Nyimbo 223
Okhulupirika Anu Adzakulemekezani
1. Okhulupirika anu
Yehova Mulungu.
Amalengezatu ntchito
Ndi ulemerero.
Muli wapamwamba,
Wotamandika zedi,
Zosasanthulika,
Ntchito zanu, njira zanu.
Okhulupirika anu;
Aimba mokondwa.
Afuna kuuza anthu
Zimene adziŵa.
2. Mulungu wasankha mbadwo
Kuti umtamande.
Mbadwowo tsono ulipo,
Woyenda ndi M’lungu.
Kapolo wakeyo,
Amadyetsa nkhosazo
Popyola m’dzikoli,
Mbusa wawo patsogolo.
Monga okhulupirika,
Atamanda dzina.
Amalengeza mokondwa
Za ukulu wanu.
3. Ya Mulungu ndiwabwino;
Sitikayikira.
Adzapulumutsa anthu
—Titame ukoma.
Amaleza mtima;
Anthu ake adziŵa.
Tiyamike zedi
Kuti atifuna ife!
Polefuka atidzutsa
Nakhutitsa mtima.
Timdalitsa tsiku lonse;
Timlemekezadi.