Mutu 8
Kodi Chimachitika Nchiyani pa Imfa?
1. Kodi ndimafunso otani amene anthu amafunsa kawirikawiri ponena a akufa?
MWINA MWAKE mukudziwa lingaliro losowa chochita limene limadza limodzi ndi kutaya wokondwedwa mu imfa. Mungamve kukhala wachisoni ndi wosowa chithandizo kwambiri chotani nanga! Nkwachibadwa chabe kufunsa kuti: Kodi nchiyani chimene chimachitikira munthu pamene amwalira? Kodi iye amakhalabe wamoyo kwina? Kodi amoyo adzakhalanso okhoza kusangalala padziko lapansi utsamwali wa awo amene ali akufa tsopano?
2. Kodi nchiyani chimene chinachitikira munthu woyambayo, Adamu, pa imfa yake?
2 Kuti tiyankhe mafunso oterowo, chidzakhala chithandizo kwa ife kudziwa chimene chinachitikira Adamu pa imfa yake. Pamene anachimwa, Mulungu anamuuza kuti: “Udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti mmenemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.” (Genesis 3:19) Taganizirani zimene zimenezo zikutanthauza. Mulungu asanamlenge kuchokera ku fumbi, kunalibe Adamu. Iye sanakhaleko. Motero, atamwalira, Adamu anabwerera ku mkhalidwe umodzimodzi womwewo wa kusakhalako.
3. (a) Kodi imfa nchiyani? (b) Kodi Mlaliki 9:5, 10 amanenanji ponena za mkhalidwe wa akufa?
3 Kunena mosavuta, imfa ndiyo chosemphana ndi moyo. Baibulo limasonyeza chimenechi pa Mlaliki 9:5, 10. Malinga ndi kunena kwa Revised Union Nyanja Version, mavesi amenewa amati: “Pakuti amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bi, sadzalandira mphotho; pakuti angoiwalika. Chirichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingalira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.”
4. (a) Kodi nchiyani chimene chimachitikira mphamvu zoganiza za munthu pa imfa? (b) Kodi nchifukwa ninji mphamvu za munthu zimaleka zonse kugwira ntchito pa imfa?
4 Zimenezi zikutanthauza kuti akufa sangachite chirichonse ndipo sangamve chirichonse. Iwo samakhalanso ndi maganizo alionse, monga momwe Baibulo likufotokozera: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye. Mpweya wake uchoka, abwerera kumka ku nthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.”(Salmo 146:3, 4) Pa imfa mzimu wa munthu, mphamvu yake ya moyo, imene imachirikizidwa ndi kupuma, ‘imatuluka.’ Simakhalakonso. Motero mphamvu za munthu za kumva, kuwona, kukhudza, kununkhiza ndi kulawa, zimene zimadalira pa kukhala kwake wokhoza kuganiza, zonse zimaleka kugwira ntchito. Malinga ndi kunena kwa Baibulo, akufa amalowa mkhalidwe wa kusadziwa kanthu kotheratu.
5. (a) Kodi ndimotani mmene Baibulo limasonyezera kuti mkhalidwe wa anthu akufa ndi nyama zakufa ngwofanana? (b) kodi nchiyani chimene chiri “mzimu” umene umapangitsa anthu ndi nyama zomwe kukhala ndi moyo?
5 Pamene izo ziri zakufa, anthu ndi nyama zomwe amakhala mu mkhalidwe umodzimodziwu wa kusadziwa kanthu kotheratu. Wonani mmene Baibulo likunenera nkhani imeneyi: “Monga winayo angofa momwemo zinazo zifanso; inde onsewo ali ndi mpweya umodzi; ndipo munthu sapambana nyama pakuti zonse ndichabe. Onse apita ku malo amodzi; onse achokera m’fumbi ndi onse abwereranso kufumbi.” (Mlaliki 3:19, 20) “Mpweya” [“mzimu”] umene umapangitsa nyama kukhala ndi moyo ngwofanana ndi uja umene umapangitsa anthu kukhala ndi moyo. Pamene “mzimu” umenewu, kapena mphamvu ya moyo yosawoneka, uchoka, munthu ndi nyama yomwe zimabwerera kufumbi kumene izo zinapangidwa.
MOYO UMAFA
6. Kodi ndimotani mmene Baibulo limasonyezera kuti nyama ndizo miyoyo?
6 Anthu ena anena kuti chimene chimapangitsa munthu kusiyana ndi nyama nchakuti munthu ali ndi moyo koma nyama ziribe. Komabe, Genesis 1:20 ndi 30 amanena kuti Mulungu analenga “zamoyo” kuti zikhale m’madzi, ndi kuti nyama ziri ndi “moyo monga chamoyo.”M’mavesi amenewa Mabaibulo ena amagwiritsira ntchito mawuwo “chamoyo” ndi “moyo” m’malo mwa “moyo” [“soul”], koma mawu awo amtsinde amavomereza kuti liwulo “moyo” [“soul”] ndilo limene limapezeka m’chinenero choyamba. Pakati pa kutchula Kwabaibulo nyama kukhala miyoyo pali Numeri 31:28, NW. Pamenepo limatchula “moyo umodzi mwa mazana asanu, a anthu ndi a ng’ombe ndi a abulu ndi a nkhosa.”
7. Kodi Baibulo limanenanji kutsimikizira kuti miyoyo yanyama ndi miyoyo yaanthu yomwe imafa?
7 Popeza kuti nyama ndizo miyoyo, pamene izo zifa miyoyo yawo imafa. Monga momwe Baibulo limanenera: “Moyo wamoyo uliwonse unafa, inde, zinthu zam’nyanja.” (Chivumbulutso 16:3, NW) Bwanji ponena za miyoyo yaanthu? Monga momwe tinaphunzirira m’mutu wapitawo, Mulungu sanalenge munthu ali ndi moyo. Munthu ndiye moyo. Motero, monga momwe tikayembekezerera, pamene munthu afa, moyo wake umafa. Mobwerezabwereza Baibulo limanena kuti zimenezi nzowona. Baibulo silimanena kuti moyo ngwosafa kapena kuti sungafe. “Iwo onse otsikira kufumbi adzawerama, ndipo palibe aliyense adzasunganso moyo wake wa iye mwini wamoyo,” Salmo 22:29 NW, limatero. “Moyo wochimwawo ndiwo udzafa,” akufotokoza Ezekieli 18:4 ndi 20. Ndipo ngati mupita ku Yoswa 10:28-39, mudzapeza malo asanu ndi awiri amene moyo ukutchulidwa kukhala ukuphedwa kapena kuwonongedwa.
8. Kodi tikudziwa motani kuti moyo waumunthu, Yesu Kristu, unafa?
8 Mu ulosi wonena za Yesu Kristu, Baibulo limati: “Anathira moyo wakufa kuimfa . . . ananyamula machimo a ambiri.” (Yesaya 53:12) Chiphunzitso cha dipo chimatsimikizira kuti unali moyo (Adamu) umene unachimwa, ndi kuti kuti awombole anthu panafunikira kukhala moyo (munthu) wolingana woperekedwa nsembe. Kristu, mwa ‘kuthira moyo wake kuimfa,’ anapereka mtengo wadipo. Yesu, moyo waumunthu, anafa.
9. Kodi nchiyani chimene chikutanthauzidwa ndi mawuwo, ‘mzimu weniweniwo umabwerera kwa Mulungu amene anaupereka’?
9 Monga momwe tawonera, “ mzimu” ndikanthu kena kosiyana ndi moyo wathu. Mzimu ndiwo mphamvu yathu yamoyo. Mphamvu yamoyo imeneyi ili mu lirilonse la maselo athupi la anthu ndi nyama zomwe. Umachirikizidwa, kapena kukhalitsidwa wamoyo, mwa kupuma. Pamenepa, kodi zikutanthauzanji, pamene Baibulo limanena kuti pa imfa “fumbi ndi kubwerera pansi. . . mzimu ndi kubwerera kwa Mulungu amene anaupereka”? (Mlaliki 12:7) Pa imfa mphamvu yamoyo m’kupita kwa nthawi imachoka m’maselo onse athupi ndipo thupi limayamba kuwola. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti mphamvu yathu yamoyo imachokadi padziko lapansi ndipo imayenda kudutsa m’mlengalenga kumka kwa Mulungu. M’malo mwake, mzimu umabwerera kwa Mulungu m’lingaliro lakuti tsopano chiyembekezo chathu cha moyo wamtsogolo chimakhala kotheratu ndi Mulungu. Kokha mwa mphamvu yake mzimuwo, kapena mphamvu yamoyo, ungabwezeretsedwe kuti tikhalenso ndi moyo.—Salmo 104:29, 30.
LAZALO—MUNTHU WAKUFA KWA MASIKU ANAI
10. Ngakhale kuli kwakuti Lazalo adamwalira, kodi Yesu ananenanji ponena za mkhalidwe wake?
10 Zimene zinachitikira Lazalo, amene anali wakufa kwa masiku anai, zingatithandize kuzindikira mkhalidwe wa akufa. Yesu anali atauza ophunzira ake kuti: “Lazaro bwenzi lathu ali m’tulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo take.” Komabe, ophunzirawo anayankha kuti: “Ambuye, ngati ali m’tulo adzachira.” Atatero, Yesu anawauza mwachimvekere: “Lazalo wamwalira.” Kodi nchifukwa ninji Yesu anati Lazalo analinkugona pamene iye kwenikweni adafa? Tiyeni tiwone.
11. Kodi Yesu anachitiranji Lazalo wakufayo?
11 Pamene Yesu anayandikira mudzi umene Lazalo analinkukhala, iye anachingamiridwa ndi Malita, mlongo wa Lazalo. Posapita nthawi iwo, limodzi ndi ena ambiri, anapita kumanda kumene Lazalo adaikidwa. Anali phanga, ndipo mwala unatsekapo. Yesu anati: “Chotsani mwala.” Popeza kuti Lazalo anali wakufa kwa masiku anai, Malita anatsutsa: “Ambuye, adayamba kununkha.” Koma mwalawo unachotsedwa, ndipo Yesu anapfuula: “Lazalo, tuluka!” Ndipo iye anatulukadi! Anatuluka wamoyo, wokutidwabe mu nsali zakumanda. “M’masuleni iye, ndipo mlekeni amuke,” Yesu anatero.—Yohane 11:11-44.
12, 13. (a) Kodi nchifukwa ninji tingatsimikizirire kuti Lazalo anali wosadziwa kanthu pamene anali wakufa? (b) Kodi nchifukwa ninji Yesu ananena kuti Lazalo anali m’tulo pamene, kwenikweni, iye anali wakufa?
12 Tsopano taganizirani izi: Kodi mkhalidwe wa Lazalo unalo wotani mkati mwa masiku anai amenewo amene iye anali wakufa? Kodi iye adali kumwamba? Iye anali munthu wabwino. Komabe Lazalo sadanene chirichonse ponena za kukhala kumwamba, zimenedi akananena ngati chirichonse ponena za kukhala kumwamba, zimenedi akananena ngati akadakhala analiko. Ayi, Lazalo analidi wakufa, monga momwedi Yesu ananenera kuti anali. Pamenepa kodi nchifukwa ninji Yesu poyamba anauza ophunzira ake kuti Lazalo analinkugona chabe?
13 Eya, Yesu anadziwa kuti Lazalo wakufayo anali wosadziwa kanthu, monga momwe Baibulo limanenera: “Akufa sadziwa kanthu bi.” (Mlaliki 9:5) Koma munthu wamoyo angathe kudzutsidwa ku tulo tatikulu. Motero Yesu anali kukasonyeza kuti, mwa njira ya mphamvu ya Mulungu yoperekedwa kwa iye, bwenzi lake Lazalo akatha kuukitsidwa kuimfa.
14. Kudziwa mphamvu ya Kristu ya kuukitsa akufa kuyenera kutisonkhezera kuchita chiyani?
14 Pamene munthu ali m’tulo tatikulu kwambiri, samakumbukira kanthu. Nkofanana ndi akufa. Iwo samakhala ndi malingaliro konse. Iwo samakhalakonso. Koma, m’nthawi yokwanira ya Mulungu, akufa amene anawomboledwa ndi Mulungu adzaukitsidwa. (Yohane 5:28) Ndithudi chidziwitso chimenechi chiyenera kutisonkhezera kufuna kupeza chiyanjo cha Mulungu. Ngati titero, ngakhale ngati tingamwalire, tidzakumbukiridwa ndi Mulungu ndi kubwezeretsedwa ku moyo.—1 Atesalonika 4:13, 14.
[Chithunzi patsamba 76]
ADAMU—anapangidwa kuchokera kufumbi . . . anabwerera kufumbi
[Chithunzi patsamba 78]
Kodi mkhalidwe wa Lazalo unali wotani Yesu asanamuukitse?