Mutu 93
Pamene Mwana wa Munthu Avumbulutsidwa
PAMENE Yesu akali kumpoto (mwinamwake ku Samariya kapena ku Galileya), Afarisi akumfunsa za kudza kwa Ufumu. Iwo amakhulupirira kuti udzadza ndi ulemerero waukulu ndi dzoma, koma Yesu akuti: “Ufumu wa Mulungu sukudza ndi mawonekedwe; ndipo sadzanena Tawonani uwu, kapena uwo! Pakuti, tawonani, Ufumu wa Mulungu uli mkati mwa inu.”
Mawu a Yesu akuti “mkati mwa inu” nthaŵi zina atembenuzidwa kuti “mkati mwanu.” Chotero ena alingalira kuti Yesu anatanthauza kuti Ufumu wa Mulungu umalamulira m’mitima ya atumiki a Mulungu. Koma, mwachiwonekere, Ufumu wa Mulungu suli m’mitima ya Afarisi osakhulupirira ameneŵa kwa amene Yesu akulankhula nawo. Komabe, uwo uli pakati pawo, popeza kuti Mfumu yosankhidwa ya Ufumu wa Mulungu, Yesu Kristu, ali pakati pawo pomwepo.
Mwinamwake kuli pambuyo pakuchoka kwa Afarisiwo kuti Yesu akulankhulanso ndi ophunzira ake za kudza kwa Ufumuwo. Iye makamaka akulingalira za kukhalapo kwake kwamtsogolo m’mphamvu ya Ufumu pamene akuchenjeza kuti: “Ndipo adzanena ndi inu, Tawonani ilo! Tawonani ili! musachoka kapena kuwatsata [Amesiya onama ameneŵa]; pakuti monga mphezi ing’anipa kuchokera kwina pansi pa thambo, niunikira kufikira kwina pansi pa thambo, kotero adzakhala Mwana wa munthu m’tsiku lake.” Chifukwa chake, Yesu akusonyeza kuti monga momwe mphezi imawonekerera padera lalikulu, umboni wa kukhalapo kwake m’mphamvu ya Ufumu udzakhala wowonekera bwino lomwe kwa onse ofuna kuuwona.
Pamenepo Yesu akuchititsa kufanana kwa zochitika zakale kusonyeza chimene chidzakhala mkhalidwe wa anthu mkati mwa kukhalapo kwake kwamtsogolo. Iye akufotokoza kuti: “Ndipo monga kunakhala masiku a Nowa, momwemo kudzakhalanso masiku a Mwana wa munthu . . . Monga momwenso kunakhala masiku a Loti; anadya, anamwa, anagula, anagulitsa, anabzala, anamanga nyumba; koma tsiku limene Loti anatuluka m’Sodoma udavumba moto ndi sulfure zochokera kumwamba ndipo zinawononga onsewo; momwemo kudzakhala tsiku la kuvumbuluka Mwana wa munthu.”
Yesu sakunena kuti anthu a m’tsiku la Nowa ndi m’tsiku la Loti anawonongedwa kokha chifukwa chakuti iwo analondola zochitika zozoloŵereka za kudya, kumwa, kugula, kugulitsa, kubzala, ndi kumanga. Nowa ndi Loti ndi mabanja awo anachitanso zinthu zimenezi. Komano enawo anachita ntchito zawo zatsiku ndi tsiku zotere popanda kupereka chisamaliro chirichonse kuchifuniro cha Mulungu, ndipo chinali chifukwa cha chimenechi chimene iwo anawonongedwera. Kaamba ka chifukwa chimodzimodzicho, anthu adzawonongedwa pamene Kristu avumbulutsidwa pa chisautso chachikulu chadongosolo lino la zinthu.
Pogogomezera kufunika kwa kulabadira mofulumira umboni wa kukhalapo kwake kwamtsogolo mumphamvu ya Ufumu, Yesu akuwonjezera kuti: “Tsikulo iye amene adzakhala pamwamba pa chindwi, ndi akatundu ake m’nyumba, asatsike kuwatenga; ndipo iye amene ali m’munda modzimodzi asabwere ku zake za m’mbuyo. Kumbukirani mkazi wa Loti.”
Pamene umboni wa kukhalapo kwa Kristu uwonekera, anthu sayenera kulola kukonda chuma chawo chakuthupi kuwadodometsa kuchitapo kanthu mofulumira. Mwachiwonekere potuluka mu Sodomu, mkazi wa Loti anacheukira kumbuyo akumakhumba zinthu zosiyidwa kumbuyo, ndipo iye anasanduka mwala wa mchere.
Popitirizabe mafotokozedwe ake a mkhalidwe umene ukakhalako mkati mwa kukhalapo kwake kwamtsogolo, Yesu akuuza ophunzira ake kuti: “Usiku womwewo adzakhala amuna aŵiri pakama mmodzi; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa. Padzakhala akazi aŵiri akupera pamodzi, mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa.”
Kutengedwa kumagwirizana ndi kuloŵa kwa Nowa ndi banja lake m’chingalaŵa ndi kutengedwa kwa Loti ndi banja lake kochitidwa ndi angelo kuwatulutsa mu Sodomu. Kumatanthauza chipulumutso. Kumbali ina, kusiyidwa kumatanthauza chiwonongeko.
Pamfundo ino, ophunzirawo akufunsa kuti: “Kuti, Ambuye?”
“Pamene pali mtembo, pomweponso miimba idzasonkhanidwa,” Yesu akuyankha motero. ‘Otengedwawo’ kaamba ka chipulumutso ali ofanana ndi miimba yowona patali m’chakuti iwo amasonkhana ‘pamtembowo.’ Thupilo limatanthauza Kristu wowona pakukhalapo kwake kosawoneka m’mphamvu ya Ufumu ndi phwando lauzimu limene Yehova amapereka. Luka 17:20-37; Geneses 19:26.
▪ Kodi ndimotani mmene Ufumu unaliri pakati pa Afarisi?
▪ Kodi ndim’njira yotani mmene kukhalapo kwa Kristu kuliri kofanana ndi mphezi?
▪ Kodi nchifukwa ninji anthu adzawonongedwa kaamba ka ntchito zawo mkati mwa kukhalapo kwa Kristu?
▪ Kodi kutengedwa kumatanthauzanji, ndi kusiyidwa?