Mutu 11
“Muthange Mwafuna Ufumu”
PAMENE Yesu anali kukamba nkhani ku Galileya zaka zoposa 1,900 zapitazo, analimbikitsa omvera ake kuti: “Koma muthange mwafuna Ufumu [wa Mulungu] ndi chilungamo chake.” N’chifukwa chiyani anafunika kuchita changu chonchi? Kodi nthaŵi yoti Kristu alandire mphamvu za Ufumu sinali kutsogolo kwambiri? Inde, koma Ufumu Waumesiya unali njira imene Yehova adzatsimikizira kuti ndi woyenera kulamulira ndiponso adzakwaniritsa cholinga chake chachikulu cha dziko lapansi kupyolera mwa Ufumuwo. Aliyense amene anamvetsadi kufunika kwa zimenezi akanaona Ufumuwo kukhala chinthu chofunika kwambiri pa moyo wake. Ngati zinthu zinali chonchi m’zaka 100 zoyambirirazo, kuli bwanji nanga masiku ano, pamene Kristu waikidwa pa mpando kukhala Mfumu! Ndiye funso n’lakuti, Kodi moyo wanga umasonyeza kuti ndikufunafuna Ufumu wa Mulungu choyamba?—Mateyu 6:33.
2 Lerolino, anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse lapansi akufunafunadi Ufumu choyamba. Akusonyeza kuti akugwirizana ndi ulamuliro wa Ufumuwo mwa kuika moyo wawo wonse pa kuchita chifuniro cha Yehova, pokhala atadzipatulira kwa iye. Kumbali ina, anthu miyandamiyanda amakonda kumangofunafuna zinthu za pamoyo wawo. Amafunafuna ndalama komanso katundu ndi zosangalatsa zimene angagule ndi ndalamazo. Kapena amathera mphamvu zawo zonse pa kufunafuna nzeru zatsopano zopititsira patsogolo luso lawo pantchito. Moyo wawo umasonyeza kuti amangosamala za iwo eni, chuma chawo, ndi zosangalatsa. Amaika Mulungu pa malo achiŵiri, ngatitu amamukhulupirira n’komwe.—Mateyu 6:31, 32.
3 Komabe, Yesu analangiza ophunzira ake kuti: “Musadzikundikire nokha chuma padziko lapansi,” chifukwa chuma choterocho sichikhala mpaka kalekale. “Koma,” iye anatero, “mudzikundikire nokha chuma m’Mwamba” mwa kutumikira Yehova. Yesu analimbikitsa otsatira ake kukhala ndi diso “la kumodzi” mwa kuika maganizo awo ndiponso kuthera mphamvu zawo pa kuchita chifuniro cha Mulungu. “Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma,” anawauza motero. Nanga bwanji zinthu zofunika pamoyo, monga chakudya, zovala, ndi malo ogona? “Musadere nkhaŵa,” Yesu anawalangiza motero. Anawauza kuti aone mmene mbalame zimakhalira, kuti Mulungu amazidyetsa. Yesu analimbikitsa otsatira ake kutengera phunziro pa maluŵa, kuti Mulungu amawaveka. Kodi anthu okhala ndi nzeru amene amatumikira Yehova saposa zonsezi? Yesu anati: “Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse [zofunika pamoyo] zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mateyu 6:19-34) Kodi zimene mumachita zimasonyeza kuti mumakhulupiriradi zimenezi?
Musalole Kuti Choonadi cha Ufumu Chitsamwitsidwe
4 Sikulakwa ngati munthu akufuna kuti akhale ndi zinthu zokwanira zofunika pamoyo wake ndi wa banja lake. Komabe pangakhale ngozi yaikulu ngati munthu adera nkhaŵa kwambiri zinthu zofunika pamoyo. Ngakhale angamanene kuti amakhulupirira Ufumu, ngati mumtima mwake zinthu zina ndizo zimakhala zoyamba, choonadi cha Ufumu chidzatsamwitsidwa. (Mateyu 13:18-22) Mwachitsanzo, panthaŵi ina wolamulira wachinyamata wolemera anafunsa Yesu kuti: “Ndidzachita chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?” Anali wakhalidwe labwino ndipo ankachitira zabwino anthu ena, koma mtima wake wonse unali pa chuma chake. Analephera kusiya chumacho kuti akhale wotsatira wa Kristu. Motero anataya mwayi umene ukanamuchititsa kukhala limodzi ndi Kristu mu Ufumu wakumwamba. Panthaŵi imeneyo Yesu anati: “Okhala nacho chuma adzaloŵa mu Ufumu wa Mulungu ndi [kuvutika] nanga!”—Marko 10:17-23.
5 Patapita zaka zochuluka, mtumwi Paulo analembera kalata Timoteo amene panthaŵiyo anali ku Efeso, komwe kunali kuchimake kwa malonda. Paulo anamukumbutsa kuti: “Sitinatenga kanthu poloŵa m’dziko lapansi, ndiponso sitikhoza kupita nako kanthu pochoka pano; koma pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimenezi zitikwanire.” Kugwira ntchito kuti munthu upeze “zakudya ndi zofunda” zako komanso za banja lako ndi koyenera. Koma Paulo anachenjeza kuti: “Iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi m’msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chitayiko.” Satana ndi wochenjera kwambiri. Poyamba anganyengerere munthu m’zinthu zing’onozing’ono. Kenako angam’panikize kwambiri. Mwachitsanzo angamupatse mwayi wokwezedwa pantchito kapena kupeza ntchito ina yabwino ya malipiro ambiri koma imene imatenga nthaŵi yomwe poyamba anali kuigwiritsa ntchito pa zinthu zauzimu. Ngati sitidzipenyerera “chikondi cha pandalama” chingatsamwitse zinthu zofunika kwambiri za Ufumu. Paulo anati: “Ena pochikhumba, anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zoŵaŵa zambiri.”—1 Timoteo 6:7-10.
6 Pokhala ndi chikondi chenicheni pa mbale wake wachikristu, Paulo analimbikitsa Timoteo kuti: “Thaŵa izi” ndiponso kuti, “Limba nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro.” (1 Timoteo 6:11, 12) Khama lenileni n’lofunika kuti tipewe kutengeka ndi moyo wokondetsa chuma umene uli m’dziko lotizingali. Koma ngati tidziperekadi pa chikhulupiriro chathu, Yehova sadzatisiya konse. Ngakhale zinthu zikwere mitengo ndiponso kupeza ntchito kukhale kovuta kwambiri, iye adzaonetsetsa kuti tili ndi zinthu zimene timafunikiradi. Paulo analemba kuti: “Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti [Mulungu] anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu. Kotero kuti tinena molimbika mtima, Mthandizi wanga ndiye Ambuye; sindidzaopa; adzandichitira chiyani munthu?” (Ahebri 13:5, 6) Ndipo Mfumu Davide analemba kuti: “Ndinali mwana ndipo ndakalamba: ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.”—Salmo 37:25.
Ophunzira Oyambirira Amatipatsa Chitsanzo
7 Yesu ataphunzitsa atumwi ake mokwanira ndithu, anawatumiza kukalalikira uthenga wabwino mu Israyeli ndi kulengeza kuti: “Ufumu wa Kumwamba wayandikira.” Unalitu uthenga wosangalatsa kwambiri! Yesu Kristu, Mfumu Yaumesiya, anali pakati pawo. Popeza kuti atumwiwo anali kudzipereka kuti atumikire Mulungu, Yesu anawalimbikitsa kukhala n’chidaliro chakuti Mulungu akawasamalira. Motero iye anati: “Musanyamule kanthu ka paulendo, kapena ndodo, kapena thumba, kapena mkate, kapena ndalama; ndipo musakhale nawo malaya aŵiri. Ndipo m’nyumba iliyonse mukalowemo, khalani komweko, ndipo muzikachokera kumeneko.” (Mateyu 10:5-10; Luka 9:1-6) Yehova adzaonetsetsa kuti Aisrayeli anzawo, omwe anali ndi chizoloŵezi chochereza alendo, akuwapatsa zinthu zofunikazo.
8 Pambuyo pake, pamene anali pafupi kufa, Yesu anachenjeza atumwi ake kuti m’tsogolo zinthu zidzasintha pa ntchito yawo. Chifukwa chakuti akuluakulu a boma adzatsutsa ntchito yawo, kudzakhala kovuta kuti anthu mu Israyeli awalandire monga poyamba. Ndiponso, posakhalitsa adzatengera uthenga wa Ufumu ku mayiko a anthu Akunja. Tsopano iwo anafunika kutenga “thumba la ndalama” ndi “thumba la kamba.” Ngakhale zinali choncho, iwo choyamba anafunika kufunafuna Ufumu wa Yehova ndi chilungamo chake, akukhulupirira kuti Mulungu adzadalitsa khama lawo lopeza chakudya ndi chofunda.—Luka 22:35-37.
9 Mtumwi Paulo anali chitsanzo chabwino kwambiri pa kugwiritsa ntchito malangizo a Yesu. Paulo anaika moyo wake wonse pa utumiki. (Machitidwe 20:24, 25) Akapita kukalalikira kudera linalake, anali kudzipezera zinthu zofunika pamoyo wake; anali kuchita kugwira ntchito yosoka mahema. Sanayembekezere kuti anthu ena azimusamalira. (Machitidwe 18:1-4; 1 Atesalonika 2:9) Komatu, anali kuyamikira ena akam’chereza ndi kum’patsa mphatso poonetsa chikondi chawo. (Machitidwe 16:15, 34; Afilipi 4:15-17) Paulo analimbikitsa Akristu kuti posamalira udindo wawo wolalikira asanyalanyaze udindo wawo wa pabanja, koma kuti aziyendetsa maudindo onse mosalemerera mbali imodzi. Anawalangiza kuti azigwira ntchito, azikonda mabanja awo, ndi kuti azigaŵana zinthu ndi ena. (Aefeso 4:28; 2 Atesalonika 3:7-12) Anawalimbikitsa kudalira Mulungu osati chuma, ndi kuti moyo wawo aziugwiritsa ntchito m’njira yosonyeza kuti analidi kuzindikira zomwe zinali zinthu zofunika kwambiri. Mogwirizana ndi zimene Yesu anaphunzitsa, zimenezi zinatanthauza kufunafuna choyamba Ufumu wa Mulungu ndi chilungamo chake.—Afilipi 1:9-11.
Ufumu Ukhale Woyamba M’moyo Wanu
10 Kodi ifeyo, aliyense payekha, timalimbikira kwambiri motani pouza ena uthenga wabwino wa Ufumu? Mwa zina, zimadalira mmene moyo wathu ulili ndiponso kuyamikira kwathu Ufumuwo. Kumbukirani kuti Yesu sananene kuti, ‘Funafunani Ufumu mukakhala mulibe chochita.’ Podziŵa kufunika kwa Ufumuwo, iye anafotokoza chifuniro cha Atate wake kuti: “Tafunafunani [nthaŵi zonse, NW] Ufumu wake.” (Luka 12:31) Ngakhale kuti ambiri a ife tifunika kugwira ntchito kuti tizipeza zinthu zofunika pamoyo wathu ndiponso pabanja lathu, ngati tili ndi chikhulupiriro moyo wathu wonse udzakhala pa kugwira ntchito ya Ufumu imene Mulungu watipatsa. Panthaŵi imodzimodziyo tidzasamalira maudindo athu pabanja.—1 Timoteo 5:8.
11 Ena timathera nthaŵi yambiri tikulalikira uthenga wabwino wa Ufumu kuposa ena. Koma Yesu m’fanizo lake lonena za nthaka yosiyanasiyana anaonetsa kuti onse amene mitima yawo ili yofanana ndi nthaka yabwino adzabereka zipatso. Zochuluka motani? Anthu ali ndi moyo wosiyanasiyana. Msinkhu wa munthu, thanzi lake, ndi maudindo a banja amene ali nawo ndi zina mwa zinthu zimene zingakhudze mmene akubalira zipatso. Koma pamene anthu ayamikira uthenga wa Ufumu moonadi, angathe kuchita zambiri.—Mateyu 13:23.
12 Ndi bwino kukhala ndi zolinga zimene zingatithandize kuwonjezera zomwe timachita mu utumiki wa Ufumu. Achinyamata ayenera kuganiza mozama za chitsanzo cha Timoteo, Mkristu wachinyamata wachanguyo. (Afilipi 2:19-22) N’chiyaninso chabwino kwambiri chimene iwo angachite kuposa kuyamba utumiki wa nthaŵi zonse pamene amaliza sukulu yawo? Achikulire nawo adzapindula akakhala ndi zolinga zabwino zauzimu.
13 M’malo moderera zochita za anthu amene timaona kuti akhoza kuchita zambiri, chikhulupiriro chiyenera kutichititsa kuwongolera zimene ifeyo timachita kotero kuti tithe kutumikira Mulungu kwambiri monga mmene moyo wathu ukutilolera. (Aroma 14:10-12; Agalatiya 6:4, 5) Monga mmene nkhani ya Yobu imasonyezera, Satana amati zimene timafuna kwambiri ndizo chuma, kukhala ndi moyo wabwino, komanso kukhala ndi thanzi labwino ndipo amati dyera ndilo limatichititsa kutumikira Mulungu. Koma ngati tikufunafunadi Ufumu choyamba, tikuthandiza nawo kusonyeza kuti Mdyerekezi alidi wabodza. Tikupereka umboni wakuti chofunika kwambiri pa moyo wathu ndi kutumikira Mulungu. Motero mwa zolankhula zathu ndi zochita zathu timasonyeza kuti Yehova timamukonda kwambiri, kuti ndife okhulupirika pochirikiza ulamuliro wake, ndi kutinso timakonda anthu anzathu.—Yobu 1:9-11; 2:4, 5; Miyambo 27:11.
14 Kukhala ndi nthaŵi yeniyeni yochitira zinthu kungatithandize kuchita zambiri. Yehova mwiniyo “anaika nthaŵi” yokwaniritsira cholinga chake. (Eksodo 9:5; Marko 1:15) Ngati n’kotheka, ndi bwino kupita mu utumiki wakumunda ulendo umodzi kapena maulendo angapo mlungu uliwonse pa nthaŵi imene munaika. Mboni za Yehova miyandamiyanda padziko lonse zikuchita upainiya wothandiza, ndipo zimalalikira uthenga wabwino kwa maola pafupifupi aŵiri patsiku. Enanso miyandamiyanda akuchita upainiya wokhazikika, ndipo amalengeza uthenga wa Ufumu kwa maola pafupifupi aŵiri ndi theka patsiku. Apainiya apadera ndi amishonale amathera nthaŵi yoposa pamenepa ali mu utumiki wa Ufumu. Tingafunefunenso mipata yoti anthu alionse amene angamvetsere tiwauze za chiyembekezo cha Ufumu mwamwayi. (Yohane 4:7-15) Tizilakalaka kugwira nawo ntchito imeneyi kwambiri monga mmene moyo wathu ungatilolere, chifukwa Yesu ananeneratu kuti: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.”—Mateyu 24:14; Aefeso 5:15-17.
15 Mogwirizana, m’madera onse a dziko lapansi, mosasamala kanthu za dziko limene iwo akukhala, a Mboni za Yehova akuchita utumiki umenewu. Iwo amagwiritsa ntchito malangizo ouziridwa a m’Baibulo aŵa: “Khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthaŵi zonse, podziŵa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.”—1 Akorinto 15:58.
Bwerezani Zimene Mwakambirana
• Kodi pamene Yesu ananena kuti “muthange mwafuna Ufumu,” anali kusonyeza kuti n’chiyani chiyenera kuikidwa pamalo achiŵiri?
• Kodi maganizo athu ayenera kukhala otani pankhani yopeza zinthu zofunika pamoyo wathu ndi pa banja lathu? Kodi Mulungu adzatithandiza motani?
• Kodi tingachite nawo mbali ziti za utumiki wa Ufumu?
[Mafunso]
1. (a) N’chifukwa chiyani Yesu analimbikitsa omvera ake kuthanga afuna Ufumu? (b) Ndi funso lotani limene tiyenera kudzifunsa?
2. Kodi ndi zinthu ziti zimene anthu ambiri amazifunafuna ndi mtima wonse?
3. (a) Kodi Yesu analimbikitsa ophunzira ake kufunafuna chuma chotani, nanga n’chifukwa chiyani? (b) N’chifukwa chiyani sitifunika kuda nkhaŵa kwambiri ndi zinthu zofunika pamoyo?
4. Ngati munthu aika mtima wake wonse pa zofunika pamoyo, kodi chingachitike n’chiyani?
5. (a) Kodi Paulo analimbikitsa Timoteo kukhala wokhutira ndi zinthu ziti, nanga n’chifukwa chiyani? (b) Kodi Satana amagwiritsa ntchito motani “chikondi cha pandalama” kuti chikhale msampha wowononga?
6. (a) Kodi tiyenera kuchitanji kuti tipewe kugwera mu msampha wokonda chuma? (b) Kodi tingakhale ndi chidaliro chotani ngakhale dzikoli lili ndi mavuto a zachuma?
7. Kodi Yesu anapatsa ophunzira ake malangizo otani okhudza kulalikira, nanga n’chifukwa chiyani malangizoŵa anali oyenerera?
8. (a) Pamene Yesu anali pafupi kufa, n’chifukwa chiyani anapereka malangizo atsopano pa kulalikira? (b) N’chiyani chimene chinafunikabe kukhala choyamba pamoyo wa otsatira a Yesu?
9. Kodi Paulo anatani kuti akhoze kuika Ufumu choyamba m’moyo wake uku akupeza zinthu zofunika pamoyo, ndipo ndi malangizo otani amene anapereka pankhaniyi?
10. Kodi kufunafuna Ufumu choyamba kumatanthauzanji?
11. (a) Kodi Yesu anapereka fanizo lotani posonyeza kuti anthu onse sakachita zofanana pofalitsa uthenga wa Ufumu? (b) Kodi ndi zinthu ziti zimene zimakhudza kuchuluka kwa zimene munthu angachite?
12. Kodi achinyamata akulimbikitsidwa kuganizira cholinga chabwino chiti chauzimu?
13. (a) Kodi ndani amasankha zimene ifeyo patokha tingathe kuchita mu utumiki wa Ufumu? (b) Kodi timasonyeza chiyani tikamafunafunadi Ufumu choyamba?
14. (a) N’chifukwa chiyani kukhala ndi nthaŵi yeniyeni yoloŵera mu utumiki wakumunda n’kopindulitsa? (b) Kodi Mboni zambiri zikuchita nawo utumiki wakumunda mokulira motani?
15. Pankhani ya utumiki wathu, n’chifukwa chiyani mukuona kuti malangizo omwe ali pa 1 Akorinto 15:58 ndi a panthaŵi yake?
[Chithunzi patsamba 107]
M’dziko lililonse, Mboni za Yehova lerolino zikulalikira uthenga wabwino chimaliziro chisanafike