Mutu 65
Ulendo Wakachetechete wa ku Yerusalemu
NDIMPHAKASA ya 32 C.E., ndipo Phwando la Misasa layandikira. Yesu walekezeretsa ntchito zake kwakukulukulu m’Galileya chiyambire Paskha wa 31 C.E., pamene Ayuda anayesa kumupha. Mwachiwonekere, chiyambire pamenepo Yesu wakhala akupita ku Yerusalemu kokha kukakhalapo pa mapwando atatu apachaka a Ayuda.
Tsopano abale a Yesu akumfulumiza kuti: “Chokani pano, mumuke ku Yudeya.” Yerusalemu ndiwo mzinda waukulu wa Yudeya ndi phata la chipembezo cha dziko lonselo. Abale akewo akumuuza kuti: “Pakuti palibe munthu achita kanthu mobisika, nafuna yekha kukhala poyera.”
Ngakhale kuti Yakobo, Simoni, Yosefe, ndi Yudase sakukhulupilira kuti mkulu wawo, Yesu, alidi Mesiya, iwo akufuna kuti iye asonyeze mphamvu zake zozizwitsa kwa osonkhana onsewo paphwandolo. Komabe Yesu, akudziŵa za upanduwo. “Dziko lapansi silingathe kudana ndi inu,” iye akutero, “ine lindida popeza ine ndilichitira umboni, kuti ntchito zake ziri zoipa.” Motero Yesu akuuza abale akewo kuti: “Kwerani inu kumka kuphwando; sindikwera ine kuphwando ili tsopano apa.”
Phwando la Misasa nla masiku asanu ndi aŵiri. Patsiku lachisanu ndi chitatu limatha ndi zochitika za madzoma. Phwandolo limasonyeza kutha kwa chaka chaulimi ndipo ndiyo nthaŵi ya chisangalalo chachikulu ndi kupereka chiyamiko. Masiku angapo abale a Yesu atachoka limodzi ndi kagulu kokulirapoko ka apaulendo kukakhalapo, iye ndi ophunzira ake akupita mwakachetechete, mosawonedwa ndi anthu. Iwo akutenga njira yodzera ku Samariya, mmalo mwa njira imene anthu ochuluka amatenga yapafupi ndi Mtsinje wa Yordano.
Popeza kuti Yesu ndi otsagana naye adzafuna malo ogona m’mudzi wa a Samariya, akutumiza amithenga patsogolo kuti akapange makonzedwe. Komabe anthuwo, akukana kuchitira Yesu kalikonse atamva kuti akupita ku Yerusalemu. Moipidwa, Yakobo ndi Yohane akufunsa kuti: “Ambuye, Kodi mufuna kuti ife tiuze moto utsike kumwamba ndi kuwanyeketsa iwo?” Yesu akuwadzudzula kaamba ka kupereka lingaliro loterolo, ndipo akuyendabe kumka kumudzi wina.
Pamene akuyenda panjirapo, mlembi wina akuti kwa Yesu: “Mphunzitsi, ndidzakutsatani inu kulikonse mumukako.”
“Ankhandwe ali nazo nkhwimba zawo, ndi mbalame za mlengalenga zisa zawo,” Yesu akuyankha motero, “koma Mwana wa munthu alibe potsamira mutu wake.” Yesu akufotokoza kuti mlembiyo adzakumana ndi mavuto ngati akhala wotsatira Wake. Ndipo kukuwonekera kuti mlembiyo ngwonyada kwambiri kosakhoza kulandira mkhalidwe umenewu wa moyo.
Kwa munthu winanso, Yesu akuti: “Unditsate ine.”
“Mundilole ine, Ambuye, ndithange ndamuka kukaika maliro a atate wanga,” munthuyo akuyankha motero.
Yesu akuyankha kuti: “Leka akufa aike akufa a eni okha; koma muka iwe nubukitse mbiri yake ya ufumu wa Mulungu.” Mwachiwonekere atate wake wa mwamunayo anali asanamwalire, popeza kuti akadatero, bwenzi mwana wakeyo sakadakhala kunoko akumamvetsera kwa Yesu. Mwachiwonekere mwanayo akupempha nthaŵi yakuti akadikirire imfa ya atate wake. Iye sali wokonzekera kuika Ufumu wa Mulungu m’malo oyamba m’moyo mwake.
Pamene akupitirizabe ulendo womka ku Yerusalemu, munthu wina akuuza Yesu kuti: “Ambuye ndidzakutsatani inu; koma muthange mwandilola kulaŵirana nawo a kunyumba kwanga.”
Poyankha Yesu akuti: “Palibe munthu wa kugwira chikhasu, nayang’ana zakumbuyo, ayenera Ufumu wa Mulungu.” Awo amene adzakhala ophunzira a Yesu ayenera kusumika maso awo pautumiki Waufumu. Monga momwe mzera ungakhalire wokhota ngati mlimi sapenya molunjika kutsogolo, chotero, munthu aliyense wopenya kumbuyo kudongosolo la zinthu lakale ili angaphunthwe ndi kuchoka pamsewu womka kumoyo wamuyaya. Yohane 7:2-10; Luka 9:51-62; Mateyu 8:19-22.
▪ Kodi ndani ali abale a Yesu, ndipo iwo akulingalira motani za iye?
▪ Kodi nchifukwa ninji Asamariya ali amwano kwambiri, ndipo kodi nchiyani chimene Yakobo ndi Yohane akufuna kuchita?
▪ Kodi ndikukambitsirana kutatu kotani kumene Yesu akuchita panjira, ndipo kodi akugogomezera motani kufunika kwa utumiki wodzimana?