Mutu 80
Makola Ankhosa ndi Mbusa
YESU wadza ku Yerusalemu kaamba ka Phwando la Kukonzanso kapena Hanukkah, phwando lokumbukira kupatuliranso kachisi kwa Yehova. Mu 168 B.C.E., pafupifupi zaka 200 zapitazo, Antiochus IV Epiphanes analanda Yerusalemu ndi kululuzitsa kachisiyo ndi guwa lake lansembe. Komabe, zaka zitatu pambuyo pake Yerusalemu anabwezeretsedwanso ndipo kachisi anapatulidwanso. Pambuyo pake, phwando la kupatulidwanso lachaka ndi chaka linachitidwa.
Phwando la Kukonzanso limeneli limachitika pa Chislev 25, mwezi Wachiyuda umene umayenderana ndi mbali yomalizira ya November ndi mbali yoyambirira ya December pakalendala yathu yamakono. Motero, kwatsala masiku oposa pang’ono zana limodzi kufika pa Paskha wosaiŵalika wa 33 C.E. Chifukwa chakuti iri nyengo yozizira mtumwi Yohane akuitcha “nyengo yachisanu.”
Yesu tsopano akugwiritsira ntchito fanizo mu limene akutchula za makola ankhosa atatu ndi mbali yake monga Mbusa Wabwino. Khola lankhosa loyamba limene akulankhula likuphatikizapo kakonzedwe ka pangano Lachilamulo cha Mose. Chilamulocho chinatumikira monga mpanda, wakulekanitsa Ayuda kuzizolowezi zoipitsa za anthu amene sanali m’pangano lapadera limeneli ndi Mulungu. Yesu akufotokoza kuti: “Indetu, indetu ndinena ndi inu, Iye wosaloŵa m’khola la nkhosa pakhomo, koma akwerera kwina, iyeyu ndiye wakuba ndi wolanda. Koma iye wakuloŵera pakhomo, ndiye mbusa wankhosa.”
Ena anadza nadzinenera kukhala Mesiya, kapena Kristu, koma iwo sanali mbusa wowona za amene Yesu akupitirizabe kunena kuti: “Wapakhomo amtsegulira ndi nkhosa zimva mawu ake; ndipo aitana nkhosa za iye yekha maina awo, nazitsogolera kunja. . . . Koma mlendo sizidzamtsata, koma zidzamthaŵa; chifukwa sizidziŵa mawu a alendo.”
“Wapakhomo” wakhola la nkhosa loyamba anali Yohane Mbatizi. Monga wapakhomo, Yohane ‘anatsegulira’ Yesu mwa kumudziŵikitsa iye kwa nkhosa zophiphiritsira zimenezo zimene akatsogolera kumsipu. Nkhosa zimene Yesu anadziitana ndi dzina zimenezi ndi kuzitsogolera potsirizira pake zikuloŵetsedwa m’khola lina la nkhosa, monga momwe akufotokozera kuti: “Indetu, indetu, ndinena ndi inu, ine ndine khomo la nkhosa,” ndiko kuti, khomo la khola la nkhosa latsopano. Pamene Yesu akuyambitsa pangano latsopano ndi ophunzira ake ndipo kuchokera kumwamba akutsanulira mzimu woyera pa Pentekoste wotsatira, iwo akuloŵetsedwa m’khola latsopano limeneli.
Popitiriza kufotokoza ntchito yake, Yesu akuti: “Ine ndine khomo; ngati wina aloŵa ndi ine, adzapulumutsidwa, nadzaloŵa, nadzatuluka, nadzapeza busa. . . . Ndadza ine kuti akhale ndi moyo, ndi kukhala nawo wochuluka. . . . Ine ndine mbusa wabwino; ndipo ndizindikira zanga, ndi zanga zizindikira ine, monga Atate andidziŵa ine, ndi Ine ndimdziŵa Atate; ndipo nditaya moyo wanga chifukwa cha nkhosa.”
Osati kale kwambiri, Yesu anali atatonthoza otsatira ake, kuti: “Musaopa, kagulu kankhosa inu; chifukwa Atate wanu akonda kukupatsani ufumu.” Kagulu kankhosa kameneka, kamene potsirizira pake kakufikira chiŵerengero cha 144,000, kakuloŵa m’khola la nkhosa latsopano iri, kapena lachiŵiri. Koma Yesu akupitirizabe kunena kuti: “Nkhosa zina ndiri nazo, zimene siziri za nkhola iri; izinso ndiyenera kuzitenga, ndipo zidzamva mawu anga; ndipo zidzakhala gulu limodzi, mbusa mmodzi.”
Popeza kuti “nkhosa zina” “siziri za khola iri,” ziyenera kukhala za khola lina, lachitatu. Makola aŵiri omalizira ameneŵa, kapena miteba ya nkhosa, iri ndi zolinga zosiyana. “Kagulu ka nkhosa” m’khola lina kadzalamulira ndi Kristu kumwamba, ndipo “nkhosa zina” m’khola lina zidzakhala padziko lapansi mu Paradaiso. Komabe, mosasamala kanthu za kukhala m’makola aŵiri, nkhosazo sizimachitirana nsanje, kapena kusankhana, pakuti monga momwe Yesu akunenera, iwo ‘amakhala gulu limodzi’ pansi pa “mbusa mmodzi.”
Mbusa Wabwino, Yesu Kristu, mofunitsitsa apereka moyo wake kaamba ka makola aŵiri ankhosa. “Ndiutaya ine ndekha,” iye akutero. “Ndiri nayo mphamvu yakuutaya, ndi mphamvu ndiri nayo yakuutenganso; lamulo iri ndinalandira kwa Atate wanga.” Pamene Yesu akunena izi pakukhala kugaŵikana pakati pa Ayuda.
Ambiri a m’kagulu akunena kuti: “Ali ndi chiŵanda, nachita misala; mukumva iye bwanji?” Koma ena akuyankha kuti: “Mawu awa sali a munthu wogwidwa chiŵanda.” Pamenepo, mwachiwonekere akusonya kumiyezi iŵiri yapitayo pamene anachiritsa munthu wosawona chibadwire, iwo akuwonjezera kuti: “Kodi chiŵanda chikhoza kumtsegulira maso osawona?” Yohane 10:1-22; 9:1-7; Luka 12:32; Chivumbulutso 14:1, 3; 21:3, 4; Salmo 37:29.
▪ Kodi Phwando la Kukonzanso nchiyani, ndipo ndiliti pamene limachitidwa?
▪ Kodi khola la nkhosa loyamba nchiyani, ndipo kodi ndani amene ali wapakhomo wake?
▪ Kodi ndimotani mmene wosunga pakhomo amatsegulirira Mbusa, ndipo kodi nkhosazo potsirizira pake zikuloŵetsedwa kuti?
▪ Kodi ndani amene amapanga makola aŵiri a Mbusa Wabwino, ndipo kodi iwo amafikira kukhala magulu ankhosa angati?