Nyimbo 10
Khalani Okhazikika, Osasunthika!
1. Popeza ‘masiku ngomaliza,’
Tifulumire muntchito yathu.
Tikhaletu osagwedezeka,
Ndi okhulupirika (mutumiki).
(Korasi)
2. Zosangalatsa m’dziko nzambiri.
Tikhale olama maganizo.
Ngati tikhazikika kwa M’lungu,
Adzatitetezera. (nthaŵi zonse).
(Korasi)
3. Tiyeni titumikire M’lungu.
Tigalamuke tisawodzere.
Tigwiritsitse Mbiri Yabwino.
Masikuwa adzatha. (posachedwa).
(KORASI)
Tiyenera kulimba; Tisiyane ndi dziko,
Tidye chowonadi tisunge umphumphu.