Mutu 47
Misozi Isanduka Chikondwerero Chachikulu
PAMENE Yairo awona mkazi wochucha mwaziyo atachiritsidwa, mosakayikira chidaliro chake m’mphamvu zozizwitsa za Yesu chikuwonjezereka. Pachiyambiyambi m’tsikulo, Yesu anali atapemphedwa ndi Yairo kudzathandiza mwana wake wamkazi wokondedwayo wa zaka 12 zakubadwa, amene anali kudwala kwakayakaya. Komabe, tsopano, chimene Yairo akuwopa koposa chachitika. Pamene Yesu adakali chilankhulire ndi mkaziyo, amuna ena akufika mwakachetechete nauza Yairo kuti: “Mwana wako wafa; uvutiranjinso Mphunzitsi?”
Ndimbiri yovutitsa maganizo chotani nanga! Tangolingalirani: Mwamunayu, amene ali wolemekezeka kwambiri m’chitaganyacho, tsopano akusoŵa chochita kotheratu pamene amva za imfa ya mwana wake wamkazi. Komabe, Yesu, akumva kukambitsiranako. Chotero, potembenukira kwa Yairo, iye akunena molimbikitsa kuti: “Usawope, khulupirira kokha.”
Yesu akutsagana ndi mwamuna wogwidwa ndi chisoniyo kubwerera kunyumba kwake. Pamene akufika, iwo akupeza phokoso la kulira ndi kukuwa. Khamu la anthulo lasonkhana, ndipo akudziguguda pachifuŵa pomva chisoni. Pamene Yesu aloŵa m’nyumbamo, akufunsa kuti: “Mubuma ndi kulira bwanji? Mwana sanafa, koma ali m’tulo.”
Pakumva izi, anthuwo akuyamba kuseka Yesu momnyodola chifukwa chakuti akudziŵa kuti msungwanayo wafadi. Komabe, Yesu, akunena kuti iye wangogona chabe. Mwakugwiritsira ntchito mphamvu zake zopatsidwa ndi Mulungu, iye adzasonyeza kuti anthu angaukitsidwe kuchokera ku imfa mosavuta monga momwe angadzutsidwire kutulo tatikulu.
Yesu tsopano akutulutsa munthu aliyense m’nyumbamo kusiyapo Petro, Yakobo, Yohane, ndi amake a msungwana wakufayo ndi atate wake. Pamenepo iye akutengera asanu ameneŵa kumene msungwana wachichepereyo wagonekedwa. Pogwira dzanja lake, Yesu akuti: “Talita koumi,” ndiko kunena pomasulira, “Buthu, ndinena ndi iwe, Uka.” Ndipo pomwepo msungwanayo akuuka nayamba kuyenda! Chochitikacho chichititsa pafupifupi kusokonezeka maganizo kwa makolo ake limodzi ndi chikondwerero chachikulu.
Atalangiza kuti mwanayo apatsidwe kanthu kena koti adye, Yesu akulamulira Yairo ndi mkazi wake kusauza aliyense zimene zachitika. Koma mosasamala kanthu za zimene Yesu akunena, nkhaniyo ikufalikira m’chigawo chonsecho. Chimenechi chiri chiukiriro chachiŵiri chimene Yesu akuchita. Mateyu 9:18-26; Marko 5:35-43; Luka 8:41-56.
▪ Kodi Yairo akulandira mbiri yotani, ndipo Yesu akumlimbikitsa motani?
▪ Kodi ndimkhalidwe wotani umene ulipo pamene iwo akufika panyumba ya Yairo?
▪ Kodi nchifukwa ninji Yesu akunena kuti mwana wakufayo wangogona chabe?
▪ Kodi ndani amene ali asanu okhala ndi Yesu amene akuchitira umboni za chiukirirocho?