Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • uw mutu 11 tsamba 87-94
  • ‘Pitirizanibe Kufunafuna Choyamba Ufumuwo’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Pitirizanibe Kufunafuna Choyamba Ufumuwo’
  • Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Musalole Chowonadi cha Ufumu Kutsamwitsidwa
  • Ophunzira Oyambirira Apereka Chitsanzo
  • Chititsani Ufumu Kukhala Woyamba m’Moyo mwanu
  • “Muthange Mwafuna Ufumu”
    Lambirani Mulungu Woona Yekha
  • Kodi Chikhulupiriro Chanu mwa Mulungu N’cholimba Motani?
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Uthenga Umene Tiyenera Kulengeza
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Muzifunafuna Ufumu Osati Zinthu Zina
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
Onani Zambiri
Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
uw mutu 11 tsamba 87-94

Mutu 11

‘Pitirizanibe Kufunafuna Choyamba Ufumuwo’

1. (a) Kodi nchifukwa ninji zaka 1 900 zapitazo Yesu ananena za kufunafuna choyamba Ufumu? (b) Kodi ndiphunziro lotani limene tiyenera kudzifunsa?

ZOPOSA zaka 1 900 zapitazo, m’nkhani yokambidwira mu Galileya, Yesu anafulumiza ophunzira ake kuti: “Pitirizani, kufunafuna choyamba ufumu ndi chilungamo chake.” Koma chifukwa ninji? Kodi nthawi ya kuikidwa pa mpando wachifumu kwa Kristu siinali zaka mazana ambiri mtsogolo? Inde. Koma Ufumu Waumesiya umenewo ndiwo njira mwa imene dzina lopatulika la Yehova iyemwiniyo lidzalemekezedwera ndipo chifuno chake chachikulu kulinga kudziko lapansi chidzakwaniritsidwira. Aliyense amene amazindikira mowonadi kufunika kwa ichi adzapereka ku Ufumuwo malo oyamba m’moyo wake. Zinali choncho m’zaka za zana loyamba ndipo ziridi choncho tsopano popeza kuti Ufumuwo ukulamulira. Kodi njira yanu yamoyo imasonyeza kuti mukufunafuna ufumu wa Mulungu choyamba?—Mat. 6:33, NW.

2. Kodi nchiyani chimene chiri zinthu zimene anthu kawirikawiri amafunafuna mwaphamphu?

2 Anthu mofala ali okondwerera koposerapo m’zinthu zina. Amafunafuna mwaphamphu chuma ndi zovala, chakudya ndi zinthu zina zakuthupi ndi zikondwerero zimene ndalama zingagule. (Mat. 6:31, 32) Njira yawo yamoyo imasonyeza kutanganitsidwa ndi iwo eni ndi zokondweretsa. M’miyoyo yawo, Mulungu amaikidwa pamalo achiwiri—ngati amamkhulupirira nkomwe.

3. (a) Kodi ndi chuma chamtundu wanji chimene Yesu analimbikitsa ophunzira ake kufunafuna, ndipo chifukwa ninji? (b) Kodi nchifukwa ninji panalibe kufunikira kwa kudera nkhawa mopambanitsa ndi zosowa zakuthupi?

3 Koma kwa ophunzira ake Yesu anapereka uphungu uwu: “Musadzikundikire nokha chuma padziko lapansi,” chifukwa chakuti palibe chirichonse cha chuma chotero chimakhala kosatha. “Mmalo mwake,” iye anati, “mudzikundikire nokha chuma m’mwamba,” mwa kutumikira Yehova. Iye analimbikitsa ophunzira ake kusunga diso lawo “bwino,” kusumika chisamaliro chawo pa chinthu chimodzi chokha kuchitidwa kwa chifuniro cha Mulungu. “Simungakhoze kutumikira Mulungu ndi chuma,” iye anawauza choncho. Koma bwanji ponena za zosowa zakuthupi—chakudya, zovala ndi malo ogona? “Musadere nkhawa,” Yesu anapereka uphungu. Iye anawasonyeza mbalame—Mulungu amazidyetsa. Analimbikitsa otsatira ake kuphunzira ku maluwa—Mulungu amawaveka mokongola. Kodi atumiki aumunthu aluntha a Yehova saali amtengo wokulirapo koposa chirichonse cha zimenezi? “Pamenepo, pitirizani, kufunafuna choyamba ufumu ndi chilungamo chake,” Yesu anatero, “ndipo zinthu zina zonsezi [zofunika] zidzawonjezeredwa kwa inu.” (Mat. 6:19-34, NW) Kodi mumakhulupirira zimenezo? Kodi zochita zanu zimakusonyeza?

Musalole Chowonadi cha Ufumu Kutsamwitsidwa

4. Ngati munthu aika chigogomezero chopambanitsa pazinthu zakuthupi, kodi nchiyani chingakhale chotulukapo? Perekani chitsanzo.

4 Ngati munthu adera nkhawa mopambanitsa ndi zinthu zakuthupi, chotulukapo chingakhale chowononga. Ngakhale kuli kwakuti anganene kuti amakondwera ndi Ufumu, ngati mu mtima mwake aika zinthu zina poyamba, chowonadi cha Ufumu chidzatsamwitsidwa. (Mat. 13:18, 19, 22) Mwachitsanzo, panthawi ina wolamulira wachichepere adafunsa Yesu kuti, “Ndidzachita chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?” Kulabadira kwake ku yankho la Yesu kunasonyeza kuti anali wa makhalidwe abwino ndipo anachitira anthu ena zabwino. Koma anali womamatira mopambanitsa ku chuma chake chakuthupi. Iye sakanakhoza kulekana nacho kuti akhale wotsatira Kristu. Chotero anaphonya mwayi umene ukanatsogolera kukukhala kwake wolamulira limodzi ndi Kristu mu Ufumu wakumwamba. Monga momwe Yesu panthawi imeneyo ananenera: “Okhala nacho chuma adzalowa ufumu wa Mulungu ndi kuvuta nanga!”—Marko 10:17-23.

5. (a) Kodi ndizinthu ziti zimene Paulo analimbikitsa Timoteo kukhala wokhutira nazo, ndipo chifukwa ninji? (b) Kodi ndimotani mmene Satana amagwiritsirira ntchito “chikondi cha pandalama” monga msampha wowononga?

5 Zaka zingapo pambuyo pake, mtumwi Paulo analembera Timoteo, amene panthawiyo anali mu Efeso, paphata pa ulemerero wa zamalonda. Anamkumbutsa kuti: “Sitinatenga kanthu polowa m’dziko lapansi, ndiponso sitikhoza kupita nako kanthu pochoka pano. Koma pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimenezi zitikwanire.” Kugwira ntchito kuti tidzipezere “zakudya ndi zofunda” ife eni ndi banja lathu nkoyenera. Koma Paulo anachenjeza: “Iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi m’msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chitaiko.” Satana ali wochenjera. Poyamba angakope munthu m’njira zochepa. Izi kawirikawiri zimatsatiridwa ndi chitsenderezo chokulirapo—mwinamwake mwayi wa kukwezedwa pantchito imene imapatsa munthu malipiro ochulukirapo koma imene imafuna nthawi imene poyamba inali kupatulidwira zinthu zauzimu. Kusiyapo ngati tikhala maso, “chikondi cha pandalama” chingatsamwitse zinthu zofunika koposa za Ufumu. Monga momwe Paulo akunenera, “Ena pochikhumba [chikondi cha pandalama], anasokera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zowawa zambiri.”—1 Tim. 6:7-10.

6. (a) Kuti tipewe kutcheredwa msampha, kodi tiyenera kuchitanji? (b) Kodi limenelo liri lingaliro logwirizana ndi zenizeni tikalingalira mkhalidwe wachuma wadziko lerolino?

6 Ndi chikondi chowona kwa mbale wake Wachikristu, Paulo analimbikitsa Timoteo kuti: “Thawa izi,” ndipo “limba nayo nkhondo yabwino yachikhulupiriro.” (1 Tim. 6:11, 12) Kuyesayesa kwaphamphu nkofunika ngati titi tipewe kutengeka ndi njira yamoyo yokondetsa zinthu zakuthupi yadziko lotizinga. Koma ngati tipanga kuyesayesa mogwirizana ndi chikhulupiriro chathu, Yehova sadzatitaya. Mosasamala kanthu za mitengo yokwerayo ndi kufalikira kwa ulova, adzatsimikizira kuti tikupeza zimene tikusowadi.—Aheb. 13:5, 6.

Ophunzira Oyambirira Apereka Chitsanzo

7. Pamene Yesu anatumiza atumwi kukalalikira mu Israyeli, kodi anawapatsa malangizo otani, ndipo kodi nchifukwa ninji amenewa anali oyenerera?

7 Yesu atapereka kwa ophunzira ake malangizo oyenerera anawatumiza kulowa m’Israyeli kukalalikira mbiri yabwino. “Ufumu wakumwamba wayandikira.” Ha ndiuthenga wochititsa nthumanzi wotani nanga! Yesu Kristu, Mfumu Yaumesiya, anali pakati pawo. Popeza atumwi anali kudzipereka eni ake ku utumiki wa Mulungu, Yesu anawalimbikitsa kukhala ndi chidaliro chakuti Mulungu akawasamalira. Iye anati: “Musanyamule kanthu ka paulendo, kapena ndodo, kapena thumba, kapena mkate, kapena ndalama; ndipo musakhale nawo malaya awiri. Ndipo m’nyumba iriyonse mukalowemo, khalani komweko, ndipo muzikachokera kumeneko.” (Mat. 10:5-10; Luka 9:1-6; 10:4-7) Yehova akatsimikizira kuti zosowa zawo zikukwaniritsidwa kupyolera mwa Aisrayeli anzawo, amene kuchereza alendo pakati pawo kunali kozolowereka.

8. (a) Kodi nchifukwa ninji Yesu anapereka malangizo osiyana imfa yake itatsala pang’ono kuchitika? (b) Komabe, kodi nchiyani chimene chinafunikira kukhala m’malo oyamba m’miyoyo yawo?

8 Pambuyo pake, imfa yake itangotsala pang’ono, Yesu anachenjeza atumwi ake za chenicheni chakuti akakhala akugwira ntchito m’mikhalidwe yosintha. Chifukwa cha chitsutso cha boma, kucherezako sikungachitidwe mosavuta mu Israyeli. Ndiponso, mwamsanga akakhala akupititsa uthenga wa Ufumu ku maiko Achikunja. Tsopano anafunikira kunyamula “thumba landalama” ndi “thumba lakamba.” Komabe, anafunikira kupitirizabe kufunafuna choyamba Ufumu wa Yehova ndi chilungamo chake, ali ndi chidaliro chakuti Mulungu akadalitsa zoyesayesa zawo za kupeza zakudya ndi zovala zofunikazo.—Luka 22:35-37.

9. (a) Kodi ndimotani mmene Paulo anachititsira Ufumu kukhala m’malo oyamba? (b) Kodi ndimotani mmenezosowa zake zakuthupi zinasamalilidwira? (c) Kodi ndiuphungu wotani umene anapereka kwa ena pankhani izi?

9 Mtumwi Paulo anapereka chitsanzo chabwino kwambiri cha mmene uphungu wa Yesu ungagwiritsidwire ntchito. Paulo anasumika moyo wake pauminisitala. (Mac. 20:24, 25) Pamene anapita m’chigawo kukalalikira anasamalira zosowa za iye mwini mwa kugwira ntchito yopanga mahema. Iye sanayembekezere ena kumsamalira. (Mac. 18:1-4; 1 Ates. 2:9; 1 Akor. 9:18) Komabe anavomereza moyamikira kuchereza ndi mphatso pamene ena anafuna kusonyeza chikondi chawo ndi chiyamikiro m’njira iyi. (Mac. 16:15, 34; Afil. 4:15-17) Iye sanalimbikitse akazi ndi amuna Achikristu kunyalanyaza mathayo awo abanja kuti apite kukalalikira, koma m’malo mwake kusamalira mathayo awo osiyanasiyana mwa njira yachikatikati. Anawapatsa uphungu wa kugwira ntchito ndi manja awo, kukonda mabanja awo ndi kukhala oolowa manja m’kugawana ndi ena. (Aef. 4:28; 2 Ates. 3:7-12; Tito 2:3-5) Iye anawafulumizanso kuika chidaliro chawo, osati m’chuma chakuthupi, koma mwa Mulungu ndi kugwiritsira ntchito miyoyo yawo mwa njira imene idzasonyeza kuti akuzindikiradi zimene ziri zinthu zofunika kwambiri m’moyo. Mogwirizana ndi ziphunzitso za Yesu, zimenezo zinatanthauza kufunafuna choyamba Ufumu wa Mulungu ndi chilungamo chake.—Afil. 1:9-11.

Chititsani Ufumu Kukhala Woyamba m’Moyo mwanu

10. (a) Kodi kumatanthauzanji ‘kufunafuna choyamba Ufumu’? (b) Koma kodi nchiyani chimene sichiyenera kunyalanyazidwa?

10 Kodi ife enife timagawira ena mbiri yabwino ya Ufumu mokulira chotani? Mwinatu, zimenezo zimadalira, pa mikhalidwe yathu ndipo, mokulira, pakuya kwa chiyamikiro chathu. Kumbukirani kuti Yesu sananene kuti, ‘Funafunani Ufumu pamene mulibe chirichonse chochita.’ Ndiponso sananene kuti, ‘Malinga ngati mulankhula za Ufumu kamodzi kamodzi, mukuchita zonse zofunika.’ Ndiponso sananene kuti, ‘Yambani mwachangu zinthu za Ufumu; koma ngati Dongosolo Latsopano liwonekera kukhala litachedwa kudza, pitirizani kuchita zocheperapo mu utumiki wa Mulungu koma khalani ndi moyo mofanana ndendende ndi anthu ena.’ Pozindikira bwino kufunika kwa Ufumu, iye anasonyeza chifuniro cha Atate wake m’nkhaniyi, kumati: “Funani mosalekeza ufumu wake.” Kapena, monga momwe mtumwi Mateyu analembera: “Pamenepa, pitirizani, kufunafuna choyamba ufumu ndi chilungamo chake.” (Luka 12:31; Mat. 6:33) Ngakhale kuli kwakuti unyinji wa ife umakupeza kukhala kofunika kuchita ntchito yakutiyakuti kusamalira zosowa zakuthupi za ife eni ndi mabanja athu, ngati tiridi ndi chikhulupiriro, miyoyo yathu idzasumikidwa pantchito imene Mulungu watipatsa mogwirizana ndi Ufumu wake. Panthawi imodzimodziyo sitidzanyalanyaza mathayo athu abanja.—1 Tim. 5:8; Miy. 29:15.

11. (a) Kodi ndimotani mmene Yesu analongosolera mwafanizo chenicheni chakuti sionse akakhala okhoza kuchita mlingo wofanana m’kufalitsa uthenga wa Ufumu? (b) Kodi izi zimadalira pa zochitika ziti?

11 Ena a ife tiri okhoza kuwonongera nthawi yochuluka koposa ena mu uminisitala wakumunda. Koma m’fanizo lake lonena za mitundu yosiyanasiyana yanthaka Yesu anasonyeza kuti onse amene mitima yawo iri yofanana ndi nthaka yabwino adzabala zipatso. Kumlingo wotani? Mikhalidwe ya anthuwo imasiyana modalira pamsinkhu, thanzi ndi mathayo abanja. Koma pamene pali chiyamikiro chenicheni, zochulukirapo zingachitidwe.—Mat. 13:19, 23.

12. Kodi nchonulirapo chauzimu chopindulitsa chotani chimene makamaka achichepere akulimbikitsidwa kulingalira?

12 Nkwabwino kukhala ndi zonulirapo zimene zidzatithandiza kufutukula kukhala kwathu ndi mbali mu uminisitala wa Ufumu. Achichepere ayenera kulingalira mwamphamvu chitsanzo chabwino koposa cha Mkristu wachichepere wachanguyo Timoteo. (Afil. 2:19-22) Kodi nchiyani chimene chikakhala chabwino kwambiri kwa iwo koposa kulowa mu uminisitala wanthawi yonse pamene amaliza sukulu yawo yakuthupi? Nawonso, achikulire adzapindula mwa kuika zonulirapo zauzimu zothandiza.

13. (a) Kodi ndani amasankha chimene inu mwininu mudzachita mu utumiki wa Ufumu? (b) Ngati tifunafunadi choyamba Ufumu, kodi uku ndiko umboni wa chiyani?

13 M’malo mwa kusuliza awo amene tingawalingalire kuti akanatha kuchita zochuluka, tiyenera kusonkhezeredwa ndi chikhulupiriro kulimbikira kudziwongolera ife eni kotero kuti titumikire Mulungu mokwanira monga momwe mikhalidwe yathu ingatilolere. (Aroma 14:10-12; Agal. 6:4) Monga momwe kwasonyezedwera m’nkhani ya Yobu, Satana amanenatu kuti ife tiri okondweretsedwa kwakukulukulu ndi chuma chathu chakuthupi, kupeza bwino kwathu ndi thanzi lathu la ife eni, ndi kuti cholinga chathu m’kutumikira Mulungu chiri chadyera. Koma ngati tifunafunadi choyamba Ufumu, tikukhala ndi mbali m’kutsimikizira Mdyerekezi kukhaladi wabodza lamkunkhuniza. Tikupereka umboni wakuti chimene chiri choyamba m’miyoyo yathu sindicho chuma chakuthupi kapena chitonthozo chaumwini koma utumiki wa Mulungu. Chotero mwa mawu ndi ntchito tikutsimikizira chikondi chathu chakuya cha pa Yehova, chichirikizo chathu chokhulupirika cha ulamuliro wake ndi chikondi chathu cha pamunthu mnzathu.—Miy. 27:11; Yobu 1:9-11; 2:4, 5.

14. (a) Kodi nchifukwa ninji programu yautumiki wakumunda iri yothandiza? (b) Kodi Mboni zambiri zikukhala ndi phande ku mlingo wotani mu uminisitala wakumunda, ndipo chifukwa ninji?

14 Programu ingatithandize kukwaniritsa zambiri koposa zimene mwinamwake tingachite popanda. Yehova iyemwiniyo ali ndi ‘nthawi zoikika’ za kuchita chifuno chake, ndipo tikuchita bwino kumtsanzira. (Eks. 9:5; Marko 1:15; Agal. 4:4) Ngati nkotheka, kuli bwino kukhala ndi phande mu uminisitala wakumunda panthawi imodzi kapena kuposa zoikidwiratu mlungu uliwonse. Mboni za Yehova zikwi makumi ambiri pa dziko lonse lapansi zalembetsa monga apainiya othandiza ndipo zikusangalala ndi kuthera maola awiri kapena kuposa patsiku, paavereji, m’kulalikira mbiri yabwino. Ena amatero mokhazikika; ena, nthawi zingapo chaka chirichonse. Ena zikwi zambiri amatumikira monga apainiya okhazikika, akumagwiritsira ntchito maola okwanira atatu patsiku, pa avereji, kulengeza uthenga wa Ufumu. Ena, monga apainiya apadera ndi amishonale, amathera nthawi yowonjezereka mu utumiki wa Ufumu. Ndipo kaya tiri mu uminisitala wakumunda kapena ayi, tingakhoze kufunafuna mipata ya kugawira aliyense amene adzamvetsera chiyembekezo cha Ufumu panthawi iriyonse yoyenera. (Yerekezerani ndi Yohane 4:7-15.) Tonsefe tiyenera kulingalira mwamphamvu za tanthauzo la ulosi wa Yesu wakuti “mbiri yabwino imeneyi yaufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni ku mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.” Chikhumbo chathu chiyenera kukhala cha kukhala ndi phande lokwanira m’ntchitoyo monga momwe mikhalidwe yathu ilolera.—Mat. 24:14, NW; Aef. 5:15-17.

15. Mogwirizana ndi uminisitala wathu, kodi nchifukwa ninji mukulingalira kuti uphungu wa pa 1 Akorinto 15:58 uli wapanthawi yake?

15 Mogwirizana, mbali zonse zadziko lapansi, mosasamala kanthu za mtundu mu umene zikukhalamo, Mboni za Yehova mokangalika zikukhala ndi phande mokangalika m’mwayi waukulu uwu wa utumiki. Zimagwiritsira ntchito kwa iwo eni uphungu wouziridwa wa Baibulo uwu: “Khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthawi zonse, podziwa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.”—1 Akor. 15:58.

Makambitsirano Openda

● Pamene Yesu ananena za kufunafuna choyamba Ufumu, kodi anali kusonyeza kuti nchiyani chikayenera kuikidwa m’malo achiwiri?

● Kodi ndilingaliro lotani limene tiyenera kukhala nalo kulinga ku zosowa zakuthupi za ife eni ndi zamabanja athu? Kodi nchithandizo chotani chimene Mulungu adzatipatsa?

● Kodi kuchuluka kwa zimene timachita mu utumiki wa Ufumu kulibe kanthu malinga ngati tikukhala ndi phande pang’ono? Chifukwa ninji?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena