Nyimbo 33
‘Yehova Iye Mwini Wakhala Mfumu!’
1. Anthu, thokozani Yehova.
Lengezani zochita zakezo.
Imbirani Mulungu wathu mokondwa,
Eya, kuthiranso mang’ombe.
(Korasi)
2. Nena ulemerero wake.
Ndi chipulumutso apeleka.
Yehova ndiwamkulu atamandidwe
Koposa ndi milungu yonse.
(Korasi)
3. Mphamvu ndi kumveka nza M’lungu.
M’thokozeni kamba ka Mwana’ke.
M’malo oyera gwadirani Mulungu,
Nenani mokweza Yehova.
(KORASi)
Miyamba ikondwe, Dziko likondwere,
Chifukwa Yehova ali Mfumu!
Miyamba ikondwe, Dziko likondwere,
Chifukwa Yehova ali Mfumu!