Mutu 63
Uphungu Wowonjezereka wa Kuwongolera
PAMENE Yesu ndi atumwi ake adakali m’nyumba ku Kapernao, kanthu kena kowonjezeredwa pamkangano wa atumwiwo wonena za kuti ndani amene ali wamkulu kakukambitsiridwa. Ichi ndichochitika chimene chingakhale chinachitikanso paulendo wawo wobwerera ku Kapernao, pamene Yesu iye mwiniyo padalibe. Mtumwi Yohane akusimba kuti: “Tinawona munthu alikutulutsa ziwanda m’dzina lanu ndipo tinamletsa, chifukwa sanali kutsata ife.”
Mwachiwonekere Yohane akuwona atumwiwo kukhala kagulu kapadera ka ochiritsa, kokhala ndi dzina laulemu. Motero iye akulingalira kuti mwamunayo anali kuchita ntchito zamphamvu mosayenerera chifukwa chakuti iye sanali mbali ya kaguluko.
Komabe, Yesu akupereka uphungu kuti: “Musamamletsa iye; pakuti palibe munthu adzachita champhamvu m’dzina langa, nadzakhoza msanga kundinenera zoipa. Pakuti iye wosatsutsana ndi ife athandizana nafe. Pakuti munthu aliyense adzakumwetsani inu chikho cha madzi m’dzina langa, chifukwa muli ake a Kristu, indetu ndinena ndi inu, kuti iye sadzataya konse mphotho yake.”
Sikunali kofunikira kwa munthu uyu kutsatira Yesu mowonekera kuti akhale kumbali yake. Mpingo Wachikristu unali usanakhazikitsidwebe, chotero kusakhala kwake mbali ya kagulu kawo sikunatanthauze kuti anali wampingo wosiyana. Munthuyu analidi ndi chikhulupiriro m’dzina la Yesu ndipo motero anali ndi chipambano m’kutulutsa ziwanda. Iye anali kuchita kanthu kena kamene kanali kofanana ndendende ndi zimene Yesu ananena kuti zinali zoyenerera mphotho. Yesu akusonyeza kuti kaamba ka kuchita zimenezi, sadzataya mphotho yake.
Koma bwanji ngati munthuyo anakhumudwitsidwa ndi mawu ndi zochita za atumwiwo? Izi zikanakhala zowopsa zedi! Yesu akuti: “Yense amene adzalakwitsa kamodzi ka tiana timeneto takukhulupilira kuli bwino kwa iye makamaka kuti mwala waukulu wamphero ukoloŵekedwe m’khosi mwake, naponyedwe iye m’nyanja.”
Yesu akuti otsatira ake ayenera kuchotsa m’miyoyo yawo chirichonse chokondeka kwa iwo chonga dzanja, phazi, kapena diso chomwe chingawaphunthwitse. Kuli bwino kukhala wopanda chinthu chokondeka chimenechi ndi kuloŵa mu Ufumu wa Mulungu koposa kukhala nacho ndi kuponyedwa ku Gehena (dzala la zinyalala loyaka moto lokhala pafupi ndi Yerusalemu), amene amaphiphiritsira chiwonongeko chamuyaya.
Yesu akuchenjezanso kuti: “Yang’anirani kuti musanyoze mmodzi wa aang’ono awa; pakuti ndinena kwa inu, kuti angelo awo apenya chipenyere nkhope ya Atate wanga wakumwamba.” Ndiyeno akuchitira fanizo kuŵerengeredwa mtengo kwa “ana aang’ono” pamene akuwauza za munthu wina wokhala ndi nkhosa zana limodzi nataikiridwa ndi imodzi. Munthuyo adzasiya 99 zinazo kukafunafuna yotaikayo, Yesu akufotokoza motero, ndipo ataipeza adzasangalala nayo koposa ndi 99 zinazo. “Chomwecho,” Yesu akumaliza kuti, “sichiri chifuniro cha Atate anga wakumwamba kuti mmodzi wa aang’ono aŵa atayike.”
Mwinamwake pokhala akukumbukira mkangano wa pakati pa atumwi ake, Yesu akufulumiza kuti: “Khalani nawo mchere mwa inu nokha, ndipo khalani ndi mtendere wina ndi mnzake.” Chakudya chosakoma chimakometsedwa ndi mchere. Motero, mchere wophiphiritsira umapangitsa zonena za munthu kulandiridwa mosavuta. Kukhala ndi mchere woterowo kudzathandizira kusungitsa mtendere.
Koma chifukwa cha kupanda ungwiro kwaumunthu, nthaŵi zina padzabuka mikangano yaikulu. Yesu akuperekanso zitsogozo za kuzisamalira. “Ngati mbale wako akuchimwira iwe,” Yesu akutero, “pita, numlangize panokha iwe ndi iye; ngati akumvera iwe, wambweza mbale wako.” Ngati samvera, Yesu akulangiza kuti, “wonjeza kutenga ndi iwe wina mmodzi kapena aŵiri, kuti atsimikizidwe mawu onse pakamwa pa mboni ziŵiri kapena zitatu.”
Yesu akunena kuti, kokha monga sitepe lomalizira, “uuze mpingo,” ndiko kuti, kwa oyang’anira a mpingo a thayo omwe angapereke chosankha cha chiweruzo cholungama. Ngati wochimwayo sadzamvera chosankha chawo, Yesu akumaliza kuti, “akhale kwa iwe monga munthu wa kunja ndi wamsonkho.”
Popanga chosankha choterocho, oyang’anira afunikira kumamatira kwambiri kumalangizo a Mawu a Yehova. Motero, pamene apeza munthu kukhala waliwongo ndi woyenerera chilango, chiweruzocho ‘chidzakhala chitamangidwa kale kumwamba.’ Ndipo pamene ‘azimasula padziko lapansi,’ ndiko kuti, apeza munthu kukhala wopanda liwongo, zidzakhala “zomasulidwa [kale] kumwamba.” Poweruza mlandu wotero, Yesu akuti, “kumene kuli aŵiri kapena atatu asonkhanira m’dzina langa, ndiri komweko pakati pawo.” Mateyu 18:6-20; Marko 9:38-50; Luka 9:49, 50.
▪ Kodi nchifukwa ninji kunali kosafunika m’tsiku la Yesu kugwirizana naye m’kagulu kake?
▪ Kodi nkhani ya kukhumudwitsa aang’ono njaikulu motani, ndipo kodi ndimotani mmene Yesu akuchitira fanizo za kufunika kwa aang’ono oterowo?
▪ Kodi nchiyani mwinamwake chimene chikusonkhezera Yesu kulimbikitsa atumwi ake kukhala ndi mchere mwa iwo okha?
▪ Kodi nditanthauzo lotani limene liripo lonena za ‘kumanga’ ndi ‘kumasula’?