NYIMBO 123
Tizigonjera Mulungu Mokhulupirika
Losindikizidwa
1. Tikamalengeza za choonadi
Cha Ufumu wa Mulungu padziko,
Tizitsatira malangizo ake.
Tizichita zonse mogwirizana.
(KOLASI)
Tizigonjera Mulungu wathu
Mokhulupirika.
Amatikonda, amateteza,
Tizikhulupirika.
2. M’lungu watipatsa mzimu woyera,
Watipatsanso kapolo wanzeru.
Choncho tizisangalatsa Yehova
Polalikira mokhulupirika.
(KOLASI)
Tizigonjera Mulungu wathu
Mokhulupirika.
Amatikonda, amateteza,
Tizikhulupirika.
(Onaninso Luka 12:42; Aheb. 13:7, 17.)