukuzindikiradi kuti Yehova ndiye Gwero lake? Kodi ‘mudzayenda m’mabande ake’ kufika pati?
Kukutheka Bwanji?
7 Cholinga cha Yehova n’chakuti zolengedwa zonse zanzeru zigwirizane pa kulambira koona. Tikuyembekezera mwachidwi tsiku limene onse okhalako adzalambira Mulungu woona yekha! (Salmo 103:19-22) Koma izi zisanachitike, Yehova ayenera kuchotsa kaye onse amene amakana kuchita chifuniro chake cholungama. Mwachifundo, iye amaneneratu zomwe adzachita, kotero kuti anthu kulikonse akhale ndi mwayi wosintha khalidwe lawo. (Yesaya 55:6, 7) N’chifukwa chake masiku athu ano pempho likuperekedwa “kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu” kuti achitepo kanthu mofulumira. Pempholo limati: “Opani Mulungu, m’patseni ulemerero; pakuti yafika nthaŵi ya chiweruziro chake; ndipo m’lambireni Iye amene analenga m’mwamba ndi mtunda ndi nyanja ndi akasupe amadzi.” (Chivumbulutso 14:6, 7) Kodi mwalabadira pempholi? Ngati mwatero ndiye kuti muli ndi mwayi wopemphanso ena kuti adziŵe Mulungu woona ndi kum’lambira.
8 Yehova safuna kulambiridwa ndi anthu amene amati amamukhulupirira koma amachitabe zofuna zawo. Mulungu amafuna kuti anthu ‘azindikire chifuniro chake’ ndi kuti moyo wawo uzionetsa zimenezi. (Akolose 1:9, 10) Motero, anthu oyamikira amati akadziŵa ziphunzitso zoyambirira zazikulu za m’Baibulo, amafunabe kukula msinkhu kuti akhale Akristu okhwima. Amafuna kumudziŵa kwambiri Yehova, kumvetsetsa Mawu ake mwakuya, ndiponso kuwagwiritsa ntchito kwambiri pa moyo wawo. Amalakalaka kuti azikhala ndi makhalidwe amene Atate wathu wakumwamba ali nawo ndi kumaona zinthu monga mmene iye amazionera. Zimenezi zimawalimbikitsa kufunafuna njira zogwirira ntchito yopulumutsa moyo imene iye akuonetsetsa kuti ikuchitika pa dziko lapansi masiku athu ano. Kodi izi n’zimene inunso mukukhumba?—Marko 13:10; Ahebri 5:12–6:3.
9 Baibulo limasonyeza kuti amene amatumikira Yehova ayenera kukhala anthu ogwirizana. (Aefeso 4:1-3) Kugwirizana kumeneku kuyenera kukhalapo tsopano lino, ngakhale kuti tikukhala m’dziko logaŵikana ndiponso tikulimbanabe ndi kupanda ungwiro kwathu. Yesu anapemphera ndi mtima wonse kuti ophunzira ake onse akakhale amodzi, ogwirizana zenizeni. Kodi zimenezi zinatanthauzanji? Choyamba, kuti iwo akakhala ndi ubwenzi wabwino ndi Yehova ndi Mwana wake. Chachiŵiri, kuti iwo akakhala ogwirizana pakati pawo. (Yohane 17:20, 21) Kuti zimenezi zitheke, Yehova amalangiza anthu ake kupyolera mu mpingo wachikristu.
Kodi Mfundo Zimene Zimathandiza Kuti Pakhale Kugwirizana Ndi Ziti?
10 M’munsimu muli mfundo zikuluzikulu zisanu ndi ziŵiri zimene zimathandiza kuti pakhale kugwirizana pa kulambira. Pamene mukuyankha mafunsowo, ganizirani mmene mfundo iliyonse ikukhudzira ubwenzi wanu ndi Yehova komanso ndi Akristu anzanu. Kulingalira mfundo zimenezi komanso kuŵerenga malemba amene angosonyezedwa koma osagwidwa mawu kudzakuthandizani kukulitsa nzeru zaumulungu, luso la kulingalira, ndi kuzindikira—makhalidwe amene tonse timafunika kukhala nawo. (Miyambo 5:1, 2; Afilipi 1:9-11) Pendani mfundozi imodziimodzi.
(1) Timakhulupirira kuti Yehova ali ndi ufulu woika muyezo wa chabwino ndi choipa. “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzawongola mayendedwe ako.”—Miyambo 3:5, 6.
N’chifukwa chiyani tiyenera kufunafuna uphungu wa Yehova ndi malangizo ake posankha zochita? (Salmo 146:3-5; Yesaya 48:17)
(2) Tili ndi Mawu a Mulungu kuti azititsogolera. “Pakulandira mawu a Uthenga wa Mulungu, simunawalandira monga mawu a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mawu a Mulungu, amenenso achita mwa inu okhulupirira.”—1 Atesalonika 2:13.
Kodi pamakhala ngozi yotani pamene tingochita zimene “tikuganiza” kuti n’zolondola? (Miyambo 14:12; Yeremiya 10:23, 24; 17:9)
Ngati sitikudziŵa malangizo amene Baibulo limapereka pa nkhani inayake, kodi tiyenera kuchitanji? (Miyambo 2:3-5; 2 Timoteo 3:16, 17)
(3) Tonse timapindula ndi dongosolo limodzimodzi lolandirira chakudya chauzimu. “Ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova.” (Yesaya 54:13) “Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku [la chiwonongeko] lili kuyandika.”—Ahebri 10:24, 25.
Kodi ndi phindu lotani limene anthu omwe amagwiritsa ntchito bwino makonzedwe omwe Yehova wapanga otidyetsa mwauzimu amapeza? (Yesaya 65:13, 14)
(4) Yesu Kristu, osati munthu wina aliyense, ndiye Mtsogoleri wathu. “Inu musatchedwa Rabi; pakuti Mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale. Ndipo inu musatchule wina atate wanu pansi pano, pakuti alipo mmodzi ndiye Atate wanu wa Kumwamba. Ndipo musatchedwa atsogoleri, pakuti alipo mmodzi Mtsogoleri wanu, ndiye Kristu.”—Mateyu 23:8-10.
Kodi ife tonse tiyenera kuganiza kuti timaposa anzathu? (Aroma 3:23, 24; 12:3)
(5) Timayembekezera kuti boma la Ufumu wa Mulungu ndilo lokha lidzathandize anthu. “Chifukwa chake pempherani inu chomwechi: Atate wathu wa Kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano. Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake.”—Mateyu 6:9, 10, 33.
Kodi ‘kufuna Ufumu’ choyamba kumathandiza motani kuteteza mgwirizano wathu? (Mika 4:3; 1 Yohane 3:10-12)
(6) Mzimu woyera umapatsa olambira Yehova makhalidwe ofunika kwambiri kuti Akristu akhale ogwirizana. “Chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso.”—Agalatiya 5:22, 23.
Kodi tiyenera kuchitanji kuti mzimu wa Mulungu ubale zipatso zake mwa ife? (Machitidwe 5:32)
Kodi kukhala ndi mzimu wa Mulungu kumakhudza motani ubwenzi wathu ndi Akristu anzathu? (Yohane 13:35; 1 Yohane 4:8, 20, 21)
(7) Onse olambira Mulungu moonadi amalalikira uthenga wabwino wa Ufumu wake. “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.”—Mateyu 24:14.
Kodi chimene chiyenera kutilimbikitsa kufuna kugwira kwambiri ntchito yolalikira imeneyi n’chiyani? (Mateyu 22:37-39; Aroma 10:10)
11 Kulambira Yehova mogwirizana kumatithandiza kuyandikira pafupi naye ndi kukhala ndi mayanjano olimbikitsa ndi okhulupirira anzathu. Salmo 133:1 limati: “Onani, n’kokoma ndi kokondweretsa ndithu kuti abale akhale pamodzi!” N’zosangalatsatu kwambiri kusiya dzikoli ndi zochitika zake zonse zadyera, makhalidwe ake oipa, ndiponso chiwawa chake n’kumasonkhana ndi anthu amene amakondadi Yehova ndi kumvera malamulo ake!
Peŵani Zinthu Zogaŵanitsa
12 Kuti tisawononge mgwirizano wathu wa padziko lonse wamtengo wapataliwo, tiyenera kupeŵa zinthu zimene zingatigaŵanitse. Chimodzi cha zimenezi ndi mtima wofuna kudzidalira m’malo modalira Mulungu ndi malamulo ake. Yehova amatithandiza kupeŵa mtima woterewu mwa kuvumbula yemwe amauyambitsa, Satana Mdyerekezi. (2 Akorinto 4:4; Chivumbulutso 12:9) Satana ndiye anachititsa Adamu ndi Hava kuti anyalanyaze zonena za Mulungu ndi kusankha kuchita zosagwirizana ndi chifuniro cha Mulunguyo. Zimenezi zinawadzetsera tsoka iwowo ndi ife tomwe. (Genesis 3:1-6, 17-19) Dzikoli ladzala ndi mzimu wofuna kudzidalira m’malo modalira Mulungu ndi malamulo ake. Choncho tisalole mzimu woterowo.
13 Mwachitsanzo, talingalirani lonjezo losangalatsa la Yehova loti adzachotsa dziko loipa lilipoli ndi kubweretsa miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano mmene “mukhalitsa chilungamo.” (2 Petro 3:13) Kodi zimenezi siziyenera kutichititsa kuyamba panopa kukonzekera kudzakhala ndi moyo nthaŵi imeneyo pamene chilungamo chidzakhala ponseponse? Izi zikutanthauza kuti tiyenera kulabadira malangizo omveka bwino a Baibulo akuti: “Musakonde dziko lapansi, kapena za m’dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichili mwa iye.” (1 Yohane 2:15) Motero timapeŵa mzimu wa dzikoli—kutanthauza maganizo ake ofuna kudzidalira, kumangoganiza za iwe mwini basi, makhalidwe ake onyansa ndi chiwawa chake. Timakonda kumvera Yehova ndi kulabadira ndi mtima wonse zimene amatiuza, ngakhale kuti thupi lathu lopanda ungwiro limafuna kuchita zina. Moyo wathu wonse umapereka umboni wakuti maganizo athu ndi zolinga zathu zili pa kuchita chifuniro cha Mulungu.—Salmo 40:8.
14 Nthaŵi ya Yehova ikadzafika yowononga dziko loipali limodzi ndi onse amene amakonda njira zake, iye sadzazengereza. Nthaŵiyo sadzaisunthira m’tsogolo; ndiponso sadzasintha miyezo yake n’cholinga choganizira amene akuumirirabe dzikoli kwinaku akuphunzira ndi kuchita chifuniro cha Mulungu ndi mitima iŵiri. Ino ndiyo nthaŵi yochitapo kanthu! (Luka 13:23, 24; 17:32; 21:34-36) Motero n’zokondweretsa kwambiri kuona khamu lalikulu likugwiritsa ntchito mwayi wamtengo wapatali umenewu mwa kufunafuna mwachidwi malangizo amene Yehova amapereka m’Mawu ake ndi m’gulu lake ndiponso mwa kuyenda mogwirizana m’mabande ake kupita ku dziko latsopano. Ndipo tikamaphunzira zambiri za Yehova, tidzamukondanso kwambiri ndipo tidzafunitsitsa kumutumikira.
Bwerezani Zimene Mwakambirana
• Kodi cholinga cha Yehova pa nkhani ya kulambira n’chotani?
• Titadziŵa ziphunzitso zoyambirira zazikulu za m’Baibulo, kodi tiyenera kuchita khama kuti tipitebe patsogolo motani?
• Kuti tizichita zinthu mogwirizana ndi olambira ena a Yehova, kodi aliyense ayenera kuchitanji?
[Mafunso]
1, 2. (a) Kodi zosangalatsa zimene zikuchitika masiku athu ano n’zotani? (b) Kodi anthu okhulupirika ali ndi chiyembekezo chabwino chiti?
3. Kodi kugwirizana kwenikweni pa kulambira kukutheka bwanji?
4. (a) Kodi kusonkhanitsidwa kwa anthu ambirimbiri kuti azilambira mogwirizana masiku athu ano kukutanthauzanji makamaka? (b) Kodi Baibulo limati chiyani za kusonkhanitsa anthu kumeneku?
5, 6. (a) Kodi mitundu ikupitadi kwa Yehova mwa njira yanji? (b) Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati?
7. (a) Kodi potsirizira pake kugwirizana pa kulambira kudzafika pati? (b) N’chifukwa chiyani munthu afunika kufulumira kukhala wolambira Yehova tsopano lino, nanga ena tingawathandize motani kuchita zimenezi?
8. Titadziŵa ziphunzitso zoyambirira zazikulu za m’Baibulo, kodi tiyenera kuchita khama kuti tipitebe patsogolo motani?
9. Kodi kugwirizana kwenikweni kukutheka motani lerolino?
10. (a) Kodi timakulitsa chiyani pamene patokha tigwiritsa ntchito Baibulo kuti tipeze mayankho a mafunso amene amatikhudza? (b) Pendani mfundo zimene zimathandiza kuti Akristu akhale ogwirizana mwa kuyankha mafunso amene ali m’ndime ino.
11. Kodi chimachitika n’chiyani tikamagwiritsa ntchito choonadi cha m’Baibulo pa moyo wathu?
12. N’chifukwa chiyani tifunika kupeŵa mtima wofuna kudzidalira?
13. Kodi n’chiyani chimasonyeza kuti tikukonzekeradi kudzakhala m’dziko latsopano lolungama la Mulungu?
14. (a) N’chifukwa chiyani m’pofunika kugwiritsa ntchito mwayi umene ulipo panopa kuphunzira njira za Yehova ndi kuzitsatira pa moyo wathu? (b) Kodi malemba amene asonyezedwa m’ndimeyi akutanthauzanji kwa ifeyo?
[Chithunzi patsamba 4]
‘Ofatsa adzalandira dziko lapansi nadzakondwera nawo mtendere wochuluka’