Nyimbo 8
Kudzigonjetsera Mokhulupirika Kudongosolo Lateokratiki
1. Anthu a Yehova akulengeza
Chowonadi cha Ufumu wabwino.
Onse amveredi kulamulolo
Akhale mu’modzi, adalirike.
(Korasi)
2. Kristu Mtsogoleri alamulira;
Alimbitsa asilikali ake.
Nkhondo njauzimu, tikangalike
Monga gulu liri logwirizana.
(Korasi)
3. Tiri ndi “mdindo” ndi mzimu woyera.
Awa adzatitsogoza m’Chikristu.
Choncho tiime nji, tikondwetse Ya,
Kulengeza mawu ake onsewo!
(KORASI)
Kugonjeradi modalirika,
Kwa Mulungu wathu.
Atetezera, ngwachifundodi.
Timamkhulupilira.