Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Makola a Nkhosa ndi Mbusa
YESU ali m’Yerusalemu pa nthaŵi ya Phwando la Kuperekedwa, kapena Hanukkah, phwando lomwe limakumbukira kuperekedwanso kwa Yehova kwa kachisi. Mu 168 B.C.E., chifupifupi zaka 200 kumayambiriro, Antiochus IV Epiphanes anali atalanda Yerusalemu ndi kudetsa kachisi ndi guwa lake la nsembe. Ngakhale kuli tero, zaka zitatu pambuyo pake Yerusalemu analandidwanso ndipo kachisi anaperekedwanso. Pambuyo pake, phwando la kuperekedwanso la pa chaka linapangidwa.
Phwando la Kuperekedwa limeneli limachitika pa Chislev 25, mwezi wa Chiyuda womwe umafanana ndi mbali yomalizira ya November ndi mbali yoyambirira ya December pa kalenda yathu yamakono. Chotero, kokha masiku oposa pang’ono pa zana limodzi anatsalira kufikira Paskha yofunikayo ya 33 C.E. Chifukwa iri nyengo ya nthaŵi yozizira, mtumwi Yohane akuitcha iyo “nthaŵi ya chisanu.”
Yesu tsopano akugwiritsira ntchito fanizo mu limene iye akutchula makola a nkhosa atatu ndi mbali yake monga Mbusa Wabwino. Khola la nkhosa loyamba limene iye akulitchula likuzindikiritsidwa ndi kakonzedwe ka pangano la Chilamulo cha Mose. Chilamulocho chinatumikira monga mpanda womwe unapatula Ayuda kuchokera ku machitachita oipa a anthu awo omwe sanali m’pangano lapadera ndi Mulungu. Yesu akulongosola kuti: “Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wosalowa m’khola la nkhosa pakhomo koma akwerera kwina, iyeyu ndiye wakuba ndi wolanda. Koma iye wakulowera pakhomo, ndiye mbusa wa nkhosa.’
Ena anabwera ndi kudzinenera kukhala Mesiya, kapena Kristu, koma iwo sanali mbusa wowona za amene Yesu akupitiriza kulankhula kuti: “Wapakhomo amtsegulira, ndi nkhosa zimva mawu ake, ndipo aitana nkhosa za iye yekha maina awo nazitsogolera kunja. . . . Mlendo sizidzamtsata koma zidzamthaŵa, chifukwa sizidziŵa mawu a alendo.”
“Wapakhomo” wa khola la nkhosa loyambalo anali Yohane Mbatizi. Monga wapakhomo, Yohane ‘anatsegulira’ Yesu mwa kumzindikiritsa iye kwa nkhosa zophiphiritsira zimenezo zomwe iye akazitsogolera ku busa. Nkhosa zimenezi zimene Yesu anaziitana ndi maina ndi kuzitsogolera kunja zikulandiridwa ku khola la nkhosa lina, monga mmene iye akulongosolera: “Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ine ndine khomo la nkhosa,” kunena kuti, khomo la khola la nkhosa latsopano. Pamene Yesu wakhazikitsa pangano latsopano ndi ophunzira ake ndipo kuchokera kumwamba kutsanulira mzimu woyera pa iwo Pentekoste yotsatira, iwo akuvomerezedwa m’khola la nkhosa latsopano limeneli.
Mowonjezera akumalongosola mbali yake, Yesu akunena kuti: “Ine ndine khomo; ngati wina alowa ndi ine adzapulumutsidwa, nadzalowa nadzatuluka nadzapeza busa. . . . Ndadza ine kuti akhale ndi moyo ndi kukhala nawo wochuluka. . . . Ine ndine mbusa wabwino, ndipo ndizindikira [nkhosa] zanga ndipo [nkhosa] zanga zindizindikira ine, monga Atate andidziŵa ine ndi ine ndimdziŵa Atate; ndipo nditaya moyo wanga chifukwa cha nkhosa.”
Posachedwapa, Yesu anatonthoza atsatiri ake, akumanena kuti: “Musawopa, kagulu ka nkhosa, chifukwa Atate wanu akonda kukupatsani ufumu.” Kagulu ka nkhosa kameneka, kamene kenaka kanafika chiŵerengero cha 144,000, kabwera m’khola la nkhosa latsopano limeneli, kapena lachiŵiri. Koma Yesu akupitiriza kuwona: “Ndipo nkhosa zina ndiri nazo, zimene siziri za khola iri; izinso ndiyenera kuzitenga, ndipo zidzamva mawu anga, ndipo zidzakhala gulu limodzi, ndi mbusa mmodzi.”
Popeza kuti “nkhosa zina” “siziri za khola iri,” izo ziyenera kukhala za khola lina, lachitatu. Makola aŵiri omalizira amenewa, kapena motsekera nkhosa, ali ndi ziyembekezo zosiyana. “Kagulu ka nkhosa” m’khola limodzi kadzalamulira ndi Kristu kumwamba, ndipo “nkhosa zina” m’khola lina zidzakhala ndi moyo padziko lapansi la Paradaiso. Komabe, mosasamala kanthu za kukhala m’makola aŵiri, nkhosazo ziribe nsanje, ndipo sizidzimva kukhala zopatulidwa, popeza monga mmene Yesu akunenera, izo “zikhala gulu limodzi” pansi pa “mbusa mmodzi.”
Mbusa Wabwino, Yesu Kristu, mofunitsitsa akupereka moyo wake kaamba ka makola onse aŵiri a nkhosa. “Ndiutaya ine ndekha,” iye akutero. “Ndiri nayo mphamvu ya kuutaya, ndi mphamvu ndiri nayo ya kuutenganso. Lamulo iri ndinalandira kwa Atate wanga.” Pamene Yesu anena ichi, mpatuko utulukapo pakati pa Ayuda.
Ambiri m’khamulo anena kuti: “Ali ndi chiwanda nachitsa misala. Mukumva iye bwanji?” Koma ena akuvomereza: “Mawu awa siali a munthu wogwidwa ndi chiwanda.” Kenaka, mwachiwonekere akumalozera kumbuyo miyezi ingapo ku kuchiritsa kwake munthu wobadwa wakhungu, iwo akuwonjezera: “Kodi chiwanda chikhoza kumtsegulira maso wosawona?” Yohane 10:1-22; 9:1-7; Luka 12:32; Chivumbulutso 14:1, 3; 21:3, 4; Salmo 37:29.
◆ Nchiyani chomwe chiri Phwando la Kuperekedwa, ndipo ndi liti pamene limasangalalidwa?
◆ Nchiyani chomwe chiri khola la nkhosa loyamba, ndipo ndani yemwe ali wapakhomo wake?
◆ Ndimotani mmene wapakhomo akutsegulira kwa Mbusa, ndipo nkuuti kumene nkhosazo pambuyo pake zikulowetsedwa?
◆ Ndani amene amapanga makola aŵiri a Mbusa Wabwino, ndipo ndi magulu angati amene iwo amakhala?