Zoloŵa M’malo mwa Kuthiriridwa Mwazi Zabwino
Mungalingalire kuti, ‘kuthiriridwa mwazi nkwaupandu, koma kodi pali zoloŵa m’malo zirizonse zabwino kwambiri?’ Funso labwino, wonani liwulo “zabwino.”
Aliyense, kuphatikizapo Mboni za Yehova, amafuna chisamaliro chamankhwala champhamvu chabwino kwambiri. Dr. Grant E. Steffen anasonyeza zinthu ziŵiri zazikulu: “Chisamaliro chabwino chamankhwala ndicho ukulu wa mbali za chisamaliro chimenecho cha kupeza zonulirapo zololeka zamankhwala ndi zosakhala zamankhwala.” (The Journal of the American Medical Association, July 1, 1988) “Zonulirapo zosakhala zamankhwala” zikaphatikizapo kusaswa makhalidwe abwino kapena chikumbumtima chozikidwa pa Baibulo cha wodwala.—Machitidwe 15:28, 29.
Kodi pali njira zoyenera ndi zamphamvu zochitira ndi mavuto aakulu azamankhwala popanda kugwiritsira ntchito mwazi? Mokondweretsa, yankho ndilo inde.
Ngakhale kuti madokotala a opaleshoni ochuluka anena kuti anapereka mwazi kokha pamene kunali kofunika kotheratu, mliri wa AIDS utabuka kugwiritsira ntchito kwawo mwazi kunatsika mofulumira. Mawu a mkonzi wina m’Mayo Clinic Proceedings (September 1988) ananena kuti “limodzi la mapindu oŵerengeka a mliriwo” linali lakuti iro “unachititsa njira zosiyanasiyana kwa odwala ndi madokotala kupeŵa kuthiriridwa mwazi.” Mkulu wina wa nkhokwe ya mwazi akufotokoza kuti: “Chimene chasintha ndicho ukulu wa uthengawo, kulabadira kwa azipatala kuuthengawo (chifukwa cha kuzindikiridwa kwa zoloŵa m’malo.”—Transfusion Medicine Reviews, October 1989.
Wonani kuti, pali zoloŵa m’malo! Zimenezi zimakhala zomveka pamene tipenda chifukwa chake mwazi umathiriridwa.
Hemoglobin yokhala m’maselo ofiira imaloŵetsa okosijeni yofunika kaamba ka thanzi labwino ndi moyo. Chotero ngati munthu wataya mwazi wambiri, kungawonekere kukhala koyenelera kungoubwezeretsa. Mozoloŵereka inu muli ndi pafupifupi magramu 14 kapena 15 a hemoglobin m’masentimitala 100 alionse a mwazi. (Mpimo wina wa kuchuluka ndiwo hematocrit, imene mofala iri pafupifupi 45 peresenti.) “Njira” yovumerezedwa inali kuthirira mwazi wodwala opaleshoni isanachitike ngati hemoglobin yake inali pansi pa 10 (kapena 30 peresenti ya hematocrit). Magazini Yachiswiss Vox Sanguinis (March 1987) inasimba kuti “65% ya [akatswiri ochititsa dzanzi] inafunikiritsa odwala kukhala ndi hemoglobin opaleshoni isanachitidwe ya 10 gm/dl kaamba ka kuchita opaleshoni yosankhidwa.”
Koma pamsonkhano wa 1988 wonena za kuthirira mwazi, Pulofesala Howard L. Zauder anafunsa kuti: “Kodi Tinapeza Motani ‘Nambala Yapaderayi’?” Iye anafotokoza momvekera bwino kuti: “Chochititsa cha chofuna chakuti wodwala akhale ndi magramu 10 hemoglobin (Hgb) choyambilira asanachititsidwe dzanzi ndicho chozikidwa m’miyambo, chokutidwa mumdima, chosatsimikiziridwa kwambiri ndi azipatala kapena umboni wa kupenda.” Tangoyerekezerani zikwi zambiri za odwala zimene kuthiriridwa mwazi kwawo kunayambitsidwa ndi chofuna ‘chosadziŵika bwino, chosatsimikizirika kwambiri!’
Ena angadabwe kuti, ‘Kodi nchifukwa ninji mlingo wa hemoglobin wa 14 uli woyenera ngati ungakhalebe ndi moyo ndi wotsikirapo?’ Eya, inu motero muli ndi mphamvu yokhoza kuloŵetsa okosijeni yochuluka kwambiri kotero kuti muli wokonzekera kugwiritsira ntchito thupi kapena ntchito yamphamvu. Mapendedwe onena za odwala a kuchepekeredwa ndi mwazi amavumbuladi kuti “nkovuta kudziŵa kupereŵera muukulu wa ntchito ndi hemoglobin yotsikira kufika pa 7 g/dl. Ena apeza umboni wa kugwira ntchito kufooketsedwa mwapang’ono chabe.”—Contemporary Transfusion Practice, 1987.
Pamene kuli kwakuti achikulire amakhoza kusunga mlingo wotsika wa hemoglobin, bwanji ponena za ana? Dr. James A. Stockman III akuti: “Kupatulapo oŵerengeka, makanda obadwa osakwana miyezi adzakhala ndi kutsika kwa hemoglobin m’mwezi umodzi kufikira itatu . . . Zizindikiro za kuthiriridwa mwazi m’malo olelerawo sizimafotokozedwa bwino lomwe. Ndithudi, makanda ambiri amawonekera kukhala akulolera kutsika kwakukulu kwa kuchuluka kwa heboglobin popanda mavuto owoneka a zachipatalawo.”—Pediatric Clinics of North America, February 1986.
Mawu oterowo samatanthauza kuti palibe chirichonse chimene chifunikira kuchitidwa pamene munthu ataya mwazi wochuluka pangozi kapena mkati mwa opaleshoni. Ngati kutayikako kuli kofulumira ndi kwakukulu, mphamvu yopopa mwazi ya munthu imatsika, ndipo iye angalephethuke. Kwakukulukulu chimene chikufunika nchakuti kukha mwaziko kuimitsidwe ndipo mlingowo m’thupi mwake ubwezeretsedwe. Kumeneko kudzaletsa kulephethuka ndi kuchititsabe maselo ofiira otsala ndi zinthu zina zikuzungulira.
Kubwezeretsa kuchuluka kwa mwazi kungachitidwe popanda kugwiritsira ntchito mwazi wathunthu kapena madzi a m’mwazi.a Madzi osiyanasiyana osakhala mwazi ngowonjezeretsa kuchuluka kwa mwazi. Osavuta kwambiri ndiwo madzi a saline (amchere), umene uli ponse paŵiri wosadula ndi wogwirizana ndi mwazi wathu. Palinso madzi okhala ndi zinthu zapadera, monga ngati dextran, Haemaccel, ndi madzi a Ringer. Hetastarch (HES) ndiwo chowonjezeretsa mwazi chatsopanopo, ndipo “angavomerezedwe bwino lomwe kwa odwala [akupsa] ndi moto awo amene amakana zinthu za mwazi.” (Journal of Burn Care & Rehabilitation, January/February 1989) Madzi oterowo ali ndi mapindu enieni. “Madzi otchedwa crystaloid [monga ngati saline ndi madzi a Ringer enieni], Dextran ndi HES ali kwenikweni opanda poizoni ndi osadula, opezeka mosavuta, angasungidwe m’tempirichala ya m’nyumba, safunikira kupenda kogwirizanitsa ndipo alibe upandu wa nthenda zopatsana mwa kuthiriridwa mwazi.”—Blood Transfusion Therapy—A Physician’s Handbook, 1989.
Komabe, inu mungafunse kuti, ‘Kodi nchifukwa ninji zoloŵa m’malo zamadzi zosakhala mwazi zimagwira ntchito bwino, popeza kuti ndifunikira maselo ofiira kuti aloŵetse okosijeni m’thupi langa lonse?’ Monga momwe kwatchulidwira, muli ndi zonyamula okosijeni zotsala. Ngati mutaya mwazi, mchitidwe wodabwitsa wobwezeretsa umayambika. Mtima wanu umapopa mwazi wowonjezereka limodzi ndi kugunda kulikonse. Popeza kuti mwazi wotayikawo unaloŵedwa m’malo ndi madzi oyenerera, mwazi wosungunulidwa tsopanowo umayenda mosavuta kwambiri, ngakhale m’mitsempha yaing’ono. Chifukwa cha kusintha kwa zinthu, okosijeni wowonjezereka imatulutsidwira kutiminyeŵa. Masinthidwe ameneŵa ngamphamvu kwambiri kwakuti ngati theka lokha la maselo anu ofiira litsala, kuperekedwa kwa okosijeni kungakhale pafupifupi 75 peresenti kwa nthaŵi zonse. Wodwala wogona amagwiritsira ntchito 25 peresenti yokha ya okosijeni yopezeka m’mwazi wake. Ndipo mankhwala ochititsa dzanzi ochuluka amachepetsa kufunikira kwa thupi okosijeni.
KODI MADOKOTALA ANGATHANDIZE MOTANi?
Madokotala aluso angathandize munthu amene wataya mwazi ndipo chotero ali ndi maselo ofiira ocheperapo. Pamene kuchuluka kwa mwazi kwabwezeretsedwa, madokotala angapereke okosijeni wochuluka. Kumeneku kumapangitsa wambiri kupezeka kaamba ka thupi ndipo Madokotala Achibririshi anagwiritsira ntchito zimenezi pamkazi wina amene adataya mwazi wochuluka kwakuti “haemoglobin yake inatsikira mpaka pa 1.8 g/dlitre. Iye anachiritsidwa bwino lomwe . . . [limodzi ndi] kuikidwa paokosijeni wambiri ndi kuthiriridwa madzi ochuluka a gelatin [Haemaccel].” (Anaesthesia, January 1987) Lipotilo limanenanso kuti anthu ena okhala ndi kutayika kwakukulu kwa mwazi achiritsidwa bwino lomwe m’malo oloŵetsera okosijeni.
Madokotala angathandizenso odwala awo kuumba maselo ofiira owonjezereka. Motani? Mwakuwapatsa zinthu zokhala ndi iron (m’minyeŵa kapena mitsempha), zimene zingathandizire thupi kupanga maselo ofiira mofulumira kuŵirikiza nthaŵi zitatu kapena zinayi kuposa mwamasiku onse. Posachedwapa chithandizo china chakhala chopezeka. Impso zanu zimatulutsa hormone yotchedwa erythropoietin (EPO), imene imasonkhezera mafuta a m’mafupa kuumba maselo ofiira. Tsopano EPO yopangidwa njopezeka. Madokotala angapereke imeneyi kwa odwala opereŵera mwazi ena, motero akumawathandiza kuumba mwamsanga kwambiri maselo ofiira obwezeretsa.
Ngakhale mkati mwa opaleshoni, madokotala aluso ndi ozindikira ndi akatswiri ochititsa dzanzi angathandize mwa kugwiritsira ntchito njira zosungitsa mwazi zopititsidwa patsogolo. Njira yosamalitsa yochitira opaleshoni, monga ngati kuwotcha mitsempha ndi magetsi kuchepetsa kukha mwazi, sikungagogomezeredwe mopambanitsa. Nthaŵi zina kuyenderera kwa mwazi kumka pachironda kungatsopedwe ndi chipangizo, kusefedwa, ndi kuloŵetsedwanso m’kuzungulira kwake.b
Odwala oikidwa pamakina a mtima ndi mapapu oikiridwa madzi osakhala mwazi angapindule ndi kusukuluka kwa mwazi kotsatirapo, maselo ofiira ocheperapo akumakhala atatayika.
Ndipo pali njira zina zothandizira. Kusisiritsa wodwalayo kuti muchepetse kufunikira kwake okosijeni mkati mwa opaleshoni. Kuchititsa dzanzi kochepetsa kupopedwa kwa magazi. Mankhwala othandizira kuundana kwa magazi. Desmopressin (DDAVP) kuchepetsa nthaŵi yochucha mwazi. “Timalumo” ta laser. Mudzawona mpambowo ukumakula pamene madokotala ndi odwala odera khaŵa afunafuna kupeŵa kuthiriridwa mwazi. Tikukhulupilira kuti inu simudzataya mwazi wochuluka. Koma ngati mutero, nkwachiwonekere kuti madokotala aluso akatha kukusamalirani popanda kugwiritsira ntchito kuthirira mwazi, kumene kuli ndi maupandu ambiri.
OPALESHONI, INDE—KOMA YOSATHIRIRA MWAZI
Anthu ambiri lerolino sadzalandira mwazi. Kaamba ka zifukwa zathanzi, iwo akupempha zimene Mboni zimafunafuna kwakukulukulu pazifukwa zachipembedzo: chisamaliro chamankhwala chabwino mogwiritsira ntchito kuchiritsa kwaluso kwa zoloŵa mmalo zopanda mwazi. Monga mmene tawonera, opaleshoni yaikulu njothekerabe. Ngati muli ndi zikayikiro zovutitsa maganizo zirizonse, umboni winanso wochokera m’mabukhu azamankhwala ungazichotse.
Nkhani yakuti “Kubwezeretsa Mfundo Kwakukulu Kunayi m’Chiŵalo cha Mboni za Yehova” (Orthopaedic Review, August 1986) inasimba wodwala wosoŵa magazi wina wokhala ndi “kuwonongeka kwakukulu mawondo ndi chuuno chomwe.” Iron dextran inagwiritsiridwa ntchito opaleshoni yolinganizidwayo isanayambe ndi pambuyo pake, imene inali yachipambano. British Journal of Anaesthesia (1982) inasimba Mboni ina ya usinkhu wa zaka 52 yokhala ndi kuchuluka kwa hemoglobin kosafika pa 10. Limodzi ndi kugwiritsira ntchito kuchititsa dzanzi kochepetsa kupopedwa kwa mwazi kuchepetsa kutayika kwa mwazi, iye anabwezeretsedwa kotheratu chuuno ndi pheŵa. Kagulu ka madokotala a opaleshoni pa University of Arkansas (U.S.A.) kanagwiritsiranso ntchito njira imeneyi m’kubwezeretsa ziuno zana pa Mboni, ndipo odwala onse anachira. Pulofesala wotsogoza dipatimentiyo akunena kuti: “Zimene taphunzira kwa odwala amenewo (Mboni), tsopano tikuzigwiritsira ntchito kwa odwala athu onse amene timawachita opaleshoni yamchuuno.”
Chikumbumtima cha Mboni zina chimazilola kuvomereza kuikiridwa ziŵalo ngati kupangidwa popanda mwazi. Lipoti lina la oikidwa impso 13 linati: “Zotulukapo zonse zikuperekera lingaliro lakuti kuikiridwa impso kungachitidwe bwino lomwe ndi mokhutiritsa kwa Mboni za Yehova zochuluka.” (Transplantation, June 1988) Mofananamo, kukana mwazi sikunakhale chopinga ngakhale m’njira za kuikiridwa mtima kwachipambano.
‘Bwanji nanga za opaleshoni yopanda mwazi ya mitundu ina?’ inu mungadabwe. Medical Hotline (April/May 1983) inasimba opaleshoni yochitiŵalo za akazi zobalira ndi ya kubala mwana [pa Wayne State University, U.S.A.] popanda kuthiriridwa mwazi.” Kalatayo inasimba kuti: “Panalibenso imfa ndi matenda kuposa mwa akazi amene anachitidwa maopaleshoni ofananawo ndi kuthiriridwa mwazi.” Kalatayo inati: “Zotulukapo za kupenda uku zingafunikiritse kupendanso kwatsopano pakugwiritsiridwa ntchito kwa mwazi kaamba ka akazi onse ochitidwa opaleshoni ya kubala mwana ndi ya ziŵalo zobalira.”
Pachipatala cha ku Göttingen University (Germany), odwala 30 amene anakana mwazi anachitidwa opaleshoni yozoloŵereka. “Palibe zovuta zimene zinabuka zimene sizikanabukanso ndi odwala amene amavomereza kuthiriridwa mwazi. . . . Chakuti kutembenukira kuchithandizo cha mwazi sikuli kothekera sikuyenera kukukumazidwa, ndipo motero sikuyenera kutsogolera kukukana opaleshoni imene iri yofunika ndi yoyenerera.”—Risiko in der Chirurgie, 1987.
Ngakhale kuchitidwa opaleshoni yaubongo popanda kugwiritsira ntchito mwazi kwachitidwa pa akulu ndi ana ochuluka, mwachitsanzo, pa New York University Medical Center. Mu 1989 Dr. Joseph Ransohoff, mkulu wa opaleshoni yaubongo, analemba kuti: “Nkomvekera bwino kuti m’zochitika zambiri kupeŵedwa kwa zinthu zamwazi kungachitidwe ndi upandu wochepa mwa odwala amene ali ndi zikhulupiliro zamphamvu zachipembedzo pakugwiritsirirdwa ntchito kwazinthu zimenezi, makamaka ngati opaleshoniyo ingachitidwe machangu ndipo limodzi ndi nyengo yanthaŵi yaifupi kwambiri yochita opaleshoni. Chokondweretsa kwambiri ndicho chenicheni chakuti kaŵirikaŵiri ndimaiŵala kuti wodwalayo ndi Mboni kufikira panthaŵi ya kutulutsidwa pamene amandithokoza chifukwa cha kukhala nditalemekeza zikhulupiliro zawo zachipembedzo.”
Potsirizira, kodi opaleshoni yocholoŵanacholoŵana yamtima ndi yamtsempha waukulu yopanda mwazi ingachitidwe pa akulu ndi ana? Dr. Denton A. Cooley anali woyambirira m’kuchita zimenezozo. Monga mmene mungawonere m’nkhani yazamankhwala yosindikizidwa m’Zowonjezeredwa, patsamba 27-9, yozikidwa pakupenda kwapapitapo, lingaliro la Dr. Cooley linali “lakuti upandu wa opaleshoni mwa odwala a kagulu ka Mboni za Yehova sunakhale waukulu kwambiri koposa wa ena.” Tsopano, pambuyo pa kuchita 1,106 a maopaleshoni ameneŵa, akulemba kuti: “M’chochitika chirichonse chivomerezo changa kapena chipangano ndi wodwalayo chimasungidwa,” ndiko kuti, kusagwiritsira ntchito mwazi.
Madokotala a opaleshoni anena kuti kaimidwe ka maganizo kabwino ndiko mbali ina ya Mboni za Yehova. “Kaimidwe ka maganizo ka odwala ameneŵa kakhala kabwino,” analemba motero Dr. Cooley mu October 1989. “Iwo samakhala ndi mantha a zovuta kapena ngakhale imfa amene odwala ochuluka ali nawo. Iwo ali ndi chikhulupiliro chachikulu ndi champhamvu m’chiphunzitso chawo ndi mwa Mulungu wawo.”
Zimenezi sizimatanthauza kuti izo zimalandira kuyenera kwa kufa. Izo zimafunafuna mwamphamvu chisamaliro chabwino chifukwa chakuti zimafuna kuchira. Nzokhutiritsidwa maganizo kuti kumvera lamulo la Mulungu la mwazi nkwanzeru, lingaliro limene lirindi chiyambukiro chotsimikizirika mu opaleshoni yopanda mwazi.
Pulofesala Dr. V. Schlosser, wa chipatala chochitira opaleshoni pa University of Freiburg (Germany), anati: “Pakati pa kagulu kameneka ka odwala, chochitika cha kuchucha mwazi mkati mwa nyengo ya kuchita opaleshoni sichinali chachikulu; zovutazo, ngati zinalipo, zinali zochepa. Lingaliro lapadera la utenda, khalidwe la Mboni za Yehova, linali ndi chiyambukiro chotsimikizirika mkati mwa kuchitidwa opaleshoniko.”—Herz Kreislauf, August 1987.
[Mawu a M’munsi]
a Mboni sizimavomereza kuthiriridwa mwazi wathunthu, maselo ofiira, maselo oyera, zinthu za m’mwazi kapena madzi a m’mwazi. Ponena za zinthu zochepa, monga ngati immune globulin, wonani Nsanja ya Olonda ya June 1, 1990, tsamba 30-1.
b Nsanja ya Olonda ya March 1, 1989, tsamba 30-1, imafotokoza chowonadi chamaziko Chabaibulo chimene chimakhudza njira yosunga mwazi ndi chipangizo choyendetsa mwazi kunja kwa thupi (extracorporeal).
[Bokosi patsamba 13]
“Tiyenera kunena kuti pakali pano pali odwala ambiri olandira zinthu zopangidwa ndi mwazi amene alibe mwaŵi wa kupindula ndi kuthiriridwa mwazi (mwazi sukufunika) ndipo komabe ali ndi upandu wotsimikizirika wa chiyambukiro chosakhumbika. Palibe dokotala amene modziŵa akapatsa wodwala mankhwala amene sangathandize koma angavulaze, koma zimenezo ndizo zimenedi zimachitika pamene mwazi uthiriridwa mosafunikira.”—“Transfusion-Transmitted Viral Diseases,” 1987.
[Bokosi patsamba 14]
“Olemba mabukhu ena anena kuti muyezo wa “hemoglobin” wotsika mpaka pa 2 kufikira 2.5 gm./100ml. ungakhale wovomerezeka. . . . Munthu wathanzi angapirire kutayika kwa 50 peresenti ya maselo ofiira a mwazi ndi kukhala pafupifupi wosazindikirika ngati kutayika kwa mwazi kuchitika mkati mwa nyengo yaitali.”—“Techniques of Blood Transfusion,” 1982.
[Bokosi patsamba 15]
“Malingaliro akale onena za kuyendetsedwa kwa okosijeni m’minyeŵa kwa okosijeni m’minyeŵa, kuchiritsa chironda, ndi ‘phindu lodyetsa’ la mwazi akusiyidwa. Chokumana nacho cha odwala amene ali Mboni za Yehova chimasonyeza kuti kusoŵeka kwa mwazi kwakukulu kumapiriridwa bwino lomwe.”—“The Annals of Thoracic Surgery,” March 1989.
[Bokosi patsamba 16]
Ana achicheperenso? “Njira 48 za maopaleshoni otsegula mtima pa ana zinachitidwa ndi maluso opanda mwazi mosasamala kanthu za kuvuta kwa opaleshoni.” Anawo anali aang’ono kufikira pamakilogalamu 4.7. “Chifukwa cha chipambano chosalekeza mwa Mboni za Yehova ndi chenicheni chakuti kuthirira mwazi kuli ndi upandu wa matenda aakulu, pakali pano tikuchita ambiri a maopaleshoni athu amtima a ana popanda kuthirira mwazi.”—“Circulation,” September 1984.
[Chithunzi patsamba 15]
Makina a mtima ndi mapapu akhala chithandizo mkuchita opaleshoni ya mtima pa odwala amene samafuna mwazi