Nyimbo 192
Kudziŵitsa Chowonadi Chaufumu
1. Tinali osadziŵatu
Njira yoyenda Akristu.
Yehova anaŵalitsa,
Chowonadi Chaufumu.
2. Mwaŵi wathu tiwuwona
Kugwilira Teokrase,
Nenani mbiri ya M’lungu,
Chotero kumlemekeza.
3. Tilalikira kwa onse,
Panyumba ndi pakhwalala.
Timaphunzitsa anthu za
Chowonadi chomasula.
4. Tikuyesa kukulitsa
kulambira kowonako,
Titumikire momvana,
Kufikira ntchito ithe.