Nyimbo 65
Kusonkhana Muumodzi
1. Nkokomatu kuwona
Abale pamodzi,
Kusonyeza chikondi
Kugwira mu’modzi!
Madalitso a Yehova
Ali ngati mame
Omagwera pa Ziyoni
Amaziziritsa.
2. Tisonkhane pamodzi;
Tilimbikitsane.
Kulengeza poyera
Chiyembekezocho.
Tiri achangu kukonza
Misonkhano yathu,
Tikhale okonzekera
Kupatsa Cho’nadi.
3. M’lungu wodalirika;
Mawu ake ngo’na.
Tiphunzire pamodzi
Za chiyembekezo.
Osaleka kusonkhana
Pamodzi abale,
Makamaka pakuwona
Tsiku liyandika.