Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 123
  • “Tawonani Munthuyu!”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Tawonani Munthuyu!”
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani Yofanana
  • “Taonani Munthuyu!”
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Pilato Ananena Kuti: “Taonani! Mwamuna Uja ndi Uyu!”
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Kodi Pontiyo Pilato Anali Ndani?
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Kuchokera kwa Pilato Kunka kwa Herode Nkubwereranso
    Nsanja ya Olonda​—1990
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 123

Mutu 123

“Tawonani Munthuyu!”

ATACHITA chidwi ndi kudzisungira kwa Yesu ndi kuzindikira kupanda mlandu kwake, Pilato akuyesanso njira ina ya kummasula. “Muli nawo makhalidwe,” iye akuuza makamuwo, “akuti ndimamasulira inu mmodzi pa paskha.”

Baraba, wambanda wodziŵika, wamangidwanso monga wandende, chotero Pilato akufunsa kuti: “Mufuna kuti ndikumasulileni yani? Baraba kodi, kapena Yesu, wotchedwa Kristu?”

Mosonkhezeredwa ndi akulu ansembe amene akuwasonkhezera, anthuwo akupempha kuti Baraba amasulidwe koma kuti Yesu aphedwe. Mosalepa, Pilato akuyankha, akumafunsanso kuti: “Mufuna kuti ndikumasulireni uti wa aŵiri?”

“Baraba,” iwo akufuula motero.

“Nanga ndidzachita chiyani ndi Yesu, wotchedwa Kristu?” Pilato akufunsa mothedwa nzeru.

Ndi kufuula kogonthetsa m’khutu, iwo akuyankha: ‘Apachikidwe.’ ‘Mpachikeni, Mpachikeni.’

Atadziŵa kuti akupempha kuphedwa kwa munthu wosalakwa, Pilato akuchonderera kuti: “Nanga munthuyu anachita choipa chiyani? Sindinapeza chifukwa cha kufera iye; chotero ndidzamkwapula iye ndi kummasula.”

Mosasamala kanthu za zoyesayesa zake, khamu lokwiyalo, losonkhezeredwa ndi atsogoleri awo achipembedzo, likupitirizabe kufuula kuti: ‘Apachikidwe!’ Litaloŵetsedwa m’chipolowe ndi ansembe, khamulo likufuna kukhetsa mwazi. Ndipo kuganiza kuti, ndimasiku asanu okha apitawo, pamene ena a iwo mwinamwake anali pakati pa awo amene anachingamira Yesu kuloŵa mu Yerusalemu monga Mfumu! Pakali pano, ophunzira a Yesu, ngati alipo, akukhala chete ndipo osadziŵika.

Pilato, powona kuti mapempho ake sakuphula kanthu, koma, mmalomwake mfuu ikukulakulabe, akutenga madzi nasamba manja ake pamaso pakhamulo akumati: “Ine ndilibe kuchimwira mwazi wa munthu uyu wolungama, mudziwonere nokha.” Atatero, anthuwo akuyankha kuti: “Mwazi wake uli pa ife ndi pa ana athu.”

Chotero, mogwirizana ndi zopempha zawo—ndi kufuna kukhutiritsa khamulo koposa kuchita zimene iye adziŵa kuti nzolungama—Pilato akuwamasulira Baraba. Akutenga Yesu ndipo akumvula ndiyeno akumkwapula. Uku sikunali kukwapula wamba. The Journal of the American Medical Association imafotokoza chizoloŵezi cha Aroma cha kukwapula motere:

“Chiŵiya chozoloŵereka chinali chikoti chachifupi (mkwapulo) chokhala ndi zingwe zingapo zachikopa zong’amba kapena zolukidwa za mautali osiyanasiyana, kuchimene machaka kapena zidutswa zamafupa ankhosa akuthwa anamangiriridwa kunsonga zake. . . . Pamene asilikali a Aroma anamenya mobwerezabwereza kumsana kwa mkholewo ndi mphamvu zonse, machakawo ankachititsa zilonda zakuya, ndipo zingwe zachikopazo, ndi mafupa ankhosa ankacheka khungu ndi minyewa yakhungu. Pamenepo, pamene kukwapula kunapitiriza, kuvulazako kunali kufika paminyewa yapansi zikumachititsa kunyenyeka kwa mnofu wochucha magazi.”

Pambuyo pakumenyedwa kozunza kumeneku, Yesu akutengeredwa ku pretorio ya kazembe, ndipo bungwe lonse la asilikali ankhondo likuitanidwira pamodzi. Kumeneko asilikaliwo akuwonjezera kumchitira nkhaza mwa kumpangira korona waminga ndi kukanikizira pamutu wake. Iwo akuika bango m’dzanja lake lamanja, ndipo akumveka chibakuwa, mtundu umene umavalidwa ndi mafumu. Ndiponso iwo monyodola akunena kuti: “Tikuwoneni, Mfumu ya Ayuda!” Ndiponso iwo akumlavulira malovu ndi kumuwomba makofi kumaso. Akuchotsa bango lolimbalo m’dzanja lake, akuligwiritsira ntchito kummenyera m’mutu, akumalowetsadi kwambiri m’mutu mwake minga yakuthwa ya “korona” wake womluluzira.

Kulama maganizo kwapadera ndi nyonga poyang’anizana ndi kuchitiridwa moipa kumeneko kwa Yesu kukuchititsa Pilato chidwi kwambiri kotero kuti akusonkhezeredwa kupanga kuyesayesa kwina kwakumulanditsa. “Tawonani ndidza naye kwa inu kunja kuti mudziŵe kuti sindipeza mwa iye chifukwa chirichonse,” iye akuuza makamuwo. Mwinamwake akuyerekezera kuti kuwona kwawo mkhalidwe wa kuzunzidwa kwa Yesu kudzafeŵetsa mitima yawo. Pamene Yesu akuimirira pamaso pa gulu lankhalwe la chiwawalo, atavala korona waminga ndi chibakuwa ndipo nkhope yake ikuchucha magazi ndipo yaululu, Pilato akufuula kuti: “Tawonani munthuyu!”

Ngakhale kuti wavulazidwa ndi kumenyedwa, nayu pano munthu wapadera koposa m’mbiri yonse, ndithudi munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako! Inde, Yesu akusonyeza kulama maganizo kwakukulu ndi bata zimene zimasonyeza ukulu umene ngakhale Pilato ayenera kuvomereza, pakuti mawu ake mwachiwonekere ndiwo msanganizo wa zonse ziŵiri ulemu ndi chifundo. Yohane 18:39–19:5; Mateyu 27:15-17, 20-30; Marko 15:6-19; Luka 23:18-25.

▪ Kodi ndim’njira yotani mu imene Pilato akuyesera kumasula Yesu?

▪ Kodi ndimotani mmene Pilato akuyesera kudziwonjola pathayo?

▪ Kodi nchiyani chimene chimaphatikizidwa m’kukwapulidwa?

▪ Kodi Yesu akusekedwa motani pambuyo pakukwapulidwa?

▪ Kodi ndikuyesayesa kwina kotani kumene Pilato akupanga kumasula Yesu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena