Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 9/1 tsamba 30-31
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Nkhani Yofanana
  • N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Sakondwerera Masiku Akubadwa?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
  • Tsiku la Kubadwa
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Kodi Ndi Mapwando Onse Amene Amakondweretsa Mulungu?
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 9/1 tsamba 30-31

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi Mboni za Yehova zimapeŵa kusunga masiku akubadwa chifukwa chakuti mchitidwewo unali ndi tanthauzo lachipembedzo munthaŵi zakale?

Kusunga masiku akubadwa kuli ndi chiyambi chake m’kukhulupirira malaulo ndi chipembedzo chonyenga, koma chimenecho sichiri chifukwa chokha kapena chifukwa chachikulu chimene Mboni za Yehova zimapeŵera mchitidwewo.

Miyambo ina imene panthaŵi ina inali mumpangidwe wachipembedzo sirinso yotero m’malo ambiri. Mwachitsanzo, mphete yaukwati panthaŵi ina inali ndi tanthauzo lachipembedzo, koma lerolino m’malo ambiri, sirinso yotero. Chifukwa cha chimenecho, Akristu owona ambiri amavomereza mwambo wa kumaloko wa kuvala mphete yaukwati kupereka umboni wakuti munthuyo ngwamuukwati. M’nkhani zotero, chimene kaŵirikaŵiri chiri kanthu kwenikweni ndicho chakuti kaya mchitidwewo tsopano ngwogwirizanitsidwa ndi chipembedzo chonyenga kapena ayi.​—Wonani “Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga” mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 1972 (m’Chingelezi), ndi October 15, 1991.

Komabe, sitingalandule, kuti mabukhu ambiri a maumboni amavumbula mbiri ya kukhulupirira malaulo ndi yachipembedzo ya kusungidwa kwa masiku akubadwa. The Encyclopedia Americana (lotulutsidwa mu 1991) limati: “Dziko lakale la Igupto, Girisi, Roma, ndi Perisiya linasunga masiku akubadwa kwa milungu, mafumu, ndi anthu omveka.” Limanena kuti Aroma anasunga tsiku la kubadwa kwa Atemi ndi tsiku la Apolo. Mosiyana, “ngakhale kuli kwakuti Aisrayeli akale anasunga zolembapo za misinkhu ya nzika zawo zachimuna, palibe umboni wakuti anachita mapwando a chaka ndi chaka a kukumbukira deti la kubadwa.”

Mabukhu ena amaumboni amafotokoza mwatsatanetsatane ponena za chiyambi cha zikondwerero za tsiku la kubadwa: ‘Mapwando a tsiku la kubadwa anayamba zaka zambiri zapitazo mu Ulaya. Anthu anakhulupirira mizimu yabwino ndi yoipa, panthaŵi zina yotchedwa abathwa abwino ndi oipa. Munthu aliyense anali kuwopa mizimu imeneyi, kuti ikavulaza wochita phwando patsiku la kubadwa, ndipo motero anazingidwa ndi mabwenzi ndi achibale amene mafuno awo abwino, ndi kukhalapo kwawo kwenikweniko, kukamtetezera kuupandu wosadziŵika umene tsiku la kubadwalo linali nawo. Kupereka mphatso kunabweretsadi chitetezero chokulira. Kudyera pamodzi kunagaŵira chitetezero chowonjezereka ndi kuthandizira kudzetsa madalitso a mizimu yabwino. Chotero phwando la tsiku la kubadwa poyambirira linalinganizidwira kupangitsa munthuyo kukhala wotetezereka kuupandu ndi kumtsimikiziritsa chaka china chabwino chirinkudza.’​—Birthday Parties Around the World, 1967.

Bukhulo limafotokozanso chiyambi cha miyambo yambiri ya tsiku la kubadwa. Mwachitsanzo: “Chifukwa [cha kugwiritsira ntchito makandulo] chinayambira kwa Agiriki ndi Aroma oyambirira amene analingalira kuti makandulo anali ndi mikhalidwe ina ya matsenga. Anali kupereka mapemphero ndi kupanga mafuno oti amke kwa milungu ndi malaŵi a makandulo. Pamenepo milunguyo ikawatsanulira madalitso ndipo mwinamwake kuyankha mapempherowo.” Mawu ena a chidziŵitso chotero akupezeka patsamba 362 ndi 363 la Kukambitsirana za m’Malemba, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

Komabe, monga momwe kwatchulidwira, zambiri zikuphatikizidwa m’funso limeneli koposa ndi kuti kaya kukondwerera masiku a kubadwa kunali kapena kudakali kwachipembedzo. Baibulo limafotokoza za masiku a kubadwa, ndipo Akristu okula msinkhu mwanzeru angafune kulabadira zisonyezero zimene limapereka.

Atumiki a Mulungu akale ankasunga cholembapo pamene munthu wina anabadwa, zimene zinawatheketsa kuŵerengera zaka za kubadwa. Timaŵerenga kuti: “Nowa anali wa zaka mazana asanu; ndipo Nowa anabala Semu ndi Hamu ndi Yafeti.” “Chaka cha mazana asanu ndi limodzi cha moyo wa Nowa, . . . akasupe onse a madzi aakulu anasefuka.”​—Genesis 5:32; 7:11; 11:10-26.

Monga momwedi Yesu ananenera, pakati pa anthu a Yehova kubadwa kwa mwana kunali chochitika chokondweretsa, chodalitsika. (Luka 1:57, 58; 2:9-14; Yohane 16:21) Komabe, anthu a Yehova sanasunge deti la kubadwa; iwo anasunga zikumbukiro zina koma osati masiku a kubadwa. (Yohane 10:22, 23) Encyclopaedia Judaica imati: “Chikondwerero cha masiku a kubadwa nchosadziŵika m’dzoma la mwambo Wachiyuda.” Customs and Traditions of Israel imati: “Chikondwerero cha masiku a kubadwa chabwerekedwa kumachitachita a mitundu ina, popeza kuti palibe kutchulidwa kulikonse kwa mwambo umenewu kumene kukupangidwa pakati pa Ayuda kaya m’Baibulo, mu Talmud, kapena m’malembo a Anzeru apambuyo pake. Kweniweni, unali mwambo wakale wa ku Igupto.”

Kuphatikizidwa kwa Aigupto nkowonekera bwino ndi kusunga tsiku la kubadwa kosimbidwa m’Baibulo, limene olambira owona sanali kusunga. Linali phwando la tsiku la kubadwa kwa Farao amene anali kulamulira pamene Yosefe anali m’ndende ya ku Igupto. Ena a achikunja amenewo angakhale anali kukondwerera phwandolo, komabe tsiku la kubadwalo linagwirizanitsidwa ndi kudulidwa mutu wa mkulu wa ophika mikate wa Farao.​—Genesis 40:1-22.

Lingaliro lina loipa likuperekedwa patsiku lina la chikondwerero lofotokozedwa m’Malemba​—lija la Herode Antipa, mwana wa Herode Wamkulu. Chikondwerero cha tsiku la kubadwa limeneli sichimasonyezedwadi m’Baibulo kukhala phwando chabe. Mmalomwake, chinachititsa kudulidwa mutu kwa Yohane Mbatizi. Pamenepo, “ophunzira ake anadza, natola mtembo, nauika; ndipo anadza nauza Yesu,” amene ‘anachoka kumeneko kumka kumalo achipululu a yekha.’ (Mateyu 14:6-13) Kodi mungayerekezere kuti ophunzira amenewo kapena Yesu akakopeka ndi chizolowezi cha kuchita mapwando a tsiku la kubadwa?

Polingalira chiyambi chodziŵika cha chikondwerero cha masiku a kubadwa, ndipo chofunika koposa, mbiri yake yoipa imene Baibulo limaperekera, Mboni za Yehova ziri ndi chifukwa choyenera chosasungira mchitidwewo. Safunikira kutsatira mwambo waudziko umenewu, pakuti angathe ndipo amakhala ndi mapwando panthaŵi iriyonse mkati mwa chaka. Kupereka mphatso kwawo sikuli koumiriza kapena kokakamizidwa ndi kusonkhana kocheza; iwo amagaŵana modzifunira mphatsozo panthaŵi iriyonse chifukwa cha kuwoloŵa manja ndi chikondi chenicheni.​—Miyambo 17:8; Mlaliki 2:24; Luka 6:38; Machitidwe 9:36, 39; 1 Akorinto 16:2, 3.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena