Mutu 3
Kodi Dongosolo Lamakonoli Lidzakhala Kwautali Wotani?
KULI kwachibadwa kufuna kudziŵa kuti kudzakhala kwautali wotani kufikira pamene zochitika zolongosoledwa momvekera bwino kwambiri m’Baibulo ndi zimene zikutsirizikira mu Armagedo zidzachitika. Kodi ndiliti pamene dongosolo loipa lamakonoli lidzachotsedwa? Kodi tidzakhala ndi moyo kuwona dziko lapansi likukhala malo amene okonda chilungamo angakhale ndi mtendere wotheratu ndi chisungiko?
2 Yesu Kristu anapereka maumboni apadera amene akuyankha mafunso amenewo. Iye anatero pamene atumwi ake anafunsa kuti: “Kodi chizindikiro cha kufika kwanu chidzakhala chiyani ndi cha mathedwe a dongosolo la zinthu?” Ponena za kuchotsedwa kwenikweni kwa dongosolo loipa liripoli, Yesu mwachimvekere anati: “Ponena za tsikulo ndi ola palibe adziŵa, ngakhale angelo a kumwamba kapena Mwana, koma Atate yekha.” (Mateyu 24:3, 36, NW) Komabe anafotokoza mwatsatanetsatane kwambiri mbadwo umene ukawona “mapeto [Chigiriki: syn·teʹlei·a] a dongosolo la zinthu,” nyengo yanthaŵi yofika ku “mapeto [Chigiriki: teʹlos].” Dziŵerengereni m’Baibulo lanu pa Mateyu 24:3–25:46, ndiponso m’zolembedwa zofanana nazo pa Marko 13:4-37 ndi Luka 21:7-36.
3 Pamene mukuŵerenga zolembedwa zimenezi, mudzazindikira kuti, mwapang’ono chabe, Yesu analinkufotokoza zochitika zophatikizapo ndi zotsogolera ku chiwonongeko cha Yerusalemu ndi kachisi wake mu 70 C.E. Nkwachiwonekere kuti iyenso ankalingalira kanthu kena kakakulu kwambiri. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti pa Mateyu 24:21 iye akutchula “chisautso chachikulu chonga chimene sichinachitike chiyambire chiyambi cha dziko kufikira tsopano, inde, sichidzachitikanso.” Chimenecho chimafuna zambiri koposa chiwonongeko cha mzinda umodzi ndi anthu otsekerezedweramo. Ndipo pa Luka 21:31 zochitika zofotokozedwa zikunenedwa kukhala zikusonya ku kudza kwa “ufumu wa Mulungu” woyembekezeredwa kwanthaŵi yaitali. Kodi “chizindikiro” chapaderacho nchiyani chimene Yesu anati tichiyang’anire?
CHIZINDIKIRO CHACHIUNGWE
4 Ananeneratu za nkhondo, kupereŵera kwa zakudya, miliri yofala, zivomezi zazikulu, ndi mzimu wopanda chikondi mkati mwa nthaŵi ya kusamvera malamulo kowonjezereka, koma palibe chimodzi chirichonse cha zimenezi chimene chiri “chizindikiro.” Mbali zonse ziyenera kukwaniritsidwa mkati mwa nthaŵi ya moyo wa mbadwo umodzi kuti chithunzithunzicho chikwanire. Chophatikizidwamonso, chikakhala, “nsautso ya mitundu, yosadziŵa njira yotulukira . . . pamene anthu akukomoka ndi mantha” chifukwa cha zochitika zochitika kuthambo ndi m’nyanja zowazinga. (Luka 21:10, 11, 25-32; Mateyu 24:12; yerekezerani ndi 2 Timoteo 3:1-5, NW.) Mosiyana ndi zonsezi, koma monga mbali ya chizindikirocho, Yesu ananeneratu kulalikidwa kwapadziko lonse lapansi kwa mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu mosasamala kanthu za kuzunzidwa kwa atsatiri ake kwa m’mitundu yonse. (Marko 13:9-13) Kodi kafotokozedwe kachiungwe kameneko kamayeneranadi ndi nthaŵi imene tirimo?
5 Onyoza angaseke, akumanena kuti pakhala nkhondo, njala, zivomezi, ndi zinthu zotero, mobwerezabwereza m’mbiri ya anthu. Koma zochitika zoterozo zikukhala ndi tanthauzo lapadera pamene izo zonse zikuwonekera pamodzi, osati kokha m’malo oŵerengeka a apo ndi apo, koma padziko lonse lapansi mkati mwa nthaŵi yaitali imene ikuyamba ndi chaka chonenedweratu kale pasadakhale.
6 Lingalirani maumboni awa: Nkhondo imene inaulika mu 1914 inali yaikulu kwambiri chakuti inazadziŵika kukhala nkhondo yadziko yoyamba, ndipo chiyambire pamenepo mtendere sunabwereredi ku dziko lapansi. Pambuyo pa Nkhondo Yoyamba Yadziko panadza imodzi ya njala zazikulu koposa imene anthu sanawonepo chiyambire, ndipo ngakhale lerolino anthu okwanira mamiliyoni 40 pachaka alinkufa ndi njala. Flu Yaspanya ya 1918 inapha ambiri pamlingo wosafanana ndi wina uliwonse m’mbiri ya nthenda, ndipo mosasamala kanthu za kufufuza kwa asayansi, mamiliyoni makumi ambiri a anthu ngakhale tsopano alinkuvutika ndi kensa, nthenda yamtima, nthenda zonyansa zopatsirana mwakugonana, malungo, likodzo ndi kuchita khungu. Kubwerezabwereza kwa zivomezi zazikulu kwawonjezereka ndi pafupifupi nthaŵi 20 kuposa zimene zinali pa avereji mkati mwa zaka zikwi ziŵiri 1914 isanafike. Mantha ndi nsautso padziko lonse lapansi zikukantha anthu a misinkhu yonse. Pakati pa zifukwazo pali vuto landalama, chiwawa ndi chiwopsezo cha kufafanizidwa m’nkhondo yanyukliya yokhala ndi zida zoponyedwa kuchokera m’sitima zapansi panyanja kapena zakugwa kuchokera kumwamba—kanthu kena kosatheka zaka za zana la 20 zisanafike.
7 Pakati pa zonsezi kulengezedwa kwapadera kwa mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu kulinkuchitidwa, monga momwe Yesu ananeneratu. M’maiko ofikira 200 ndi zisumbu za m’nyanja, Mboni za Yehova zimathera maola mamiliyoni mazana ambiri chaka chirichonse, popanda malipiro, kuthandiza anthu a mikhalidwe yonse kuzindikira tanthauzo la zochitika zadziko zimenezi mothandizidwa ndi Mawu a Mulungu. Mokhulupirika Mboni zimasonyera anthu njira ya kupulumuka “chisautso chachikulu” monga nzika za Ufumu wa Mulungu. Ndipo Mbonizo zimachita zimenezi mosasamala kanthu za chenicheni chakuti, monga momwe lipoti lina lanyuzi ya ku Canada linanenera, izo “mwinamwake zimapirira chizunzo chachikulu kaamba ka zophophonya zazing’ono koposa gulu lina lirilonse lachipembedzo m’dziko.”
8 Tiyeneranso kulingalira kuti, monga mbali ya ulosi wake, Yesu anasonyeza kutha kwa nyengo yanthaŵi yotsimikizirika, akumati: “Yerusalemu adzaponderezedwa ndi mitundu, kufikira nthaŵi zoikidwiratu za mitundu zitakwanira.” (Luka 21:24, NW) Kodi “nthaŵi zoikidwiratu” zimenezo zinatha?
“NTHAŴI ZOIKIDWIRATU ZA MITUNDU”
9 Kuti tidziŵe yankho, tiyenera kuzindikira tanthauzo la Yerusalemu weniweniyo. Mzinda wokhala ndi malo ake achifumu pa Phiri la Ziyoni unatchedwa “mudzi wa Mfumu yaikulu . . . mzinda wa Yehova.” (Salmo 48:2, 8; Mateyu 5:34, 35) Mafumu a banja lachifumu la Davide analinkunenedwa kuti ankakhala “pa mpando wachifumu wa Yehova.” Chifukwa cha chimenecho Yerusalemu anali chizindikiro chowonekera chakuti Yehova anali kulamulira m’dziko lapansi. (1 Mbiri 29:23) Motero pamene magulu ankhondo Ababulo analoledwa ndi Mulungu kuwononga Yerusalemu, kuloŵetsa mfumu yake mu ukapolo ndi kusiya dzikolo liri labwinja, iwo analinkupondereza Ufumu wa Mulungu wochitidwa mwa mbadwa yachifumu ya Mfumu Davide. Pamene zimenezo zinachitika, mu 607 B.C.E., zinasonyeza chiyambi cha “nthaŵi zoikidwiratu za mitundu [Yachikunja].” Chiyambire nthaŵi imeneyo mbadwa ya Davide sinalamulire monga mfumu m’Yerusalemu.
10 Pamenepa, kodi nchiyani, chimene mapeto a ‘kupondereza Yerusalemu’ kumeneko akatanthauza? Kuti Yehova adakhazikanso pampando wachifumu mfumu yodzisankhira mwini, mbadwa ya Davide, tsopano kuti ilamulire, osati kokha pakati pa Ayuda, koma pakati pa anthu onse. Ameneyo ndi Ambuye Yesu Kristu. (Luka 1:30-33) Koma kodi iye akalamulira ali kuti? Kodi akakhala mu mzinda wapadziko lapansi wa Yerusalemu? Yesu anafotokoza momvekera bwino kuti mwaŵi wogwirizanitsidwa ndi Ufumu wa Mulungu unali kudzachotsedwa mu Israyeli wakuthupi. (Mateyu 21:43; wonaninso 23:37, 38.) Pambuyo pake, olambira Mulungu wowona anayang’ana ku “Yerusalemu wakumwamba,” gulu lakumwamba la Mulungu la zolengedwa zauzimu zokhulupirika, monga amayi wawo. (Agalatiya 4:26) Mukakhala m’Yerusalemu wakumwamba ameneyo m’mene Yesu akakhazikitsidwa pampando wachifumu, kuti alamulire dziko lapansi. (Salmo 110:1, 2) Zimenezo zikachitika pamapeto a “nthaŵi zoikidwiratu za mitundu.” Kodi amenewo akakhala liti?
11 Zaka makumi ambiri pasadakhale kunadziŵika kuti ameneŵa akadza mu 1914 pamapeto a kukwaniritsidwa kwakukulu kwa “nthaŵi zisanu ndi ziŵiri” za Danieli 4:10-17.a Koma kuzindikiridwa kokwanira kwa tanthauzo lake kunadza mwapang’onopang’ono mkati mwa zaka zimene zanatsatira. Mopita patsogolo ophunzira Baibulo anawona kukwaniritsidwa kwa chizindikiro chachiungwe pamaso pawo chimene Yesu anati chikasonyeza kukhalapo kwake kwakumwamba m’mphamvu Yaufumu. Kunakhala kwachiwonekere kuti iwo, ndithudi, adaloŵa m’nthaŵi ya “mathedwe a dongosolo la zinthu,” kuti Kristu adayamba kulamulira monga Mfumu mu 1914 ndi kuti mapeto a dziko loipali akadza mkati mwa mbadwo umene unawona chiyambi cha zinthu zimenezi.
KODI ZIYEMBEKEZO ZANU NZODALIRIKA MOTANI?
12 Ena amene amazindikira zinthu zimenezi m’kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yesu amawona kukhala kovuta kulandira lingaliro limene zimenezi zikusonyako. Kodi nchifukwa ninji. Chifukwa chakuti iwo anayembekezera kanthu kenanso. Iwo anaphunzitsidwa kuti kudza kwachiŵiri kwa Kristu kukakhala kowoneka ndipo kukachititsa kutembenuzidwa kwa nakatindi wa anthu. M’zaka za zana loyamba nawonso Ayuda anali ndi ziyembekezo zimene sizinakwaniritsidwe. Iwo anayembekezera kuti kudza kwa Mesiya kukakhala ndi chiwonetsero cha mphamvu imene ikawamasula ku Roma. Pomamatira ku ziyembekezo zawo zolakwa, iwo anakana Mwana wa Mulungu. Kukakhala kupusa chotani nanga kubwereza cholakwa chimenecho pamene Kristu wafika m’mphamvu Yaufumu! Kuli bwino kwambiri chotani nanga kuwona chimene kwenikweni Malemba enieniwo akunena!
13 Baibulo limasonyeza kuti kukakhala pakati pa adani ake pamene Kristu akayamba kulamulira. (Salmo 110:1, 2) Limasimba kutulutsidwa kwa Satana ndi ziŵanda zake kumwamba kudza chifupi ndi dziko lathu lapansi Yesu atapatsidwa ulamuliro Waufumu; motero kukakhala nyengo ya tsoka lowonjezereka kaamba ka dziko lapansi. (Chivumbulutso 12:7-12) Mkati mwa nthaŵi imeneyo mukakhala kulalikidwa kwa uthenga Waufumu kokulitsidwa, kuti apatse anthu mwaŵi wa kuchitapo kanthu ndi cholinga cha kupulumuka. (Mateyu 24:14; Chivumbulutso 12:17) Koma kodi zimenezo zikachititsa kutembenuzidwa kwa dziko lonse? Mosemphana ndi zimenezo, Baibulo limasonyeza kuti kudzatsatiridwa ndi chiwonongeko chosafanana ndi china chirichonse m’mbiri ya anthu. Ngakhale kuti anthu sadzawona Yesu Kristu wolemekezedwayo ndi maso awo enieni, onse amene sanalandire mofunitsitsa maumboni onena za kukhalapo mu ufumu kwa Kristu adzakakamizidwa “kuwona” kuti ndiye amene, monga momwe kunanenedweratu, akudzetsa chiwonongeko pa iwo.—Chivumbulutso 1:7; Mateyu 24:30; yerekezerani ndi 1 Timoteo 6:15, 16; Yohane 14:19.
14 Koma kodi tsopano kutha kwa zaka 70 chiyambire 1914 sikukusonyeza kuti pangakhale chikayikiro chakuti kaya tiridi “m’masiku otsiriza” chiyambire chaka chimenecho ndipo kaya ngati kudza kwa Kristu monga wolipsira kuli pafupi? Kutalitali! Ponena za awo amene akawona kukwaniritsidwa kwa “chizindikiro” kuyambira chiyambi chake, kuyambira 1914, Yesu anati: “Indetu ndinena ndi inu, Mbadwo uno sudzapita kufikira izi zonse zitachitika.” (Marko 13:30) Ziŵalo za mbadwo umenewo zidakalipo, ngakhale kuli kwakuti zikuchepachepa mofulumira m’chiŵerengero.
15 Nzowona kuti ziŵerengero zimasoyeza kuti avereji ya utali wa moyo padziko lonse lapansi tsopano ndiwo zaka 60 zokha, koma mabiliyoni ambiri a anthu amakhala ndi moyo kupitirira msinkhu umenewo. Malinga ndi kunena kwa ziŵerengero zopezeka, mu 1980 pafupifupi 250 000 000 a iwo amene anali amoyo mu 1914 anali amoyobe. Mbadwo umenewo sunathebe. Komabe, mokondweretsa, mwa iwo obadwa mu 1900 kapena mmbuyomo, ziŵerengero zofalitsidwa ndi Mitundu Yogwirizana zimasonyeza kuti kokha oyerekezeredwa kukhala 35 316 000 anali amoyobe mu 1980. Motero chiŵerengerocho chimatsika mofulumira pamene anthu akufika zaka zawo makumi asanu ndi aŵiri ndi makumi asanu ndi atatu. Pamene zilingaliridwa limodzi ndi maumboni onse a chizindikiro cholosera cha Yesu, maumboni ameneŵa amasonyeza mwamphamvu kuti mapeto ayandikira.—Luka 21:28.
16 Tsopano sindiyo nthaŵi yakukhala wamphwayi. Ndinthaŵi yakuchita ndi changu! Monga momwe Yesu anachenjezera ophunzira ake: “Khalani okonzekera, chifukwa pa ola limene simuganizira kukhala ilo, Mwana wa munthu [Yesu Kristu] akudza.”—Mateyu 24:44, NW.
[Mawu a M’munsi]
a Kaamba ka tsatanetsatane, wonani bukhulo “Let Your Kingdom Come,” tsamba 127-39, 186-9.
[Mafunso]
1. Ponena za malonjezo a Baibulo, kodi nchiyani chimene ambirife tafunsa?
2. (a) Kodi ndifunso lofanana lotani limene atumwi a Yesu anafunsa? (b) Kodi tikudziŵa kwenikweni pamene dongosolo loipa liripoli lidzatha? (c) Koma kodi ndichidziŵitso chothandiza kwambiri chotani chimene Yesu anapereka?
3. Kodi tikudziŵa motani kuti yankho la Yesu silinali kungofotokoza zochitika za m’zaka za zana loyamba zokha?
4. Kodi “chizindikiro” chimene Yesu anapereka nchiyani?
5. Kodi nchiyani chimene chikapanga zochitika zimenezi kukhala zoposa kubwerezedwa kwa zochitika za m’mbiri?
6, 7. Kodi ndizochitika ndi mikhalidwe zotani za m’zaka za zana la 20 zimene zimayeneranadi ndi chizindikiro chachiungwe chimenecho? (Poyankha, gwiritsirani ntchito Baibulo lanu ndi kusonyeza mbali za ulosi wa Yesu zimene mukufotokoza.)
8. Kodi ndinyengo yanthaŵi yotani imene inaphatikizidwanso mu ulosi umenewu?
9. (a) Kodi nchiyani chimene chiri “Yerusalemu” amene “anaponderezedwa” ndi mitundu? (b) Kodi ‘kupondereza’ kumeneko kunayamba liti?
10. (a) Kodi mapeto a ‘kuponderezako’ akatanthauzanji? (b) Kodi Yesu panthaŵi imeneyo akalamulira ali mu “Yerusalemu” uti, ndipo chifukwa ninji?
11, ndi tchati (pa tsamba 27). (a) Kodi kutha kwa “nthaŵi zoikidwiratu” kukuŵerengeredwa motani? (b) Motero, kodi nchiyani chimene chinayamba pamene “nthaŵi zoikidwiratu” zimenezo zinatha? (c) Kodi ndimotani mmene olemba mbiri amalingalirira 1914? (Wonani tsamba 29.)
12. Kodi ndiziyembekezo zolakwa zotani zimene zimapangitsa lingaliro limeneli kukhala lovuta kwa ena kulilandira? (Mateyu 24:26, 27; Yohane 14:3, 19)
13. Kodi ndizochitika zotani zimene Baibulo lenilenilo limagwirizanitsa ndi kukhala pafupi kwa Kristu?
14, 15. Kodi nchifukwa ninji kupita kwa zaka chiyambire 1914 sikumapereka chifukwa cha kukayikirira kuti tiridi “m’masiku otsiriza”?
16. Motero, kodi lingaliro lathu liyenera kukhala lotani?
[Bokosi patsamba 29]
Mmene Olemba Mbiri Akulingalirira 1914
Kaamba ka zifukwa zabwino, nkhondo imene inayamba mu 1914 yatchedwa Nkhondo Yaikulu ndi Nkhondo Yoyamba Yadziko. Palibe nkhondo yopululutsa imene idamenyedwapo motero kalelo. Chiyambire panthaŵi imeneyo nkhondo zangopitiriza chimene chinayamba mu 1914. Lingalirani mawu awa onena za ziyambukiro za chaka chosaiŵalika chimenecho.
● “Sikokha kuti nkhondoyo idasintha mapu a Yuropu ndi kuyambitsa zipanduko zimene zinawononga maufumu atatu, koma ziyambukiro zake zachindunji ndi zosakhala zachindunji zinaposa pamenepo pafupifupi m’mbali iriyonse. Pambuyo pa nkhondoyo ponse paŵiri atsogoleri andale zadziko ndi ena anayesa kuchepetsa kapena kuimika kusinthako ndi kubwezeretsanso zinthu ku mkhalidwe ‘wamasiku onse,’ ” kudziko limene linakhalako 1914 asanafike. Koma zimenezo zinali zosatheka. Chivomezicho chinali champhamvu kwambiri ndi chotalikitsidwa kwambiri chakuti dziko lakale lidapasulidwa kufikira ku maziko ake. Panalibe aliyense amene akanalimanganso monga momwe linaliri, limodzi ndi magulu ake a anthu, malingaliro ake ochuluka ndi makhalidwe ake.
“. . . Chachikulu kwambiri chinali kusintha kwa makhalidwe kumene kunachitika ndi kumene kudakhazikitsa muyezo watsopano kotheratu wa mkhalidwe mmbali zambirimbiri . . . Sanali asilikali okha omenya nkhondo amene anali ankhalwe ndi osasamala chuma cha mnansi. Sikokha kuti zinyengo zambiri, tsankhu lambiri ndi makhalidwe ambiri onyenga zinathetsedwa komanso miyezo yambiri yakale ya moyo ndi makhalidwe a anthu. Makhalidwe anali kusintha, chirichonse chinawonekera kukhala chikululuzika, monga ngati kuti zinthu zinalibenso maziko alionse olimba—kunalinso chomwecho m’mbali yandalama kudzanso makhalidwe akugonana, ndi ziphunzitso zandale zadziko kudzanso malamulo a ntchito zaluso. . . .
“Kupanda chisungiko kwakukulu kumene kunali kowanda panthaŵiyo kunali kowoneka bwino lomwe m’mbali ya zachuma. Munomu nkhondo idawononga mwankhanza dongosolo locholoŵanacholoŵana, lokhoza kusintha ndi lokhazikika bwino limodzi ndi malamulo amphamvu ndi makhalidwe enieni. . . . Sikunali kotheka m’mbali imeneyi kubwerera ku mkhalidwe ‘wamasiku onse.’”—Världshistoria—Folkens liv och Kultur (Stockholm; 1958), Vol. VII, tsamba 421, 422.
● “Theka la zaka zana limodzi lapita, komabe chipsera chimene tsoka la Nkhondo Yaikulu inasiya pathupi ndi moyo za mitundu sichinazimiririke . . . Ukulu weniweni ndi wamakhalidwe wa vuto limeneli unali waukulu kwambiri chakuti palibe chirichonse chosiyidwa chimene chinali chimodzimodzi ngati kale. Chitaganya chonse chathunthu: madongosolo aboma, malire amitundu, malamulo, magulu ankhondo, maunansi apakati pa maboma, komanso malingaliro, moyo wabanja, chuma, malo, maunansi a anthu—chirichonse chinasintha kuyambira pamwamba kufikira pansi. . . . Anthu potsiriza pake anataya kukhazikika kwawo, osadzabwereranso kufikira lerolino.”—General Charles de Gaulle, wolankhula mu 1968 (Le Monde, November 12, 1968).
● “Chiyambire chija 1914, aliyense wozindikira mikhalidwe m’dziko wavutika maganizo kwambiri ndi chimene chawonekera ngati ulendo wolinganizidwiratu ndi wotsimikizirika womka kutsoka lokulirapo mowonjezerekawonjezereka. Anthu ambiri olingalira kwambiri afika pa kulingalira kuti palibe chimene chingachitike kupeŵa kuloŵa m’chiwonongeko. Iwo akuwona mtundu wa anthu, mofanana ndi ngwazi yanthano Yachigiriki, yosonkhezeredwa ndi milungu yokwiya ndi kusapulumuka.”—Bertrand Russell, New York Times Magazine, September 27, 1953.
● “Poyang’ana mmbuyo kuchokera patsopano lino tikuwona bwino lomwe kuti kuulika kwa Nkhondo Yoyamba Yadziko kunaloŵetsa ‘Nthaŵi ya Mavuto’ m’zaka za zana lamakumi aŵiri—mogwirizana ndi mawu ofotokoza a wolemba mbiri wa ku Britain Arnold Toynbee—mmene mwanjira iriyonse kutsungula kwathu sikunachokere kufikira tsopano. Molunjika kapena mosalunjika nkhondo zonse za theka la zaka zana limodzi zimachokera ku 1914.”—The Fall of the Dynasties: The Collapse of the Old Order (New York; 1963), lolembedwa ndi Edmond Taylor, tsamba 16.
Koma kodi nchiyani chimene chimachititsa kusintha kwa zochitika kowononga dziko koteroko?
Baibulo limapereka malongosoledwe okhutiritsa.
[Tchati patsamba 27]
1914—Chaka Chosonyezedwa ndi Kuŵerenga Zaka Kwabaibulo ndi Zochitika Zadziko
Kuŵerenga Zaka
→ Baibulo linaneneratu nyengo ya “nthaŵi
zisanu ndi ziŵiri,” pambuyo pake Mulungu
akapereka ulamuliro kwa iye amene
anasankha (Danieli 4:3-17)
→ “Nthaŵi zisanu ndi ziŵiri” = zaka 2,520
(Yerekezerani ndi Chivumbulutso 11:2, 3;
12:6, 14; Ezekieli 4:6.)
→ Chiyambi cha “nthaŵi zisanu ndi ziŵiri”:
607 B.C.E. (Ezekieli 21:25-27; Luka 21:24)
→ Mapeto a “nthaŵi zisanu ndi ziŵiri”: 1914 C.E.
Yesu Kristu panthaŵi imeneyo
anakhazikitsidwa pampando wachifumu
kumwamba, anayamba kulamulira pakati pa
adani ake (Salmo 110:1, 2)
Satana anatulutsidwa kumwamba; tsoka
kwa anthu (Chivumbulutso 12:7-12)
Masiku otsiriza anayamba (2 Timoteo 3:1-5)
Zochitika Zonenedweratu Kusonyeza Masiku Otsiriza
→ Nkhondo (Nkhondo yoyamba yadziko
inayamba mu 1914; mtendere
sunabwerere kwenikweni)
→ Njala (Tsopano ikupha okwanira
mamiliyoni 40 pachaka)
→ Miliri yanthenda (Mosasamala kanthu za
kufufuza kwa asayansi kopititsidwa
patsogolo)
→ Zivomezi (Pa avereji, zachuluka pafupifupi
kuŵirikiza nthaŵi 20 pachaka chiyambire 1914)
→ Kuwopa (Upandu, kutha mphamvu
kwandalama, kupululutsa kwa nyukliya)
Dziko loipa liyenera kuwonongedwa ndi Mulungu mbadwo umene unawona 1914 usanathe (Mateyu 24:3-34; Luka 21:7-32)