Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 66
  • Paphwando la Misasa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Paphwando la Misasa
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani Yofanana
  • Pa Phwando la Misasa
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Zimene Zinachitika Yesu Atapita ku Chikondwerero cha Misasa ku Yerusalemu
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • “Nthaŵi Yake Siinafike”
    Nsanja ya Olonda—2000
  • “Palibe Munthu Amene Analankhulapo Ngati Iyeyo”
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 66

Mutu 66

Paphwando la Misasa

YESU wakhala wotchuka mkati mwa zaka pafupifupi zitatu chiyambire ubatizo wake. Anthu zikwi zambiri awona zozizwitsa zake, ndipo mbiri ya ntchito zake yafalikira mozungulira dziko lonselo. Tsopano, pamene anthu akusonkhana kaamba ka Phwando la Misasa mu Yerusalemu, akumfunafuna kumeneko. ‘Munthu uja ali kuti?’ iwo afuna kudziŵa.

Yesu wakhala mkhole wokanganirana. “Ali wabwino,” ena akutero. “Iyayi, koma asocheretsa khamu la anthuwo,” ena akutsimikizira motero. Pali kulankhula kokangana koteroko m’masiku oyambilira a phwandolo. Komabe palibe ngakhale mmodzi amene ali wolimba mtima kulankhula poyera motetezera Yesu. Zimenezi ziri chifukwa chakuti anthu akuwopa kulipsira kochokera kwa atsogoleri Achiyuda.

Pamene phwandolo litafika pakati, Yesu akufika. Iye akumka kukachisi, kumene anthu akudabwa chifukwa chaluso lake labwinolo lophunzitsa. Popeza kuti Yesu sanapite kumasukulu achirabi, Ayudawo akuzizwa kuti: “Ameneyu adziŵa bwanji zolemba, wosaphunzira?”

“Chiphunzitso changa sichiri changa,” Yesu akufotokoza motero, “koma cha iye amene anandituma ine. Ngati munthu aliyense afuna kuchita chifuniro chake, adzazindikira za chiphunzitsocho, ngati chichokera kwa Mulungu, kapena ndilankhula zochokera kwa ine ndekha.” Chiphunzitso cha Yesu chikumamatira kotheratu kulamulo la Mulungu. Motero, kuyenera kukhala kwachiwonekere kuti iye akufunafuna ulemerero wa Mulungu, osati wake. “Si Mose kodi anakupatsani inu chilamulo?” Yesu akufunsa motero. Mwa kuwadzudzula, iye akuti: “Kulibe mmodzi wa inu achita chilamulo.”

“Mufuna kundipha chifukwa ninji?” Yesu akufunsa motero.

Anthu okhala m’khamulo, mwinamwake alendo odza kuphwandolo, sakudziŵa za zoyesayesa zoterozo. Iwo akuziwona kukhala zosatheka kuti wina aliyense angafune kupha mphunzitsi wabwino chotero. Chotero iwo akukhulupilira kuti kanthu kena nkolakwika kuti Yesu alingalire motero. “Muli ndi chiŵanda,” iwo akutero. “Afuna ndani kukuphani inu?”

Atsogoleri Achiyuda akufuna kuti Yesu aphedwe, ngakhale kuti khamulo silingadziŵe. Pamene Yesu anachiritsa munthu pa Sabata chaka chimodzi ndi theka zapitazo, atsogoleriwo anayesa kumupha. Chotero Yesu tsopano akusonyeza kupanda nzeru kwawo mwa kuwafunsa kuti: “Ngati munthu alandira mdulidwe tsiku la Sabata, kuti chilamulo cha Mose chingapasulidwe; kodi mundikwiyira ine, chifukwa ndamchiritsadi munthu tsiku la Sabata? Musaweruze monga mawonekedwe, koma weruzani chiweruzo cholungama.”

Nzika za Yerusalemu, zodziŵa mkhalidwewo, tsopano zikuti: “Kodi suuyu amene afuna kumupha? ndipo tawona amalankhula poyera, ndipo sanena kanthu kwa iye. Kapena kodi akulu adziŵa ndithu kuti ndiye Kristu ameneyo?” Nzika za mu Yerusalemu zimenezi zikufotokoza chifukwa chimene sizikukhulupililira kuti Yesu ali Kristuyo: “Ameneyo tidziŵa uko achokera: koma Kristu pamene akadza, palibe mmodzi adzadziŵa uko achokera.”

Yesu akuyankha kuti: “Mundidziŵa ine, ndiponso mudziŵa uko ndichokera; ndipo sindinadza ine ndekha, koma iye wondituma ine amene inu simumdziŵa, ali wowona. Ine ndimdziŵa iye; chifukwa ndiri wochokera kwa iye, nandituma ine iyeyu.”  Atamva  izi iwo akuyesa kumgwira, mwinamwake kuti amponye m’ndende kapena kuti aphedwe. Komabe sakupambana chifukwa chakuti sinthaŵi yakuti Yesu afe.

Komabe, ambiri akukhulupilira Yesu, monga momwedi ayenera kuchitira. Eya, iye anayenda pamadzi, anaimitsa mphepo, anatontholetsa namondwe panyanja, anadyetsa zikwi za anthu mozizwitsa ndi mitanda yamikate yoŵerengeka ndi tinsomba, anachiritsa odwala, anachititsa opuwala kuyenda, anatsegula maso a akhungu, anachiritsa akhate, ndipo anaukitsadi akufa. Chotero iwo akufunsa kuti: “Pamene Kristu akadza kodi adzachita zizindikiro zambiri zoposa zimene adazichita ameneyo?”

Pamene Afarisiwo akumva khamulo likunena mong’ung’udza zinthu zimenezi, iwo ndi akulu ansembe akutuma asilikali kuti agwire Yesu. Yohane 7:11-32.

▪ Kodi ndiliti pamene Yesu akufika pa phwando, ndipo kodi anthu akunenanji za iye?

▪ Kodi nchifukwa ninji ena anganene kuti Yesu ali ndi chiŵanda?

▪ Kodi anthu a ku Yerusalemu akulingalira Yesu motani?

▪ Kodi nchifukwa ninji ambiri akukhulupilira Yesu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena