Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • te mutu 16 tsamba 67-70
  • Munthu Amene Anali Wakufa Masiku Anai

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Munthu Amene Anali Wakufa Masiku Anai
  • Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Chimachitika ndi Chiyani Tikamwalira?
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Yesu Anaukitsa Lazaro
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Kodi N’chifukwa Chiyani Yesu Sanapite Mofulumira?
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Kodi Chimachitika Nchiyani pa Imfa?
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
Onani Zambiri
Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
te mutu 16 tsamba 67-70

Mutu 16

Munthu Amene Anali Wakufa Masiku Anai

KODI sikuli kodabwitsa kukhala wamoyo? Kodi inuyo mumasangalala ndi moyo?—Ine ndimasangalala ndi kukhala ndi moyo. Pamene ife tiri amoyo ife tingathe kuchita zinthu zambirimbiri zokondweretsa.

Koma kodi inu munadziwa kuti palibe munthu ali yense amene wakhala ndi moyo kosatha?—Pa masiku ena osiyanasiyana anthu onse amafa. Kodi inu mukudziwa ponena za munthu wina amene wafa?—

Pa nthawi ina bwenzi labwino la Yesu linamwalira. Bwenzi limeneli linalinkukhala m’Betaniya, tauni yaing’ono yosatalikirana ndi Yerusalemu. Dzina lache linali Lazaro, ndipo iye anali ndi alongo awiri, ochedwa Marita ndi Mariya.

Tsiku lina Lazaro anadwala kwambiri. Yesu anali kutali kwambiri pa nthawiyo. Chotero Marita ndi Mariya anatumiza mau kwa iye kuti mlongo wao Lazaro anali kudwala. Kodi nchifukwa ninji iwo anachita chimenechi? Chifukwa chakuti iwo anadziwa kuti Yesu akadatha kumchiritsa mlongo wao. Yesu sanali dotolo, koma iye anali ndi mphamvu yochokera kwa Mulungu kotero kuti iye akadatha kuchiritsa mtundu uli wonse wa matenda.

Koma Yesu asanadze, Lazaro anadwala kwambiri chakuti iye anamwalira. Yesu anawauza ophunzira ache kuti Lazaro anali kugona. Koma Yesu ananena kuti iye adzapita kukamdzutsa iye. Ophunzirawo sanachizindikire chimene Yesu anachitanthauza. Chotero, pamenepo Yesu ananena momvekera bwino kuti Lazaro adamwalira. Imfa iri ngati tulo tatikulu, tulo timene tiri tatikuru kwambiri chakuti munthuyo samalota nkulota komwe.

Yesu tsopano anapita kukamzonda Marita ndi Mariya. Kunalinso mabwenzi ambiri a banjalo kumeneko. Iwo anadza kumtonthoza Marita ndi Mariya chifukwa chakuti mlongo wao Lazaro adamwalira.

Pamene Marita anamva kuti Yesu analinkudza, iye anaturuka kumchingamira iye. Posakhalitsa Mariya nayenso anaturuka kumuona Yesu. Iye anali wachisoni kwambiri ndipo anali kumalira, ndipo iye anagwa pa mapazi ache. Mabwenzi ena, amene anamtsatira Mariya, analinso kumalira. Pamene Yesu anawaona anthu onsewo akulira iye anakhala wahcisoni nayamba kuliranso.

Mphunzitsi Wamkuruyo anafunsa kumene iwo anamuika Lazaro. Atatero anthuwo anamtsogolera Yesu ku phanga kumene Lazaro anaikidwako. Pamenepo Yesu anawauza amunawo pomwepo kuti: ‘Gubuduzani mwalawo ku khomo kwa ‘phangalo.’ Kodi iwo anayenera kuchichita icho?—

Marita sanaganizire kuti icho chinali choyenera. Iye anati: ‘Ambuye, pofikira tsopano iye ayenera kununkha, pakuti iye wakhala wakufa masiku anai.’ Ndipo nzoona kuti mitembo imanunkha kwambiri patapita kanthawi.

Koma Yesu anati kwa iye: “Kodi sindinakuuze iwe kuti ngati iwe ukakhulupilira iwe ukaona ulemelero wa Mulungu?” Yesu anatanthauza kuti Marita akaona kanthu kena kamene kakapereka ulemu kwa Mulungu. Kodi nchiani chimene Yesu anali kukachichita?

Pamene mwalawo unachotsedwa, Yesu anapemphera mopfuula kwa Yehova. Pamenepo Yesu m’mau opfuula anati: “Lazaro, turuka!” Kodi iye akaturuka? Kodi iye akadatha?—

Eya, kodi inu mungathe kumdzutsa munthu wina amene ali kugona?—Inde, ngati inu muitana mopfula, iye adzagalamuka. Koma kodi inu mungathe kumdzutsa munthu wina amene ali kugona mu imfa?—Ai. Mosasamala kanthu za mmene inuyo mungaitanire mopfuula, uyo amene wafayo sadzamva. Palibe chinthu chiri chonse chimene inu kapena ine tingathe kuchita kumdzutsa wakufa.

Koma Yesu ali wosiyana. Iye ali ndi mphamvu yapadera yochokera kwa Mulungu. Chotero, pamene Yesu anamuitana Lazaro, chinthu chodabwitsa chinachitika. Munthu amene anali wakufa kwa masiku anai anaturuka m’phangamo! Iye anali atabwerezetsedwa ku moyo! Iye anakatha kupuma ndi kuyenda ndi kulankhula kachiwiri! Inde, Yesu anamuukitsa Lazaro iye atakhala wakufa masiku anai! Kodi chimenecho sichinali chodabwitsa?— —Yoh. 11:1-44, NW.

Koma inu mungafunse kuti, Kodi Lazaro anali kuti mkati mwa masiku anai amene iye anali wakufa? Kodi Lazaro anapita kumwamba pamene iye anafa? Kodi iye anali wamoyo kumwambako limodzi ndi Mulungu ndi angelo oyera?—

Ganizirani tsopano: Ngati Lazaro akadakhala kumwamba mkati mwa masiku anai amenewo, kodi iye sakadanena kanthu kena ponena za icho?—Ndipo ngati iye anali kumwamba, kodi Yesu akanamchititsa iye kubwera kuchokera ku malo odabwitsa amenewo?—Baibulo silimanena kuti Lazaro anali kumwamba.

Kumbukirani kuti, Yesu ananena kuti Lazaro anali kugona. Kodi kuli ngati chiani pamene inu muli m’tulo?—

Pamene inu muli m’tulo tatikulu kwambiri, inu simumadziwa chimene chirinkumachitika kunja, kodi mumadziwa?—Ndipo pamene inuyo mugalamuka inu simumadziwa utali umene inuyo mwakhala mukugona kufikira inu mutayang’ana pa koloko.

Kuli chomwecho ndi anthu akufa. Iwo samadziwa kanthu kali konse kamene kali kumachitika. Iwo samamva kanthu kali konse. Ndipo iwo sangathe kuchita kanthu kali konse.

Koma anthu ena amaopa akufa. Iwo sadzapita pafupi ndi manda, chifukwa chakuti iwo amanganizira kuti akufawo angawabvulaze iwo. Kodi mungathe kuchiyerekezera chimenecho? Kodi munthu wakufa angathe kumbvulaza munthu wina amene ali wamoyo?—Ai, Baibulo limanena kuti akufa ali osakhoza konse kuchita kanthu kali konse.

Kodi inu munayamba mwamumva munthu wina ali yense akunena kuti pa tsiku lina akufa anabwera monga mizimu kudzawachezera amoyo?—Anthu ena amakhulupilira chimenecho. Chotero iwo amakonza chakudya kaamba ka akufa. Kapena iwo angakhale ndi mapwando apadera pa masiku amenewo. Koma kodi inu mumaganiza kuti anthu amene amazichita zinthu zimenezowo amachikhulupiliradi chimene Mulungu amachinena ponena za akufa?—

Kodi inu mumachikhulupilira chimene Mulungu amanena?—Ngati ife timatero, ife sitidzakhala owaopa akufa, koma ife tidzakhala okondwa kuti ife tiri amoyo. Ndipo ngati ife tiridi othokoza kwa Mulungu kaamba ka moyo, tidzakusonyeza iko mwa njira imene ife tikukhalira ndi miyoyo yathu tsiku liri lonse. Ife tidzazichitia zinthu zimene Mulungu amazibvomereza.

(Kugogomezera chiyamikiro kaamba ka moyo wa tsiku ndi tsiku, poyerekezera ndi mkhalidwe wa akufa, werengani Mlaliki 9:5, 10, Ezekieli 18:4 ndi Salmo 115:17 [113:26, MO].)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena