Nyimbo 148
Kutamanda Mulungu Wathu Mfumu
1. O imbirani Yehova!
Tamani Ya tsiku lonse.
Tisonyeze dzina lake
Tiyandikire kwa iye.
Afutukula dzanjalo
Ali chire kuthandiza.
Tikhale odalirika;
Yehova ngwachisomodi.
2. Choncho tikhulupirike
Tinene ‘Nditamandanu.’
Mulungu ngwachilungamo;
Titame ukulu wake.
Atchinjiriza omkonda;
Sikudzakhala kovuta.
Atithandiza m’mavuto.
Titame Yehova Mfumu.
3. Ufumu wayandikira
Kudzetsa zinthu zabwino.
Lengeza Ufumu konse,
Iwe ‘wokhutiritsidwa.’
Yehova waika Mfumu
Yosanyozedwa ndi munthu.
Oipa adzachotsedwa.
Kulamula kudzakhala.