Moyo ndi Uminisitala za Yesu
“Taonani Munthuyu!”
ATACHITA chidwi ndi mkhalidwe wa Yesu ndikuzindikira kupanda liŵongo kwake, Pilato akuyesa njira ina yakuti ammasule. ‘Koma muli nawo mwambo,’ iye akuuza khamulo, ‘wakuti ndimamasulira inu mmodzi pa Paskha.’
Baraba, wambanda woipitsitsa, nayenso akusungidwa monga kaidi, chotero Pilato akufunsa kuti: ‘Mufuna kuti ndikumasulireni yani? Baraba kodi, kapena Yesu, wotchedwa Kristu?’
Atapangiridwa ndi ansembe aakulu amene awasonkhezera, anthuwo akupempha kuti Baraba amasulidwe koma kuti Yesu aphedwe. Osaleka, Pilato akuwayankha, mwakufunsanso kuti: ‘Mufuna kuti ndikumasulireni uti wa awa aŵiri?’
“Baraba,” iwo akufuula motero.
Pilato akufunsa mokhumudwa nati: ‘Nanga ndidzachita chiyani ndi Yesu, wotchedwa Kristu?’
Ndi mfuu imodzi yaphokoso, iwo akuyankha nati: ‘Apachikidwe pamtengo.’
Podziŵa kuti iwo akupempha imfa ya munthu wopanda liŵongo, Pilato akuchonderera kuti: ‘Nanga munthuyu anachita choipa chiyani? Sindinapeza chifukwa cha kufera iye; chotero ndidzamkwapula iye ndikummasula.’
Mosasamala kanthu za kuyesayesa kwake, khamu lokwiyalo, losonkhezeredwa ndi atsogoleri awo achipembedzo, lifuulabe kopambanitsa kuti: ‘Apachikidwe pamtengo.’ Litapangiridwa ndi ansembewo, khamulo likufuna mwazi. Ndipo tangolingalirani, masiku asanu okha pasadakhale, ena a iwo mothekera anali pakati pa aja omwe analandira Yesu m’Yerusalemu monga Mfumu! Nthaŵi yonseyi, ophunzira a Yesu, ngati alipo, akhala chete nadzibisa.
Pilato, powona kuti kuchonderera kwake sikukuphula kanthu koma, mmalo mwake, kungowonjezera kuphokoserako, atenga madzi ndikusamba manja ake pamaso pa khamulo, nati: ‘Ine ndiribe kuchimwira mwazi wa munthu uyu wolungama, mudziwonere nokha.’ Pakumva zimenezo anthuwo ayankha nati: ‘Mwazi wake uli pa ife ndi pa ana athu.’
Chotero, mogwirizana ndi zofuna zawo—ndiponso pofuna kukhutiritsa khamulo koposa kuchita chimene akuchidziŵa kukhala cholondola—Pilato akuwamasulira Baraba. Iye amtenga Yesu nalamula kuti avulidwe ndi kukwapulidwa. Uku sikunali kukwapula wamba. The Journal of the American Medical Association imalongosola motere ponena za kachitidwe Kachiroma ka kukwapula:
“Chipangizo chanthaŵi zonse chinali chikoti chachifupi (flagrum kapena flagellum) chokhala ndi malamba a chikopa olukanalukana a utali wosiyanasiyana, m’mene munamangiriridwa motsatizana timbulungira tating’onoting’ono tachitsulo kapena tizidutswa tosongoka tamafupa ankhosa. . . . Pamene asirikali Achiroma ankakwapula kumsana kwa mnkhole mobwerezabwereza ndi mphamvu zonse, timbulungira tachitsuloto tikapanga mikwingwirima yakuya, ndipo malamba achikopawo ndi mafupa ankhosa akavulaza khungu ndi mnofu wapamwamba. Kenaka, pamene kukwapulako kunapitiriza, zosongokazo zikapyoza mumnofu wamkati ndikusolola nyama zamkati zikukha mwazi.”
Pambuyo pa kumenyedwa kozunza kumeneku, Yesu akuperekedwa kunyumba ya kazembe, ndipo bungwe lonse la asirikali likuitanidwa pamodzi. Kumeneko asirikaliwo akuwonjezeranso nkhanza pa iye mwakuluka korona waminga ndikumveka pamutu. Aika bango m’dzanja lake lamanja, ndikumveka chibakuwa, chonga chomwe ankavala mafumu. Ndiyeno amuseka nati: ‘Tikuwoneni, Mfumu ya Ayuda!’ Ndiponso, amthira malovu ndikumpanda kumaso. Amlanda bangolo m’dzanja lake, nampanda nalo m’mutu, akukhomerezabe mowonjezereka kupyoza m’chigaza chake minga yakuthwa ya “korona” wake womchitira chamanyazi.
Ulemu wapadera wa Yesu ndi nyonga poyang’anizana ndi kuvutitsidwa konseku zikumgwira mtima Pilato kwakuti akusonkhezeredwa kuyesanso kumuwombola iye. ‘Tawonani, ndidza naye kwa inu kunja kuti mudziŵe kuti sindipeza mwa iye chifukwa chiri chonse,’ iye akuwauza motero makamuwo. Mothekera iye akulingalira kuti kuwona mkhalidwe wosautsidwa wa Yesu kudzafeŵetsa mitima yawo. Pamene Yesu akuima pamaso pa gulu lopanda chifundolo, atavala korona waminga ndi chovala chofiira ndi nkhope yake iri psu ndimwazi, ikupweteka, Pilato akufuula nati: “Taonani munthuyu!”
Chinkana kuti ngwochititsidwa mikwingwirima ndi kumenyedwa, panopa pakuima munthu wotchuka koposa m’mbiri yonse, ndithudi mwamuna wamkulu koposa yemwe sanakhalepo pano chikhalire! Inde, Yesu akusonyeza ulemu wodekha ndi bata zimene zikulankhulira ukulu wake umene ngakhale Pilato ayenera kuuvomereza, popeza kuti mawu ake mwachiwonekere ngosakanizana ndi zonse ziŵiri ulemu ndi chifundo. Yohane 18:39–19:5; Mateyu 27:15-17, 20-30; Marko 15:6-19; Luka 23:18-25.
◆ Kodi Pilato akuyesayesa kummasula Yesu mwanjira yotani?
◆ Kodi Pilato akuyesa motani kudzichotsera liŵongo?
◆ Kodi nchiyani chikuphatikizidwa m’kukwapulidwa?
◆ Kodi ndimotani mmene Yesu akunyodoledwera pambuyo pokwapulidwa?
◆ Kodi ndikuyesayesa kowonjezereka kotani kumene Pilato akukupanga kuti amasule Yesu?