Tsiku la Kubadwa
Tanthauzo: Tsiku la kubadwa kwa munthu kapena kufika kwa tsikulo chaka ndi chaka. Mmalo ena kufika kwa tsiku lakubadwa kwa munthu chaka chirichonse, makamaka la mwana, kumakumbukiridwa ndi phwando ndi kuperekedwa kwa mphatso. Sichiri chizoloŵezi Chabaibulo.
Kodi maumboni a Baibulo a mapwando a tsiku la kubadwa amawachititsa kukhala mumkhalidwe wovomerezeka? Baibulo limangotchula maumboni aŵiri okha a mapwando otero:
Gen. 40:20-22: “Ndipo panali tsiku lachitatu ndiro tsiku la kubadwa kwake kwa Farao, iye anakonzera anyamata ake madyerero . . . Ndipo anabwezanso wopereka chikho kuntchito yake . . . Koma anampachika wophika mkate wamkulu.”
Mat. 14:6-10: “Pakufika tsiku lakubadwa kwake kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodiya anavina pakati pawo, namkondweretsa Herode. Pomwepo iye anamlonjeza chilumbirire, kumpatsa iye chimene chirichonse akapempha. Ndipo iye, atampangira amake, nati, Ndipatseni inu kuno m’mbizi mutu wa Yohane M’batizi, . . . Anatumiza mnyamata, namdula mutu Yohane m’nyumba yandende.”
Chirichonse chimene chiri m’Baibulo chiri ndi chifukwa chake. (2 Tim. 3:16, 17) Mboni za Yehova zimazindikira kuti Mawu a Mulungu amanena mosavomereza mapwando a masiku a kubadwa ndipo chotero sizimawachita.
Kodi ndimotani mmene Akristu oyambirira ndi Ayuda a m’nthaŵi za Baibulo anawonera mapwando a masiku akubadwa?
“Lingaliro laphwando la tsiku lakubadwa linali kutali ndi malingaliro a Akristu onse a m’nyengo iyi.”—The History of the Christian Religion and Church, During the Three First Centuries (New York, 1848), Augustus Neander (lotembenuzidwa ndi Henry John Rose), p. 190.
“Ahebri apambuyo pake anawona kuchita phwando la masiku akubadwa kukhala mbali ya kulambira mafano, lingaliro limene likatsimikiziridwa kwambiri ndi zimene anawona m’mapwando wamba ogwirizanitsidwa ndi masiku amenewa.”—The Imperial Bible-Dictionary (London, 1874), lolembedwa ndi Patrick Fairbairn, Vol. I, p. 225.
Kodi nchiyani chimene chiri magwero a miyambo yofala yogwirizanitsidwa ndi mapwando a masiku akubadwa?
“Miyambo yosiyanasiyana imene anthu lerolino amachita pamasiku awo a kubadwa iri ndi mbiri yaitali. Magwero ake ndiwo matsenga ndi chipembedzo. Zizoloŵezi zakupereka mafuno abwino, kupereka mphatso ndi kuchita phwando—zonsezo limodzi ndi makandulo oyatsidwa—m’nthaŵi zakale zinali kuchitidwira kutetezera wochitiridwa phwando la kubadwayo ku ziŵanda ndi kutsimikizira chitetezero chake mkati mwa chaka chirinkudza. . . . Kufikira m’zaka za zana lachinayi Chikristu chinakana kuchita phwando la tsiku lakubadwa chifukwa cha kukhala mwambo wachikunja.—Schwäbische Zeitung (mphatika ya magazine a Zeit und Welt), April 3/4, 1981, p. 4.
“Agiriki anakhulupirira kuti aliyense anali ndi mzimu wachitetezo kapena daemon umene unasamalira kubadwa kwake ndi kumchinjiriza m’moyo. Mzimu umenewu unali ndi unansi wachinsinsi ndi mulungu amene anali ndi tsiku lakubadwa pa limene munthuyo anabadwira. Aroma anachirikizanso lingaliro limeneli. . . . Lingaliro limeneli linapitirizidwa m’zikhulupiriro za anthu ndipo limasonyezedwa mwa mngelo nkhosweyo, mulungu amayi wa choikidwiratuyo ndi mtetezi woyera mtima. . . . Chizoloŵezi cha kuyatsa makandulo kuunikira makeke chinayamba ndi Agiriki. . . . Makeke a uchi obulungira ngati mwezi ndipo ounikiridwa ndi makandulo anaikidwa pamaguwa ansembe a kachisi wa [Artemi]. . . . M’chipembedzo cha makolo, makandulo a tsiku lakubadwa, amanenedwa kukhala ndi matsenga apadera opereka mafuno abwino. . . . Makandulo oyatsidwa ndi moto wootchera nsembe zokhala ndi tanthauzo lapadera lachinsinsi kuyambira pamene munthu kwa nthaŵi yoyamba anamanga guwa lansembe kwa milingu yake. Motero makandulo a tsiku lakubadwa ndiwo ulemu ndi kulemekeza mwana wokhala ndi tsiku lakubadwa ndi kumfunira mafuno abwino. . . . Malonje ndi mafuno achimwemwe a tsiku lakubadwa ndiwo mbali yofunika ya holide imeneyi. . . . Poyambirira lingalirolo linali logwirizanitsidwa ndi matsenga. . . . Malonje a tsiku lakubadwa ali ndi mphamvu ya chabwino kapena choipa chifukwa chakuti munthuyo ngwoyandikana kwambiri ndi dziko lamizimu patsiku iri.”—The Lore of Birthdays (New York, 1952), Ralph ndi Adelin Linton, pp. 8, 18-20.
Masonkhano abwino abanja ndi mabwenzi a kudya, kumwa, ndi kukondwera panthaŵi zina ngoyenerera
Mlal. 3:12, 13: “Iwo alibe ubwino, koma kukondwa ndi kuchita zabwino pokhala ndi moyo. Ndiponso kuti munthu yense adye namwe nawone zabwino m’ntchito zake zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.”
Wonaninso 1 Akorinto 10:31.